Malangizo a Mulungu Othandiza Posankha Wokwatirana Naye
“Ine ndidzakulangiza ndi kuphunzitsa iwe za njira ukayendayo; ndidzakupangira ndi diso langa lakuyang’ana iwe.”—SALMO 32:8.
1. Kodi n’zinthu ziti zofunika kuti ukwati ukhale wabwino?
OIMBA ng’oma ayamba kuimba ng’oma zawo. Woimba akuvomereza ndi mawu anthetemya mogwirizana ndi ng’omazo. Ndipo nyimbo yomwe ikumveka pamenepo n’njotenga mtima kwabasi. Amuna aŵiri akutsitsa makatoni olemera kuchokera m’lole yaikulu. Mmodzi akuponyera mnzake katoni, ndipo mnzakeyo akuŵakha mosavuta, akuiika pansi mwamsanga ndi kuyembekezera ina. Zomwe anthu onseŵa akuchita zikuoneka ngati n’zosavuta. Komabe, kodi ndani angakwanitse kuchita zimenezo ngati sanaphunzire mmene angachitire, ngati alibe mnzake wodalirika, komanso ngati sanalandire malangizo oyenerera. Umu ndi mmenenso ukwati wabwino umakhalira. Nawonso umadalira kukhala ndi mnzako wodalirika, kuchita zinthu mogwirizana, ndiponso makamaka malangizo anzeru. Ndithudi, malangizo oyenerera ndi ofunika kwambiri.
2. (a) Kodi anakhazikitsa ukwati ndani, ndipo n’cholinga chotani? (b) Kodi maukwati ena amawalinganiza motani?
2 N’chibadwa kuti mnyamata wosakwatira kapena mtsikana wosakwatiŵa azilingalira za yemwe adzakwatirana naye—mnzake wa moyo wake wonse. Kuchokera pamene Yehova Mulungu anayambitsa ukwati, sizachilendo kuona mwamuna ndi mkazi akukwatirana. Koma mwamuna woyamba, Adamu, sanachite kusankha yekha mkazi. Mwachikondi Yehova anapatsa Adamu mkazi. (Genesis 2:18-24) Iye anafuna kuti banja loyambali likule kuti pambuyo pake anthu adzaze dziko lapansi. Banja loyambali atalikhazikitsa, kaŵirikaŵiri oyendetsa zonse za ukwati anali makolo a mkwati ndi mkwatibwi, nthaŵi zina amamva kaye malingaliro a aŵiriwo. (Genesis 21:21; 24:2-4, 58; 38:6; Yoswa 15:16, 17) Kuchita kum’funira munthu mwamuna kapena mkazi n’kofalabe m’mayiko ndi m’madera ena. Komabe, ambiri lerolino amasankha okha mnzawo woti adzakwatirane naye.
3. Kodi tingasankhe bwanji wokwatirana naye?
3 Kodi munthu angasankhe motani wokwatirana naye? Ena amakopeka ndi maonekedwe, amasankha yemwe wadolola mtima wawo ndiponso wosiririka m’maonekedwe. Ena amafuna wachuma, munthu amene adzathe kuwasamalira bwino ndi kuwapezera zofuna zawo. Koma kodi chilichonse mwa zimenezi pachokha chingathandize kupanga ubwenzi wosangalatsa ndi wokhutiritsa? Miyambo 31:30 amati: “Kukongola kungonyenga, maonekedwe okoma ndi chabe; koma mkazi woopa Yehova adzatamandidwa.” Lemba limeneli lili ndi mfundo yofunika kwambiri: Lingalirani za Yehova pamene mukusankha wokwatirana naye.
