Mutu 29
Kuimba Nyimbo Yatsopano Yokondwerera Kupambana
Masomphenya 9—Chivumbulutso 14:1-20
Nkhani yake: A 144,000 ali ndi Mwanawankhosa paphiri la Ziyoni, angelo akulengeza uthenga padziko lonse lapansi, ndipo zokolola zikusonkhanitsidwa
Nthawi ya kukwaniritsidwa kwake: Kuyambira mu 1914 mpaka pa chisautso chachikulu
1. Kodi taona kale zotani mu Chivumbulutso chaputala 7, 12 ndi 13, ndipo tsopano tiona zotani?
TSOPANO tiyeni tione masomphenya otsatira a Yohane, ndipo zimenezi zitilimbikitsa kwambiri. Tiona za atumiki okhulupirika a Yehova ndiponso ntchito yawo imene akugwira m’tsiku la Ambuye, zomwe ndi zotsitsimula tikaziyerekezera ndi magulu oipa kwambiri a chinjoka okhala ngati zilombo aja. (Chivumbulutso 1:10) Taona kale pa Chivumbulutso 7:1, 3 kuti angelo akugwira mphepo zinayi zowononga zija kuti zisawombe, mpaka akapolo onse 144,000 odzozedwa atadindidwa chidindo. Komanso lemba la Chivumbulutso 12:17 latidziwitsa kuti m’nthawi imeneyi, Satana, yemwe ndi chinjoka, akudana kwambiri ndi anthu amenewa, omwe ndi “otsala a mbewu [ya mkazi].” Ndipo Chivumbulutso chaputala 13 chasonyeza bwino mabungwe andale amene Satana wayambitsa padziko lapansili n’cholinga choti azisowetsa mtendere ndi kuzunza mwankhanza kwambiri atumiki a Yehova okhulupirika. Koma mdani wamkulu ameneyu sangalepheretse cholinga cha Mulungu. Tsopano tiona kuti ngakhale kuti Satana akuyesetsa kuchita zinthu zankhanzazi, Mulungu adzapambana ndipo anthu onse a 144,000 adzasonkhanitsidwa.
2. Malinga ndi Chivumbulutso 14:1, kodi Yohane anaoneratu zinthu ziti zosangalatsa zimene zidzachitike m’tsogolomu, ndipo ndani amene ali Mwanawankhosa?
2 Yohane, pamodzi ndi Akhristu odzozedwa masiku ano, anaonetsedwa mmene zinthu zosangalatsazi zidzachitikire. Iye ananena kuti: “Nditayang’ana, ndinaona Mwanawankhosa ataimirira paphiri la Ziyoni. Limodzi naye panali enanso 144,000 olembedwa dzina lake ndi dzina la Atate wake pamphumi pawo.” (Chivumbulutso 14:1) Monga taonera kale, Mwanawankhosa ameneyu ndi Mikayeli, yemwe anayeretsa kumwamba pochotsako Mdyerekezi ndi ziwanda zake n’kuwaponya kudzikoli. Mikayeli ameneyu ndi amene Danieli ananena kuti “waimirira kuti athandize anthu a [Mulungu],” pokonzekera kuti ‘adzaimirire’ kuti apereke ziweruzo zolungama za Yehova. (Danieli 12:1; Chivumbulutso 12:7, 9) Kuyambira mu 1914, Mwanawankhosa wa Mulungu ameneyu, yemwe ali ndi mtima wololera kuvutikira ena, waimirira paphiri la Ziyoni monga Mfumu yomwenso ndi Mesiya.
