Kalata Yopita kwa Aheberi
6 Choncho popeza tamaliza kuphunzira mfundo zoyambirira+ zokhudza Khristu, tiyeni tiyesetse mwakhama kuti tikhale aakulu mwauzimu.+ Tisayambe kuyalanso maziko, amene ndi kulapa ntchito zakufa, kukhulupirira Mulungu, 2 chiphunzitso chokhudza ubatizo, kuika manja,+ kuuka kwa akufa+ ndiponso chiweruzo chamuyaya. 3 Mulungu akalola, tiyesetsadi kuti tikule mwauzimu.
4 Pali anthu amene Mulungu anawaunikira,+ amene analandirapo mphatso yaulere yakumwamba, amene analandira mzimu woyera 5 komanso amene anamvapo mawu abwino a Mulungu ndi madalitso* amene adzaperekedwe padziko limene likubweralo. 6 Koma tsopano anthu amenewa anagwa+ ndipo nʼzosatheka kuwadzutsanso kuti alape, chifukwa akupachika kachiwiri Mwana wa Mulungu ndiponso kumunyoza poyera.+ 7 Nthaka imalandira madalitso kuchokera kwa Mulungu ikamwa madzi a mvula imene imagwera panthakapo kawirikawiri. Kenako imatulutsa zomera zimene zimathandiza amene ailima. 8 Koma ikatulutsa minga ndi zitsamba zobaya, imakanidwa ndipo imatsala pangʼono kutembereredwa. Mapeto ake imatenthedwa.
9 Koma ngakhale kuti tikulankhula chonchi, sitikukayikira kuti pa nkhani ya zinthu zobweretsa chipulumutso, inu okondedwa muli pabwino kusiyana ndi amene anagwa aja. 10 Chifukwa Mulungu si wosalungama kuti angaiwale ntchito yanu ndiponso chikondi chimene munachisonyeza pa dzina lake,+ potumikira oyera ndipo mukupitiriza kuwatumikira. 11 Koma tikufuna kuti nonsenu mupitirize kusonyeza khama limene munali nalo poyamba, kuti chiyembekezo chanu chikhale chotsimikizika+ mpaka mapeto.+ 12 Muchite zimenezi kuti musakhale aulesi,+ koma muzitsanzira anthu amene, chifukwa cha chikhulupiriro ndiponso kuleza mtima, akulandira zinthu zimene Mulungu analonjeza.
13 Pamene Mulungu analonjeza Abulahamu, analumbira pa dzina lake chifukwa panalibe wina wamkulu kuposa iyeyo amene akanamulumbirira.+ 14 Iye anati: “Ndithudi ndidzakudalitsa ndipo ndidzachulukitsa mbadwa zako.”+ 15 Choncho Abulahamu atasonyeza kuleza mtima, analandira lonjezo limeneli. 16 Chifukwa anthu polumbira amatchula winawake wamkulu kuposa iwowo, ndipo lumbiro lawo limathetsa mkangano uliwonse chifukwa lumbirolo limatsimikizira mwalamulo zomwe munthu wanena.+ 17 Mofanana ndi zimenezi, Mulungu anafuna kutsimikizira anthu olandira lonjezolo+ kuti chifuniro chake sichingasinthe. Choncho anachita kulumbira pa zimene analonjezazo. 18 Anachita zimenezo kuti pa zinthu ziwiri zosasinthika, zomwe chifukwa cha zimenezi nʼzosatheka kuti Mulungu aname,+ ife amene tathawira kumalo otetezeka tilimbikitsidwe nʼkumakhulupirira kwambiri* zinthu zimene tikuyembekezera. 19 Chiyembekezo chathuchi+ chili ngati nangula* wa miyoyo yathu ndipo nʼchotsimikizika komanso chokhazikika. Chiyembekezochi chimatilowetsa mkati, kuseri kwa katani yotchingira+ 20 kumene Yesu, yemwe ndi kalambulabwalo, anakalowa chifukwa cha ife.+ Iyeyu ndi mkulu wa ansembe mpaka kalekale mofanana ndi unsembe wa Melekizedeki.+