Oweruza
20 Zitatero, Aisiraeli onse, kuchokera ku Dani+ mpaka ku Beere-seba ndiponso kudera la Giliyadi,+ anasonkhana pamodzi mogwirizana* pamaso pa Yehova ku Mizipa.+ 2 Kenako, atsogoleri a anthu ndi mafuko onse a Isiraeli anaimirira pakati pa mpingo wonse wa anthu a Mulungu. Amuna oyenda pansi okhala ndi malupanga analipo 400,000.+
3 Anthu a fuko la Benjamini anamva kuti amuna a Isiraeli apita ku Mizipa.
Kenako amuna a Isiraeli anati: “Tafotokozani, kodi zinthu zoipa chonchi zinachitika bwanji?”+ 4 Mlevi uja,+ mwamuna wake wa mkazi wophedwa uja, anayankha kuti: “Ine ndi mkazi wanga tinafika ku Gibeya,+ mʼdera la Benjamini, kuti tigone kumeneko. 5 Ndiyeno anthu* a ku Gibeya anabwera usiku nʼkuzungulira nyumba imene ndinagona. Iwo ankafuna kundipha, koma mʼmalomwake anagwirira mkazi wanga mpaka anafa.+ 6 Choncho ndinatenga thupi la mkazi wanga nʼkuliduladula mapisi ndipo ndinatumiza mapisiwo mʼdera lililonse la cholowa cha Isiraeli.+ Ndinachita zimenezi chifukwa zomwe anachitazo nʼzoipa kwambiri komanso nʼzochititsa manyazi mu Isiraeli. 7 Tsopano inu nonse anthu a ku Isiraeli, kambiranani nkhaniyi+ nʼkuona zochita.”
8 Zitatero anthu onse ananyamuka mogwirizana,* ndipo anati: “Palibe amene abwerere kutenti yake kapena kunyumba kwake. 9 Anthu a ku Gibeya tiwachitira izi: Tichita maere+ kenako tipita kukamenyana nawo. 10 Ndipo mʼmafuko onse a Isiraeli titengemo amuna 10 pa amuna 100 alionse, amuna 100 pa amuna 1,000 alionse komanso amuna 1,000 pa amuna 10,000 alionse. Amuna amenewa azikatengera asilikali zofunika, kuti apite kukamenyana ndi anthu a ku Gibeya wa ku Benjamini chifukwa cha zinthu zochititsa manyazi zimene achita mu Isiraeli.” 11 Choncho amuna onse a Isiraeli anasonkhana nʼkupanga gulu limodzi lankhondo kuti amenyane ndi mzinda wa Gibeya.
12 Ndiyeno mafuko a Isiraeli anatumiza amuna kwa atsogoleri onse a fuko la Benjamini, kukawafunsa kuti: “Kodi zinthu zoipazi, zomwe zachitika mumzinda wanu, zachitika chifukwa chiyani? 13 Ndiyetu bweretsani anthu opanda pake a mu Gibeyawo+ kuti tiwaphe nʼkuchotsa choipachi mu Isiraeli.”+ Koma anthu a fuko la Benjamini anakana kumvera zimene Aisiraeli anzawowo ananena.
14 Ndiyeno anthu a fuko la Benjamini ananyamuka mʼmizinda yawo nʼkukasonkhana ku Gibeya kuti akamenyane ndi amuna a ku Isiraeli. 15 Tsiku limenelo anthu a fuko la Benjamini anasonkhanitsa amuna onyamula malupanga okwanira 26,000 kuchokera mʼmizinda yawo, osawerengera amuna 700 a ku Gibeya osankhidwa mwapadera. 16 Pakati pa asilikali amenewa, panali amuna amanzere 700 osankhidwa mwapadera. Aliyense wa amuna amenewa ankatha kuponya mwala nʼkugenda tsitsi limodzi osaphonya.
