Kodi Mumangowona Kawonekedwe Kakunja?
HEINZ, wa zaka zapakati pa 13 ndi 19, anapanga makonzedwe akupha atate wake opeza, chifukwa ankawada. Mosangalatsa, iye analibe kulimba mtima kwakuchita chimenecho. Zaka zingapo pambuyo pake analingalira zodzipha koma analepheranso kuchita chimenecho. Anadziloŵetsa m’kuba ndi kugulitsa anam’goneka, zimene anamangidwa nazo. Kenaka ukwati wake unalephera.
Lerolino Heinz salinso womwerekera ndi anam’goneka. Iye akukhala ndi moyo wowona mtima. Ali ndi ukwati wachimwemwe ndi unansi wabwino ndi atate wake opezawo. Kodi nchiyani chinapangitsa kusinthako? Iye anayamba kuphunzira Baibulo ndi Mboni za Yehova. Mwapang’onopang’ono, kawonedwe kake ka moyo kanayamba kusintha.
Mosakaikira, ambiri omwe anadziŵa Heinz wakale anamsuliza iye kukhala wachabe. Moyamikirika kwa anthu ambiri ofanana ndi iye, Mulungu sanamlekerere kukhala wosakhoza kuwomboledwa. Chifukwa ninji? Chifukwa chakuti: “Yehova sawona monga awona munthu; pakuti munthu ayang’ana chowoneka ndi maso, koma Yehova ayang’ana mumtima.”—1 Samueli 16:7.
Pali kusiyana kumodzi kwakukulu pakati pa munthu ndi Mulungu. Ife timaweruza kuchokera ku mawonekedwe akunja. Timafikadi pa kunena kuti “kalulu adamva mawu oyamba.” M’mawu ena, timasiyanitsa anthu kudalira pa kachitidwe kawo koyambirira. Koma Mulungu, chifukwa akhoza kudziŵa mtima, ali wolungama ndi wopanda tsankho. Ndipo ndicho chifukwa chake anatuma Mwana wake, Yesu Kristu, ku dziko lapansi kotero kuti “anthu a mitundu yonse ayenera kupulumutsidwa ndi kufika pa chidziŵitso cholongosoka cha chowonadi.” (1 Timoteo 2:4, NW) M’chigwirizano ndi chimenechi, Akristu odzipereka ali ndi mwaŵi wa kukhala “antchito anzake a Mulungu” mwa kulalikira mokangalika mbiri yabwino ya Ufumu wa Mulungu kwa mtundu wonse wa anthu. (1 Akorinto 3:9) Komabe, Akristu ali ndi polekezera—iwo sangadziŵe mitima ya anthu. Chotero iwo ayenera kukhala opanda tsankho ndi kupeŵa kukhala oweruza mwa mawonekedwe akunja.
Yakobo mbale wopeza wa Yesu anadziŵa za upandu umenewu mu mpingo wa Akristu oyambirira. Iye ananena kuti: “Abale anga, pokhala okhulupirira mwa Ambuye wathu Yesu Kristu, yemwe akulamulira mu ulemerero, simuyenera konse kukhala onyada. Mwachitsanzo, alendo aŵiri angaloŵe m’malo anu olambirira, mmodzi wovala bwino kwambiri ndi mphete za golidi, ndipo mwamuna wina wosaukayo wovala nsanza. Bwanji ngati mupereka chisamaliro chapadera kwa mwamuna wovala bwinoyo . . . Kodi simuŵona kuti mukuchita mosiyana ndipo mukuweruza ndi miyezo yonyenga?” Pa maziko ameneŵa, kodi ife nthaŵi zina timaweruza molakwa anthu omwe amabwera ku Nyumba Yaufumu kwa nthaŵi yoyamba?—Yakobo 2:1-4, The New English Bible.
