“Choyenera Anthu Onse”
“Opa Mulungu, musunge malamulo ake; pakuti choyenera anthu onse ndi ichi.”—MLALIKI 12:13.
1, 2. Kodi nchifukwa ninji kuli koyenera kuganizira za thayo lathu kwa Mulungu?
“YEHOVA afunanji nawe?” Mneneri wakalekale anafunsa funsoli. Kenako anatchula zimene Yehova anafuna—kuchita cholungama, ndi kukonda chifundo ndi kuyenda modzichepetsa ndi Mulungu.—Mika 6:8.
2 M’masiku ano amene munthu amafuna kudzigangira ndi kudzidalira, ambiri samakonda kwenikweni kumva kuti Mulungu amafuna kanthu kena kwa iwo. Samafuna kukhala omangika ndi thayo. Koma bwanji ponena za mfundo imene Solomo anafikapo m’buku la Mlaliki? “Mawu atha; zonse zamveka zatha; opa Mulungu, musunge malamulo ake; pakuti choyenera anthu onse ndi ichi.”—Mlaliki 12:13.
3. Kodi nchifukwa ninji tiyenera kulilingalira mwamphamvu buku la Mlaliki?
3 Mulimonse mmene mikhalidwe yathu kapena kaonedwe kathu ka moyo kangakhalire, tikhoza kupindula kwambiri ngati tipenda chimene chinamfikitsa pa mfundoyo. Mfumu Solomo, mlembi wa buku louziridwa limeneli, anapenda zinthu zina za m’moyo wathu wa tsiku ndi tsiku. Ena angafulumire kunena kuti kupenda kwakeko kunali kosalimbikitsa. Komabe kupendako kunali kouziridwa ndi Mulungu ndipo kukhoza kutithandiza kusanthula zochita zathu ndi zinthu zofunika, ndi kupeza chimwemwe chokulirapo.
Kukwaniritsa Zofunika Zazikulu za Moyo
4. Kodi Solomo anapendanji ndipo anafotokozanji m’buku la Mlaliki?
4 Solomo anapenda kwambiri ‘ntchito ya ana a anthu.’ “Ndipereka mtima kufunafuna ndi nzeru, ndi kulondetsa zonse zimachitidwa pansi pa thambo.” Potchula “ntchito” Solomo sanatanthauze ntchito yeniyeni, kapena ntchito yolembedwa, koma zochita zonse zimene amuna ndi akazi amada nazo nkhaŵa m’moyo wawo wonse. (Mlaliki 1:13) Tiyeni tikambitsirane zofunika zazikulu zina, kapena zochita ndiyeno tiziyerekezere ndi zochita zathu ndi zinthu zimene timaika patsogolo.
5. Kodi imodzi ya nkhaŵa zazikulu za anthu nchiyani?
5 Kunena zoona ndalama ndiyo chinthu chofunika koposa pa nkhaŵa zambiri ndi zochita zambiri za munthu. Palibe aliyense amene anganene moona mtima kuti Solomo sanadere nkhaŵa za ndalama mofanana ndi anthu ena olemera. Anazindikira mwamsanga kufunika kwa ndalama; kuti kukhala nazo zokwanira kuli bwino koposa kukhala ndi moyo wosauka kapena waumphaŵi. (Mlaliki 7:11, 12) Koma muyenera kuti mwaona kuti ndalama, limodzi ndi zinthu zomwe imagula, ingakhale cholinga chachikulu m’moyo—kwa osauka ndi olemera omwe.