3. Kodi “phiri la Ziyoni” limene ‘paimirira’ Mwanawankhosa ndi a 144,000, n’chiyani?
3 Zimenezi n’zogwirizana ndi zimene Yehova analosera, kuti: “Inetu ndakhazika mfumu yanga pa Ziyoni, phiri langa lopatulika.” (Salimo 2:6; 110:2) Phiri la Ziyoni limeneli si la padziko lapansi, lomwe linali ku Yerusalemu, mzinda umene mafumu a m’banja la Davide ankakhala pa nthawi ya ulamuliro wawo. (1 Mbiri 11:4-7; 2 Mbiri 5:2) Tikutero chifukwa mu 33 C.E., Yesu ataphedwa n’kuukitsidwa, anaikidwa monga mwala wapakona wa maziko a phiri la Ziyoni lakumwamba. Yehova anakonza zoti aike “mzinda wa Mulungu wamoyo, Yerusalemu wakumwamba,” paphiri lakumwamba limeneli. Choncho palembali, “phiri la Ziyoni” likuimira udindo wokwezeka wa Yesu ndi wa olandira cholowa anzake, omwe akupanga Yerusalemu wakumwamba, yemwe ndi Ufumu wa Mulungu. (Aheberi 12:22, 28; Aefeso 3:6) Umenewu ndi udindo wolemekezeka ndiponso wokwezeka umene Yehova wawapatsa monga mafumu m’tsiku la Ambuye. Kwa zaka zambirimbiri, Akhristu odzozedwa, omwe ndi “miyala yamoyo,” akhala akudikirira mwachidwi kuti adzaimirire paphiri la Ziyoni lakumwamba, n’kukhala limodzi ndi Ambuye Yesu Khristu ali mu ulemerero wake, mu Ufumu wake wokwezeka.—1 Petulo 2:4-6; Luka 22:28-30; Yohane 14:2, 3.
4. N’chifukwa chiyani tinganene kuti anthu onse 144,000 aimirira paphiri la Ziyoni?
4 Kuwonjezera pa kuona Yesu, Yohane anaonanso anthu onse 144,000 amene adzalandire cholowa limodzi ndi Yesuyo mu Ufumu wakumwamba, ataimirira paphiri la Ziyoni. Pa nthawi imene inachitiridwa chithunzi m’masomphenyawa, ambiri mwa anthu 144,000 amenewa, koma osati onse, anali atapita kale kumwamba. Kenako m’masomphenya omwewa, Yohane anauzidwa kuti ena mwa oyerawa adzafunika kupirira mazunzo ndiponso kufa ali okhulupirika. (Chivumbulutso 14:12, 13) Choncho, zikuoneka kuti ena mwa anthu 144,000 amenewa adakali padziko lapansi. Nanga n’chifukwa chiyani Yohane anawaona onse ataimirira ndi Yesu paphiri la Ziyoni?a N’chifukwa chakuti iwo monga mpingo wa Akhristu odzozedwa, tsopano ‘afika kuphiri la Ziyoni ndi mzinda wa Mulungu wamoyo, Yerusalemu wakumwamba.’ (Aheberi 12:22) Mofanana ndi Paulo pamene anali padziko lapansili, iwo akwezedwa kale mwauzimu kuti agwirizane ndi Khristu Yesu m’malo akumwamba. (Aefeso 2:5, 6) Komanso mu 1919, iwo anavomera pamene anaitanidwa kuti, “Kwerani kuno,” ndipo mophiphiritsa, ‘anakwera kumwamba mumtambo.’ (Chivumbulutso 11:12) Choncho mogwirizana ndi malemba amenewa, tinganene kuti mwauzimu, anthu onse 144,000 ali paphiri la Ziyoni ndi Yesu Khristu.
5. Kodi pamphumi pa a 144,000 palembedwa mayina a ndani, ndipo dzina lililonse likutanthauza chiyani?
5 A 144,000 sagwirizana mwanjira iliyonse ndi anthu amene amalambira chilombo, omwe ali ndi chizindikiro cha nambala yophiphiritsa ya 666. (Chivumbulutso 13:15-18) Mosiyana ndi anthu amenewa, Akhristu okhulupirikawa analembedwa dzina la Mulungu ndi la Mwanawankhosa pamphumi pawo. Mosakayikira, Yohane, yemwe anali Myuda, anaona dzina la Mulungu litalembedwa m’zilembo zachiheberi izi: יהוה.b Mfundo yakuti dzina la Atate ake a Yesu linalembedwa pamphumi pawo mophiphiritsa, ikusonyeza kuti Akhristu amene anadindidwa chidindowa amauza anthu onse kuti iwo ndi mboni za Yehova, ndiponso akapolo ake. (Chivumbulutso 3:12) Ndipo mfundo yakuti dzina la Yesu linalembedwanso pamphumi pawo ikusonyeza kuti iwo amavomereza kuti ndi anthu a Yesu. Iye anawalonjeza kuti adzakhala “mwamuna” wawo ndipo iwo adzakhala “mkwatibwi” wake. Mkwatibwi ameneyu ndi “cholengedwa chatsopano,” chomwe chikutumikira Mulungu poyembekezera kudzakhala ndi moyo kumwamba. (Aefeso 5:22-24; Chivumbulutso 21:2, 9; 2 Akorinto 5:17) Ubwenzi wapadera kwambiri umene ali nawo ndi Yehova ndiponso Yesu Khristu umalamulira maganizo awo onse ndiponso zochita zawo zonse.
