Mowa Umafunika Kusamala Nawo
“Vinyo achita chiphwete, chakumwa chaukali chisokosa; wosochera nazo alibe nzeru.”—MIYAMBO 20:1.
1. Kodi wamasalmo anayamikira motani zina mwa mphatso zabwino zochokera kwa Yehova?
“MPHATSO iliyonse yabwino, ndi chininkho chilichonse changwiro zichokera Kumwamba, zotsika kwa Atate wa mauniko,” analemba motero wophunzira Yakobo. (Yakobo 1:17) Mtima woyamikira mphatso zabwino zankhaninkhani zochokera kwa Mulungu unachititsa wamasalmo kuimba kuti: “Ameretsa msipu ziudye ng’ombe, ndi zitsamba achite nazo munthu; natulutse chakudya chochokera m’nthaka; ndi vinyo wokondweretsa mtima wa munthu, ndi mafuta akunyezimiritsa nkhope yake, ndi mkate wakulimbitsa mtima wa munthu.” (Salmo 104:14, 15) Mofanana ndi msipu, mkate, komanso mafuta, vinyo ndiponso mitundu ina ya mowa ndi mphatso zabwino zochokera kwa Mulungu. Kodi tiyenera kuzigwiritsa ntchito motani?
2. Kodi tikambirana mafunso otani okhudza kumwa mowa?
2 Mphatso yosangalatsa imakhala yabwino pokhapokha ngati ikugwiritsidwa ntchito moyenera. Mwachitsanzo, uchi “n’ngwabwino,” koma “kudya uchi wambiri sikuli kwabwino.” (Miyambo 24:13; 25:27) Ngakhale kuti kumwa “vinyo pang’ono” kungakhale kopanda vuto, kumwa mowa mopitirira muyeso ndi vuto lalikulu. (1 Timoteo 5:23) “Vinyo achita chiphwete,” limatichenjeza motero Baibulo, ndipo limapitiriza kuti, “chakumwa chaukali chisokosa; wosochera nazo alibe nzeru.” (Miyambo 20:1) Koma, kodi kusochera ndi mowa n’kutani?a Kodi ndi mowa wochuluka motani umene munthu atamwa tingati wamwa kwambiri? Kodi m’pofunika kusamala kotani ndi nkhaniyi?
Kodi Munthu ‘Angasochere’ Motani ndi Mowa?
3, 4. (a) Kodi n’chiyani chikusonyeza kuti Baibulo limaletsa kumwa mowa mpaka kufika poledzera? (b) Kodi zina mwa zizindikiro za kuledzera ndi ziti?
3 M’dziko la Israyeli lakale, mwana wamwamuna amene anali “womwazamwaza [“wosusuka,” NW], ndi woledzera” ankafunika kuphedwa mochita kuponyedwa miyala. (Deuteronomo 21:18-21) Mtumwi Paulo analimbikitsa Akristu kuti: “Musayanjane naye, ngati wina wotchedwa mbale ali wachigololo, kapena wosirira, kapena wopembedza mafano, kapena wolalatira, kapena woledzera, kapena wolanda, kungakhale kukadya naye wotere, iyayi.” N’zoonekeratu kuti Malemba amaletsa kumwa mowa mpaka kufika poledzera.—1 Akorinto 5:11; 6:9, 10.
4 Pofotokoza zizindikiro za kuledzera, Baibulo limati: “Usayang’ane pavinyo alikufiira. Alikung’azimira m’chikho. Namweka mosalala. Pa chitsiriziro chake aluma ngati njoka, najompha ngati mamba. Maso ako adzaona zachilendo, mtima wako udzalankhula zokhota.” (Miyambo 23:31-33) Kumwa kwambiri kumaluma ngati njoka yaululu, n’kumudwalitsa munthu, kum’sokoneza nzeru, ngakhalenso kum’komola kumene. Munthu amene ndi chidakwa angathe kumaona “zachilendo” kutanthauza kuti angamaone zilubwelubwe kapena kuganizira zinthu zosatheka kuchitika. Mwinanso sangathe kudziletsa kuti asalankhule maganizo ndi zolakalaka zokhota zimene nthawi zambiri zimangothera mumtima.
