Tumikirani Yehova Masiku Oipa Asanafike
“Kumbukira Mlengi wako Wamkulu.”—MLAL. 12:1.
1, 2. (a) Kodi Yehova anauzira Solomo kuti alembe malangizo otani opita kwa achinyamata? (b) N’chifukwa chiyani Akhristu achikulire amene ali ndi zaka zoposa 50 ayeneranso kuganizira malangizo a Solomo amenewo?
YEHOVA anauzira Mfumu Solomo kuti alembe mawu olimbikitsa achinyamata akuti: “Kumbukira Mlengi wako Wamkulu masiku a unyamata wako, asanafike masiku oipa.” Kodi ‘masiku oipawo’ ndi ati? Solomo anafotokoza zimene zimachitika m’masiku ovuta a ukalamba. Pogwiritsa ntchito mawu okuluwika, iye ananena kuti manja amanjenjemera, miyendo imagwedera, mano amaguluka, maso saona bwino, makutu samva bwino, tsitsi limachita imvi ndipo msana umapindika. Munthu sayenera kudikira kuti afike zaka zimenezo kuti adzayambe kutumikira Yehova.—Werengani Mlaliki 12:1-5.
2 Akhristu ambiri amene ali ndi zaka zoposa 50 adakali ndi mphamvu. N’kutheka kuti ali ndi imvi, koma sanayambe kukumana ndi mavuto amene Solomo anafotokoza. Kodi Akhristu achikulirewa angapindulenso ndi malangizo amene Solomo analembera achinyamata akuti: “Kumbukira Mlengi wako Wamkulu”? Kodi malangizowa akutanthauza chiyani?
3. Kodi tingakumbukire bwanji Mlengi wathu Wamkulu?
3 Ngakhale kuti tatumikira Yehova kwa zaka zambiri, ndi bwino nthawi ndi nthawi kumaganizira za Mlengi wathu Wamkulu. Iye anatilenga modabwitsa moti sitingamvetse zonse zokhudza moyo wathu. Yehova anatipatsa zinthu zosiyanasiyana zimene tingasangalale nazo pa moyo wathu. Tikamaganizira zimene analenga, timamvetsa kuzama kwa chikondi, nzeru komanso mphamvu zake. (Sal. 143:5) Koma kukumbukira Mlengi wathu Wamkulu kumaphatikizaponso kuganizira zimene tiyenera kuchita pomutumikira. Kuganizira za Mlengi wathu kumatithandiza kumuyamikira kwambiri. Choncho timafunitsitsa kuchita zonse zimene tingathe pomutumikira pa moyo wathu wonse.—Mlal. 12:13.
ACHIKULIRE ALI NDI MWAYI WAPADERA
4. Kodi Akhristu achikulire angadzifunse funso liti, ndipo n’chifukwa chiyani angatero?
4 Ngati ndinu wachikulire ndipo mwachita zambiri pa moyo wanu, mungachite bwino kudzifunsa kuti, ‘Kodi ndizichita chiyani panopa, ndidakali ndi mphamvu?’ Popeza kuti ndinu Mkhristu wachikulire, muli ndi mwayi umene anthu ena alibe. Mungaphunzitse achinyamata zimene mwaphunzira kuchokera kwa Yehova. Mungalimbikitse anthu ena powauza zinthu zosangalatsa zimene mwakumana nazo potumikira Mulungu. Mfumu Davide anapemphera kuti akhale ndi mwayi wochita zimenezi. Iye analemba kuti: “Inu Mulungu, mwandiphunzitsa kuyambira pa unyamata wanga . . . Ngakhale nditakalamba ndi kumera imvi, inu Mulungu musandisiye, kufikira nditanena za dzanja lanu lamphamvu ku m’badwo wotsatira, kufikira nditanena za mphamvu zanu kwa onse obwera m’tsogolo.”—Sal. 71:17, 18.