Kuimba Nyimbo Yokhala Ngati Yatsopano
6. Kodi Yohane anamva kuimba kotani, ndipo anakufotokoza bwanji?
6 Mogwirizana ndi mfundo imeneyi, Yohane analemba kuti: “Kenako ndinamva phokoso kumwamba ngati mkokomo wa madzi ambiri, ndiponso ngati phokoso la bingu lamphamvu. Phokoso ndinamvalo linali ngati la oimba amene akuimba motsagana ndi azeze awo. Iwo anali kuimba nyimbo yokhala ngati yatsopano pamaso pa mpando wachifumu, pamaso pa zamoyo zinayi, ndi pamaso pa akulu. Palibe anatha kuiphunzira nyimboyo, koma 144,000 amene anagulidwa padziko lapansi.” (Chivumbulutso 14:2, 3) N’zosadabwitsa kuti Yohane atamva mawu a anthu 144,000 akuimba limodzi nyimbo yosangalatsa, anaganizira za phokoso la mathithi aakulu ndiponso kugunda kwamphamvu kwa mabingu. Nyimboyo, yomwe inkaimbidwanso ndi azeze, iyenera kuti inali yokoma zedi ndiponso inkamveka bwino kwambiri. (Salimo 81:2) Palibe kwaya iliyonse padziko lapansi imene ingaimbe mokweza komanso mwanthetemya ngati mmene kwaya yaulemereroyi inaimbira.
7. (a) Kodi nyimbo yatsopano yotchulidwa pa Chivumbulutso 14:3 n’chiyani? (b) Kodi n’chifukwa chiyani nyimbo ya pa Salimo 149:1 ili yatsopano m’nthawi yathu ino?
7 Kodi ‘nyimbo yatsopanoyi’ n’chiyani? Monga momwe tinaonera pokambirana lemba la Chivumbulutso 5:9, 10, nyimboyi ikukhudzana ndi zolinga za Yehova zokhudzana ndi Ufumu wake. Ikukhudzananso ndi zinthu zosangalatsa kwambiri zimene iye anachita, kudzera mwa Yesu Khristu, n’cholinga choti anthu amene akupanga Isiraeli wauzimu akhale “mafumu ndi ansembe a Mulungu wathu.” Imeneyi ndi nyimbo yotamanda Yehova, yolengeza zinthu zatsopano zimene iye akukwaniritsa kudzera mwa Isiraeli wa Mulungu, zothandiza Isiraeli wa Mulungu yemweyo. (Agalatiya 6:16) Anthu amene akupanga Isiraeli wauzimuyu amamvera mawu a wamasalimo, akuti: “Tamandani Ya, anthu inu! Imbirani Yehova nyimbo yatsopano, muimbireni nyimbo zomutamanda mu mpingo wa anthu ake okhulupirika. Isiraeli asangalale ndi Womupanga Wamkulu, ana a Ziyoni akondwere ndi Mfumu yawo.” (Salimo 149:1, 2) N’zoona kuti mawu a nyimbo imeneyi analembedwa zaka zambirimbiri zapitazo, koma m’nthawi yathu ino, anthu amene akuimba nyimboyi akuimva m’njira yatsopano. Mu 1914 Ufumu wa Mesiya unabadwa. (Chivumbulutso 12:10) Mu 1919 anthu a Yehova padziko lapansili anayambiranso kulengeza mwakhama “mawu a ufumu.” (Mateyu 13:19) M’chaka chimenecho, iwo anayamba ‘kuimba nyimbo zotamanda Yehova m’mitima mwawo,’ chifukwa analimbikitsidwa ndi lemba la chaka cha 1919, lomwe linali Yesaya 54:17, komanso analimbikitsidwa chifukwa chakuti anabwezeretsedwa m’paradaiso wauzimu.—Aefeso 5:19.