Malangizo Achikondi Kuchokera kwa Mulungu
4. Kodi Mulungu wapereka thandizo lotani pankhani yosankha wokwatirana naye?
4 Atate wathu wakumwamba wachikondi, Yehova, wapereka Mawu ake olembedwa kuti atitsogolere pankhani iliyonse. Iye anati: “Ine ndine Yehova, Mulungu wako, amene ndikuphunzitsa kupindula, amene ndikutsogolera m’njira yoyenera iwe kupitamo.” (Yesaya 48:17) Chotero, si zodabwitsa kuti m’Baibulo muli malangizo othandiza panthaŵi yosankha mkazi kapena mwamuna. Yehova amafuna kuti maukwati athu azikhala olimba ndi achimwemwe. Pachifukwa chimenecho, watipatsa thandizo kuti timvetse ndi kugwiritsa ntchito malangizo ameneŵa. Kodi zimenezo si zomwe tingayembekezere Mlengi wachikondi kuchita?—Salmo 19:8.
5. Kodi chofunika n’chiyani kuti muukwati mukhale chimwemwe nthaŵi zonse?
5 Pokhazikitsa dongosolo laukwati, Yehova anafuna kuti usamathe. (Marko 10:6-12; 1 Akorinto 7:10, 11) N’chifukwa chake ‘amadana nako kulekana,’ koma amakuvomereza pokhapokha ngati wina wachita “chigololo.” (Malaki 2:13-16; Mateyu 19:9) Choncho, kusankha munthu wodzakwatirana naye ndi chimodzi mwa zosankha zazikulu zomwe tingapange ndipo sitiyenera kuiona ngati nkhani yamaseŵera. Pali zosankha zoŵerengeka chabe zomwe zingadzetse chimwemwe kapena chisoni. Kusankha mwanzeru kungakhutiritse ndi kukondweretsa mtima wamunthu, koma kusankha mosalingalira bwino kungadzetse mavuto osatha. (Miyambo 21:19; 26:21) Kuti chimwemwe chanu chipitirizebe, ndi bwino kusankha mwanzeru ndi kukhala wofunitsitsa kupanga pangano losatha, chifukwa chakuti Mulungu anakhazikitsa ukwati monga mgwirizano womakula muumodzi ndi kumverana.—Mateyu 19:6.
6. N’chifukwa chiyani anyamata ndi atsikana afunikira kusamala kwambiri posankha wokwatirana naye, nanga kodi angasankhe bwanji mwanzeru?
6 Makamaka anyamata ndi atsikana, afunika kusamala kwambiri kuti asasokonezeke maganizo chifukwa cha maonekedwe okongola ndiponso kuti zilakolako zamphamvu zisawalepheretse kulingalira mwanzeru posankha bwenzi. Ndithudi, okondana chifukwa chotengeka ndi zinthu zokhazi basi, chikondi chawocho chimazirala mofulumira mwina kuyamba kudana kumene. (2 Samueli 13:15) Mosiyana ndi zimenezo, tingakulitse chikondi chosatha mwa kum’dziŵa bwino mnzathuyo komanso kudziŵa bwino umunthu wathu. Tizindikirenso kuti chomwe chili chabwino kwa ife sichingakhale chomwe mtima wathu unkachifuna poyamba. (Yeremiya 17:9) N’chifukwa chaketu malangizo a Mulungu opezeka m’Baibulo ali ofunika kwambiri. Amatithandiza kuzindikira mmene tingasankhire mwanzeru zomwe tifunikira kuchita m’moyo. Wamasalmo anaimira Yehova ponena kuti: “Ine ndidzakulangiza ndi kuphunzitsa iwe za njira ukayendayo. Ndidzakupangira ndi diso langa lakuyang’ana iwe.” (Salmo 32:8; Ahebri 4:12) N’zoona kuti ukwati ungakhutiritse chibadwa chathu chofuna kukondedwa komanso kukhala ndi bwenzi. Komabe, umadzetsa mavuto omwe tingawathetse ngati ndife okhwima m’nzeru ndi ozindikira.
7. Kodi n’chifukwa chiyani ena samvera malangizo ochokera m’Baibulo okhudza kusankha wokwatirana naye, koma kodi kusamvera kumeneku kungadzetse chiyani?