5. Kodi Akhristu achikulire angaphunzitse bwanji anthu ena zimene iwo aphunzira?
5 Kodi mungaphunzitse bwanji anthu ena zinthu zimene mwaphunzira pa zaka zonse zimene mwakhala ndi moyo? Mukhoza kuitana Akhristu achinyamata kuti abwere kunyumba kwanu kudzacheza. Kapena mungawapemphe kuti ayende nanu mu utumiki kuti aone mmene mukusangalalira potumikira Yehova. M’nthawi ya Yobu, Elihu anati: “Masiku alankhule. Zaka zambiri n’zimene ziyenera kudziwitsa anthu nzeru.” (Yobu 32:7) Mtumwi Paulo analimbikitsa akazi achikulire kuti azilimbikitsa ena ndi mawu awo komanso chitsanzo chawo. Iye analemba kuti: “Akazi achikulire . . . akhale aphunzitsi a zinthu zabwino.”—Tito 2:3.
GANIZIRANI MMENE MUNGATHANDIZIRE ENA
6. N’chifukwa chiyani Akhristu amene achita zambiri pa moyo wawo ayenera kudziona kuti ndi amtengo wapatali?
6 Ngati mwatumikira Mulungu kwa nthawi yaitali, mungathandize kwambiri anthu ena. Ganizirani zinthu zimene mukudziwa panopa zomwe simunkazidziwa zaka 30 kapena 40 zapitazo. Mumatha kugwiritsa ntchito bwino mfundo za m’Baibulo pa moyo wanu. Ndipo mosakayikira, muli ndi luso lofika anthu pamtima pophunzitsa Mawu a Mulungu. Ngati ndinu mkulu, ndiye kuti mukudziwa mmene mungathandizire abale omwe akulowera njira yolakwika. (Agal. 6:1) N’kutheka kuti mwaphunzira kuyang’anira zinthu mumpingo, m’madipatimenti a pamsonkhano kapena pa ntchito yomanga Nyumba za Ufumu. Mwina muli ndi luso lolankhula ndi madokotala kuti athandize odwala popanda kuwaika magazi. N’zoona kuti achikulire ena angoyamba kumene kutumikira Mulungu, komabe aphunzira zinthu zambiri pa moyo wawo. Mwachitsanzo ngati alerapo ana, akudziwa zambiri pa nkhani imeneyi. Akhristu achikulire angalimbikitse kwambiri anthu a Yehova. Iwo angachite zimenezi powaphunzitsa, kuwatsogolera ndi kuwalimbikitsa.—Werengani Yobu 12:12.
7. Kodi Akhristu achikulire angaphunzitse achinyamata zinthu ziti?
7 Kodi mungatani kuti muthandize kwambiri anthu ena? Mwina mungasonyeze achinyamata mmene angayambitsire ndiponso kuchititsa maphunziro a Baibulo. Ngati ndinu mlongo, mungathandize alongo achitsikana powasonyeza zimene angachite kuti atumikire bwino Mulungu komanso kusamalira ana awo aang’ono. Ngati ndinu m’bale, mungaphunzitse abale achinyamata kuti azikamba nkhani zogwira mtima komanso kuti akhale aluso polalikira uthenga wabwino. Mungayende nawo limodzi popita kwa abale ndi alongo achikulire kuti mukawalimbikitse mwauzimu. Ngakhale kuti panopa mulibe mphamvu ngati kale, muli ndi mwayi waukulu wophunzitsa achinyamata. Mawu a Mulungu amati: “Kukongola kwa anyamata ndiko mphamvu zawo, ndipo ulemerero wa anthu okalamba ndiwo imvi zawo.”—Miy. 20:29.
