Mawu a Yehova Ndi Amoyo
Mfundo Zazikulu za M’buku la Miyambo
MFUMU SOLOMO ya Israyeli wakale ‘inanena miyambo zikwi zitatu.’ (1 Mafumu 4:32) Kodi tili ndi mwayi wodziwa miyambi yake yanzeruyo? Inde tili nawo. Buku la m’Baibulo la Miyambo, limene linamalizidwa kulembedwa cha m’ma 717 B.C.E., lili ndi miyambi yambiri ya Solomo. Machaputala awiri okha omalizira ndi amene analembedwa ndi anthu ena, Aguri mwana wa Yake ndi mfumu Lemueli. Komabe, ena amakhulupirira kuti Lemueli ndi dzina lina la Solomo.
Miyambi youziridwa yomwe inaikidwa pamodzi m’buku la Miyambo ili ndi zolinga ziwiri, zomwe ndi ‘kudziwitsa nzeru ndi mwambo.’ (Miyambo 1:2) Miyambi imeneyi imatithandiza kukhala ndi nzeru, limene lili luso lotha kuona zinthu bwino ndi kugwiritsa ntchito zimene tikudziwa pothetsa mavuto. Komanso, imatipatsa mwambo, ndiponso imatiphunzitsa makhalidwe abwino. Kulabadira miyambi imeneyi ndiponso kumvera malangizo ake kungakhudze mtima wathu, kungatithandize kukhala achimwemwe, ndipo tingapambane.—Ahebri 4:12.
‘TENGA NZERU NDI KUGWIRA MWAMBO’
Solomo anati: “Nzeru ifuula panja.” (Miyambo 1:20) N’chifukwa chiyani tiyenera kumvetsera mawu ake omveka bwinowo? Chaputala 2 chikunena za phindu losaneneka limene tingapeze chifukwa chotenga nzeru. Chaputala 3 chikufotokoza mmene tingachitire ubwenzi ndi Yehova. Kenako, Solomo akuti: “Nzeru ipambana, tatenga nzeru; n’kutenga kwako konseko utenge luntha. Gwira mwambo, osauleka.”—Miyambo 4:7, 13.
Kodi n’chiyani chingatithandize kupewa njira zoipa za dziko? Chaputala 5 cha Miyambo chimayankha kuti: Gwiritsa ntchito luso la kulingalira, ndipo dziwa njira zokopa za dziko. Komanso taganizirani zotsatirapo zoopsa za kuchita chiwerewere. Chaputala chotsatira chikuchenjeza za zizolowezi ndi maganizo amene amaika pangozi ubwenzi wathu ndi Yehova. Chaputala 7 chikusonyeza bwino kwambiri mmene munthu wachiwerewere amachitira zinthu. Chaputala 8, chikufotokoza mosangalatsa kwambiri kufunika ndiponso kukoma kwake kokhala ndi nzeru. Zimene zakambidwa kale zikutsirizidwa mochititsa chidwi m’chaputala 9, ndipo zikufotokozedwa monga fanizo losangalatsa limene likutilimbikitsa kulondola nzeru.
Kuyankha Mafunso a M’Malemba:
1:7; 9:10—Kodi kuopa Yehova kungakhale “chiyambi cha kudziwa” ndiponso “chiyambi cha nzeru” mwanjira yotani? Sitingadziwe chilichonse ngati sitiopa Yehova, chifukwa iye ndi Mlengi wa zinthu zonse ndiponso ndi Mlembi wa Malemba Oyera. (Aroma 1:20; 2 Timoteo 3:16, 17) Iye ndiye Gwero la chidziwitso chonse cholondola. Motero, kuzindikira kumayamba ndi mantha aulemu kwa Yehova. Kuopa Mulungu kulinso ndi chiyambi cha nzeru chifukwa sitingakhale ndi nzeru ngati sitizindikira. Kuwonjezera apo, munthu amene saopa Yehova sangathe kugwiritsa ntchito zilizonse zimene iye amadziwa kuti alemekeze Mlengi.
2:16—N’chifukwa chiyani mkazi wachiwerewere amatchedwa “mkazi wachilendo”? Miyambo 2:17 imapitiriza kufotokoza “mkazi wachilendo” ngati munthu amene ‘waiwala chipangano cha Mulungu wake.’ Aliyense amene anali kulambira milungu yonyenga kapena amene ankanyalanyaza Chilamulo cha Mose, kuphatikizapo mkazi wachiwerewere, anali kutchedwa mlendo.—Yeremiya 2:25; 3:13.