8. N’chifukwa chiyani anthu a 144,000 okha ndi amene angathe kuphunzira nyimbo yatsopano yotchulidwa pa Chivumbulutso 14:3?
8 Koma kodi n’chifukwa chiyani anthu 144,000 okha ndi amene anatha kuphunzira nyimbo yotchulidwa pa Chivumbulutso 14:3? Chifukwa ikukhudzana ndi zimene zidzawachitikire monga anthu amene asankhidwa kukhala olandira cholowa a Ufumu wa Mulungu. Iwo okha ndi amene anatengedwa kukhala ana a Mulungu n’kudzozedwa ndi mzimu woyera. Komanso iwo okha ndi amene anagulidwa padziko lapansi kuti akhale mbali ya Ufumu wakumwamba, ndipo iwo okha ndi amene ‘adzakhale ansembe . . . ndi kulamulira monga mafumu’ limodzi ndi Yesu Khristu kwa zaka 1,000 n’kuthandiza anthu kukhala angwiro. N’chifukwa chake Yohane anaona iwo okha ‘akuimba nyimbo yokhala ngati yatsopano’ pamaso penipeni pa Yehova.c Zinthu zapadera zimene zinawachitikirazi komanso zimene akuyembekezera, zimawachititsa kuti azitha kuumvetsa bwino Ufumu wa Mulungu ndi kuuyamikira kwambiri. Choncho iwo amatha kuimba nyimbo yokhudza ufumuwo m’njira yoti wina aliyense sangathe.—Chivumbulutso 20:6; Akolose 1:13; 1 Atesalonika 2:11, 12.
9. Kodi a khamu lalikulu achita chiyani atamva kuimba kwa Akhristu odzozedwa, ndipo pochita zimenezo akwaniritsa mawu ati olimbikitsa?
9 Koma palinso anthu ena amene akumvetsera nyimboyo n’kuchitapo kanthu. Kuyambira mu 1935, khamu lalikulu la nkhosa zina, limene likukulirakulira, lamva nyimbo yokondwerera kupambana ya Akhristu odzozedwa imeneyi, ndipo lakhudzidwa mtima n’kuyamba kulengeza nawo limodzi za Ufumu wa Mulungu. (Yohane 10:16; Chivumbulutso 7:9) N’zoona kuti anthu atsopanowa sangaphunzire kuimba nyimbo yatsopano yofanana ndendende ndi imene atsogoleri a m’tsogolo a Ufumu wa Mulungu aja akuimba. Koma nawonso amaimba nyimbo yokoma kwambiri yotamanda Yehova chifukwa cha zinthu zatsopano zimene Yehovayo akukwaniritsa. Choncho iwo amamvera mawu olimbikitsa a wamasalimo wina, akuti: “Imbirani Yehova nyimbo yatsopano. Imbirani Yehova, inu anthu nonse okhala padziko lapansi. Imbirani Yehova, tamandani dzina lake. Tsiku ndi tsiku lengezani uthenga wabwino wa chipulumutso chake. Lengezani ulemerero wake pakati pa anthu a mitundu ina, ndiponso ntchito zake zodabwitsa pakati pa mitundu yonse ya anthu. Vomerezani Yehova, inu mabanja a mitundu ya anthu, m’patseni Yehova ulemerero ndi kuvomereza kuti iye ndi wamphamvu. Nenani pakati pa anthu a mitundu ina kuti: ‘Yehova wakhala mfumu.’”—Salimo 96:1-3, 7, 10; 98:1-9.