Yesu Anakhazikitsa Chitsanzo
Yesu anaŵona anthu, osati monga ochimwa osakhoza kuwomboledwa, koma monga anthu othekera kukhala owona mtima ofunitsitsa kusintha atapatsidwa thandizo lofunika ndi chisamaliro choyenera. Ndicho chifukwa chake “anadzipereka yekha chiwombolo m’malo mwa onse.” (1 Timoteo 2:6) M’ntchito yake yolalikira, sanawone aliyense wa mtima wabwino kukhala wosakhoza kukopeka, wosayenerera chisamaliro. Kawonedwe kake ka anthu sikanavumbule malingaliro onyada alionse a kudzilungamitsa.—Luka 5:12, 13.
Anali wosiyana chotani nanga ndi Afarisi, omwe timaŵerenga kuti: “Ndipo alembi a kwa Afarisi, pakuwona kuti alinkudya nawo ochimwa ndi amisonkho, ananena ndi ophunzira ake, Uyu akudya ndi kumwa nawo amisonkho ndi ochimwa. Ndipo pamene Yesu anamva ichi, ananena nawo, Akulimba safuna sing’anga koma odwala ndiwo; sindinadza kudzaitana olungama, koma ochimwa.”—Marko 2:16, 17.
Ndithudi, izizo sizimatanthauza kuti Yesu analola machitachita osawona mtima ndi olakwa ochitidwa ndi ochimwa ameneŵa ndi osonkhetsa misonkho. Koma iye anadziŵa kuti anthu angagwidwe m’njira yoipa ya moyo, mwinamwake mosafunadi kapena chifukwa cha mikhalidwe yovuta kuilamulira. Chotero iye anasonyeza kumvetsetsa, “nagwidwa chifundo ndi iwo, chifukwa anali ngati nkhosa zopanda mbusa.” (Marko 6:34) Mwachikondi anapanga kusiyana pakati pa machitidwe awo oipa ndi mitima yawo yothekera kukhala yabwino.
Pochita ndi atsatiri ake, Yesu anayang’ananso mopyola pa mawonekedwe akunja. Iwo anali ochimwa omwe kaŵirikaŵiri anapanga zophophonya, koma Yesu sanali wangwiro wosalingalira, nthaŵi zonse kuwaimba mlandu pa cholakwa chochepera chirichonse. Iye anadziŵa kuti zolinga zawo zinali zabwino kapena, monga mmene tinganenere lerolino, kuti mtima wawo unali m’malo abwino. Zomwe anafunikira ndizo thandizo ndi chilimbikitso; popereka zimenezi, Yesu sanali konse waliuma. Kunenadi zowona, iye anawona anthu m’njira imene Mulungu amaŵawonera. Kodi timayesera kutsanzira chitsanzo chake chozizwitsa?
Kodi ‘Mumaweruza ndi Chiweruzo Cholungama’?
Nthaŵi ina Yesu anayang’anizana ndi gulu la odandaula odzilungamitsa amene anakwiyitsidwa naye pokhala anachiritsa pa Sabata. Iye anaŵalangiza kuti: “Musaweruze monga mawonekedwe, koma weruzani chiweruziro cholungama.” Kodi nchifukwa ninji iwo sanasangalale powona Yesu kukhala wochita ntchito zozizwitsa yemwe ‘anachiritsadi munthu’ m’malo ‘mokwiya mwachiwawa’ ndi kumuwona iye kukhala woswa lamulo la Sabata? Mwa kuweruza kuchokera ku mawonekedwe akunja, iwo anasonyeza malingaliro awo oipa. Iwo anavumbula chiweruzo chawo kukhala chodzilungamitsa ndiponso chosalungama.—Yohane 7:23, 24.