7:1, 2—Kodi “mawu anga” ndiponso “malangizo anga” akuphatikizapo chiyani? Kuwonjezera pa zimene Baibulo limaphunzitsa, akuphatikizapo malamulo kapena malangizo a m’banja, amene makolo amapereka kuti anthu a m’banjamo apindule nawo. Achinyamata amafunika kumvera malamulo amenewa komanso zinthu zochokera m’Malemba zimene makolo awo amawaphunzitsa.
8:30—Kodi ndani amene ali “mmisiri”? Nzeru imene inafotokozedwa monga munthu imadzitcha kukhala mmisiri. M’malo mongokhala ngati kalembedwe kokometsera kofotokoza mmene nzeru ilili, nzeru yofotokozedwa monga munthu imeneyi imaimira Mwana woyamba kubadwa wa Mulungu, Yesu Kristu, asanakhale munthu. Kalekale asanabadwe ngati munthu padziko lapansi, iye ‘anali ndi Mulungu poyamba njira yake.’ (Miyambo 8:22) Monga “mmisiri,” anali kugwira ntchito ndi Atate wake polenga zinthu zonse.—Akolose 1:15-17.
9:17—Kodi “madzi akuba” n’chiyani ndipo n’chifukwa chiyani ‘amatsekemera’? Popeza kuti Baibulo limayerekezera kusangalala ndi kugonana kumene kumachitika muukwati ndi kumwa madzi otsitsimula otungidwa pachitsime, madzi akuba akuimira kuchita zachiwerewere mobisa. (Miyambo 5:15-17) Maganizo ochita zachiwerewere popanda kugwidwa ndiwo amene amachititsa kuti madzi oterowo azioneka ngati otsekemera.
Zimene Tikuphunzirapo:
1:10-14. Tiyenera kupewa kukopeka ndi njira zoipa za anthu ochimwa chifukwa cha malonjezo awo oti tidzapeza chuma.
3:3. Tiyenera kuona kuti kukhala wokoma mtima mwachikondi ndi wachoonadi ndi makhalidwe amtengo wapatali, ndipo tiyenera kuwasonyeza ngati mmene tingachitire ndi mkanda wa pakhosi womwe uli wokwera mtengo. Tikufunikiranso kukhomereza makhalidwe amenewa pamtima pathu, kuwachititsa kukhala mbali yaikulu ya moyo wathu.
4:18. Kamvetsedwe ka zinthu zauzimu kamawonjezeka pang’ono ndi pang’ono. Kuti tikhalebe m’kuunika, tiyenera kupitiriza kukhala odzichepetsa ndi ofatsa.
5:8. Tiyenera kupewa chilichonse chimene chingatisonkhezere kukhala ndi makhalidwe alionse oipa, kaya ndi nyimbo, zosangalatsa, Intaneti, kapenanso mabuku ndi magazini.
5:21. Kodi munthu amene amakonda Yehova angasinthitse ubwenzi wake wabwino ndi Mulungu woona ndi nthawi yochepa ya zosangalatsa? Ayi ndithu. Timalimbikitsidwa kwambiri kupitiriza kukhala ndi makhalidwe abwino chifukwa chodziwa kuti Yehova amaona njira zathu ndipo adzatiimba mlandu pa chilichonse chimene tingachite.
6:1-5. M’mavesi amenewa, tapezamo malangizo abwino opewera ‘kuperekera mnzako chikole,’ kapena kuti kuchita malonjezo opanda nzeru oimira munthu wina akamabwereka ndalama. Ngati pambuyo pofufuza mosamala kwambiri, taona kuti zinthu zimene tachitazo zikuoneka kuti n’zopanda nzeru, nthawi yomweyo tiyenera ‘kum’dandaulira mnzathu’ pom’pempha mosaleka ndiponso kuchita zomwe tingathe kuti tikonze zinthuzo.
6:16-19. Apatu pali zinthu za mitundu isanu ndi iwiri zomwe zikukhudza tchimo la mtundu uliwonse. Tiyenera kuphunzira kudana nazo.
6:20-24. Ngati taphunzitsidwa malamulo a m’Malemba kuyambira tili ana mpaka kukula tingatetezedwe kuti tisakodwe mumsampha wa chiwerewere. Makolo sayenera kunyozera kupereka maphunziro amenewa.