10. Kodi zikutheka bwanji kuti a 144,000 aziimba nyimbo “pamaso pa” akulu 24 ophiphiritsa?
10 Kodi a 144,000 angaimbe bwanji “pamaso pa” akulu, popeza akulu 24 aja akuimira anthu a 144,000 omwewo ali m’malo awo aulemerero kumwamba? Chakumayambiriro kwa tsiku la Ambuye, anthu “amene anafa mwa Khristu” anaukitsidwa monga zolengedwa zauzimu. Choncho Akhristu odzozedwa okhulupirika amene anapambana pa nkhondo tsopano ali kumwamba, ndipo mophiphiritsa akugwira ntchito yofanana ndi imene ankagwira magulu 24 a akulu omwe analinso ansembe. Akulu amenewa anaoneka m’masomphenya amene Yohane anaona a mbali yakumwamba ya gulu la Yehova. (1 Atesalonika 4:15, 16; 1 Mbiri 24:1-18; Chivumbulutso 4:4; 6:11) Choncho a 144,000 amene adakali padziko lapansi akuimba nyimbo yatsopanoyo pamaso pa, kapena kuti moonedwa ndi, abale awo amene anaukitsidwa ndipo ali kumwamba.
11. N’chifukwa chiyani Akhristu odzozedwa opambana pa nkhondo akutchedwa akulu 24 komanso anthu a 144,000?
11 Pofika pano, tingafunsenso kuti: N’chifukwa chiyani Akhristu odzozedwa opambana pa nkhondowa akutchedwa akulu 24 ophiphiritsa komanso anthu a 144,000? N’chifukwa chakuti m’buku la Chivumbulutso, gulu limodzi lomweli limaonedwa m’njira ziwiri zosiyana. Akulu 24 aja nthawi zonse amasonyezedwa ali m’malo awo amene adzakhale mpaka kalekale, kuzungulira mpando wachifumu wa Yehova, atakhala mafumu ndi ansembe kumwamba. Iwo amaimira gulu lonse la anthu 144,000 ali m’malo awo kumwamba, ngakhale kuti panopa pali anthu ena ochepa a m’gululi amene adakali padziko lapansi pano. (Chivumbulutso 4:4, 10; 5:5-14; 7:11-13; 11:16-18) Koma chaputala 7 cha Chivumbulutso chikutsindika makamaka mfundo yoti a 144,000 amenewa anagulidwa pakati pa anthu. Chimatsindikanso cholinga chachikulu cha Yehova choti adinde chidindo munthu aliyense amene akupanga Isiraeli wauzimu ndiponso kuti apulumutse khamu lalikulu la anthu amene chiwerengero chake sichikudziwika. Ndipo chaputala 14 cha Chivumbulutso chikutipatsa chithunzi chimene chikutsimikizira kuti gulu lonse la anthu odzalamulira mu Ufumu wa Mulungu, lopangidwa ndi anthu 144,000 opambana pa nkhondo, lidzasonkhanitsidwa paphiri la Ziyoni limodzi ndi Mwanawankhosa. Chaputalachi chikufotokozanso zimene anthu amenewa ayenera kuchita kuti ayenerere kukhala m’gulu la a 144,000, monga momwe tionere tsopano.d
Otsatira Mwanawankhosa
12. (a) Kodi Yohane anapitiriza bwanji kufotokoza za a 144,000? (b) N’chifukwa chiyani a 144,000 akutchedwa anamwali?
12 Popitiriza kufotokoza anthu 144,000 amenewa, omwe “anagulidwa padziko lapansi,” Yohane anati: “Awa ndiwo amene sanadziipitse ndi akazi, ndipo ali ngati anamwali. Amenewa ndiwo amatsatira Mwanawankhosa kulikonse kumene akupita. Iwowa anagulidwa kuchokera mwa anthu, monga zipatso zoyambirira zoperekedwa kwa Mulungu ndi kwa Mwanawankhosa. M’kamwa mwawo simunapezeke chinyengo, ndipo alibe chilema.” (Chivumbulutso 14:4, 5) Mfundo yakuti anthu a 144,000 “ali ngati anamwali” sikutanthauza kuti anthu a m’gulu limeneli sakwatira. Mtumwi Paulo analembera Akhristu amene anali ndi chiyembekezo chodzapita kumwamba kuti, ngakhale kuti kukhala Mkhristu wosakwatira kapena wosakwatiwa kuli ndi ubwino wake, nthawi zina zimakhala bwino kuti munthu akwatire. (1 Akorinto 7:1, 2, 36, 37) Choncho anthu a m’gulu limeneli amadziwika bwino chifukwa chokhala anamwali auzimu. Iwo amapewa kulowerera m’ndale za m’dzikoli kapena kulowa m’zipembedzo zonyenga, chomwe ndi chigololo chauzimu. (Yakobo 4:4; Chivumbulutso 17:5) Popeza iwo analonjezedwa kuti adzakhala mkwatibwi wa Khristu, ayesetsa kukhala oyera, “opanda chilema pakati pa m’badwo wopotoka maganizo ndi wokhotakhota.”—Afilipi 2:15.