6. Kodi tingaphunzirenji ponena za ndalama pa imodzi ya mafanizo a Yesu ndi pa zokumana nazo za Solomo mwiniyo?
6 Kumbukirani fanizo la Yesu la munthu wa chuma, yemwe anagwira ntchito kuti apeze zochuluka koma osakhutira. Mulungu anamuyesa wopusa. Chifukwa ninji? Chifukwa ‘moyo suchokera m’zinthu zimene tili nazo.’ (Luka 12:15-21) Chidziŵitso cha zokumana nazo cha Solomo—mwinamwake choposa chathu—chimatsimikizira mawu a Yesu. Ŵerengani zimenezo pa Mlaliki 2:4-9. Kwa nthaŵi yaitali ndithu Solomo analimbikira kupeza chuma chambiri. Anamanga nyumba zochititsa kaso ndi kulima minda yochititsa chidwi. Anakhoza kufuna akazi okongola kukhala zitsamwali zake. Kodi chuma ndi zimene anapeza mwa chumacho zinampatsa chikhutiro chozama, lingaliro lenileni la chipambano, ndi cholinga cha moyo wake? Anayankha moona mtima: “Ndinayang’ana zonse manja anga anazipanga, ndi ntchito zonse ndinasauka pozigwira; ndipo taona, zonse zinali zachabechabe ndi kungosautsa mtima, ndipo kunalibe phindu kunja kuno.”—Mlaliki 2:11; 4:8.
7. (a) Zochitika zimasonyezanji ponena za phindu la ndalama? (b) Kodi nchiyani chimene mwadzionera nokha chimene chimachitira umboni mfundo ya Solomo?
7 Zimenezo ndi zenizeni, choonadi chimene timaona m’moyo wa anthu ambiri. Tiyenera kuvomereza kuti kungokhala nazo ndalama zochuluka sikumathetsa mavuto onse. Zingathetse ena inde, monga kugula chakudya ndi zovala mosavuta. Koma munthu amangovala chovala chimodzi chokha panthaŵi imodzi ndipo amasangalala ndi chakudya ndi chakumwa pamlingo wolinganiza chabe. Ndipo mwaŵerenga za anthu achuma amene moyo wawo umasakazidwa ndi chisudzulo, uchidakwa kapena anamgoneka, ndiponso madano ndi achibale. Mpondamatiki J. P. Getty anati: “Ndalama zilibe unansi kwenikweni ndi chimwemwe. Kapena ndi chisoni.” Ndi chifukwa chabwino, Solomo anaika chikondi cha siliva pa zinthu zopanda pake. Onani kusiyana kwa zimenezo ndi mawu a Solomo: “Tulo ta munthu wogwira ntchito ntabwino, ngakhale adya pang’ono ngakhale zambiri; koma kukhuta kwa wolemera sikumgonetsa tulo.”—Mlaliki 5:10-12.
8. Kodi nchifukwa ninji sitiyenera kuchepetsa kufunika kwa ndalama?
8 Ndalamanso ndi katundu sizimapatsa chikhutiro cha zamtsogolo. Ngati munali ndi ndalama zochuluka ndi katundu wambiri, mwina mukanaonjezera nkhaŵa poganiza za chisungiko cha zinthuzo, ndipo simukanadziŵabe zomwe zikachitika maŵa. Kodi zingataike zonse, limodzi ndi moyo wanu? (Mlaliki 5:13-17; 9:11, 12) Pokhala choncho, sikuyenera kuvuta kuona chifukwa chake moyo wathu, kapena zochita, uyenera kukhala wa mtengo wapatali wokhalitsa kuposa ndalama kapena katundu.
Banja, Kutchuka, ndi Mphamvu
9. Kodi nchifukwa ninji moyo wa banja unakhudzidwa m’kupenda kwa Solomo?
9 Kupenda moyo kwa Solomo kunaphatikizapo nkhani ya kusamala za banja. Baibulo limasonyeza kufunika kwa moyo wa banja, kuphatikizapo chisangalalo cha kukhala ndi ana ndi kuwalera. (Genesis 2:22-24; Salmo 127:3-5; Miyambo 5:15, 18-20; 6:20; Marko 10:6-9; Aefeso 5:22-33) Komabe, kodi chimenecho ndicho cholinga chachikulu cha moyo? Kukuoneka kuti ambiri amaganiza zimenezo, poona chigogomezero chimene miyambo yaika pa ukwati, ana, ndi maunansi a banja. Komabe Mlaliki 6:3 akusonyeza kuti ngakhale kukhala ndi ana zana limodzi sikungadzetse chikhutiro m’moyo. Tangolingalirani kuti ndi makolo angati amene atayirapo zinthu zambiri kuti ana awo akhale ndi chiyambi chabwino ndi moyo wofeŵerapo. Poona kufunika kwake kwa zimenezi, ndithudi Mlengi wathu sanatipange kuti cholinga chachikulu m’moyo chikhale kubalana basi, monga momwe nyama zimachitira mwachibadwa kuti zipitirize mtundu wawo.