7:4. Tiyenera kuphunzira kukonda kwambiri nzeru ndi luntha.
MIYAMBI INA YOTI IZITITSOGOLERA
Miyambi ya Solomo imene yatsalayi anainena mwachidule payokhapayokha. Yambiri yafotokozedwa mosiyanitsa zinthu, mozifananitsa, kapena mozifanizira, ndipo ili ndi maphunziro amphamvu pa kakhalidwe, kalankhulidwe ndi kaganizidwe.
Machaputala 10 mpaka 24 amatsindika kufunika kwa mantha aulemu kwa Yehova. Miyambi ya m’machaputala 25 mpaka 29 inalembedwa ndi “anthu a Hezekiya mfumu ya Yuda.” (Miyambo 25:1) Miyambi imeneyi imaphunzitsa kudalira Yehova ndipo ilinso ndi maphunziro ena ofunika.
Kuyankha Mafunso a M’Malemba:
10:6.—Ndi motani mmene ‘m’kamwa mwa oipa mumabisira chiwawa’? Zimenezi zingakhale choncho chifukwa chakuti anthu oipa amabisa zolinga zawo zofuna kuvulaza ena mwa kukamba nkhani zosangalatsa. Kapena zingatheke kuti popeza anthu oipa amadedwa, zoipa zimene anthuwo amawachitira zimangothera mumtima.
10:10—Kodi ndi motani mmene “wotsinzinira” maso amachititsira chisoni? Nthawi zina “munthu wopanda pake” sangokhala ndi “m’kamwa mokhota” koma amayesanso kubisa maganizo ake polankhula ndi thupi lake, monga ‘kutsinzinira maso ake.’ (Miyambo 6:12, 13) Chinyengo choterechi chingachititse anthu okhudzidwawo kuvutika maganizo kwambiri.
10:29—Kodi “njira ya Yehova n’chiyani”? Zimenezi zikutanthauza njira imene Yehova amachitira ndi anthu, osati njira ya moyo imene tiyenera kutsatira. Mmene Mulungu amachitira zinthu ndi anthu zimasonyeza kuti anthu owongoka mtima adzatetezedwa pamene anthu ochita zoipa adzawonongedwa.
11:31—N’chifukwa chiyani woipa ayenera kulandira mphoto koposa wolungama? Pano, mphoto ikutanthauza chilango chimene aliyense amalandira. Munthu wolungama akachimwa, mphoto imene angalandire chifukwa cha zolakwa zakezo ndi chilango. Munthu woipa amachimwa mwadala ndipo amakana kusiya zoipazo kuti ayambe kuchita zabwino. Choncho amayenera kulandira chilango chachikulu ndipo amaterodi.
12:23—Ndi motani mmene munthu ‘amabisira zomwe akudziwa’? Kubisa zomwe ukudziwa sikukutanthauza kuti munthu sasonyeza n’komwe zomwe akudziwazo ayi. M’malo mwake, zikutanthauza kuti amasonyeza zomwe akudziwazo mwanzeru, osati kudzionetsera modzikuza.
18:19—Ndi motani mmene ‘kupembedza mbale utam’chimwira kulili kovuta kuposa kulanda mudzi wolimba’? Monga mmene mudzi wolimba umavutira kulanda, mbale wochimwiridwa angakane zolimba kukhululuka tchimolo. Posatenga nthawi, mikangano pakati pa iye ndi munthu amene wachimwayo ingakhale vuto lalikulu monga “mipiringidzo ya linga.”
Zimene Tikuphunzirapo:
10:11-14. Kuti mawu athu akhale olimbikitsa, tiyenera kudzaza maganizo athu ndi chidziwitso cholondola, mitima yathu iyenera kusonkhezeredwa ndi chikondi, ndipo nzeru ziyenera kulamulira zotuluka m’kamwa mwathu.
10:19; 12:18; 13:3; 15:28; 17:28. Tiyenera kuganiza tisanalankhule, ndipo sitiyenera kulankhula zinthu zambirimbiri.
11:1; 16:11; 20:10, 23. Yehova amafuna kuti tizikhala oona mtima tikamachita malonda.
11:4. Kungakhale kupusa kufunafuna chuma tikumanyalanyaza phunziro laumwini la Baibulo, kupezeka pamisonkhano, pemphero, ndi utumiki wa kumunda.