13. N’chifukwa chiyani a 144,000 ali mkwatibwi woyenera wa Yesu Khristu, ndipo ‘amatsatira bwanji Mwanawankhosa kulikonse kumene akupita’?
13 Komanso, “m’kamwa mwawo simunapezeke chinyengo.” Pa nkhani imeneyi, iwo akufanana ndi Mfumu yawo, Yesu Khristu. Monga munthu wangwiro, “iye sanachite tchimo, ndipo m’kamwa mwake simunapezeke chinyengo.” (1 Petulo 2:21, 22) Popeza a 144,000 ndi opanda chilema ndiponso opanda chinyengo, ndi okonzekera bwino kudzakhala mkwatibwi woyera wa Mkulu wa Ansembe wamkulu wa Yehova. Yesu ali padziko lapansi, anaitana anthu a mtima wabwino kuti amutsatire. (Maliko 8:34; 10:21; Yohane 1:43) Anthu amene anamva kuitanaku anatsanzira moyo wake ndipo anamvera zimene iye ankaphunzitsa. Choncho pa nthawi imene odzozedwa ali padziko lapansi, “amatsatira Mwanawankhosa kulikonse kumene akupita,” pamene akuwatsogolera m’dziko la Satanali.
14. (a) Kodi a 144,000 ndiwo “zipatso zoyambirira zoperekedwa kwa Mulungu ndi kwa Mwanawankhosa” m’njira yotani? (b) Kodi a khamu lalikulu nawonso ndi zipatso zoyambirira m’njira yotani?
14 A 144,000 “anagulidwa padziko lapansi,” ndipo “anagulidwa kuchokera mwa anthu.” Iwo amatengedwa kukhala ana a Mulungu ndipo akaukitsidwa, sakhalanso anthu a thupi la mnofu ndi magazi. Monga momwe vesi 4 likufotokozera, iwo amakhala “zipatso zoyambirira zoperekedwa kwa Mulungu ndi kwa Mwanawankhosa.” N’zoona kuti munthawi ya atumwi, Yesu anali “chipatso choyambirira cha amene akugona mu imfa.” (1 Akorinto 15:20, 23) Koma a 144,000 ndi “zipatso zoyambirira” zochokera mwa anthu opanda ungwiro, zogulidwa ndi nsembe ya Yesu. (Yakobo 1:18) Komabe, ntchito yokolola zipatso pakati pa anthu sinathere pa iwowa. Buku la Chivumbulutso lafotokoza kale za ntchito yokolola anthu a khamu lalikulu osadziwika chiwerengero chake, amene anafuula ndi mawu akuti: “Chipulumutso chathu chachokera kwa Mulungu wathu, amene wakhala pampando wachifumu, ndi kwa Mwanawankhosa.” Anthu a khamu lalikulu amenewa adzapulumuka pa chisautso chachikulu, ndipo adzapitiriza kutsitsimulidwa ndi “akasupe a madzi a moyo” n’kumasintha pang’onopang’ono mpaka kukhala ndi moyo wangwiro padziko lapansi pano. Chisautso chachikulu chikadzadutsa, Manda adzakhuthula anthu amene ali mmenemo, ndipo anthu mamiliyoni ambiri adzaukitsidwa n’kukhala ndi mwayi womwa nawo madzi a moyo aja. Poganizira zimenezi, si kulakwa kunena kuti a khamu lalikulu ndiwo zipatso zoyambirira za nkhosa zina, chifukwa iwo ndi amene adzayambirire ‘kuchapa mikanjo yawo ndi kuiyeretsa m’magazi a Mwanawankhosa,’ ndi chiyembekezo chodzakhala ndi moyo wosatha padziko lapansi.—Chivumbulutso 7:9, 10, 14, 17; 20:12, 13.