10. Kodi nchifukwa ninji kupereka chisamaliro chopambanitsa pa banja kungakhale kopanda pake?
10 Mwachionekere Solomo anasonyeza zenizeni za m’moyo wa banja. Mwachitsanzo, mwamuna angasumike maganizo pa kupezera zofunika ana ake ndi adzukulu ake. Koma kodi iwo adzakhala anzeru? Kapena kodi adzakhala zitsiru ndi zimene iye analimbikira kuwapezera? Ngati akhala zitsiru, “ichinso ndi chabe ndi choipa chachikulu” chotani nanga!—Mlaliki 2:18-21; 1 Mafumu 12:8; 2 Mbiri 12:1-4, 9.
11, 12. (a) Kodi anthu ena asumika maganizo pa kuchita zinthu zotani m’moyo? (b) Kodi nchifukwa ninji tinganene kuti kufuna kutchuka ndiko “kungosautsa mtima”?
11 Pochitanso mopambanitsa m’mbali ina, ambiri aika banja lawo pambuyo pa zolinga zawo za kutchuka ndi kulamulira ena. Mzimu umenewu ngwofala kwambiri pakati pa amuna. Kodi mwaona zimenezi mwa anzanu pasukulu, pantchito, kapena anansi anu? Ambiri amalimbikira zolimba kuti adziŵike, kuti atchuke, kapena kuti akhale ndi ulamuliro pa ena. Koma kodi zimenezi nzothandizadi?
12 Talingalirani mmene ena amamenyera nkhondo kuti atchuke, kaya pamlingo waung’ono kapena waukulu. Timaziona pasukulu, kwa anansi, ndi m’magulu a anthu osiyanasiyana. Ulinso mzimu womwe umasonkhezera aja ofuna kutchuka m’maluso a zolembalemba ndi zopangapanga, m’zokondweretsa, ndi m’nkhani zandale. Komabe, kodi zimenezo sizili kwenikweni zopanda pake? Solomo analondola ponena kuti ndiko “kungosautsa mtima.” (Mlaliki 4:4) Ngakhale ngati wachichepere angatchuke m’kalabu, m’timu ya maseŵero, kapena m’gulu la oimba—kapena ngati mwamuna kaya mkazi atchuka pakampani kapena m’mudzi—kodi ndi angati omwe amadziŵa zimenezo? Kodi anthu ochuluka m’mbali zina za dziko (ngakhale m’dzikolo) amadziŵa nkomwe kuti munthuyo aliko? Kodi iwo samangopitiriza ndi moyo osadziŵa kalikonse za kutchuka kwake kochepako? Ndipo nchimodzimodzi ndi mphamvu kapena ulamuliro uliwonse umene munthu angapeze pantchito, m’tauni, kapena pakati pa gulu la anthu.
13. (a) Kodi Mlaliki 9:4, 5 amatithandiza motani kukhala ndi kapenyedwe koyenera ka kumenyera kutchuka kapena mphamvu? (b) Kodi ndi zenizeni ziti zimene tiyenera kuvomereza ngati moyo uno ndiwo wokha umene uliko? (Onani mawu amtsinde.)
