2 Samueli
13 Abisalomu mwana wa Davide, anali ndi mchemwali wake wokongola dzina lake Tamara.+ Ndipo mwana wina wa Davide, dzina lake Aminoni,+ anayamba kukonda kwambiri Tamara. 2 Zimenezi zinamuvutitsa maganizo kwambiri Aminoni, moti anadwala chifukwa cha mchemwali wake Tamara. Popeza Tamara anali namwali, zinkaoneka kuti palibe chimene Aminoni angachite. 3 Aminoni anali ndi mnzake dzina lake Yehonadabu,+ mwana wa Simeya,+ mchimwene wake wa Davide. Yehonadabu anali munthu wochenjera kwambiri. 4 Ndiyeno Yehonadabu anafunsa Aminoni kuti: “Nʼchifukwa chiyani iwe mwana wa mfumu tsiku lililonse ukumaoneka wosasangalala? Tandiuza.” Aminoni anayankha kuti: “Ine ndikumufuna kwambiri Tamara, mchemwali wake+ wa mʼbale wanga Abisalomu.” 5 Atatero, Yehonadabu anamuuza kuti: “Ugone pabedi lako ndipo unamizire kudwala. Bambo ako akabwera kudzakuona, udzawauze kuti, ‘Ndikupempha kuti mchemwali wanga Tamara abwere kudzandipatsa chakudya. Akadzandikonzera chakudya,* ine ndikuona, ndidzadya kuchokera mʼmanja mwake.’”
6 Choncho Aminoni anagona nʼkunamizira kudwala. Zitatero mfumu inabwera kudzamuona ndipo Aminoni anauza mfumuyo kuti: “Ndikupempha kuti mchemwali wanga Tamara abwere kudzandiphikira makeke ine ndikuona kuti ndidye chakudya kuchokera mʼmanja mwake.” 7 Zitatero, Davide anatumiza uthenga kwa Tamara wakuti: “Chonde, pita kunyumba kwa mchimwene wako Aminoni ukamukonzere chakudya.”* 8 Choncho Tamara anapita kunyumba kwa mchimwene wake Aminoni, ndipo anamupeza atagona. Ndiyeno anakanda ufa nʼkuumba makeke Aminoniyo akuona, kenako anawaphika. 9 Atamaliza, anatenga makekewo nʼkupatsa Aminoni. Koma Aminoni anakana kudya ndipo anati: “Aliyense atuluke muno!” Choncho aliyense anatuluka.
10 Ndiyeno Aminoni anauza Tamara kuti: “Bweretsa chakudya* kuchipinda kuno kuti ndidye chili mʼmanja mwako.” Choncho Tamara anatenga makeke amene anaphikawo nʼkupita nawo kwa mchimwene wake Aminoni kuchipinda. 11 Akumupatsa kuti adye, Aminoni anamugwira nʼkumuuza kuti: “Bwera ugone nane mlongo wanga.” 12 Koma Tamara anamuuza kuti: “Ayi, achimwene! Musandichititse manyazi, chifukwa zoterezi sizinachitikepo mu Isiraeli.+ Musachite zinthu zochititsa manyazi ngati zimenezi.+ 13 Kodi ine ndizikhala bwanji zimenezi zikachitika? Komanso Aisiraeli azikuonani ngati munthu woipa komanso wochititsa manyazi. Lankhulani ndi mfumu, chifukwa sangakukanizeni kuti munditenge.” 14 Koma Aminoni sanamumvere ndipo popeza anali ndi mphamvu kuposa Tamarayo, anamugwiririra. 15 Aminoni atachita zimenezo anayamba kudana naye kwambiri. Anadana naye kwambiri kuposa mmene ankamukondera, moti anamuuza kuti: “Nyamuka uzipita!” 16 Koma Tamara anamuyankha kuti: “Ayi achimwene, musatero. Kundithamangitsa panopa nʼkoipa kwambiri kuposa zimene mwachitazi!” Koma Aminoni sanamumvere.
17 Kenako Aminoni anaitana mtumiki wake nʼkumuuza kuti: “Mʼtulutse uyu muno. Ukamutulutsa ukhome chitseko.” 18 (Tamara anali atavala mkanjo wapadera umene ankavala ana aakazi a mfumu omwe anali anamwali.) Choncho mtumiki wake uja anamutulutsa nʼkukhoma chitseko. 19 Kenako Tamara anadzithira phulusa kumutu+ ndiponso kungʼamba mkanjo umene anavala uja. Ndiyeno anaika manja ake pamutu nʼkunyamuka kumapita, akulira.