17 Amuna a ku Isiraeli okhala ndi malupanga amene anasonkhanitsidwa analipo 400,000,+ osawerengera amuna amʼdera la Benjamini. Aliyense wa amenewa anali msilikali wodziwa kumenya nkhondo. 18 Ndipo Aisiraeli anapita ku Beteli kukafunsa kwa Mulungu+ kuti: “Ndani akuyenera kutitsogolera kunkhondo yokamenyana ndi fuko la Benjamini?” Yehova anayankha kuti: “Yuda akutsogolereni.”
19 Zitatero, Aisiraeli ananyamuka mʼmawa nʼkukamanga msasa kuti amenyane ndi anthu a ku Gibeya.
20 Amuna a Isiraeli anapita kukamenyana ndi fuko la Benjamini ku Gibeya, ndipo kumeneko aliyense anaima pamalo ake kukonzekera kumenya nkhondo. 21 Zitatero, anthu a fuko la Benjamini anatuluka mumzinda wa Gibeya nʼkupha amuna a Isiraeli 22,000 tsiku limenelo. 22 Koma asilikali a Isiraeli analimba mtima ndipo anapitanso kukaima pamalo omwe aja pokonzekera kumenya nkhondo ngati mmene anachitira tsiku loyamba lija. 23 Ndiyeno Aisiraeli anapita ku Beteli ndipo analira pamaso pa Yehova mpaka madzulo. Iwo anafunsa Yehova kuti: “Kodi tipitenso kukamenyana ndi abale athu a fuko la Benjamini?”+ Yehova anawayankha kuti: “Pitani mukamenyane nawo.”
24 Choncho Aisiraeli anapitanso kwa anthu a fuko la Benjamini tsiku lachiwiri. 25 Zitatero anthu a fuko la Benjamini anatuluka mumzinda wa Gibeya kudzakumana nawo tsiku lachiwirilo, ndipo anaphanso Aisiraeli 18,000.+ Onse amene anaphedwawo anali amuna okhala ndi malupanga. 26 Zitatero, amuna onse a Isiraeli anapita ku Beteli. Kumeneko analira nʼkukhala pansi pamaso pa Yehova+ ndipo anasala kudya+ mpaka madzulo. Iwo anapereka kwa Yehova nsembe zopsereza+ ndi nsembe zamgwirizano.+ 27 Kenako amuna a Isiraeli anafunsa kwa Yehova,+ chifukwa masiku amenewo likasa la pangano la Mulungu woona linali ku Beteli komweko. 28 Masiku amenewo Pinihasi,+ mwana wa Eliezara, mwana wa Aroni, ndi amene ankatumikira* pafupi ndi likasalo. Choncho amuna a Isiraeli anafunsa kuti: “Kodi tipitenso kukamenyana ndi abale athu a fuko la Benjamini kapena basi tisapitenso?”+ Yehova anayankha kuti: “Pitani, chifukwa mawa ndiwapereka mʼmanja mwanu.” 29 Zitatero Aisiraeli anaika amuna kuti abisale+ kuzungulira mzinda wonse wa Gibeya.
30 Choncho Aisiraeli anapita kwa anthu a fuko la Benjamini tsiku lachitatu, ndipo anakonzekera kumenyana ndi anthu amumzinda wa Gibeya ngati mmene ankachitira maulendo ena aja.+ 31 Anthu a fuko la Benjamini atapita kukamenyana nawo, Aisiraeliwo anachititsa kuti anthu a fuko la Benjamini atuluke nʼkupita kutali ndi mzindawo.+ Ndiyeno, mofanana ndi mmene zinkachitikira maulendo ena aja, anthu a fuko la Benjaminiwo anayamba kupha ena mwa amuna a Isiraeliwo mʼmisewu ikuluikulu. Msewu wina unali wopita ku Beteli ndipo wina unali wopita ku Gibeya. Iwo anapha amuna 30 a Isiraeli ndipo mitembo yawo inali mbwee.+ 32 Choncho anthu a fuko la Benjamini anati: “Tikuwagonjetsa ngati poyamba paja.”+ Koma Aisiraeli anati: “Tiyeni tizithawa kuti tiwapititse kumisewu ikuluikulu, kutali ndi mzindawu.” 33 Ndiyeno amuna onse a Isiraeli atafika ku Baala-tamara, anaima kuti amenyane ndi anthu a fuko la Benjamini . Pa nthawiyi Aisiraeli amene anabisala pafupi ndi mzinda wa Gibeya aja, anayamba kutuluka. 34 Choncho amuna osankhidwa mwapadera a Isiraeli, okwana 10,000 anayandikira mzinda wa Gibeya, ndipo panabuka nkhondo yoopsa. Koma anthu a fuko la Benjamini sankadziwa kuti atsala pangʼono kukumana ndi tsoka.
