2 Mbiri
5 Choncho Solomo anamaliza ntchito yonse yokhudza nyumba ya Yehova+ imene anayenera kugwira. Kenako Solomo anabweretsa zinthu zimene bambo ake Davide anaziyeretsa.+ Anatenga siliva, golide ndiponso zinthu zonse nʼkuziika mosungira chuma chapanyumba ya Mulungu woona.+ 2 Pa nthawi imeneyo Solomo anasonkhanitsa akulu a Isiraeli, atsogoleri onse a mafuko ndi atsogoleri a nyumba za makolo a Aisiraeli. Anabwera ku Yerusalemu kuti akatenge likasa la pangano la Yehova ku Mzinda wa Davide,+ komwe ndi ku Ziyoni.+ 3 Amuna onse a mu Isiraeli anasonkhana kwa mfumu pachikondwerero* cha mʼmwezi wa 7.+
4 Choncho akulu onse a Isiraeli anabwera ndipo Alevi ananyamula Likasa.+ 5 Iwo ananyamula Likasa, chihema chokumanako+ ndiponso ziwiya zonse zopatulika zimene zinali mʼchihemacho. Ansembe ndi Alevi* anabweretsa zinthuzi. 6 Mfumu Solomo ndi gulu lonse la Aisiraeli amene anawaitana, anasonkhana patsogolo pa Likasa. Iwo anapereka nsembe+ zosawerengeka za nkhosa ndi ngʼombe. 7 Kenako ansembe anabweretsa likasa la pangano la Yehova pamalo ake, kuchipinda chamkati cha nyumbayo, chomwe ndi Malo Oyera Koposa, ndipo analiika pansi pa mapiko a akerubi.+ 8 Choncho mapiko a akerubiwo anali pamwamba pa Likasa, moti akerubiwo anaphimba Likasalo ndi mitengo yake yonyamulira.+ 9 Mitengo yonyamulirayo inali yaitali moti nsonga zake zinkaonekera ku Malo Oyera kutsogolo kwa chipinda chamkati, koma sizinkaonekera panja. Mitengoyo idakali pomwepo mpaka lero. 10 Mu Likasalo munalibe chinthu china chilichonse kupatulapo miyala iwiri yosema imene Mose anaikamo ku Horebe.+ Anaiikamo pa nthawi imene Yehova anachita pangano+ ndi Aisiraeli, pamene ankachoka mʼdziko la Iguputo.+
11 Pamene ansembe anatuluka mʼmalo oyera (chifukwa ansembe onse amene analipo anali atadziyeretsa,+ mosatengera magulu awo),+ 12 Alevi onse oimba+ a mʼgulu la Asafu,+ Hemani,+ Yedutuni+ ndiponso ana awo ndi abale awo, anavala zovala zabwino kwambiri atanyamula zinganga, zoimbira za zingwe ndi azeze ndipo anaimirira kumʼmawa kwa guwa lansembe pamodzi ndi ansembe okwana 120 oimba malipenga.+ 13 Pamene anthu oimba malipenga ndi oimba pakamwa ankaimba mogwirizana potamanda ndi kuthokoza Yehova, pamene mawu a malipenga, zinganga ndi zoimbira zina ankamveka, komanso pamene ankatamanda Yehova ndi mawu akuti, “chifukwa iye ndi wabwino, chikondi chake chokhulupirika chidzakhalapo mpaka kalekale,”+ mtambo unadzaza nyumbayo, nyumba ya Yehova.+ 14 Chifukwa cha mtambowo, ansembewo analephera kupitiriza kutumikira popeza ulemerero wa Yehova unadzaza nyumba ya Mulungu woona.+