5. Kodi kumwa kwambiri n’koopsa motani?
5 Bwanji ngati munthu amamwa mowa koma mosamala moti ena sangam’zindikire kuti waledzera? Anthu ena sadziwika kwenikweni kuti aledzera ngakhale atamwa mowa wambiri. Koma, kuganizira kuti palibe vuto lililonse ngati achita zimenezi, n’kudzinyenga chabe. (Yeremiya 17:9) M’kupita kwanthawi ndiponso pang’ono ndi pang’ono, munthu akhoza kufika mpaka pomadwala akapanda kumwa mowa ndiponso angathe ‘kukodwa nacho chikondi cha pavinyo.’ (Tito 2:3) Ponenapo za mmene munthu amakhalira chidakwa, mayi wina wolemba mabuku, dzina lake Caroline Knapp, anati: “Chizolowezichi chimayamba pang’onopang’ono, mosadziwika bwinobwino ndiponso moti munthu sangathe kufotokoza.” Kumwa kwambiri ndi msampha woopsadi kwambiri.
6. N’chifukwa chiyani munthu ayenera kupewa kumwa mowa kwambiri ndiponso kudya kwambiri?
6 Komanso, taganizirani chenjezo la Yesu lakuti: “Koma mudziyang’anire nokha, kuti kapena mitima yanu ingalemetsedwe ndi madyaidya ndi kuledzera, ndi zosamalira za moyo uno, ndi kuti tsiku ilo lingafikire inu modzidzimutsa ngati msampha; pakuti lidzatero ndi kufikira anthu onse akukhala pankhope padziko lonse lapansi.” (Luka 21:34, 35) Munthu amaodzera ndiponso kufooka ndi mowa asanafike poledzera nawo, ndipo izi zingasokonezenso moyo wake wauzimu. Kodi zingakhale bwanji tsiku la Yehova litam’peza ali choncho?
Mavuto Amene Angabwere Chifukwa Chomwa Mowa Mopitirira Muyeso
7. N’chifukwa chiyani kumwa mowa mopitirira muyeso n’kotsutsana ndi langizo la m’Malemba la pa 2 Akorinto 7:1?
7 Kumwa mowa kwambiri kumadzetsa mavuto ambiri, kuphatikizaponso auzimu. Ena mwa matenda amene amayamba chifukwa chomwa mowa mopitirira muyeso ndi a kuwonongeka ndiponso kutupa chiwindi, komanso matenda ena okhudza kusokonezeka ubongo, monga kuchita zinjenje ndi kuona zilubwelubwe. Munthu akamamwa mowa wambiri kwanthawi yaitali amathanso kukhala ndi matenda a kansa, shuga, ndi matenda a mtima komanso chifu. N’zoonekeratu kuti kumwa kwambiri n’kotsutsana ndi langizo la m’Malemba lakuti: “Tidzikonzere tokha kuleka chodetsa chonse cha thupi ndi cha mzimu, ndi kutsiriza chiyero m’kuopa Mulungu.”—2 Akorinto 7:1.
8. Mogwirizana ndi Miyambo 23:20, 21, kodi n’chiyani chimene chingachitike chifukwa chomwa mowa kwambiri?
8 Kumwa mowa kwambiri kungathenso kuwonongetsa ndalama, ngakhalenso kuchotsetsa munthu pantchito kumene. Mfumu Solomo yadziko lakale la Israyeli inachenjeza kuti: “Usakhale mwa akumwaimwa vinyo, ndi ankhuli osusuka.” Chifukwa? Mfumuyi inafotokoza kuti: “Pakuti wakumwaimwa ndi wosusukayo adzasauka; ndipo kusinza kudzaveka munthu nsanza.”—Miyambo 23:20, 21.
9. N’chifukwa chiyani kuli kwanzeru kuti munthu asamwe mowa ngati akufunika kuyendetsa galimoto?
9 Pofotokoza vuto linanso, buku lofotokoza za mowa, lakuti The Encyclopedia of Alcoholism, linati: “Kafukufuku akusonyeza kuti mowa umapangitsa munthu kusayendetsa bwino galimoto, kuphatikizapo kuchita chidodo, kulobodoka, kulephera kuika maganizo pa chinthu chimodzi, kusatha kuona bwino ndiponso kuganiza moperewera.” Pamakhala mavuto aakulu kwambiri ngati munthu ayendetsa galimoto atamwa mowa. M’dziko la United States mokha, anthu ambiri amafa ndipo ena ochuluka amavulala chaka ndi chaka pangozi za pamsewu zochitika chifukwa cha mowa. Makamaka achinyamata ndiwo amakumana kwambiri ndi vutoli chifukwa chakuti amakhala alibe luso lokwanira loyendetsera galimoto komanso saatha kumwa mowa moyenerera. Kodi zingatheke kuti munthu ayendetse galimoto atamwako pang’ono n’kumanena kuti amalemekeza moyo monga mphatso yochokera kwa Yehova Mulungu? (Salmo 36:9) Poganizira za kupatulika kwa moyo, ndi bwino kuti munthu asamwe m’pang’ono pomwe ngati akufunika kuyendetsa galimoto.