Kodi ndimotani mmene nafenso tingapangire kuphophonya kumodzimodziko? Mwa kulephera kusangalala pamene munthu wolapa abwerera ku mpingo kapena pamene munthu wakudziko kwambiri aphunzira chowonadi ndi kuyamba kupindula ndi chiritso lauzimu. Nthaŵi zina tingaweruze anthu mwa kavalidwe kawo kosayenera kapena kapesedwe ndi kuŵasuliza kukhala osathekera konse kukhala Mboni. Komabe, ambiri omwe kale anali opulupudza ndi ena amakhalidwe amoyo wosayenera m’kupita kwa nthaŵi akhala Mboni Zachikristu za Yehova. Pamene kuli kwakuti oterowo akupanga masinthidwe, sitimafuna kulola ‘kuweruza monga mawonekedwe’ kutichititsa khungu ku mkhalidwe wawo wabwino wa mtima.
Kodi nkwabwinopo chotani nanga, ndi kogwirizana ndi chitsanzo chabwino cha Yesu, kuŵapempherera ndi kuŵapatsa thandizo logwira ntchito kuti afike pa uchikulire Wachikristu! Kupeza chisangalalo mwa iwo kungawoneke kukhala kovuta. Koma ngati Yehova amawakokera iwo kwa iyemwini kupyolera mwa Kristu, kodi ndife yani kuti tiŵakane iwo pa maziko a muyezo wathu wa kawonedwe kochepera? (Yohane 6:44) Kuweruza wina modzilungamitsa, pamene sitidziŵa mtima ngakhale mikhalidwe, kungatiike pa chiweruzo choipa.—Yerekezani ndi Mateyu 7:1-5.
M’malo mwa kuweruza moipa achatsopano oterowo, tiyenera kuŵathandiza, kuŵalimbikitsa, ndi kuŵalangiza mwa kupereka chitsanzo. Komabe, pamene kuli kwakuti tikukhala okoma mtima, sitiyenera konse kukweza achatsopano omwe mwinamwake ali otchuka m’dziko. Kutero kungakhale mtundu wa tsankho. Kukakhalanso chizindikiritso cha kusafikapo kwathu. Ponena za munthu mwiniyo, kodi kumkhumbira kwathu kukamthandiza iye kukhala wodzichepetsa? Kapena kodi iko, m’malomwake, kukamchititsa manyazi?—Levitiko 19:15.
Musayembekezere Zoposa Zimene Mulungu Akutero
Kawonedwe kathu ka ena kali kopereŵera kwambiri poyerekeza ndi ka Yehova, yemwe amadziŵa mtima. (1 Mbiri 28:9) Kuzindikira zimenezi kudzatichinjiriza kukhala Afarisi amakono odzilungamitsa, tikumayesa kuwumba anthu m’chikombole cha chilungamo cha munthu kotero kuti iwo ayenerere lingaliro lathu la chimene chiri cholondola. Ngati tiyesa kuwona anthu monga mmene Mulungu amaŵawonera, sitidzafuna kuchokera kwa iwo zoposa zimene iye amafuna. “[Sitidza]pitirira zimene zilembedwa.” (1 Akorinto 4:6) Izi ziri zofunikira koposa makamaka kwa akulu Achikristu kuzisamalitsa.—1 Petro 5:2, 3.
Tingachitire fanizo zimenezi m’nkhani ya kavalidwe. Chiyeneretso cha Baibulo—chiyeneretso cha Mulungu—chiri chakuti kavalidwe ka Mkristu kayenera kukhala kaukhondo ndi kaudongo, kolinganizidwa bwino lomwe ndipo kosasonyeza kusoŵeka kwa “manyazi, ndi chidziletso.” (1 Timoteo 2:9; 3:2) Pamenepa, ndithudi, akulu mu mpingo wina ‘anapitirira pa zolembedwa’ zaka zoŵerengeka kalelo mwa kufuna kuti wopereka nkhani ya Baibulo aliyense mu mpingo wawo avale shati yoyera, ngakhale kuti mitundu ina inali yololedwa m’dzikolo. Alankhuli achilendo omwe anabwera ndi shati ya mtundu wina anapemphedwa kusintha ndi kuvala mashati oyera omwe anasungidwa m’Nyumba Yaufumu kaamba ka zamwadzidzidzi zoterozo. Tiyenera kukhala osamala chotani nanga kuti tisapereke zokonda zathu zaumwini pa ena! Ndipo uphungu wa Paulo uli woyenera chotani nanga: “Kufatsa kwanu kuzindikirike kwa anthu onse”!—Afilipi 4:5.
