Kodi Mumaona Maonekedwe Akunja Okha?
1 Pamene tikuchita utumiki wathu wapoyera, malingaliro athu oyamba pa anthu ena angatipangitse kusagaŵana nawo uthenga wabwino. Mwachitsanzo, kodi mungatani ngati munthu wina wooneka woopsa nthaŵi zonse amakuyang’anani mokuzondani pamene mwapita kunyumba ya mnzake woyandikana naye yemwe anasonyeza chidwi m’choonadi? Mpainiya wamkazi amene zinamuchitikira zimenezi anaganiza zom’fikira mwamunayo ndi kulankhula naye. Iye anamupatsa moni mlongoyu mwamwano. Koma modabwitsa, anamvetsera uthenga wa Baibulo ndipo mosangalala anavomera kuphunzira. Chifukwa chakuti mlongoyu sanaweruze mwa maonekedwe akunja, njira ya mwamuna ameneyu ndi mkazi wake inatseguka kuti aphunzire choonadi.
2 Mlongo wina poyamba anachita mantha ndi maonekedwe a mnyamata wina watsitsi lalitali. Koma analimbikira kumulalikira mwachidule nthaŵi iliyonse pamene iye anafika m’sitolo limene mlongoyu anali kugwira ntchito. Khama lake linali ndi zotsatirapo zabwino, ndipo tsopano mnyamata ameneyu ndi Mboni yobatizidwa. Kodi n’chiyani chidzatiletsa kufulumira kunena kuti anthu ameneŵa sangamvetsere?
3 Kutsatira Chitsanzo cha Yesu: Yesu anadziŵa kuti akapereka moyo wake kaamba ka aliyense. Choncho, sanaleke kuchitapo kanthu chifukwa cha maonekedwe akunja a ena. Anadziŵa kuti ngakhale anthu amene ali ndi mbiri yoipa angakhale ofunitsitsa kusintha ngati apatsidwa thandizo ndi chilimbikitso choyenera. (Mat. 9:9-13) Anayesa kuthandiza olemera ndi osauka mofanana. (Mat. 11:5; Marko 10:17-22) Tisaweruze anthu amene timakumana nawo mu utumiki mwa maonekedwe awo akunja, kenako n’kulephera kuona mtima wabwino umene angakhale nawo. (Mat. 7:1; Yoh. 7:24) N’chiyani chingatithandize kutsatira chitsanzo chapadera cha Yesu?
4 Mwa kuphunzira kwathu Baibulo, tazindikira kuti Mawu a Mulungu ali ndi mphamvu yosintha maganizo, khalidwe, ndi umunthu wa munthu. (Aef. 4:22-24; Aheb. 4:12) Chotero, tiyenera kumawaganizira bwino anthu ndi kusiya zonse m’manja mwa Yehova, amene amaona mitima ya anthu.—1 Sam. 16:7; Mac. 10:34, 35.
5 Kugaŵana kwathu uthenga wabwino mosasankha ndi anthu amitundu yonse, mosasamala kanthu za maonekedwe awo akunja, kuthandize ntchito yaikulu yotuta m’masiku otsiriza ano.—1 Tim. 2:3, 4.