7 N’kwanzeru kumvera zomwe Woyambitsa ukwati akunena pankhani yosankha wokwatirana naye. Komabe, nthaŵi zina tingadye mfulumira mwa kukana uphungu wa m’Baibulo wochokera kwa makolo kapena kwa akulu achikristu. Tingalingalire kuti sakutimvetsa mokwanira, ndipo mwamakani tingaumirire kuchita zomwe mtima wathu wafuna. Koma m’kupita kwanthaŵi, titayamba kukumana ndi mavuto m’moyo, tinganong’oneze bondo kuti sitinamvere malangizo anzeru omwe akanatithandiza. (Miyambo 23:19; 28:26) Banja lathu lingakhale lopanda chikondi, tingalephere kusamalira ana, mwinanso kukwatirana ndi wosakhulupirira. Zingakhaletu zomvetsa chisoni ngati ukwati womwe unayenera kutidzetsera chimwemwe chochuluka utakhala gwero la mavuto osaneneka!
Kudzipereka Kwaumulungu N’kofunika Kwambiri
8. Kodi kudzipereka kwaumulungu kumathandiza motani kuti ukwati ukhale wolimba ndi wopatsa chimwemwe?
8 Kunena zoona, kukondana kumathandiza kulimbitsa ukwati. Koma kukhala ndi zikhulupiriro zofanana n’kofunika kwambiri kuti ukwati ukhale wolimba ndi wopatsa chimwemwe. Ngati nonse ndinu odzipereka kwa Yehova Mulungu zimathandiza kuti ukwati wanu ukhale wolimba ndiponso zimalimbikitsa mgwirizano mwapadera kwambiri kuposa china chilichonse. (Mlaliki 4:12) Ngati mwamuna ndi mkazi omwe ndi Akristu ali osasunthika pa kulambira Yehova moona m’moyo wawo, ndiye kuti ndi ogwirizana mwauzimu, mwamaganizo, ndi mwamakhalidwe. Amaphunzira limodzi Mawu a Mulungu. Amapempherera limodzi, ndipo zimenezi zimagwirizanitsa mitima yawo. Amapitira limodzi ku misonkhano yachikristu ndipo amagwirira limodzi ntchito muutumiki wakumunda. Zonsezi zimathandiza kupanga chomangira chauzimu chomwe chimawapangitsa kuyandikana wina ndi mzake. Ubwino winanso woposa ngwakuti zimadzetsa madalitso a Yehova.
9. Kodi Abrahamu anachitanji pofuna kupezera Isake mkazi, nanga zotsatira zake zinali zotani?
9 Chifukwa cha kudzipereka kwake kwaumulungu, kholo lakalelo Abrahamu anafunitsitsa kukondweretsa Mulungu nthaŵi itakwana yoti asankhe mkazi wamwana wake Isake. Abrahamu anauza mnyamata yemwe anali kumukhulupirira m’banjamo kuti: “Ndidzakulumbiritsa iwe pa Yehova, Mulungu wa kumwamba, ndi Mulungu wa dziko lapansi, kuti usadzam’tengere mwana wanga mkazi wa kwa ana aakazi a Akananiwo, amene ndikhala pakati pawo. Koma udzamke ku dziko langa, kwa abale anga, ndi kumtengera mwana wanga Isake mkazi. . . . [Yehova] adzatumiza mthenga wake akutsogolere, ndipo udzam’tengere mwana wanga mkazi kumeneko.” Rebeka anali mkazi wokongola, amene Isake anam’konda kwambiri.—Genesis 24:3, 4, 7, 14-21, 67.