Zotulukapo Zabwino Za Kuyang’ana Kopyola Mawonekedwe Akunja
Kuzindikira kuti sitingadziŵe mitima ya anthu kudzatithandiza kusungabe unansi wabwinopo ndi awo otizinga, ponse paŵiri mkati ndi kunja kwa mpingo Wachikristu. Kudzatithandiza kukhala ndi maganizo abwino ponena za ena, mosakaikira malingaliro awo, “pakuti kale ifenso tinali opusa, osamvera, onyengeka, akuchitira ukapolo zilakolako ndi zokondweretsa za mitundumitundu.” (Tito 3:3) Pozindikira zimenezi, tidzakhala ofunitsitsa kulalikira kwa aliyense, ngakhale kwa amene m’mawonekedwe akunja, angawoneke kukhala osafunikira. Ndiiko komwe, chosankha cha kulandira kapena kukana chowonadi nchawo. Thayo la kuchilalikira kwa aliyense nlathu.
Mboni za Yehova zambiri, mofanana ndi Heinz, ziri zachimwemwe kuti zinalandiridwa mu mpingo Wachikristu ndi abale ndi alongo omwe anayang’ana kupyola pa mawonekedwe akunja ndipo sanaweruze pa mawonekedwe oyambirira.
Tatengani Frank, yemwe anawonekera Sande lina pa Nyumba Yaufumu ya Mboni za Yehova kum’mwera kwa Jeremani. Kodi nchiyani chimene osonkhanawo anawona? Mwamuna wachichepere wosawoneka bwino wokhala ndi ndevu ndi tsitsi lofika m’mapewa, wovala zovala zalitsiro, wodziŵika mofala kukhala chigona m’bawa wa kumaloko ndi wosuta mopambanitsa—munthu yemwe ananyalanyaza tsamwali lake ndi makanda awo amapasa. Mosasamala kanthu za izo, iye analandiridwa ndi manja aŵiri pa msonkhanowo. Anakondweretsedwa kwambiri kwakuti mlungu umodzi pambuyo pake anabwereranso. Kodi nchiyani chimene iwo anawona tsopano? Mwamuna wachichepere wopesa mwaudongo wovala zovala zoyera. Mlungu wachitatu iwo anawona mwamuna wachichepere yemwe sanasutenso, pa nthaŵi ino atatsagana ndi tsamwali lake ndi ana awo aŵiri. Sande lachinayi, iwo anawona mwamuna wachichepere ndi mkazi wachichepere omwe anali atangotenga kumene ntchatho wozindikiritsa mwalamulo unansi wawo. Pa Sande lachisanu, iwo anawona mwamuna wachichepere yemwe anali atadula mayanjano onse ndi chipembedzo chonyenga. Lerolino, zaka zinayi pambuyo pake, iwo akuwona, monga mmene mmodzi wa Mboni za Yehova akusimbira, “banja limene limakondweretsa kwambiri lomwe mungalingalire kuti lakhala abale athu kwa zaka zambiri.”
Kuona maso a nkhono nkufatsa. Mofananamo, ubwino weniweni wa munthu sumawunikiridwadi m’mawonekedwe akunja. Akristu omwe amayesa kuwona anthu monga mmene Mulungu amachitira sadzaweruza pa mawonekedwe oyambirira. Mulungu amapereka chisamaliro ku “munthu wobisika wa mtima,” ndipo tiyenera kukhala oyamikira kaamba ka chimenecho.—1 Petro 3:3, 4.