MUNGAKATUMIKIRE KUDERA LIMENE KULIBE OFALITSA OKWANIRA
8. Kodi mtumwi Paulo anachita chiyani ali wachikulire?
8 Mtumwi Paulo ali wachikulire, anachita zonse zimene akanatha potumikira Mulungu. Pofika mu 61 C.E. pamene anatuluka m’ndende ku Roma, iye anali atakhala mmishonale kwa zaka zambiri ndipo anapirira mavuto osiyanasiyana. Choncho akanatha kungokhala ku Roma n’kumalalikira kumeneko. (2 Akor. 11:23-27) Abale a mumzinda waukuluwu akanayamikira kwambiri kutumikira limodzi ndi Paulo. Koma iye anaona kuti anthu olalikira uthenga wabwino ankafunikanso kwambiri kumayiko ena. Choncho iye anapitiriza ntchito yake yaumishonale limodzi ndi Timoteyo komanso Tito. Iwo anapita ku Efeso kenako ku Kerete ndiponso mwina ku Makedoniya. (1 Tim. 1:3; Tito 1:5) Ankafunanso kupita ku Sipaniya, koma sitikudziwa ngati anapitadi.—Aroma 15:24, 28.
9. Kodi n’kutheka kuti Petulo anasamuka ali ndi zaka zingati kuti akatumikire kudziko lina? (Onani chithunzi patsamba 22.)
9 N’kutheka kuti mtumwi Petulo anali ndi zaka zoposa 50 pamene anasamukira kudera limene kunalibe olalikira okwanira. N’chifukwa chiyani tikutero? Ngati iye anali ndi zaka zofanana ndi Yesu kapena kuposerapo pang’ono, ndiye kuti anali ndi zaka pafupifupi 50 pamene anasonkhana ndi atumwi ena ku Yerusalemu mu 49 C.E. (Mac. 15:7) Nthawi ina pambuyo pa msonkhanowu, Petulo anasamukira ku Babulo. Ayenera kuti anapita kumeneko kuti akalalikire Ayuda ambiri omwe ankakhala mumzindawu. (Agal. 2:9) Iye ankakhala kumeneko pamene analemba kalata yake yoyamba cha m’ma 62 C.E. (1 Pet. 5:13) N’zoona kuti kutumikira kudziko lina kungakhale kovuta. Komabe ngakhale kuti Petulo anali wachikulire, zimenezi sizinamulepheretse kuchita zambiri potumikira Yehova.
10, 11. Fotokozani za munthu wina wachikulire amene anasamuka kwawo kuti akathandize kudera lina.
10 Masiku anonso, Akhristu ambiri amene ali ndi zaka zoposa 50 amaona kuti zinthu zasintha pa moyo wawo ndipo akhoza kutumikira Yehova m’njira zinanso. Ena asamukira kudera limene kulibe ofalitsa okwanira. Mwachitsanzo, m’bale wina dzina lake Robert analemba kuti: “Ine ndi mkazi wanga tinali ndi zaka zoposa 50 pamene tinaona kuti tili ndi mwayi wochita zambiri mu utumiki. Mwana wathu anali atachoka pakhomo, tinalibe makolo ofunika kuwasamalira ndiponso tinali titalandira ndalama zamasiye. Ndinaona kuti tikagulitsa nyumba yathu tikhoza kubweza ngongole n’kutsalabe ndi ndalama zina. Ndalama zotsalazo zinali zokwanira kuti tizigula zinthu zofunika pa moyo mpaka titayamba kulandira ndalama za penshoni. Tinauzidwa kuti kudziko la Bolivia kuli anthu ambiri ofuna kuphunzira Baibulo komanso zinthu si zodula kumeneko. Choncho tinaganiza zosamuka. Koma kuzolowera moyo wa kumeneko sikunali kophweka. Zinthu zonse zinali zosiyana kwambiri ndi za kwathu ku North America. Komabe tinapeza madalitso ambiri.”
11 Robert anati: “Panopa timatanganidwa nthawi zonse ndi zinthu za mumpingo kapena zokhudza utumiki. Anthu ena amene tinaphunzira nawo Baibulo anabatizidwa. Banja lina limene tinaphunzira nalo ndi losauka ndipo limakhala kumudzi wakutali kwambiri. Koma mlungu uliwonse iwo amayenda ulendo wovuta wa makilomita ambiri kuti afike kutauni kumene timasonkhana. Timasangalala kwambiri poona kuti banjali likuyesetsa kutumikira Yehova komanso kuti mwana wawo wamkulu wayamba upainiya.”
