Mlaliki
12 Choncho kumbukira Mlengi wako Wamkulu masiku a unyamata wako,+ asanafike masiku oipa*+ komanso zisanafike zaka zimene udzanena kuti: “Moyo sukundisangalatsa.” 2 Uchite zimenezi kuwala kwa dzuwa, mwezi ndi nyenyezi kusanazime+ ndiponso mitambo yamvula isanabwererenso pambuyo poti mvula yagwa. 3 Pa nthawi imeneyo olondera* nyumba adzayamba kunjenjemera, amuna amphamvu adzapindika, akazi adzasiya kupera ufa chifukwa adzatsala ochepa ndipo akazi oyangʼana pawindo azidzaona mdima.+ 4 Zitseko zotulukira popita mumsewu zidzatsekedwa, phokoso la miyala yoperera ufa lidzayamba kumveka motsika ndipo munthu azidzadzuka ndi kulira kwa mbalame, ndiponso ana onse aakazi azidzaimba nyimbo ndi mawu ofooka.+ 5 Komanso munthu azidzaopa malo okwera ndipo azidzadera nkhawa zinthu zoopsa mumsewu. Mtengo wa amondi udzachita maluwa,+ chiwala chizidzayenda mochita kudzikoka ndipo zakudya sizidzakoma,* chifukwa munthu adzakhala akupita kunyumba yake yokhalitsa+ ndipo olira azidzangoyendayenda mumsewu.+ 6 Uzikumbukira Mlengi wako chingwe chasiliva chisanachotsedwe, mbale yagolide isanaphwanyidwe, mtsuko umene uli pakasupe usanaphwanyike ndiponso wilo lotungira madzi pachitsime lisanathyoke. 7 Kenako fumbi lidzabwerera kunthaka+ kumene linali, ndipo mzimu* udzabwerera kwa Mulungu woona amene anaupereka.+
8 Wosonkhanitsa anthu akunena kuti:+ “Nʼzachabechabe!* Zinthu zonse nʼzachabechabe.”+
9 Kuwonjezera pa kukhala ndi nzeru, wosonkhanitsa anthuyu nthawi zonse ankaphunzitsa anthuwo zimene iye ankadziwa+ ndipo anaganizira mozama komanso anafufuza zinthu mosamala kuti alembe* miyambi yambiri.+ 10 Wosonkhanitsa anthuyu anafufuza mawu osangalatsa+ ndipo analemba mawu olondola a choonadi.
11 Mawu a anthu anzeru ali ngati zisonga zobayira ngʼombe pozitsogolera,+ ndipo mawu awo osankhidwa bwino ali ngati misomali imene aikhomerera kwambiri. Mawuwo aperekedwa ndi mʼbusa mmodzi. 12 Mwana wanga, ponena za zinthu zina kupatula izi, ndikukuchenjeza kuti: Anthu adzapitirizabe kulemba mabuku ambiri ndipo kuwawerenga kwambiri kumangotopetsa munthu.+
13 Poti zonse zanenedwa, mfundo yaikulu ndi yakuti: Opa Mulungu woona+ ndi kusunga malamulo ake+ chifukwa zimenezi ndi zimene munthu akuyenera kuchita.+ 14 Chifukwa Mulungu woona adzaweruza chilichonse chimene anthu amachita kuphatikizapo chinthu chilichonse chobisika, kuti aone ngati chili chabwino kapena choipa.+