10. Kodi mowa ungasokoneze motani maganizo athu, ndipo n’chifukwa chiyani zimenezo zili zoopsa?
10 Kumwa mowa kwambiri kumaikanso munthu m’mavuto auzimu. Baibulo limati: “Vinyo, ndi vinyo watsopano, zichotsa mtima,” kapena kuti ziwononga nzeru. (Hoseya 4:11) Mowa umasokoneza maganizo. Buku lina lofalitsidwa ndi bungwe la National Institute on Drug Abuse la ku United States linati: “Munthu akamwa, mowa umapita m’magazi ndipo mosakhalitsa umafika ku ubongo. Umayamba kusokoneza mbali ya ubongo imene imathandiza munthu kuti aziganiza bwino. Ndiyeno munthu amayamba kuchita zinthu motayirira.” Zikafika pamenepa, sizingavute kuti ‘tisochere,’ kuchita zinthu mosokonekera, ndiponso kugwa m’mayesero ambiri.—Miyambo 20:1.
11, 12. Kodi kumwa mowa kwambiri kungadzetse mavuto otani mwauzimu?
11 Komanso, Baibulo limatilamula kuti: “Mungakhale mudya, mungakhale mumwa, mungakhale muchita kanthu kena, chitani zonse ku ulemerero wa Mulungu.” (1 Akorinto 10:31) Kodi kumwa mowa wambiri kumapereka ulemerero kwa Mulungu? Mkristu ayenera kupewa kukhala ndi mbiri yakuti amamwa mowa kwambiri. Mbiri ngati imeneyi inganyozetse dzina la Yehova, osati kulilemekezetsa.
12 Bwanji ngati Mkristu wina wakhumudwitsa wokhulupirira mnzake, mwina wophunzira watsopano, chifukwa chomwa mowa kwambiri? Yesu anachenjeza kuti: “Yense amene adzakhumudwitsa kamodzi ka tiana iti, takukhulupirira Ine, kumuyenera iye kuti mphero yaikulu ikolowekedwe m’khosi mwake, namizidwe poya pa nyanja.” (Mateyu 18:6) Kumwa kwambiri kungachititsenso kuti munthu aimitsidwe maudindo amene ali nawo mumpingo. (1 Timoteo 3:1-3, 8) Sitiyeneranso kuiwala mavuto amene amadza m’banja chifukwa chomwa mowa kwambiri.
Kodi Mungapewe Motani Mavuto Obwera ndi Khalidweli?
13. Kodi chofunika kwambiri kuti tipewe kumwa kwambiri n’chiyani?
13 Chimene chingakuthandizeni kwambiri kupewa mavuto omwe amadza chifukwa chomwa mowa kwambiri ndicho kupewa kumwa mowa kwambiri, osati kungopewa chabe kuledzera. Kodi ndani angadziwe mlingo wanu woyenerera wa mowa ndiponso mlingo umene kwa inuyo ungakhale kumwa kwambiri? Popeza kuti mfundoyi imakhudza zinthu zambiri, sipangakhale lamulo lokhwima la mlingo wa mowa umene ungakhale wochuluka kwambiri kwa munthu. Aliyense ayenera kudziwa malire ake ndipo asamapyole malire amenewo. Kodi n’chiyani chingakuthandizeni kudziwa mlingo wa mowa wambiri kwa inu? Kodi pali mfundo yomwe tingaitsatire?
14. Kodi ndi mfundo iti yomwe ingakuthandizeni kupewa kumwa mowa wambiri?
14 Baibulo limati: “Sunga nzeru yeniyeni ndi kulingalira; ndipo mtima wako udzatengapo moyo, ndi khosi lako chisomo.” (Miyambo 3:21, 22) Motero, mfundo yofunika kuitsatira ndi yakuti: Mlingo uliwonse wa mowa umene ungakusokonezeni nzeru ndiye kuti ndi mowa wopitirira muyeso kwa inuyo. Koma musadzinamize pankhani yodziikira malireyi.