MUNGACHITE ZAMBIRI POLALIKIRA ANTHU OLANKHULA CHINENERO CHINA
12, 13. Fotokozani za Mkhristu wina amene anayamba kutumikira Yehova m’njira zinanso atapuma pa ntchito.
12 Abale ndi alongo achikulire angathandize kwambiri mipingo ndiponso magulu omwe amalalikira anthu olankhula chinenero china. Kulalikira anthu amenewa kungakhale kosangalatsa kwambiri. Mwachitsanzo, m’bale wina wa ku Britain, dzina lake Brian, analemba kuti: “Nditakwanitsa zaka 65 ndinapuma pa ntchito. Koma ine ndi mkazi wanga tinkaona kuti tikusowa zinazake pa moyo wathu. Ana athu anali atachoka pakhomo ndipo mu utumiki sitinkapeza anthu ofuna kuphunzira Baibulo. Kenako ndinakumana ndi mnyamata wina wa ku China amene ankachita maphunziro ake payunivesite ina ya pafupi ndi kwathu. Iye anavomera kubwera kumisonkhano ndipo ndinayamba kuphunzira naye Baibulo. Patapita milungu ingapo, anayamba kubwera ndi mnzake wina wa ku China. Patapitanso milungu ina iwiri, anabwera ndi munthu wina wachitatu kenako anadzabwera ndi winanso wachinayi.”
13 Brian anati: “Kenako munthu winanso wa nambala 5 amene ankaphunzira payunivesiteyi anapempha kuti ndiziphunzira naye Baibulo. Pa nthawiyo, ndinayamba kuganiza kuti, ‘Kukhala ndi zaka 65 sikukutanthauza kuti ndiyenera kupuma pa ntchito ya Yehova ayi.’ Choncho ndinafunsa mkazi wanga, yemwe anali ndi zaka 63, ngati angafune kuphunzira Chitchainizi. Tinaphunzira chinenerochi pogwiritsa ntchito matepi. Tinachita zimenezo zaka 10 zapitazo. Kulalikira anthu olankhula chinenero china kunatithandiza kumva ngati tidakali achinyamata. Pofika pano taphunzira Baibulo ndi anthu 112 olankhula Chitchainizi. Ambiri a iwo afikapo pa misonkhano. Wina ndi mpainiya ndipo tikutumikira naye limodzi.”
MUZICHITA MOSANGALALA ZIMENE MUNGATHE
14. (a) Kodi Akhristu achikulire ayenera kusangalala ndi chiyani? (b) Kodi chitsanzo cha Paulo chingawalimbikitse bwanji?
14 Ngakhale kuti Akhristu ambiri a zaka zoposa 50 angathe kuchita zambiri potumikira Yehova, pali ena amene sangathe. Ena amadwaladwala ndipo ena akulera ana kapena kusamalira makolo awo okalamba. Iwo ayenera kukhala osangalala podziwa kuti Yehova amayamikira zilizonse zimene akuchita pomutumikira. Choncho m’malo motaya mtima chifukwa cholephera kuchita zinazake, muzisangalala kuchita zimene mungathe. Ganizirani chitsanzo cha mtumwi Paulo. Kwa zaka zambiri, iye anali paukaidi wosachoka panyumba ndipo sankathanso kuchita umishonale wake. Koma anthu akabwera kudzamuona, ankakambirana nawo mfundo za m’Malemba ndiponso kuwalimbikitsa.—Mac. 28:16, 30, 31.
