Mawu a Yehova Ndi Amoyo
Mfundo Zazikulu za M’buku la Genesis—Chigawo Choyamba
DZINA lakuti “Genesis” limatanthauza “chiyambi.” Limeneli ndi dzina loyenerera la buku limene limafotokoza zimene zinachitika kuti chilengedwe chikhalepo, mmene dziko analikonzera kuti anthu akhalemo, ndiponso zimene zinachitika kuti anthu akhale padzikoli. Bukuli analemba ndi Mose m’chipululu cha Sinai, ndipo ayenera kuti anamaliza kulilemba mu 1513 B.C.E.
Buku la Genesis limatiuza mmene dziko linalili Chigumula chisanachitike, ndiponso zimene zinachitika Chigumula chitatha, pamene nyengo yatsopano inayamba. Limatiuzanso mmene Yehova Mulungu anachitira zinthu ndi Abrahamu, Isake, Yakobo, ndi Yosefe. Nkhani ino ifotokoza mfundo zazikulu za m’Genesis 1:1–11:9, kufika panthaŵi imene Yehova anayamba kuchita zinthu ndi kholo lakale, Abrahamu.
MMENE DZIKO LINALILI CHIGUMULA CHISANACHITIKE
Mawu oyamba a m’buku la Genesis akuti, “pachiyambi” akunena za kale kwambiri, zaka mabiliyoni ambiri m’mbuyomo. Zochitika za “masiku” asanu ndi aŵiri a kulenga, kapena kuti nyengo ya ntchito yolenga yapadera, azifotokoza monga mmene zikanaonekera kwa munthu woonerera akanakhala kuti analipo padziko lapansi. Pamapeto pa tsiku lachisanu ndi chimodzi, Mulungu analenga munthu. Ngakhale kuti Paradaiso anatayika pasanapite nthaŵi yaitali chifukwa cha kusamvera kwa anthu, Yehova anapereka chiyembekezo. Ulosi woyambirira wa m’Baibulo umanena za “mbewu” imene idzachotsa zotsatira za uchimo ndi kulalira mutu wa Satana.
M’zaka 1,600 zotsatira, Satana anakwanitsa kupatutsa anthu onse kuchoka kwa Mulungu kupatulapo anthu ochepa chabe okhulupirika monga Abele, Enoke, ndi Nowa. Mwachitsanzo, Kaini anapha mbale wake Abele amene anali wolungama. “Anthu anayamba kutchula dzina la Yehova,” ndipo mwachionekere anatero monyoza. Posonyeza mmene anthu panthaŵiyo analili achiwawa, Lameke analemba ndakatulo yofotokoza mmene anaphera mnyamata, n’kunena kuti anatero pofuna kudziteteza. Zinthu zinaipiraipira pamene angelo osamvera, ana a Mulungu, anakwatira akazi ndi kubala zimphona zotchedwa Anefili kapena kuti anthu akuluakulu. Komabe, Nowa wokhulupirika anamanga chingalawa, anachenjeza anthu ena molimba mtima za Chigumula chimene chinatsala pang’ono kuchitika, ndipo iye ndi banja lake anapulumuka chiwonongekocho.
Kuyankha Mafunso a M’Malemba:
1:16—Kodi Mulungu anapanga bwanji kuwala pa tsiku loyamba ngati anali asanapange zounikira kufika mpaka tsiku lachinayi? Liwu la Chihebri limene analimasulira kuti “anapanga” m’vesi 16 n’losiyana ndi liwu limene analimasulira kuti “adalenga” limene analigwiritsa ntchito pa Genesis chaputala 1, mavesi 1, 21 ndi 27. “Kumwamba” komwe kunalinso zounikira kunalengedwa kale, “tsiku loyamba” lisanayambe n’komwe. Koma kuwala kwa zounikirazo sikunkafika padziko lapansi. Patsiku loyamba, “kunayera” chifukwa chakuti kuwala koonekera mbali zonse kunadutsa m’mitambo ndipo kunayamba kuonekera padziko lapansi. Motero dzikoli, lomwe limazungulira, linayamba kukhala ndi usana ndi usiku. (Genesis 1:1-3, 5) Zomwe zinachititsa kuti kuyere sizinali kuonekabe padziko lapansi. Koma patsiku lachinayi la nyengo yolenga, zinthu zinasintha kwambiri. Dzuŵa, mwezi, ndi nyenyezi tsopano anazipanga “kuti ziunikire pa dziko lapansi.” (Genesis 1:17) “Mulungu anapanga” zimenezi m’lingaliro lakuti tsopano zinayamba kuoneka padziko lapansi.