15. Kodi ndi panthawi iti pamene ngakhale mgwidyo umodzi wa mowa ungakhale kumwa kwambiri?
15 Nthawi zina, pangafunike kusamwa mowa ngakhale mgwidyo umodzi weniweniwu. Poona ngozi imene ingakhalepo kwa mwana wosabadwa, mayi woyembekezera angasankhe kusamwa mowa ngakhale pang’ono. Ndipo kodi sikungakhale kukoma mtima ngati munthu samwa mowa pamaso pa munthu wina amene kale anali ndi vuto lauchidakwa kapena amene kumwa mowa kumavutitsa chikumbumtima chake? Yehova analamula anthu ogwira ntchito zaunsembe pa chihema kuti: ‘Musamamwa vinyo, kapena choledzeretsa, . . . mmene mulowa m’chihema chokomanako, kuti mungafe.’ (Levitiko 10:8, 9) Motero musamwe mowa mutatsala pang’ono kupita kumisonkhano yachikristu, pamene muli mu utumiki, ndiponso pochita ntchito zina zauzimu. Komanso, m’mayiko amene kuli malamulo oletsa kumwa mowa, kapena oletsa anthu amene sanakwanitse zaka zinazake kumwa mowa, Akristu ayenera kutsatira malamulo a dzikolo.—Aroma 13:1.
16. Kodi mukapatsidwa mowa muyenera kutani?
16 Mukapatsidwa mowa, funso loyamba kufunsa lizikhala lakuti: ‘Kodi ndimwe n’komwe?’ Ngati mwaganiza zoti mumwe, kumbukirani malire anu, ndipo musapyole malirewo. Musalole kumwa chifukwa cha kuwolowa manja kwa munthu amene akukucherezani. Ndipo samalani ndi mowa waulere, umene umakhala wambirimbiri pa zochitika ngati pa madyerero aukwati. M’madera ambiri, malamulo amalola ana kumwa mowa. Ndi udindo wa makolo kulangiza ana awo za kumwa mowa ndiponso kuwayang’anira mmene akuchitira pankhani imeneyi.—Miyambo 22:6.
Mungathane Nalo Vutoli
17. Kodi n’chiyani chingakuthandizeni kuzindikira ngati muli ndi vuto la kumwa mowa kwambiri?
17 Kodi muli ndi vuto la kumwa vinyo kapena chakumwa chaukali mopitirira muyeso? Dziwani kuti, ngati kumwa mosayenerera kukukhala tchimo lam’tseri, m’kupita kwanthawi lidzakhala ndi zotsatirapo zake. Motero dzipendeni bwinobwino modekha. Dzifunseni mafunso othandiza kudzipenda monga awa: ‘Kodi masiku ano ndimamwa pafupipafupi kusiyana ndi kale? Kodi panopa ndimamwa mowa waukali kwambiri kusiyana ndi womwe ndinkamwa kale? Kodi ndimamwa pofuna kuti ndisakhale ndi nkhawa kapena kuti ndiiwale mavuto? Kodi wina m’banja langa kapena mnzanga wandifotokozerapo kuti akuda nkhawa ndi mmene ndimamwera? Kodi m’banja langa muli vuto lililonse chifukwa chakuti ine ndimamwa? Kodi ndimavutika ndikapanda kumwa kwa mlungu umodzi, mwezi, kapena miyezi ingapo? Kodi ndimabisira anthu ena kuti ndimamwa vinyo kapena mowa wochuluka motani?’ Bwanji ngati mayankho a ena mwa mafunsowa ndi akuti inde? Musakhale ngati munthu ‘woyang’anira nkhope yake ya chibadwidwe chake m’kalilole; n’kuiwala pom’paja kuti anali wotani.’ (Yakobo 1:22-24) Chitani zinthu zoti muthetse vutolo. Kodi mungachite chiyani?
18, 19. Kodi mungatani kuti musiye kumwa mowa kwambiri?
18 Mtumwi Paulo analimbikitsa Akristu kuti: “Musaledzere naye vinyo, mmene muli chitayiko; komatu mudzale naye Mzimu.” (Aefeso 5:18) Pezani mlingo wokuyenererani wa mowa, ndipo dziikireni malire. Tsimikizani mtima kuti musapitirire malirewo; khalani wodziletsa. (Agalatiya 5:22, 23) Kodi muli ndi anzanu amene amakukakamizani kumwa mowa kwambiri? Samalani. Baibulo limati: “Ukayenda ndi anzeru udzakhala wanzeru: Koma mnzawo wa opusa adzapwetekedwa.”—Miyambo 13:20.
19 Ngati mumamwa mowa pofuna kuiwala vuto linalake, njira yabwino n’kungolimbana ndi vutolo. Mungathetse mavuto potsatira malangizo a m’Mawu a Mulungu. (Salmo 119:105) Musanyalanyaze kukafunsira thandizo kwa mkulu wodalirika wachikristu. Gwiritsani ntchito mwanzeru zinthu zimene Yehova watipatsa kuti mulimbitsire moyo wanu wauzimu. Limbitsani ubwenzi wanu ndi Mulungu. Pempherani kwa iye nthawi zonse, makamaka mapemphero okhudza zimene zimakuvutani. M’pempheni Mulungu kuti ‘ayeretse impso zanu ndi mtima wanu.’ (Salmo 26:2) Monga momwe taonera m’nkhani yapitayi, yesetsani kuyenda mu umphumphu.