10. Kodi ndi maudindo ati a m’Malemba omwe apatsidwa kwa amuna ndi akazi apabanja?
10 Ngati ndife Akristu osakwatira kapena kukwatiŵa, kudzipereka kwaumulungu kudzatithandiza kukulitsa mikhalidwe yomwe idzatithandiza kukwaniritsa ziyeneretso za m’Malemba zokhudza ukwati. Ena mwa maudindo a amuna komanso akazi omwe mtumwi Paulo anatchula ndi aŵa: “Akazi inu, mverani amuna anu a inu eni, monga kumvera Ambuye. . . . Amuna inu, kondani akazi anu, monganso Kristu anakonda Eklesia, nadzipereka yekha m’malo mwake . . . amuna azikonda akazi awo a iwo okha monga ngati matupi a iwo okha. . . .Yense payekha, yense akonde mkazi wake wa iye yekha, monga adzikonda yekha; ndipo mkaziyo akumbukire kuti aziopa mwamuna.” (Aefeso 5:22-33) Monga momwe tikuonera, mawu ouziridwa a Pauloŵa akutsindika kufunika kwa chikondi ndi ulemu. Kuchita mogwirizana ndi malangizo ameneŵa kumaphatikizapo kuopa Yehova. Kumafuna kudzipereka ndi mtima wonse m’nthaŵi ya mtendere ndi yamavuto yomwe. Akristu omwe akulingalira zoloŵa muukwati ayenera kukhala okhoza kukwaniritsa udindo umenewu.
Kusankha Nthaŵi Yokwatiwa
11. (a) Kodi ndi malangizo otani okhudza nthaŵi yokwatira kapena kukwatiwa omwe akupezeka m’Malemba? (b) Kodi ndi chitsanzo chiti chomwe chikusonyeza nzeru zotsatira uphungu wa m’Baibulo wolembedwa pa 1 Akorinto 7:36?
11 Kudziŵa ngati tili okonzeka kukwatira kapena kukwatiwa n’kofunika kwambiri. Popeza nthaŵi yomwe munthu angakhale wokonzeka kukwatira kapena kukwatiwa imasiyanasiyana, Malemba satchula zaka. Komabe, amasonyeza kuti ndi bwino kudikira kufikira ‘titapitirira pa unamwali,’ pamene zilakolako zamphamvu za kugonana zingathe kutilepheretsa kulingalira mwanzeru. (1 Akorinto 7:36) Michelle anati: “Ndinkati ndikaona anzanga, ambiri a iwo osakwana zaka makumi aŵiri, ali ndi zibwenzi kenako n’kukwatiŵa, nthaŵi zina zinali zovuta kwambiri kutsatira malangizo ameneŵa. Koma ndinazindikira kuti malangizowo ngochokera kwa Yehova, ndi kuti amatiuza zokhazo zomwe tingapindule nazo. Pamene ndinali kuyembekezera kukwatiŵa, ndinali wokhoza kulingalira mozama za ubwenzi wanga ndi Yehova ndi kuzoloŵerana ndi zinthu zina m’moyo, zomwe mwachionekere munthu wa zaka zosakwana makumi aŵiri sangazidziŵe. Patadutsa zaka zingapo, ndinali wokonzeka bwino lomwe kukwaniritsa maudindo komanso kuthetsa ndi mavuto omwe angabuke m’banja.”
12. N’chifukwa chiyani si bwino kuthamangira kukwatiwa tidakali aang’ono?
12 Omwe amathamangira kukwatiwa adakali aang’ono kaŵirikaŵiri amaona kuti zofuna zawo ndi zokhumba zawo zimasintha akamakula. Kenako amazindikira kuti zinthu zomwe poyamba ankaziona ngati zosiririka n’zosafunikanso kwenikweni. Mtsikana wina wachikristu anatsimikiza mtima kukwatiwa ali ndi zaka 16. Agogo ake komanso amayi ake anakwatiwa ali ndi zaka zomwezo. Mnyamata yemwe ankakondana naye atakana kumukwatira pamsinkhu umenewo, mtsikanayu anasankha mwamuna wina amene anafunitsitsa kumukwatira. Koma patapita nthaŵi, ananong’oneza bondo chifukwa chothamangira kukwatiwa.
13. Kodi oloŵa m’banja akadali aang’ono angakhale opereŵera m’mbali ziti?
13 Pamene tikulingalira zokwatira kapena kukwatiŵa, n’kofunika kuzindikira mwauchikulire zofunika zonse. Kuloŵa m’banja tisanakhwime kungadzetse mavuto ochuluka omwe achinyamata okwatiranawo sangathe kuwathetsa. Angakhale osazindikira bwino zinthu ndi osakhwima maganizo zomwe n’zofunika pothana ndi mavuto am’banja komanso polera ana. Tiyenera kukwatira kapena kukwatiwa pokhapokha ngati ndife okonzeka mwakuthupi, mwamalingaliro, ndi mwauzimu kuti banja lathu likhale lolimba.
