Bokosi la Mafunso
◼ Kodi phunziro la Baibulo lokhazikika liyenera kuchititsidwa kwa utali wotani m’buku la Chidziŵitso kwa munthu?
Yehova akudalitsa gulu lake lerolino. Timaona umboni wa zimenezi chaka chilichonse pamene atsopano zikwi zambiri amaima kumbali ya choonadi. Buku la Chidziŵitso lilidi chiŵiya champhamvu pa kukwaniritsa zimenezi. Kope la January 15, 1996, la Nsanja ya Olonda linanena kuti bukuli lalinganizidwa kuti lithandize wophunzira Baibulo kupita patsogolo mwauzimu mwamsanga ndithu, mwinamwake kufika pa kubatizidwa m’miyezi yochepa.
Chifukwa cha zimenezi, Nsanja ya Olonda imodzimodziyo, patsamba 17, inalangiza kuti: “Munthu atamaliza phunziro lake la Baibulo m’buku la Chidziŵitso ndipo wabatizidwa, sipangafunikire kuchititsanso phunziro kwa iye m’buku lachiŵiri.”
Bwanji ponena za munthu amene sakubatizidwa atamaliza buku la Chidziŵitso? Utumiki Wathu Waufumu wa June 1996, patsamba 6, ndime 23, unatikumbutsa za mfundo yotchulidwa mu Nsanja ya Olonda yonena za kusaphunzira mabuku ena ndi wophunzira wofananayo atamaliza buku la Chidziŵitso. Kodi zimenezi zikutanthauza kuti sitikufuna kuthandizanso wophunzira Baibulo kupyola pamenepa? Ayi. Tikufuna kuti anthu alandire chidziŵitso choyambirira cha choonadi. Komabe, tikuyembekezera kuti m’nthaŵi yaifupi, mphunzitsi wabwino adzakhoza kuthandiza wophunzira wabwino woona mtima kupeza chidziŵitso chokwanira kuti apange chosankha chanzeru cha kutumikira Yehova. Mwinamwake chifukwa cha mikhalidwe yawo yaumwini, ophunzira Baibulo ena amakhumba kumaphunzira ngakhale nthaŵi zoposa kamodzi pa mlungu.
Zoona, ophunzira ena amachedwa kwambiri kupita patsogolo kuposa ena. Koma ngati pambuyo pa kuphunzira buku la Chidziŵitso, mwinamwake kumene kwatenga nthaŵi yaitali kuposa mmene kukanakhalira, munthuyo sanasankhe kuti akufuna kugwirizana ndi mpingo, wofalitsa angachite bwino kukambitsirana nkhaniyo ndi mmodzi wa akulu a m’Komiti Yautumiki Yampingo. Ngati pali mikhalidwe yochititsa yomveka kapena yapadera, pangafunike thandizo lina. Zimenezi nzogwirizana ndi pulinsipulo la zotchulidwa m’ndime 11 ndi 12 patsamba 17 la Nsanja ya Olonda ya January 15, 1996.
Kuzindikira phindu la kuloŵetsa ngakhale chidziŵitso choyambirira cha choonadi kuyenera kusonkhezera wophunzira kufika pamisonkhano yachikristu. Zimenezi zingachititse wophunzira kupereka umboni woonekeratu wa chikhumbo chake cha kutumikira Yehova. Ngati chiyamikiro chauzimu chimenechi sichikuonekera pambuyo pa kuchititsa phunziro m’buku la Chidziŵitso kwa nthaŵi yaitali, kungakhale bwino kuleka phunzirolo.