20 Zitatero, mchimwene wake Abisalomu+ anamufunsa kuti: “Kodi unali ndi mchimwene wako Aminoni? Ingokhala chete mchemwali wanga. Ameneyu ndi mchimwene wako.+ Usadandaule nazo kwambiri, ingozisiya.” Ndiyeno Tamara ankangokhala kunyumba kwa mchimwene wake Abisalomu ndipo sankacheza ndi aliyense. 21 Mfumu Davide atamva zimene zinachitikazo, anakwiya kwambiri.+ Koma sanafune kukhumudwitsa mwana wake Aminoni chifukwa ankamukonda popeza anali woyamba kubadwa. 22 Abisalomu sanalankhule chilichonse kwa Aminoni, kaya chabwino kapena choipa. Abisalomu+ anadana ndi Aminoni chifukwa chogwiririra mchemwali wake Tamara.+
23 Patatha zaka ziwiri, antchito a Abisalomu ankameta ubweya wa nkhosa ku Baala-hazori, pafupi ndi Efuraimu.+ Ndipo Abisalomu anaitana ana onse aamuna a mfumu.+ 24 Abisalomu anapita kwa mfumu nʼkunena kuti: “Ine mtumiki wanu, antchito anga akumeta ubweya wa nkhosa. Ndikupempha kuti inu mfumu ndi atumiki anu mupite nane limodzi.” 25 Koma mfumu inayankha Abisalomu kuti: “Ayi mwana wanga. Tikapita tonse, tikakuvutitsa.” Ngakhale kuti Abisalomu anachondererabe, mfumuyo sinalole kupita koma inamudalitsa. 26 Kenako Abisalomu anati: “Poti inuyo simupita, ndikupempha kuti mchimwene wanga Aminoni apite nafe.”+ Mfumu inamufunsa kuti: “Nʼchifukwa chiyani ukufuna kuti apite nawe?” 27 Koma Abisalomu anachonderera, choncho mfumu inalola kuti Aminoni ndi ana onse a mfumu apite naye.
28 Kenako Abisalomu analamula atumiki ake kuti: “Mukhale tcheru ndipo Aminoni akangofika posangalala ndi vinyo, ine ndikuuzani kuti, ‘Mupheni Aminoni!’ Zikatero mumuphe. Musaope. Ine ndi amene ndakulamulani. Muchite zinthu mwamphamvu komanso molimba mtima.” 29 Choncho atumiki a Abisalomu anapha Aminoni mogwirizana ndi zimene Abisalomuyo anawalamula. Zitatero, ana onse a mfumu ananyamuka ndipo aliyense anakwera nyulu* yake nʼkuthawa. 30 Anawa ali mʼnjira, uthenga unafika kwa Davide wakuti: “Abisalomu wapha ana onse a mfumu ndipo palibe amene wapulumuka.” 31 Mfumu itamva zimenezi inaimirira nʼkungʼamba zovala zake ndipo inagona pansi. Atumiki ake onse anaimirira pafupi ndi mfumuyo nawonso atangʼamba zovala zawo.
32 Koma Yehonadabu+ mwana wa Simeya,+ mchimwene wake wa Davide anati: “Mbuyanga, musaganize kuti ana onse a mfumu aphedwa, Aminoni yekha ndi amene wafa+ ndipo walamula zimenezi ndi Abisalomu. Iye anaganiza zochita zimenezi+ kuyambira tsiku limene Aminoniyo anagwiririra mchemwali wake+ Tamara.+ 33 Mbuyanga mfumu, musamvere zimene akunenazi zoti, ‘Ana onse a mfumu afa.’ Amene wafa ndi Aminoni yekha.”
34 Pa nthawiyi nʼkuti Abisalomu atathawa.+ Kenako mlonda wina, atakweza maso anaona anthu ambiri akubwera kumbuyo kwake mumsewu umene unali pafupi ndi phiri. 35 Ndiyeno Yehonadabu+ anauza mfumu kuti: “Mwaona, ana a mfumu akubwera. Ndimanena zija ndi zimenezi.” 36 Atangomaliza kulankhula, ana a mfumu aja anafika akulira mokweza. Mfumunso ndi atumiki ake onse analira kwambiri. 37 Koma Abisalomu anathawa nʼkupita kwa Talimai,+ mwana wamwamuna wa Amihudi mfumu ya ku Gesuri. Davide analira mwana wake kwa masiku ambiri. 38 Abisalomu atathawira ku Gesuri,+ anakhalako zaka zitatu.
39 Kenako mfumu Davide inalakalaka kupita kwa Abisalomu, chifukwa Davideyo anali atayamba kuiwala za imfa ya Aminoni.