14. Kodi chofunika n’chiyani kuti tithetse mavuto m’banja?
14 Paulo analemba kuti omwe akukwatira kapena kukwatiwa “adzakhala nacho chisautso m’thupi.” (1 Akorinto 7:28) Mavuto adzabuka ndithu chifukwa chakuti umunthu wa aŵiriwo m’banjamo umasiyana, ndipo adzasiyana maganizo. Chifukwa cha kupanda ungwiro kwa anthufe, kungakhale kovuta nthaŵi zina kukwaniritsa udindo wathu wa m’Malemba m’banja. (1 Akorinto 11:3; Akolose 3:18, 19; Tito 2:4, 5; 1 Petro 3:1, 2, 7) Zimafuna kukhwima m’nzeru ndi kukhala wolimba mwauzimu kuti tifunefune ndi kutsatira malangizo a Mulungu pothetsa mavuto mwachikondi.
15. Kodi makolo angachite mbali yofunika iti pokonzekeretsa ana awo ukwati? Perekani chitsanzo.
15 Makolo angakonzekeretse ana awo ukwati mwa kuwathandiza kumvetsetsa kufunika kotsatira malangizo a Mulungu. Mwa kugwiritsa ntchito Malemba ndiponso zofalitsa zachikristu mwaluso, makolo angathandize mwana wawo kuzindikira ngati iyeyo kapena yemwe akuyembekezera kudzakwatirana nayeyo ali wokonzeka kupanga pangano laukwati.a Blossom wa zaka 18 ankalingalira kuti anali kukondana ndi mnyamata wina mumpingo wawo. Mnyamatayu anali mpainiya wanthaŵi zonse, ndipo anagwirizana zokwatirana. Koma makolo a mtsikanayu anam’pempha kuti ayembekeze chaka chimodzi, polingalira kuti anali adakali wamng’ono. Patapita nthaŵi Blossom analemba kuti: “Ndikuthokoza kwambiri kuti ndinamvera malangizo anzeru amenewo. Chaka chisanathe, ndinayamba kuzindikira ndi kuona kuti mnyamata ameneyu analibe makhalidwe ofunika mwa mwamuna wabwino woti n’kukwatirana naye. Pambuyo pake anachoka m’gulu, ndipo ine ndinapulumuka lomwe likanakhala tsoka lalikulu m’moyo wanga. N’zokondweretsa kwabasi kukhala ndi makolo anzeru omwe amapereka malingaliro odalirika!”
‘Kwatiwani Kokha mwa Ambuye’
16. (a) Kodi Akristu angayesedwe motani pankhani ya ‘kukwatiwa mwa Ambuye’? (b) Ngati akuyesedwa kuti akwatiwe ndi wosakhulupirira, kodi Akristu ayenera kukumbukira chiyani?
16 Yehova wapereka malangizo omveka bwino kwa Akristu, akuti: ‘Kwatiwani kokha mwa Ambuye.’ (1 Akorinto 7:39) Makolo achikristu komanso ana awo angayesedwe pambali imeneyi. Motani? Wachinyamata angafune kukwatiwa, koma osapeza mnzake wamumpingo woti amange naye banja. Kwenikweni zikuoneka kuti zilidi choncho. M’dera lina kungakhale amuna ochepa poyerekeza ndi akazi, kapena kumbali zina kungakhale kulibiretu aliyense woyenera. Mnyamata amene si Mkristu wodzipatulira mumpingo angasonyeze chidwi mwa mtsikana wachikristu (kapena mtsikana kukopeka ndi mnyamata yemwe si wachikristu), zikatere mtsikana wachikristu limodzi ndi makolo akewo angaone ngati chapafupi ndi kungonyalanyaza miyezo imene Yehova wakhazikitsa. Zoterezi zitachitika, tingachite bwino kukumbukira chitsanzo cha Abrahamu. Njira imodzi yomwe inam’thandiza kukhalabe bwenzi labwino la Mulungu ndiyo kuonetsetsa kuti mwana wake Isake wakwatira wolambira Yehova weniweni. Isake nayenso anachita chimodzimodzi ndi mwana wake Yakobo. Zonsezi zinafuna khama la onse okhudzidwawo, koma zinakondweretsa Mulungu ndipo zinawadzetsera madalitso ake.—Genesis 28:1-4.