3:8—Kodi Yehova Mulungu ankalankhula ndi Adamu mwachindunji? Baibulo limanena kuti pamene Mulungu ankalankhula ndi anthu, nthaŵi zambiri ankatero kudzera mwa mngelo kapena kuti mthenga. (Genesis 16:7-11; 18:1-3, 22-26; 19:1; Oweruza 2:1-4; 6:11-16, 22; 13:15-22) Wolankhulira wamkulu wa Mulungu anali Mwana wake wobadwa yekha, wotchedwa “Mawu.” (Yohane 1:1) Mulungu ayenera kuti analankhula kwa Adamu ndi Hava kudzera mwa ‘Mawuyo.’—Genesis 1:26-28; 2:16; 3:8-13.
3:17—Kodi nthaka inatembereredwa motani, ndipo kwanthaŵi yaitali bwanji? Kutembereredwa kwa nthaka kunatanthauza kuti kulima nthaka tsopano kukanakhala kovuta kwambiri. Mbadwa za Adamu zinamvetsa bwino zotsatira za kutembereredwa kwa nthaka, imene inabala minga ndi mitula, moti bambo ake a Nowa, Lameke, anatchulapo za “zovuta za manja athu, chifukwa cha nthaka imene anaitemberera Yehova.” (Genesis 5:29) Chigumula chitatha, Yehova anadalitsa Nowa ndi ana ake, ndipo anafotokoza cholinga Chake choti adzaze dziko lapansi. (Genesis 9:1) Mwachionekere, temberero la Mulungu pa nthaka linatha.—Genesis 13:10.
4:15—Kodi Yehova “anaika chizindikiro pa Kaini” motani? Baibulo silinena kuti Mulungu anaika chizindikiro pa thupi la Kaini mwa njira iliyonse. Chizindikirocho chiyenera kuti chinali lamulo lamphamvu limene ena analidziŵa ndi kulitsatira ndipo cholinga chake chinali chakuti iye asaphedwe pom’bwezera zimene anachita.
4:17—Kodi Kaini anapeza kuti mkazi wake? Adamu “anabala ana amuna ndi akazi.” (Genesis 5:4) Motero, Kaini anakwatira m’modzi mwa alongo ake kapena mwina m’modzi mwa ana aakazi a alongo ake. Patapita nthaŵi, Chilamulo chimene Mulungu anapereka kwa Aisrayeli sichinaloleze munthu kukwatira mlongo wake.—Levitiko 18:9.
5:24—Kodi Mulungu ‘anam’tenga Enoke’ motani? Mwachionekere, Enoke anali pangozi yoti aphedwa, koma Mulungu sanalole kuti adani ake amuphe. Mtumwi Paulo analemba kuti: “Enoke anatengedwa kuti angaone imfa.” (Ahebri 11:5) Zimenezi sizikutanthauza kuti Mulungu anam’tenga Enoke kupita naye kumwamba kumene anapitiriza kukhala ndi moyo. Yesu anali munthu woyamba kupita kumwamba. (Yohane 3:13; Ahebri 6:19, 20) ‘Kutengedwa kwa Enoke kuti angaone imfa’ kungatanthauze kuti Mulungu anam’chititsa kuona masomphenya aulosi ndiyeno n’kuchotsa moyo wake akadali m’masomphenyawo. Mwakuchita zimenezi, Enoke sanavutike, kapena ‘kuona imfa’ mwa kuphedwa ndi adani ake.
6:6—Kodi tinganene kuti Yehova “anamva chisoni” chifukwa cholenga munthu m’lingaliro lotani? Liwu la Chihebri limene analimasulira apa kuti “anamva chisoni” limatanthauza kusintha maganizo kapena zolinga. Yehova ndi wangwiro ndipo motero sanalakwitse polenga anthu. Komabe, iye anasintha maganizo ake okhudza anthu oipa amene analipo Chigumula chisanachitike. Mulungu anasintha maganizo ake okhala Mlengi wa anthu n’kukhala wowawononga chifukwa choipidwa ndi kuipa kwawo. Kupulumutsa kwake anthu ena kunasonyeza kuti anamva chisoni chifukwa cha anthu amene anali oipa okha basi.—2 Petro 2:5, 9.
