Aamoni—Anthu Amene Anabwezera Udani pa Kukoma Mtima
MZINDA wamakono wotchedwa Amman, likulu la ufumu wa Chihashemiti wa Jordan, umakumbutsa munthu za anthu amene azimiririka padziko lapansi. Iwo anali kutchedwa kuti Aamoni. Kodi iwo anali ayani, ndipo kodi ndi maphunziro otani amene tingapeze pa kuwonongeka kwawo?
Aamoni anali mbadwa za munthu wolungama Loti. (Genesis 19:35-38) Popeza kuti Loti anali mwana wa mphwake wa Abrahamu, munganene kuti Aamoni anali abale awo a Aisrayeli. Komabe, mbadwa za Lotizo zinayamba kulambira milungu yonama. Chikhalirechobe, Yehova Mulungu anawakondabe. Pamene mtundu wa Israyeli unayandikira Dziko Lolonjezedwa, Mulungu anawachenjeza kuti: “Usawavuta [Aamoni], kapena kuutsana nawo; popeza sindidzakupatsako dziko la ana a Amoni likhale lakolako; popeza ndinapatsa ana a Loti ili likhale lawolawo.”—Deuteronomo 2:19.
Kodi Aamoni anayamikira kukoma mtima kumeneko? Ayi, iwo anakana kuvomereza kuti Yehova anawapatsa kanthu kena. Anabwezera kukoma mtima kwa Mulungu ndi udani wosatha pa anthu a Mulungu, Aisrayeli. Ngakhale kuti Aisrayeli analemekeza lamulo la Yehova ndi kusawaukira, Aamoni ndi abale awo Achimoabu anaganiza kuti anali pangozi. Zoona, Aamoni sanachite nkhondo, koma iwowo anapempha mneneri wina wotchedwa Balamu kuti atemberere Israyeli!—Numeri 22:1-6; Deuteronomo 23:3-6.
Ndiyeno panachitika kanthu kena kachilendo. Baibulo limasimba kuti Balamu sanathe kunena temberero lake. Anangowadalitsa, akumati: “Wodalitsika aliyense wakudalitsa iwe, wotemberereka aliyense wakutemberera iwe.” (Numeri 24:9) Awo amene anakhudzidwa, kuphatikizapo Aamoni, akanafunikira kutengapo phunziro lamphamvu pa zimenezi: Pamene anthu a Mulungu anaukiridwa, iyeyo anali wokonzekera kuloŵererapo kuwathandiza!
Komabe, Aamoni anapitiriza kufunafuna njira zolimbanirana ndi Israyeli. Mkati mwa nyengo ya Oweruza, Amoni anagwirizana ndi Moabu ndi Amaleki nalanda Dziko Lolonjezedwa, kufikira ku Yeriko. Komabe, chipambanocho chinali chakanthaŵi, popeza kuti Woweruza Wachiisrayeli Ehudi anathamangitsa olanda dzikowo. (Oweruza 3:12-15, 27-30) Pangano la mtendere losalimba linakhalako kufikira m’masiku a Woweruza Yefita. Panthaŵiyo mtundu wa Israyeli unali utaloŵa m’kulambira mafano, chotero Yehova anachotsa chitetezo chake. Motero kwa zaka 18, Mulungu “[a]nawagulitsa . . . m’dzanja la ana a Amoni.” (Oweruza 10:6-9) Kachiŵirinso Aamoni anagonjetsedwa mowopsa pamene Aisrayeli analeka kulambira mafano nachirikiza utsogoleri wa Yefita.—Oweruza 10:16–11:33.
Nyengo ya Israyeli ya kulamulira kwa oweruza inatha ndi kuikidwa kwa mfumu yake yoyamba, Sauli. Posakhalitsa pamene Sauli anayamba kulamulira, Aamoni anayambitsanso udani. Mfumu Nahasi anakwerera mzinda wa Israyeli wa Yabezi Gileadi. Pamene anthu a mzindawo anapempha pangano la mtendere, Nahasi Mwamoni anapereka pempho lomkitsa ili lakuti: “Ndidzapangana nanu, ngati mulola kuti maso akudzanja lamanja anu onse akolowoledwe.” Wolemba mbiri Flavius Josephus amanena kuti anachita zimenezi kumbali ina monga njira yodzitetezera, kotero kuti “pamene maso awo akumanzere ataphimbidwa ndi zikopa zawo, akhale osatha kuchita kanthu mu nkhondo.” Komabe, chifuno chachikulu cha pempho lankhanza limeneli chinali cha kunyazitsa Aisrayeli ameneŵa.—1 Samueli 11:1, 2.
Aamoni kachiŵirinso anabwezera udani pa kukoma mtima kwa Yehova. Yehova sananyalanyaze chiwopsezo chankhanza chimenechi. “Mzimu wa Mulungu unamgwera Sauli mwamphamvu, pamene anamva mawu awa [a Nahasi], ndi mkwiyo wake unayaka kwambiri.” Motsogoleredwa ndi mzimu wa Mulungu, Sauli anasonkhanitsa amuna ankhondo 330,000 amene anakanthiratu Aamoni kwakuti “osatsala pamodzi ngakhale aŵiri.”—1 Samueli 11:6, 11.
Zochita zadyera za Aamoni ndi zolinga zawo, nkhanza yawo, ndi umbombo wawo potsirizira pake zinachititsa kuwonongedwa kwawo kotheratu. Monga momwe mneneri wa Yehova Zefaniya analoserera, anakhala “ngati Gomora, . . . bwinja losatha; . . . chifukwa anatonza, nadzikuza pa anthu a Yehova wa makamu.”—Zefaniya 2:9, 10.
Atsogoleri adziko lerolino ayenera kudziŵa zimene zinachitikira Amoni. Mofananamo Mulungu wasonyeza kukoma mtima kwake pa mitundu poilola kukhala ndi moyo pa chopondapo mapazi ake, dziko lapansi. Koma m’malo mwa kusamalira dziko lapansi, mitundu yadyerayo ikuliwononga, ngakhale kuika pulanetili pangozi ya kuwonongedwa ndi zida za nyukiliya. M’malo mwa kusonyeza kukoma mtima kwa olambira Yehova apadziko lapansi, kaŵirikaŵiri mitundu imasonyeza udani, ikumawazunza mwankhanza. Chotero phunziro lopezedwa pa Aamoni nlakuti Yehova samapeputsa kubwezera udani pa kukoma mtima kwake. Ndipo panthaŵi yake adzachitapo kanthu, monga momwe anachitira nthaŵi zakale.—Yerekezerani ndi Salmo 2:6-12.
[Chithunzi patsamba 9]
Mabwinja a Roma ku Amman, dera la Raba, likulu la Aamoni
[Mawu a Chithunzi]
Pictorial Archive (Near Eastern History) Est.
[Chithunzi patsamba 10]
Aamoni anakhala m’dera ili
[Mawu a Chithunzi]
Pictorial Archive (Near Eastern History) Est.
[Mawu a Chithunzi patsamba 8]
Pictorial Archive (Near Eastern History) Est.