15. Kodi pali kufanana kotani pakati pa magulu atatu a zipatso zoyambirira, ndi zikondwerero zimene anthu ankachita pomvera Chilamulo cha Mose?
15 N’zochititsa chidwi kuti m’zikondwerero zimene anthu ankachita potsatira Chilamulo cha Mose, timapezamo mfundo zimene zikufanana m’njira zina ndi magulu atatu a zipatso zoyambirira amenewa (Yesu Khristu, a 144,000, ndi a khamu lalikulu). Pa Nisani 16, pa Chikondwerero cha Mikate Yopanda Chofufumitsa, Aisiraeli ankapereka kwa Yehova mtolo wa zokolola zawo zoyambirira za balere. (Levitiko 23:6-14) Komanso Yesu anaukitsidwa pa Nisani 16. Pa tsiku la 50 kuchokera pa Nisani 16, m’mwezi wachitatu, Aisiraeli ankachita chikondwerero cha zokolola, chokondwerera zipatso zoyamba kucha za tirigu. (Ekisodo 23:16; Levitiko 23:15, 16) Chikondwerero chimenechi chinayamba kutchedwa Pentekosite (kuchokera ku mawu achigiriki otanthauza “cha 50”), ndipo pa Pentekosite wa mu 33 C.E., m’pamene anthu oyambirira a 144,000 anadzozedwa ndi mzimu woyera. Pomaliza, m’mwezi wa 7, akakolola zinthu zonse za m’munda, Aisiraeli ankachita Chikondwerero cha Misasa. Imeneyi inali nthawi yosangalala ndiponso yothokoza Mulungu, ndipo Aisiraeliwo ankakhala mlungu umodzi m’misasa imene ankaimanga ndi zinthu zosiyanasiyana, kuphatikizapo nthambi za kanjedza. (Levitiko 23:33-43) Mofanana ndi zimenezi, a khamu lalikulu, amene ndi ena mwa anthu amene apezeka pa ntchito yaikulu yokolola, amathokoza Mulungu pamaso pa mpando wachifumu “atanyamula nthambi za kanjedza m’manja mwawo.”—Chivumbulutso 7:9.
Kulengeza Uthenga Wabwino Wosatha
16, 17. (a) Kodi Yohane anaona mngelo akuuluka kuti, ndipo mngeloyo akulengeza za chiyani? (b) Kodi ndani amene akugwira nawo ntchito yolalikira za Ufumu, ndipo ndi zochitika zotani zimene zikusonyeza zimenezi?
16 Kenako Yohane analemba kuti: “Ndinaona mngelo winanso akuuluka chapafupi m’mlengalenga. Iye anali ndi uthenga wabwino wosatha woti aulengeze monga nkhani yosangalatsa kwa anthu okhala padziko lapansi, ndi kudziko lililonse, fuko lililonse, chinenero chilichonse, ndi mtundu uliwonse. Iye anali kunena mofuula kuti: ‘Opani Mulungu ndi kumupatsa ulemerero, chifukwa ola lakuti apereke chiweruzo lafika. Chotero lambirani Iye amene anapanga kumwamba, dziko lapansi, nyanja, ndi akasupe amadzi.’” (Chivumbulutso 14:6, 7) Mngeloyu akuuluka “chapafupi m’mlengalenga,” mmene mbalame zimauluka. (Yerekezerani ndi Chivumbulutso 19:17.) Choncho mawu ake akhoza kumveka padziko lonse lapansi. Mawu a mngelowa akufika kulikonse padziko lapansili, ndipo palibe TV iliyonse imene ingathe kuulutsa nkhani zake mpaka kufika malo ambiri choncho.
