Pamene Zosoŵa Zidzakhutiritsidwa
ZAKA zambiri zapitazo ulosi uwu unapangidwa: “Maso a akhungu adzatsegudwa, ndi makutu a ogontha adzatsegulidwa.”
‘Koma chimenecho nchosatheka,’ inu munganene choncho. Ngati mutero, mwinamwake mudzadabwa kudziŵa kuti akatswiri a zamoyo ambiri a zana la 20 sakuchiwonanso icho kukhala chosatheka. Kodi nchifukwa ninji?
Kuwona kaamba ka Akhungu?
Ngati mwafunsidwa kuti kodi ndi chiŵalo chiti chimene mumawonera zinthu, mwachiwonekere kwambiri inu mudzayankha kuti: ‘Ndi maso anga.’ Komabe, katswiri wa zamoyo, ngakhale kuli tero, mwachiwonekere kwambiri akayankha kuti: ‘Ndi ubongo wanga.’ Ndipo iye akakhala wolondola kwenikweni. Popeza kuti pamene kuli kwakuti diso liri chiŵalo chodziŵira zinthu chomwe chimatenga kuwunika ndi kutulutsa mphamvu ya magetsi, iri mbali ya kumbuyo kwa ubongo wathu imene imatipatsa chithunzi chowoneka.
Magazini Yachifalansa yakuti Science et Vie posachedwapa inaika m’mawu ofupikitsa kufufuza komwe kwachitidwa kuthandiza akhungu kuwona kosakhala kwachibadwa. Titaikidwa m’malo a magwero a kuwona mu ubongo, timaelectrode tating’ono timene timalumikizidwa ku video camera tiri tokhoza kutumiza zizindikiro kuchokera ku camera mwachindunji kuloŵa mu ubongo. Mphamvu ya kuwunika imatulutsidwa, mokulira monga mmene “tingawonere nyenyezi” pamene tipandidwa pamutu. Mwakupanga kulumikiza koyenerera, ubongo udzaŵerenga kung’anima kwa kuwunika monga mmene timaŵerengera zizindikiro zopangidwa ndi magulobu ambiri a magetsi. Pamene kuli kwakuti awo amene maso awo akhala akhungu angathandizidwe kuwona, anthu amene magwero awo a kuwona mu ubongo awonongedwa sangapindule ndi njira imeneyi.
Kumva kaamba ka Agonthi?
“Kwa khutu, vutolo mwinamwake liri lochepera kuposa diso,” akudzinenera tero Dr. Jean- Michel Bader. Masitepi abwino achitidwa m’kupangidwa kwa kuika cochlear kuti kubwezeretse mlingo wa kumva kwa anthu ena okhala ndi kuvulazika kwa kumva. Koma bwanji ponena za aja amene ugonthi wawo uli kaamba ka mavuto a kusanduliza kudukizadukiza kwa mawu kukhala mphamvu ya magetsi kuti atumizidwe ku ubongo?
Kaamba ka phindu la oterewo, ntchito imapita patsogolo kupanga khutu la mkati la electronic. Ndi thandizo la chiŵiya chokhala ndi maikolofoni ya mthumba yomwe imatembenuza mawu kukhala mphamvu ya magetsi, zizindikiro zimaperekedwa kupyola m’waya kupita ku transmitter yaing’ono yolumikizidwa ku khungu pafupi ndi khutu. Kolandira mawu kakang’ono koikidwa kunsi kwa khungu ndi kolumikizidwa mwachindunji ku mtsempha womverera kamapititsa mauthenga kupita ku ubongo, mopitirira njira yachibadwa.
Kufunikira kwa Thandizo Lodalirika Mokulira
Mosasamala kanthu za ziyembekezo zimene kufufuza koteroko kukuwonekera kupereka, asayansi mowona mtima akuzindikira kuti zoyesayesa za kukonza zilema za thupi kaŵirikaŵiri zimalephera chifukwa chakuti sayansi simamvetsetsa choloŵanecholoŵane wa njira imene ziŵalo zathu zakuthupi ndi nzeru zodziŵira zinthu zimagwirira ntchito. Monga chotulukapo, liŵiro liripobe la kupanga chithunzithunzi chokwanira mokulira cha kagwiridwe ka ntchito za thupi lathu.