17. Kodi n’chifukwa chiyani kukwatira kapena kukwatiwa ndi wosakhulupirira kungadzetse mavuto osaneneka, nanga n’chifukwa chofunika kwambiri chiti ‘chokwatirira kapena kukwatiwa kokha mwa Ambuye’?
17 Mwakamodzikamodzi, wosakhulupirira pambuyo pake amakhala Mkristu. Komabe, omwe amakwatira kapena kukwatiwa ndi osakhulupirira kaŵirikaŵiri amakumana ndi mavuto aakulu. Omangidwa m’goli ndi wosakhulupirira amasiyana zikhulupiriro, mfundo zachikhalidwe, kapena zolinga. (2 Akorinto 6:14) Zimenezi zingadzetse vuto lalikulu kwambiri pa mgwirizano ndi chimwemwe cha m’banjamo. Mwachitsanzo, mkazi wina wachikristu amamva chisoni chifukwa chakuti akapita kunyumba pambuyo pa misonkhano yolimbikitsa, sizitheka kukambirana zinthu zauzimu ndi mwamuna wake wosakhulupirira. Chifukwa china chofunika kwambiri ‘chokwatirira kapena kukwatiwa mwa Ambuye’ n’chakuti timasonyeza kukhulupirika kwathu kwa Yehova. Tikachita mogwirizana ndi Mawu a Mulungu, mitima yathu siititsutsa, chifukwa chakuti tikuchita “zom’kondweretsa pamaso pake.”—1 Yohane 3:21, 22.
18. Ngati tikuganiza zokwatira kapena kukwatiwa, kodi tiyenera kulingalira mosamala mbali zofunika ziti, nanga n’chifukwa chiyani?
18 Ngati tikuganiza zokwatira kapena kukwatiŵa, tiyenera kulingalira mosamala kwambiri za makhalidwe komanso uzimu wa amene tikuyembekezera kukwatirana naye. Umunthu wachikristu, limodzi ndi kukonda Mulungu ndiponso kudzipereka kwa iye ndi mtima wonse, n’zomwe zili zofunika kwambiri kuposa kukongola m’maonekedwe. Mulungu amayanja anthu amene amazindikira ndi kukwaniritsa udindo wawo wokhala mwamuna ndi mkazi okondana ndi olimba mwauzimu. Ndipotu banja lingakhale lamphamvu kwambiri, ngati onse aŵiriwo atadzipereka mwachikondi kwa Mlengi ndi kulabadira malangizo ake ndi mtima wonse. Mwa njira imeneyi Yehova amalemekezeka, ndipo ukwatiwo umayambira pa maziko olimba kwambiri auzimu omwe amathandiza kuti banja likhale lolimba.
[Mawu a M’munsi]
Kodi Mungayankhe Motani?
• N’chifukwa chiyani pakufunika malangizo a Mulungu kuti tisankhe munthu wabwino wokwatirana naye?
• Kodi kudzipereka kwaumulungu kungalimbitse motani ukwati?
• Kodi makolo angakonzekeretse motani ana awo ukwati?
• N’chifukwa chiyani ‘kukwatira kapena kukwatiwa kokha mwa Ambuye’ kuli kofunika?
[Zithunzi patsamba 17]
Kugwiritsa ntchito malangizo a Mulungu posankhawoti mukwatirane naye kungadzetse chimwemwe chochuluka
[Zithunzi patsamba 18]
Madalitso ochuluka amadza mwa ‘kukwatira kapena kukwatiwa kokha mwa Ambuye’