15. N’chifukwa chiyani timaona kuti Akhristu achikulire ndi amtengo wapatali?
15 Yehova amayamikira zimene achikulire akuchita pomutumikira. N’zoona kuti Solomo ananena kuti nthawi yovuta ya ukalamba si nthawi yabwino. Komabe, Mulungu amaona kuti zimene Akhristu achikulire akuchita pomutamanda n’zamtengo wapatali kwambiri. (Luka 21:2-4) Abale ndi alongo amayamikira kwambiri chitsanzo cha achikulire amene atumikira Yehova mokhulupirika kwa nthawi yaitali.
16. Kodi Anna analibe mwayi wochita zinthu ziti, koma ankatha kuchita chiyani polambira Mulungu?
16 Baibulo limanena za mayi wina wachikulire dzina lake Anna amene anapitiriza kutamanda Yehova mokhulupirika mpaka atakalamba. Pamene Yesu ankabadwa n’kuti Anna ali ndi zaka 84 ndipo anali wamasiye. Koma ayenera kuti anamwalira pasanathe nthawi yaitali. Choncho sanakhale wotsatira wa Yesu, sanadzozedwe ndi mzimu woyera kapena kukhala ndi mwayi wolalikira uthenga wabwino wa Ufumu. Koma Anna ankasangalala kuchita zimene angathe. Paja Baibulo limati: “Sanali kusowa pakachisi. Anali kuchita utumiki wopatulika usana ndi usiku.” (Luka 2:36, 37) Ansembe ankapereka nsembe zofukiza m’kachisi m’mawa ndi madzulo tsiku lililonse. Pa nthawiyi, Anna ayenera kuti ankakhala m’bwalo la kachisi pamodzi ndi anthu ena ndipo ankapemphera chamumtima kwa pafupifupi mphindi 30. Ataona Yesu ali wakhanda, Anna anayamba kulankhula “za mwanayo kwa onse amene anali kuyembekezera chipulumutso cha Yerusalemu.”—Luka 2:38.
17. Kodi tingathandize bwanji Akhristu achikulire komanso odwaladwala kuti nawonso azitumikira Mulungu?
17 Masiku ano, tiyenera kuthandiza Akhristu achikulire kapena odwaladwala. Ena amafunitsitsa kupezeka pa misonkhano ya mpingo komanso ikuluikulu koma sangakwanitse. M’madera ena, amakonza zoti achikulirewo azimvetsera misonkhano ya mpingo kudzera pa telefoni. Koma m’madera ena, zimenezi sizingatheke. Ngakhale zili choncho, Akhristu amene sangakwanitse kupezeka pa misonkhano akhoza kuchita zinthu zina potumikira Mulungu. Mwachitsanzo, mapemphero awo amathandiza kuti zinthu ziziyenda bwino mumpingo wachikhristu.—Werengani Salimo 92:13, 14.
18, 19. (a) Kodi Akhristu achikulire angalimbikitse bwanji ena? (b) Kodi ndi ndani amene ayenera kutsatira malangizo akuti: “Kumbukira Mlengi wako Wamkulu”?
18 Mwina Akhristu achikulire sakudziwa kuti amalimbikitsa kwambiri ena. Mwachitsanzo, taona kuti Anna anali wokhulupirika kwa zaka zambiri ndipo ankapezeka pakachisi nthawi zonse. Koma mwina iye sankadziwa kuti zimene akuchitazo zidzalimbikitsa ena mpaka m’tsogolo. Zimene Anna ankachita posonyeza kuti amakonda Yehova zinalembedwa m’Malemba. Mosakayikira Akhristu anzanu sadzaiwalanso zimene mukuchita posonyeza kuti mumakonda Mulungu. N’chifukwa chake Mawu a Mulungu amanena kuti: “Imvi ndizo chisoti chachifumu cha ulemerero zikapezeka m’njira yachilungamo.”—Miy. 16:31.
19 Tonsefe tili ndi zinthu zina zimene sitingakwanitse kuchita potumikira Yehova. Komabe, tonse amene tidakali ndi mphamvu tizikumbukira mawu opezeka m’Baibulo akuti: “Kumbukira Mlengi wako Wamkulu . . . asanafike masiku oipa.”—Mlal. 12:1.