Pamene kuli kwakuti ambiri angaike chiyembekezo chawo pa sayansi kaamba ka kubwezeretsa kuwona kwa akhungu ndi kumva kwa agonthi, pali maziko odalirika mokulira kaamba ka chiyembekezo. Liri lonjezo la Mlengi wa nzeru zodziŵira zinthu za munthu, Yehova Mulungu. Iye ali amene kale kwambiri anawuzira ulosi wakuti: “Pamenepo maso a akhungu adzatsegudwa, ndi makutu a ogontha adzatsegulidwa.” (Yesaya 35:5) Koma kodi ndimotani mmene tingatsimikizire kuti mawu amenewa adzakhala owona? Kodi nchiyani chimene chiri “pamenepo” pamene chalonjezedwa kudzachitika?
Zowonekeratu za Mtsogolo
Ngati chinthu china chinachitika nthaŵi yapita, kodi chimenecho sichidakakupatsani chidaliro kuti chingachitikenso kachiŵiri, makamaka ngati yemwe anali wathayo kaamba ka icho ananena kuti chikachitika? Chabwino, m’zana loyamba la Nyengo yathu Ino, Yesu Kristu anabwezeretsa nzeru zodziŵira zinthu kwa aja omwe anatayikiridwa izo, monga mmene iye nthaŵi ina anasimbira kuti: “Anthu akhungu alandira kuwona kwawo, opunduka miyendo ayenda, akhate akonzedwa, ogontha akumva.” (Luka 7:22) Kuchiritsa kumeneku sikunadalire pa luso la zopangapanga lamakono.
Nthaŵi ina Yesu anachiritsa mwamuna yemwe anabadwa wakhungu. Anansi ambiri ndi mabwenzi anazindikira chozizwitsacho. Mwamuna amene kuwona kwake kunabwezeretsedwa ananena kuti: “Kuyambira pachiyambi sikunamveka kuti wina anatsegulira maso munthu wosawona chibadwire. Ngati uyu sanachokera kwa Mulungu, sakadakhoza kuchita kanthu.” Inde, Yesu anabwezeretsa kuwona kwa mwamunayo kupyolera m’mphamvu ya Mulungu!—Yohane 9:32, 33.
Kodi chimenechi chinatsimikizira chiyani? Nkulekeranji, kuti ndi mphamvu ya Mulungu, onse ovutika ndi kuwonongeka kwa nzeru zodziŵira zinthu angachiritsidwe! Chotero, Yesu Kristu anachita zozwitsa zimenezi kuwonetsa pa mlingo waung’ono chimene chidzachitika pa dziko lonse lapansi pansi pa kulamulira kwa Ufumu wa Mulungu. Chiri “pamenepo,” mkati mwa kulamulira kwa Ufumu wa Mulungu, pamene padzakhala kukwaniritsidwa kwakukulu mlingaliro lenileni kwa ulosi wa Baibulo wakuti: “Maso a akhungu adzatsegudwa, ndi makutu a ogontha adzatsegulidwa.”—Yesaya 35:5.
Kudziŵa lonjezo la Mulungu kaamba ka mtsogolo limodzinso ndi kubwera mu unansi waumwini ndi iye kumapangitsa munthu wolemala kudzimva kuti kupunduka sikuyenera kukhala kodetsa nkhaŵa mopambanitsa. Iko kumamtheketsa iye kukhala ndi moyo wachimwemwe, wokwanira tsopano. Ndithudi, chidzakhala chodabwitsa chotani nanga pamene awo amene pa nthaŵi ina anali ndi nzeru zodziŵira zinthu zowonongeka adzatumpha ndi kusangalala pamene chisoni chonse ndi kuwusa moyo zidzapita!—Yesaya 35:10.
[Chithunzi patsamba 10]
Chidzakhala chodabwitsa chotani nanga pamene awo amene anali ndi nzeru zodziŵira zinthu zowonongeka adzatumpha ndi kusangalala!