13 Kodi kutchuka koteroko kapena ulamuliro kumafikitsa kuti potsirizira pake? Monga mbadwo wina upita ndi wina ufika, anthu otchuka kapena amphamvu amapitanso ndi kuiŵalika. Zimenezo nzoona ponena za omanga, oimba nyimbo ndi amaluso a zolembalemba ndi zopangapanga, osonkhezera anthu kuwongolera zinthu, ndi ena otero, monganso atsogoleri ambiri andale ndi ankhondo. Pantchito zimenezo, kodi ndi anthu angati omwe mudziŵa omwe anakhalako m’zaka za ma 1700 ndi 1800? Solomo anapenda bwino zinthu, pamene anati: “Galu wamoyo aposa mkango wakufa. Pakuti amoyo adziŵa kuti tidzafa; koma akufa sadziŵa kanthu bi, . . . angoiŵalika.” (Mlaliki 9:4, 5) Ndipo ngati moyo uno ndiwo wokha umene ulipo, ndiye kuti kumenyera kutchuka ndi mphamvu kulidi chabe.a
Cholinga Chathu ndi Thayo Lathu
14. Kodi nchifukwa ninji buku la Mlaliki liyenera kutithandiza mwaumwini?
14 Solomo sanalankhule za zochita zambiri, zonulirapo, ndi zokondweretsa zimene anthu amasumikapo maganizo kwambiri. Komabe, zomwe analembazo nzokwanira. Kupenda kwathu bukulo kusaonedwe monga nkofuna kuchititsa anthu chisoni kapena kungofuna kuipitsa zinthu, pakuti buku lomwe talipenda moona mtimalo ndi buku la Baibulo limene Yehova Mulungu anasankha kuliuzira kuti litipindulitse. Lingathandize aliyense wa ife kuwongolera kaonedwe kathu ka moyo ndi zimene timasumikapo maganizo. (Mlaliki 7:2; 2 Timoteo 3:16, 17) Zimenezo nzoona makamaka poona mfundo zimene Yehova anathandiza Solomo kuzifikira.
15, 16. (a) Kodi Solomo anali ndi lingaliro lotani ponena za kusangalala ndi moyo? (b) Kodi Solomo anati chofunika nchiyani kuti munthu asangalale ndi moyo?
15 Mfundo ina imene Solomo anaisonyeza kaŵirikaŵiri inali yakuti atumiki a Mulungu woona ayenera kupeza chimwemwe pamaso Pake m’zochita zawo. “Ndidziŵa kuti iwo alibe ubwino, koma kukondwa ndi kuchita zabwino pokhala ndi moyo. Ndiponso kuti munthu yense adye namwe naone zabwino m’ntchito zake zonse; ndiwo mtulo wa Mulungu.” (Mlaliki 2:24; 3:12, 13; 5:18; 8:15) Onani kuti Solomo sanali kulimbikitsa kuchita zikondwerero zaphokoso; ndiponso sanavomereze mzimu wakuti ‘Tidye, timwe, ndi kusekera, pakuti maŵa timwalira.’ (1 Akorinto 15:14, 32-34) Anatanthauza kuti tiyenera kusangalala ndi zokondweretsa zoyenera, monga kudya ndi kumwa, ‘pochita zabwino m’moyo.’ Mosakayika, zimenezo zimasumika moyo wathu pa chifuniro cha Mlengi, amene amadziŵa chimene chilidi chabwino.—Salmo 25:8; Mlaliki 9:1; Marko 10:17, 18; Aroma 12:2.
16 Solomo analemba kuti: “Tiye, idya zakudya zako mokondwa, numwe vinyo wako mosekera mtima; pakuti Mulungu wavomerezeratu zochita zako.” (Mlaliki 9:7-9) Inde, mwamuna kapena mkazi amene alidi ndi moyo wopindulitsa ndi wokhutiritsa amakhala wokangalika pantchito zokondweretsa Yehova. Zimenezo zimafuna kuti timkumbukire nthaŵi zonse. Ha, kaonedwe ka zinthu kameneka nkosiyana bwanji nanga ndi anthu ochuluka, amene amaona moyo malinga ndi malingaliro a anthu!
17, 18. (a) Kodi anthu ambiri amachita motani poyang’anizana ndi zochitika m’moyo? (b) Kodi nzotsatirapo zotani zimene tiyenera kukumbukira nthaŵi zonse?