7:2—Kodi anagwiritsa ntchito mfundo yotani posiyanitsa nyama zodyedwa ndi zosadyedwa? Mfundo imene anagwiritsa ntchito posiyanitsa nyamazo mwachionekere inali yokhudza kupereka nsembe polambira osati mfundo yakuti nyamayo ndi yoti anthu angadye kapena ayi. Chigumula chisanachitike, anthu sankadya nyama. Mawu akuti “zodyedwa” kapena “zosadyedwa” pankhani ya chakudya anagwira ntchito pa nthaŵi ya Chilamulo cha Mose yokha, ndipo zimenezi zinatha pamene anathetsa Chilamulocho. (Machitidwe 10:9-16; Aefeso 2:15) Mwachionekere, Nowa ankadziŵa nyama zimene zinali zoyenera kupereka nsembe polambira Yehova. Atangotuluka m’chingalawa, iye “anamanga guwa la nsembe la Yehova; natengapo nyama zodyedwa zonse ndi mbalame zodyedwa zonse napereka nsembe zopsereza paguwapo.”—Genesis 8:20.
7:11—Kodi madzi amene anachititsa Chigumula padziko lonse anachokera kuti? Mkati mwa nyengo yachiŵiri yolenga kapena kuti “tsiku,” pamene “thambo” la pamwamba pa dziko linalengedwa, panali madzi “pansi pa thambolo” ndiponso “pamwamba pa thambolo.” (Genesis 1:6, 7) Madzi amene anali ‘pansiwo’ ndi amene anali kale padziko lapansi. Madzi amene anali “pamwamba” anali chinyontho chachikulu chimene chinali mumlengalenga pamwamba pa dziko lapansi, chimene chinapanga “madzi akulu.” Madzi ameneŵa ndi amene anagwa padziko lapansi m’masiku a Nowa.
Zimene Tikuphunzirapo:
1:26. Popeza anthu tinapangidwa m’chifanizo cha Mulungu, tingathe kusonyeza makhalidwe a Mulungu. Inde, tiyenera kuyesetsa kukulitsa makhalidwe monga chikondi, chifundo, kukoma mtima, ubwino, ndi kuleza mtima, potsatira Amene anatipanga.
2:22-24. Mulungu ndi amene anayambitsa ukwati. Ukwati suyenera kutha ndiponso ndi wopatulika, ndipo mwamuna ndiye mutu wabanja.
3:1-5, 16-23. Kuti tikhale ndi chimwemwe pamoyo wathu tiyenera kusonyeza kuzindikira kuti Yehova ndiye woyenera kulamulira chilengedwe chonse.
3:18, 19; 5:5; 6:7; 7:23. Zimene Yehova amanena zimachitikadi.
4:3-7. Yehova anakondwera ndi nsembe ya Abele chifukwa chakuti Abele anali munthu wolungama ndiponso anali ndi chikhulupiriro. (Ahebri 11:4) Koma Kaini analibe chikhulupiriro, malinga ndi mmene zochita zake zinasonyezera. Ntchito zake zinali zoipa, anali wansanje, waudani, ndiponso wakupha. (1 Yohane 3:12) Ndiponso, ayenera kuti sanaikirepo mtima kwenikweni pa nsembe imene anapereka ndipo anangopereka mwamwambo chabe. Kodi pamenepa sitikuona kuti nsembe zathu zoyamika kwa Yehova tiyenera kuzipereka ndi mtima wonse ndiponso tiyenera kukhala ndi maganizo oyenera ndi khalidwe labwino?
6:22. Ngakhale kuti anatenga zaka zambiri kuti amange chingalawa, Nowa anachita zimene Mulungu anamulamula kuti achite. Motero, Nowa ndi banja lake anapulumutsidwa pamene Chigumula chinawononga. Yehova amalankhula nafe kudzera m’Mawu ake olembedwa ndiponso amapereka malangizo kudzera m’gulu lake. Kumvera kudzatipindulitsa ifeyo.
7:21-24. Yehova sawononga olungama pamodzi ndi oipa.
ANTHU ANALOŴA M’NYENGO YATSOPANO
Zinthu zonse zimene zinalipo Chigumula chisanachitike zitatha, anthu analoŵa m’nyengo yatsopano. Anawaloleza kudya nyama koma anawalamula kuti asale magazi. Yehova anakhazikitsa lamulo loti munthu wakupha mnzake nayenso aphedwe ndipo anaika pangano la utawaleza, kulonjeza kuti sadzabweretsanso Chigumula china. Ana atatu a Nowa anakhala makolo a anthu onse, koma mdzukulu wake, Nimrode, anakhala “mpalu wamphamvu pamaso pa Yehova.” M’malo moti afalikire ndi kudzaza dziko lapansi, anthu anaganiza zomanga mzinda wotchedwa Babele komanso nsanja kuti adzipangire dzina. Yehova analepheretsa zolinga zawo pamene anasokoneza chinenero chawo ndi kuwabalalitsa padziko lonse lapansi.