20. Kodi mungafunike kuchita chiyani kuti muthetse vuto la kumwa mowa kwambiri ngati likupitirirabe?
20 Kodi mungatani ngati vuto la kumwa mowa kwambiri likupitirirabe ngakhale kuti mukuyesetsa kulithetsa? Muyenera kutsatira malangizo amene Yesu anapereka. Iye anati: “Ngati dzanja lako likulakwitsa iwe, ulidule: n’kwabwino kwa iwe kulowa m’moyo wopunduka dzanja, koposa kukhala ndi manja ako awiri ndi kulowa m’gehena.” (Marko 9:43) Yankho lake ndi lakuti: Musiye kumwa. Izi ndi zomwe mayi wina amene timutche kuti Irene anatsimikiza mtima kuchita. Iye anafotokoza kuti: “N’takhala pafupifupi zaka ziwiri ndi theka osamwa mowa, ndinayamba kuganiza kuti palibe vuto ngati nditamwa botolo limodzi lokha, kuti ndingoona mmene zikhalire. Koma ndikangoganiza choncho, ndimapemphera kwa Yehova za nkhaniyi nthawi yomweyo. Ndinatsimikiza kuti sindidzamwanso mowa mpaka m’dziko latsopano, ndipo mwinanso ngakhale m’dziko latsopanolo sindidzamwa.” Kuli bwino kusiyiratu mowa kusiyana n’kuti tidzalephere kukhala m’dziko lapansi latsopano ndi lolungama la Mulungu.—2 Petro 3:13.
“Thamangani Kuti Mukalandire”
21, 22. Kodi n’chiyani chingatilepheretse kumaliza mpikisano wokalandira moyo, ndipo tingapewe bwanji vuto limeneli?
21 Poyerekezera moyo wa Mkristu ndi mpikisano wothamanga, mtumwi Paulo anati: “Kodi simudziwa kuti iwo akuchita makani a liwiro, athamangadi onse, koma mmodzi alandira mfupo? Motero thamangani, kuti mukalandire. Koma yense wakuyesetsana adzikanizira zonse. Ndipo iwowa atero kuti alandire korona wakuvunda; koma ife wosavunda. Chifukwa chake ine ndithamanga chotero, si monga chosinkhasinkha. Ndilimbana chotero, si monga ngati kupanda mlengalenga; koma ndipumphuntha thupi langa, ndipo ndiliyesa kapolo; kuti, kapena ngakhale ndalalikira kwa ena, ndingakhale wotayika ndekha.”—1 Akorinto 9:24-27.
22 Anthu okhawo amene amaliza bwino mpikisano wothamanga ndiwo amalandira mphoto. Pampikisano wokalandira moyo, kumwa mowa mopitirira muyeso kungatilepheretse kumaliza mpikisanowo. Tiyenera kukhala odziletsa. Kuti tithamange mosakayikayika timafunika kupewa “maledzero.” (1 Petro 4:3) Mosiyana ndi zimenezi, tiyenera kudziletsa m’zinthu zonse. Pankhani yomwa mowa, tingachite bwino ‘kukana chisapembedzo ndi zilakolako za dziko lapansi, kukhala . . . odziletsa, ndi olungama, ndi opembedza.’—Tito 2:12.
[Mawu a M’munsi]
a M’nkhaniyi mawu akuti “mowa” akuimira chakumwa chilichonse chaukali kuphatikizapo vinyo.
Kodi Mukukumbukira?
• Kodi kumwa mowa kwambiri n’kutani?
• Kodi ndi vuto lotani limene limakhalapo chifukwa chomwa mowa kwambiri?
• Kodi mungatani kuti mupewe mavuto amene amakhalapo chifukwa chomwa mowa kwambiri?
• Kodi munthu angatani kuti athetse vuto la kumwa mowa kwambiri?
[Chithunzi patsamba 19]
Vinyo ‘akondweretsa mtima wa munthu’
[Chithunzi patsamba 20]
Tiyenera kudziwa malire athu ndipo tisamapyole malire amenewo
[Chithunzi patsamba 21]
Ikiranitu malire
[Chithunzi patsamba 22]
Pempherani nthawi zonse kwa Yehova za zimene zikukuvutani
[Chithunzi patsamba 23]
Makolo ali ndi udindo wolangiza ana awo za kumwa mowa