17 Ngakhale kuti zipembedzo zina zimaphunzitsa za moyo wa pambuyo pa imfa, anthu ambiri amakhulupirira kuti moyo uno ndiwo chinthu chokha chomwe angatsimikizire. Mwina mwawaona akuchita mofanana ndi zimene Solomo anafotokoza: “Popeza sambwezera choipa chake posachedwa atamtsutsa munthu, ana a anthu atsimikizadi mitima yawo kuchita zoipa.” (Mlaliki 8:11) Ngakhale aja omwe samaloŵa m’machitachita oipa amasonyeza kuti kwenikweni amadera nkhaŵa za moyo uno. Ndicho chifukwa chake ndalama, chuma, kutchuka, ulamuliro pa ena, banja, kapena zinthu zina zotero zimakhala zofunika kwambiri kwa iwo. Komabe, Solomo sanaimire pamenepo. Anawonjeza kuti: “Angakhale wochimwa achita zoipa zambirimbiri, masiku ake ndi kuchuluka, koma ndidziŵitsadi kuti omwe aopa Mulungu naopa pamaso pake adzapeza bwino; koma woipa sadzapeza bwino ngakhale kutanimphitsa masiku ake ngati mthunzi; chifukwa saopa pamaso pa Mulungu.” (Mlaliki 8:12, 13) Mwachionekere, Solomo anakhulupirira kuti tidzapeza bwino ngati ‘tiopa Mulungu woona.’ Kupeza bwino motani? Tingapeze yankho poona zosiyana zimene ananena. Yehova akhoza ‘kutanimphitsa masiku athu.’
18 Aja omwe adakali achicheperepo afunikira makamaka kusinkhasinkha mfundo yoona ndi yodalirika yakuti adzapeza bwino ngati aopa Mulungu. Monga momwe inu mwini mwina mwaonera nokha, wothamanga kuposa onse pampikisano akhoza kupunthwa ndi kulephera. Gulu lankhondo lamphamvu likhoza kulakidwa. Wamalonda wochenjera akhoza kukhala mmphaŵi. Ndipo zinthu zambiri zokayikitsa zimachititsa moyo kukhala wosatsimikizika. Koma mutha kukhala wotsimikiza za ichi: Njira yanzeru ndi yotsimikizika koposa ndiyo kusangalala ndi moyo pamene muchita zabwino malinga ndi malamulo a Mulungu pamakhalidwe ndi mogwirizana ndi chifuniro chake. (Mlaliki 9:11) Zimenezi zimaphatikizapo kuphunzira m’Baibulo za chifuniro cha Mulungu, kupatulira moyo kwa iye, ndi kukhala Mkristu wobatizidwa.—Mateyu 28:19, 20.
19. Kodi achichepere angagwiritsire ntchito motani moyo wawo, koma njira yanzeru ndi yotani?
19 Mlengi sadzakakamiza achichepere kapena ena kuti atsatire chitsogozo chake. Iwo angamwerekere m’maphunziro, ngakhale kuphunzira mabuku ambirimbiri a maphunziro aumunthu kwa moyo wawo wonse. Potsirizira pake zimenezo zidzakhaladi zongotopetsa. Kapena akhoza kuyenda m’njira za mtima wawo wopanda ungwiro kapena kutsatira zokoma m’maso. Zimenezo mosalephera zidzakhala zopweteka, ndipo moyo wotero m’kupita kwa nthaŵi udzakhala wachabe. (Mlaliki 11:9–12:12; 1 Yohane 2:15-17) Motero Solomo akulimbikitsa achichepere—chilimbikitso chimene tiyenera kuchilingalira mwamphamvu, mosasamala kanthu za msinkhu wathu: “Ukumbukirenso Mlengi wako masiku a unyamata wako, asanadze masiku oipa, ngakhale zisanayandikire zakazo zakuti udzati, Sindikondwera nazo.”—Mlaliki 12:1.
