Genesis
18 Kenako Yehova+ anaonekera kwa Abulahamu pakati pa mitengo ikuluikulu ya ku Mamure.+ Pa nthawiyi nʼkuti Abulahamu atakhala pansi pakhomo la tenti yake masana dzuwa likuswa mtengo. 2 Atakweza maso, anaona amuna atatu ataima chapatali ndi iye.+ Atawaona, ananyamuka pakhomo la tentiyo nʼkuthamanga kukakumana nawo. Atafika, anagwada nʼkuwerama mpaka nkhope yake pansi. 3 Ndiyeno anati: “Yehova, ngati mungandikomere mtima, chonde, musangondipitirira ine mtumiki wanu. 4 Dikirani pangʼono tibweretse madzi kuti tikusambitseni mapazi.+ Kenako mupumeko pansi pa mtengo. 5 Popeza mwafika kwa mtumiki wanu, ndiloleni ndikubweretsereni kachakudya kuti mupezenso mphamvu. Kenako mukhoza kupitiriza ulendo wanu.” Pamenepo iwo anati: “Chabwino, chita mmene waneneramo.”
6 Choncho Abulahamu anathamangira kutenti kumene kunali Sara nʼkumuuza kuti: “Fulumira! Tenga ufa wosalala wokwana miyezo itatu,* uukande nʼkupanga mikate.” 7 Kenako Abulahamu anathamangira kumene kunali ziweto, nʼkusankha ngʼombe yaingʼono yamphongo yabwino kwambiri. Atatero, anaipereka kwa mtumiki wake, ndipo iye anaikonza mwamsanga. 8 Ndiyeno Abulahamu anatenga mafuta amumkaka, mkaka ndi ngʼombe yaingʼono yamphongo imene anakonza ija nʼkukaziika pamene panali alendowo. Atatero iye anaimirira chapafupi pa nthawi imene alendowo ankadya atakhala pansi pa mtengo.+
9 Alendowo anamufunsa kuti: “Kodi mkazi wako Sara ali kuti?”+ Iye anayankha kuti: “Ali mutentimu.” 10 Ndiyeno mmodzi wa iwo anati: “Ndithu ndidzabweranso kwa iwe chaka chamawa nthawi ngati yomwe ino, ndipo Sara mkazi wako adzakhala ndi mwana wamwamuna.”+ Pa nthawiyi nʼkuti Sara akumvetsera ali pakhomo la tenti imene inali kumbuyo kwa mlendoyo. 11 Abulahamu ndi Sara anali okalamba ndipo anali ndi zaka zambiri.+ Sara anali atadutsa msinkhu woti nʼkubereka mwana.+ 12 Choncho Sara anayamba kuseka mumtima mwake nʼkunena kuti: “Kodi mmene ndatheramu komanso mmene mbuyanga wakalambiramu, zoona ndingakhaledi ndi mwayi wobereka mwana?”+ 13 Ndiyeno Yehova anafunsa Abulahamu kuti: “Nʼchifukwa chiyani Sara waseka nʼkunena kuti, ‘Kodi nʼzoona kuti ineyo, mmene ndakalambiramu, ndingaberekedi mwana?’ 14 Kodi pali chosatheka ndi Yehova?+ Ndidzabweranso kwa iwe pa nthawi ngati yomwe ino chaka chamawa, ndipo Sara adzakhala ndi mwana wamwamuna.” 15 Koma Sara anachita mantha nʼkukana kuti: “Sindinaseketu ine!” Koma mlendoyo anati: “Inde! Unaseka iwe.”
16 Amunawo ananyamuka kuti azipita ndipo Abulahamu anawaperekeza. Atafika pamalo ena amunawo anayangʼana ku Sodomu.+ 17 Kenako Yehova anati: “Bwanji ndimuuze Abulahamu zimene ndikufuna kuchita?+ 18 Pajatu Abulahamu adzakhala mtundu waukulu ndi wamphamvu, ndipo mitundu yonse yapadziko lapansi idzadalitsidwa kudzera mwa iye.+ 19 Ndapalana ubwenzi ndi Abulahamu kuti aphunzitse ana ake ndi mbadwa zake zonse* kuyenda mʼnjira ya Yehova. Azichita zimenezi pochita zabwino ndi zachilungamo+ kuti Yehova adzakwaniritse zimene ananena zokhudza Abulahamu.”
20 Kenako Yehova anati: “Ndamva madandaulo ambiri+ akuti machimo a anthu amene akukhala mʼmizinda ya Sodomu ndi Gomora ndi oipa kwambiri.+ 21 Ndiye ndipitako kuti ndikaone ngati akuchitadi zimene ndamvazo. Ndikufuna ndidziwe ngati zochita zawo zilidi zoipa choncho.”+
22 Kenako amunawo anachoka pamalowo nʼkulowera ku Sodomu, koma Yehova+ anatsala ndi Abulahamu. 23 Zitatero Abulahamu anamuyandikira nʼkumufunsa kuti: “Kodi zoona muwonongadi olungama pamodzi ndi oipa?+ 24 Bwanji ngati mumzindamo mutapezeka anthu olungama 50? Kodi muwawonongabe, osakhululukira mzindawo chifukwa cha olungama 50 amenewo? 25 Simungachite zimenezo, simungaphe munthu wolungama limodzi ndi woipa. Sizingatheke kuti wolungama alangidwe limodzi ndi woipa.+ Simungachite zimenezo.+ Ndinu Woweruza wa dziko lonse lapansi. Ndiye kodi simuchita chilungamo?”+ 26 Pamenepo Yehova anayankha kuti: “Ngati ndingapeze anthu olungama 50 mu Sodomu, ndikhululukira mzinda wonsewo chifukwa cha iwo.” 27 Koma Abulahamu anapitiriza kuti: “Pepanitu, musaone ngati ndatha mantha kulankhula ndi Yehova pamene ndine fumbi komanso phulusa. 28 Nanga bwanji pa olungama 50 aja pataperewera 5, kodi muwononga mzinda wonsewo chifukwa choti paperewera anthu 5?” Pamenepo iye anayankha kuti: “Sindiwononga mzindawo ndikapezamo olungama 45.”+
29 Koma iye anafunsabe kuti: “Nanga mutapezeka 40?” Iye anayankha kuti: “Sindingawononge chifukwa cha 40 amenewo.” 30 Iye anapitiriza kuti: “Chonde Yehova, musandipsere mtima,+ koma ndiloleni ndilankhulebe. Nanga atapezeka 30 okha?” Iye anayankha kuti: “Sindiwononga ndikapezamo 30.” 31 Iye anapitirizabe kuti: “Pepani, musaone ngati ndatha mantha kulankhula ndi Yehova. Nanga mutapezeka 20 okha?” Iye anayankha kuti: “Sindiwononga mzindawo chifukwa cha 20 amenewo.” 32 Pomaliza anati: “Pepanitu Yehova, musandipsere mtima, ndiloleni ndilankhule komaliza kokha. Nanga mutapezeka 10 okha?” Iye anayankha kuti: “Sindiwononga mzindawo chifukwa cha 10 amenewo.” 33 Yehova atamaliza kulankhula ndi Abulahamu, ananyamuka nʼkumapita,+ ndipo Abulahamu anabwerera kwawo.