13:4. “Kukhumba” udindo mumpingo kapena kukhumba moyo m’dziko latsopano pa iko kokha sikokwanira. Tiyeneranso kugwira ntchito molimbika ndi kuchita khama kuti tikwaniritse zofunika zake pa zokhumba zathuzo.
13:24; 29:15, 21. Kholo limene limakonda mwana wake silimulekerera akachita zoipa. M’malo mwake bambo kapena mayi amachitapo kanthu kuti athandize mwana wawo kusiya zoipazo zisanazike mizu m’maganizo mwake.
14:10. Popeza kuti sitingathe kusonyeza bwinobwino mmene tikumvera nthawi zonse, ndiponso si nthawi zonse pamene ena angamvetse mmene tikumvera, chitonthozo chimene anthu ena angatipatse chimakhala ndi malire. Tingafunike kupirira mavuto ena mwa kudalira Yehova basi.
15:7. Sitiyenera kuuza munthu zonse zimene tikudziwa nthawi imodzi, monga mlimi sangodzala mbewu zake zonse malo amodzi. Munthu wanzeru amawanditsa nzeru zake pang’onopang’ono mogwirizana ndi zimene zikufunika.
15:15; 18:14. Kupitiriza kukhala ndi maganizo abwino kungatithandize kupeza chimwemwe, ngakhale titakumana ndi mavuto.
17:24. Mosiyana ndi “wopusa,” amene maso ndi maganizo ake sakhazikika malo amodzi n’kumaganiza zinthu zofunika, tiyenera kufunafuna luntha kuti tithe kuchita zinthu mwanzeru.
23:6-8. Tiyenera kupewa kuchereza alendo mwachinyengo.
27:21. Zimene timachita akatiyamikira zimasonyeza kuti ndife anthu otani. Kutiyamikira kukatichititsa kudziwa kuti tatha kuchita zimenezo chifukwa cha Yehova ndi kutilimbikitsa kupitiriza kum’tumikira, timasonyeza kuti ndife odzichepetsa. Ngati tayamikiridwa ndiye n’kumadzimva ngati ndife opambana, timasonyeza kuti ndife odzitukumula.
27:23-27. Pogwiritsa ntchito moyo wa ku ubusa, miyambi imeneyi ikutsindika kufunika kokhutira ndi moyo wosalira zambiri womwe timakhala nawo chifukwa chogwira ntchito mwakhama. Iyenera makamaka kukhomereza mwa ife kufunika kodalira Mulungu.a
28:5. Ngati ‘tifuna Yehova’ kudzera m’pemphero ndi kuphunzira Mawu ake, ‘tingathe kumvetsetsa zonse’ zofunikira kuti tim’tumikire movomerezeka.
‘MAUTHENGA’ OFUNIKA KWAMBIRI
Buku la m’Baibulo la Miyambo likumaliza ndi ‘mauthenga’ awiri ofunika kwambiri. (Miyambo 30:1; 31:1) Pogwiritsa ntchito mafanizo ochititsa chidwi, uthenga wa Aguri ukufotokoza kuti munthu sungathe kukhutiritsa dyera, ndipo ukusonyezanso mmene njira zimene mwamuna angakopere nazo namwali zingakhalire zovuta kuzizindikira.b Ikuchenjezanso ponena za kudzikuza ndi kulankhula mopsa mtima.
Uthenga wofunika umene Lemueli analandira kuchokera kwa mayi ake uli ndi malangizo abwino onena za kumwa vinyo ndi zakumwa zoledzeretsa komanso za kuweruza molungama. Mawu ofotokoza za mkazi wabwino akutha motere: “Mum’patse zipatso za manja ake; ndi ntchito zake zim’tame.”—Miyambo 31:31.
Pezani nzeru, mverani chilango, opani Mulungu, dalirani Yehova. Amenewa ndi maphunziro ofunika kwambiri amene miyambi youziridwa imeneyi imaphunzitsa. Mwanjira iliyonse, tiyeni tigwiritse ntchito malangizo ake ndipo tikatero tidzakhala ndi chimwemwe chimene “munthu wakuopa Yehova,” amakhala nacho.—Salmo 112:1.
[Mawu a M’munsi]
[Zithunzi patsamba 16]
Yehova ndiye Gwero la chidziwitso chonse cholondola
[Chithunzi patsamba 18]
Kodi ‘kuwanditsa nzeru’ kumatanthauza chiyani?