20. Kodi kaonedwe koyenera ndi kotani ponena za uthenga wa m’buku la Mlaliki?
20 Choncho, kodi zonsezi zitifikitsa pamfundo iti? Chabwino, bwanji nanga mfundo imene Solomo anafikapo? Iye anaona, kapena kuti anapenda, “ntchito zonse zipangidwa kunja kuno; ndipo zonsezo ndi chabe ndi kungosautsa mtima.” (Mlaliki 1:14) M’bukuli la Mlaliki sitikupezamo mawu a munthu wosakondwa kapena wosakhutira. Ndi mbali ya Mawu ouziridwa a Mulungu ndipo tifunikira kuwapenda.
21, 22. (a) Kodi Solomo anafotokoza mbali ziti za moyo? (b) Kodi ndi mfundo yanzeru yotani yomwe anafikapo? (c) Kodi kupenda mfundo za Mlaliki kwakukhudzani motani?
21 Solomo anafufuza zotopetsa za munthu, zolimbana nazo, ndi zokalimira zake. Anafotokoza mmene zinthu zimakhalira mwa njira yozoloŵereka, zotsatirapo zolefula ndi zopanda pake zimene anthu ambiri amakumana nazo. Anapenda mkhalidwe weniweni wa kupanda ungwiro kwa anthu wochititsa imfa. Ndipo analongosola za chidziŵitso chochokera kwa Mulungu ponena za mkhalidwe wa akufa ndi ziyembekezo za moyo wa mtsogolo uliwonse. Zonsezi zinayesedwa ndi munthu yemwe anali ndi nzeru yaumulungu, inde, mmodzi wa anthu anzeru koposa onse amene anakhalako. Ndiyeno mfundo yomwe anafikapo inaikidwa m’Malemba Oyera kaamba ka phindu la onse ofuna moyo wopindulitsa kwenikweni. Kodi sitikuvomereza?
22 “Mawu atha, zonse zamveka zatha; opa Mulungu, musunge malamulo ake; pakuti choyenera anthu onse ndi ichi. Pakuti Mulungu adzanena mlandu wa zochita zonse, ndi zobisika zonse, ngakhale zabwino ngakhale zoipa.”—Mlaliki 12:13, 14.
[Mawu a M’munsi]
a Nsanja ya Olonda yachingelezi panthaŵi ina inapereka ndemanga yaluntha yakuti: “Tisawonongere moyo uno pa zinthu zachabechabe . . . Ngati moyo uno ndiwo wokha umene uliko, palibe chinthu chofunika. Uli ngati mpira woponyedwa m’mwamba umene umangogweranso pansi. Uli ngati mthunzi wodutsa, duŵa limene limafota, udzu woti akaudula ufota. . . . Pamiyeso ya nthaŵi yomka muyaya moyo wathu uli ngati kachitsotso kopanda pake. M’kuyenda kwa nthaŵi uli ngati dontho laling’onong’ono. Ndithudi [Solomo] ali bwino popenda nkhaŵa zambiri za moyo wa munthu ndi zochita zake ndi kunena kuti zili chabe. Timapita msanga ndipo ndi bwino kusabadwa nkomwe, mabiliyoni adzafika ndi kupita, oŵerengeka chabe ndiwo amadziŵa kuti tinali pano. Lingaliro limeneli silimasonyeza kupanda chidaliro kapena kusonyeza chisoni kapena kuchititsa mantha. Chili choonadi, chenicheni, lingaliro lenileni, ngati moyo uno ndiwo wokha umene uliko.”—August 1, 1957, tsamba 472.
Kodi Mukukumbukira?
◻ Kodi kupenda kwanzeru ntchito ya chuma m’moyo wanu nkotani?
◻ Nchifukwa ninji sitiyenera kuona banja, kutchuka, kapena ulamuliro pa ena kukhala zinthu zofunika kopambana?
◻ Kodi Solomo analimbikitsa kaonedwe kaumulungu kotani kulinga ku zokondweretsa?
◻ Kodi mwapindula motani mwa kupenda buku la Mlaliki?
[Zithunzi patsamba 15]
Ndalama ndi katundu sizimakhutiritsa
[Chithunzi patsamba 17]
Achichepere angatsimikize kuti adzapeza bwino ngati aopa Mulungu