17 Aliyense akulimbikitsidwa kuti aope Yehova, osati chilombo ndi chifaniziro chake, chifukwa Yehovayo ndi wamphamvu kwambiri moti sitingamuyerekezere n’komwe ndi chilombo chilichonse chophiphiritsa cholamulidwa ndi Satana. Pajatu Yehova ndi amene analenga kumwamba ndi dziko lapansi, ndipo tsopano nthawi yoti aweruze dziko lapansi yakwana. (Yerekezerani ndi Genesis 1:1; Chivumbulutso 11:18.) Pamene Yesu anali padziko lapansi, ananeneratu za nthawi yathu ino, kuti: “Uthenga wabwino uwu wa ufumu udzalalikidwa padziko lonse lapansi kumene kuli anthu, kuti ukhale umboni ku mitundu yonse, kenako mapeto adzafika.” (Mateyu 24:14) Mpingo wa Akhristu odzozedwa ukugwira ntchito imeneyi. (1 Akorinto 9:16; Aefeso 6:15) Apa buku la Chivumbulutso likusonyeza kuti angelo osaoneka akugwira nawonso ntchito yolalikira. Ndipotu, nthawi zambiri zimachita kuonekeratu kuti angelo athandiza kuti munthu wa Mboni za Yehova afike pakhomo linalake pamene munthu wina amene ali pa mavuto anali kulakalaka, mwinanso kupemphera kumene, kuti apeze thandizo lauzimu.
18. Mogwirizana ndi zimene mngelo amene akuuluka chapafupi m’mlengalenga uja analengeza, kodi ola limene lafika ndi lotani, ndipo ndani amene alengeze zinthu zinanso?
18 Mogwirizana ndi zimene mngelo amene akuuluka chapafupi m’mlengalenga uja analengeza, ola lakuti Mulungu apereke chiweruzo lafika. Kodi tsopano iye apereka chiweruzo chotani? Makutu athu achita kuti woo! tikamva zimene mngelo wachiwiri, wachitatu, wachinayi, ndi wachisanu alengeze.—Yeremiya 19:3.
[Mawu a M’munsi]
a Monga mmene lemba la 1 Akorinto 4:8 likusonyezera, Akhristu odzozedwa sayamba kulamulira monga mafumu adakali padziko lapansi. Komabe, mogwirizana ndi nkhani imene ikufotokozedwa pa Chivumbulutso 14:3, 6, 12 ndi 13, iwo amaimba nawo nyimbo yatsopanoyo polalikira uthenga wabwino pamene akupirira mpaka pamapeto a moyo wawo wapadziko lapansi.
b Zimenezi zikugwirizana ndi mfundo yakuti mayina achiheberi anagwiritsidwanso ntchito m’masomphenya ena. Mwachitsanzo, Yesu anapatsidwa dzina lachiheberi lakuti “Abadoni” (kutanthauza “Chiwonongeko”) ndipo adzaweruza adani ake “kumalo amene m’Chiheberi amatchedwa Haramagedo.”—Chivumbulutso 9:11; 16:16.
c Lembali limati nyimboyo inali “yokhala ngati yatsopano,” chifukwa nyimboyo inalembedwa kalekale m’maulosi. Koma panalibe amene anali woyenerera kuiimba. Tsopano pamene Ufumuwo wakhazikitsidwa ndiponso pamene oyera akuukitsidwa, maulosiwo ayamba kukwaniritsidwa, ndipo ndi nthawi yoti nyimbo yosangalatsayo iimbidwe mwanthetemya.
d Tingayerekezere zimenezi ndi gulu la kapolo wokhulupirika ndi wanzeru limene limapereka chakudya kwa antchito apakhomo pa nthawi yoyenera. (Mateyu 24:45) Gulu la kapoloyu lili ndi udindo wopereka chakudya, koma antchito apakhomo, omwe ndi munthu aliyense amene ali m’gulu la kapoloyo, amalimbikitsidwa akamadya chakudya chauzimu chimenecho. Choncho magulu awiri onsewa akunena za anthu omweomwewo, kungoti pena awafotokoza ngati gulu, pena ngati munthu mmodzimmodzi.
[Zithunzi patsamba 202, 203]
A 144,000
Akulu 24
Anthu amene adzalandire cholowa limodzi ndi Mwanawankhosa, Khristu Yesu, akuonedwa m’njira ziwiri zosiyana