35 Yehova anagonjetsa anthu a fuko la Benjamini+ pamaso pa Aisiraeli, moti tsiku limeneli Aisiraeli anapha anthu a fuko la Benjamini 25,100. Onsewa anali amuna okhala ndi malupanga.+
36 Anthu a fuko la Benjamini+ ankaganiza kuti popeza kuti Aisiraeli akuthawa, ndiye kuti akugonja. Koma Aisiraeliwo ankathawa chifukwa ankadalira anzawo amene anabisala pafupi ndi mzinda wa Gibeya+ aja. 37 Amuna amene anabisala aja, anathamanga nʼkukalowa mumzinda wa Gibeya. Atatero, anamwazikana ndipo anapha anthu onse amumzindawo ndi lupanga.
38 Aisiraeli anali atagwirizana ndi amuna amene anabisala aja kuti akayatse moto mumzindamo kuti utsi wake ukhale chizindikiro.
39 Aisiraeli atayamba kuthawa, anthu a fuko la Benjamini anayamba kuwathamangitsa ndipo anapha amuna 30 a Isiraeli.+ Anthu a fuko la Benjaminiwo ankanena kuti: “Zikuonekeratu kuti tikuwagonjetsa ngati poyamba paja.”+ 40 Zili choncho, utsi wa chizindikiro uja unayamba kukwera mʼmwamba kuchokera mumzindawo ndipo unkaoneka ngati chipilala. Anthu a fuko la Benjamini atatembenuka, anangoona mzinda wonse ukuyaka moto. 41 Zitatero Aisiraeli anatembenuka, ndipo anthu a fuko la Benjamini anasokonezeka chifukwa anazindikira kuti zinthu zawavuta. 42 Choncho anthu a fuko la Benjamini anatembenuka nʼkuyamba kuthawa Aisiraeli ndipo ankalowera kuchipululu. Koma anapanikizidwa kwambiri chifukwa amuna a Isiraeli amene anali mumzinda aja nawonso anabwera nʼkuyambanso kuwapha. 43 Iwo anazungulira anthu a fuko la Benjamini ndipo anawathamangitsa osawasiya moti anawagonjetsera pafupi penipeni ndi mzimda wa Gibeya, chakumʼmawa. 44 Pamapeto pake, amuna 18,000 a fuko la Benjamini anaphedwa ndipo onsewa anali asilikali amphamvu.+
45 Anthu a fuko la Benjaminiwo anatembenuka nʼkuyamba kuthawira kuchipululu, kuthanthwe la Rimoni.+ Aisiraeli anaphanso Abenjamini 5,000 mʼmisewu ikuluikulu, ndipo anapitiriza kuwathamangitsa mpaka kukafika ku Gidomu nʼkuphanso amuna ena 2,000. 46 Anthu onse a fuko la Benjamini amene anaphedwa tsiku limeneli, anakwana 25,000. Onsewa anali asilikali amphamvu okhala ndi malupanga.+ 47 Koma amuna 600 anathawira kuchipululu kuthanthwe la Rimoni ndipo anakhala komweko kwa miyezi 4.
48 Amuna a Isiraeli anabwerera kukapha ndi lupanga anthu a fuko la Benjamini amene anatsala mumzinda komanso ziweto. Anapha chilichonse chimene anapeza. Kuwonjezera apo, anayatsa moto mizinda yonse imene ankaipeza mʼnjira.