Kuyankha Mafunso a M’Malemba:
8:11—Ngati mitengo inawonongeka ndi Chigumula, kodi njiwa inakatenga kuti tsamba la azitona? Pangakhale mayankho aŵiri a zimene ziyenera kuti zinachitika. Popeza mtengo wa azitona ndi wolimba kwambiri, mwina unali ukadali moyo m’kati mwa madzi kwa miyezi ingapo m’nthaŵi ya Chigumula. Pamene madziwo anali kuphwera, mtengo wa azitona umene unamira ukanakhalanso panthaka youma ndipo ukanayamba kutulutsa masamba. Tsamba la azitona limene njiwa inapititsa kwa Nowa likhozanso kukhala kuti njiwayo inathyola pa mphukira ya azitona imene inatuluka madzi a chigumula atachepa.
9:20-25—N’chifukwa chiyani Nowa anatemberera Kanani? Kanani ayenera kuti anachita zonyansa kwa agogo ake, Nowa. Ngakhale kuti bambo a Kanani, Hamu, anaona zimenezi, sanam’letse mwana wawoyo m’malo mwake zikuoneka kuti anafalitsa nkhaniyo. Komabe, ana ena aŵiri a Nowa, Semu ndi Yafeti, anakafunditsa bambo awowo. Anadalitsidwa chifukwa cha zimenezi, koma Kanani anamutemberera, ndipo Hamu anavutika chifukwa cha manyazi amene anali pa mwana wake.
10:25—Kodi dziko lapansi “linagawanikana” motani m’masiku a Pelege? Pelege anakhala ndi moyo kuyambira mu 2269 mpaka mu 2030 B.C.E. Munali “m’masiku ake” pamene Yehova anagawanitsa anthu posokoneza chinenero cha anthu amene anali kumanga Babele ndi kuwabalalitsa padziko lonse lapansi. (Genesis 11:9) Motero, “dziko lapansi [kapena kuti anthu amene anali padziko lapansi] linagawanikana” m’masiku a Pelege.
Zimene Tikuphunzirapo:
9:1; 11:9. Palibe chilichonse chimene munthu angachite chimene chingalepheretse cholinga cha Yehova.
10:1-32. Nkhani ziŵiri zofotokoza mizere yobadwira, Chigumula chisanachitike ndiponso chitachitika, m’machaputala 5 ndi 10, zikugwirizanitsa anthu onse ndi munthu woyamba, Adamu, kudzera mwa ana atatu a Nowa. Asuri, Akaldayo, Ahebri, Aaramu, ndi mafuko ena a Aluya, ndiwo mbadwa za Semu. Aitiopiya, Aigupto, Akanani, ndi mafuko ena a ku Africa ndi a Aluya anachokera kwa Hamu. Anthu a m’mayiko a azungu anachokera kwa Yafeti. Anthu onse ndi apaubale ndipo onse amabadwa ali ofanana pamaso pa Mulungu. (Machitidwe 17:26) Mfundo yoona imeneyi iyenera kukhudza mmene timaonera ndiponso mmene timachitira zinthu ndi anthu ena.
Mawu a Mulungu ali ndi Mphamvu
Mbali yoyamba ya buku la Genesis ndiyo ili ndi nkhani yokhayo yolondola yofotokoza mbiri yoyambirira ya anthu. M’mbali imeneyi ya bukuli timapezamo cholinga cha Mulungu poika munthu padziko lapansi. N’zokhazika mtima pansi kuona kuti palibe zochita za anthu, monga zimene anachita Nimrode, zimene zingalepheretse cholinga chimenecho kuti chikwaniritsidwe.
Pamene mukuŵerenga Baibulo mlungu ndi mlungu pokonzekera Sukulu ya Utumiki wa Mulungu, kupenda zimene zafotokozedwa m’chigawo chakuti “Kuyankha Mafunso a M’Malemba,” zidzakuthandizani kumvetsa ndime zina za m’Malemba zovuta kwambiri. Mfundo za m’chigawo chakuti “Zimene Tikuphunzirapo,” zikusonyezani mmene mungapindulire pa kuŵerenga Baibulo kwa mlunguwo. Ngati n’koyenera, mungagwiritsenso ntchito mfundo zimenezi pa nkhani ya zosoŵa za pampingo pa Msonkhano wa Utumiki. Mawu a Yehova ndi amoyodi ndipo angakhale ndi mphamvu pa moyo wathu.—Ahebri 4:12.