Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga
◼ Asayansi amati nyenyezi zina zimapsya kapena kuphulika, chotero nchifukwa ninji Yesaya 40:26 amati “palibe imodzi [ya nyenyezi] isoŵeka”?
Pano Yehova salankhula zakuti kaya iye amalola nyenyezi kuzimiririka kapena ayi. Iye akugogomezera ukulu wa nzeru zake ndi luntha.
Kwa Mfumu Hezekiya mneneri Yesaya analongosola chenjezo la Mulungu lakuti Ababulo akatengera Ayuda mu undende. (Yesaya 39:5-7) Kodi Ababulo akakhala okhoza kusunga anthu a Mulungu ku nthaŵi yosadziŵika? Ayi. Sikokha kuti Yehova analinganiza kuwamasula patapita zaka 70 komanso akachichita chimenechi. Palibe chirichonse chomwe chikatsekereza Iye amene ‘angayese madzi m’dzanja lake nayesa thambo ndi chikhato.’ Iye sakafunikira kupempha uphungu kwa munthu wina, popeza “amitundu akunga dontho la m’mtsuko” kwa iye. (Yesaya 40:12-17) Kuti agogomezere ukulu wake wochititsa mantha, Yehova anaitanira chisamaliro ku mphamvu zake zosonyezedwa m’chilengedwe, zimene Hezekiya anali atavomereza kalelo. (Yesaya 37:16, 17) Mulungu analengeza kuti:
“Mudzandifanizira ine ndi yani tsono, kuti ndilingane naye, ati Woyerayo. Kwezani maso anu kumwamba, muwone amene analenga izo, amene atulutsa khamu lawo ndi kuziŵerenga; azitcha zonse maina awo, ndi mphamvu zake zazikulu, ndi popeza ali wolimba mphamvu, palibe imodzi isoweka.”—Yesaya 40:25, 26.
Asayansi amayerekeza kuti muli nyenyezi zikwi mamiliyoni ambiri a mu m’lalang’amba wathu wa Milky Way, ndipo pali milalang’amba mamiliyoni mazana chikwi chimodzi. Komabe, Mulungu amadziŵa nyenyezi iriyonse ndi dzina, kaya dzina laumwini kapena chizindikiritso chonga dzina, mwinamwake m’chinenero chaumulungu. Iye ngolamulira mkhalidwe wawo. Mofanana ndi kazembe wankhondo wokhoza kusonkhanitsa magulu ankhondo, Yehova akatha kusonkhanitsa nyenyezi. Ngati iye anatero, palibe iriyonse imene ‘ingasoŵe.’ Akumadziŵa mkhalidwe wa nyenyezi iriyonse, ngakhale ngati zina za izo zingafike kumapeto mwanjira yozoloŵereka, sichiri chodabwitsa kwa Iye amene adziŵa zonse zimene zikuchitika.—Yerekezani ndi Yesaya 34:16.
Akatswiri a zakuthambo ndi a akatswiri a sayansi yachilengedwe amalingalira kuti nyenyezi zimapsyerera kapena kuphulika. Mu Red Giants and White Dwarfs, Robert Jastrow anapereka nthanthi ya mmene ichi chingachitikire: “Mkati mwa . . . nyenyezi nthandadza ya zochitika za nyukliya imapangika, mu imene zinthu zina zonse za chilengedwe chonse zinapangidwa kuchokera ku nsanganizo yamaziko, hydrogen. Pomalizira pake zochitika za nyukliya zimenezi zinazimiririka, ndipo moyo wa nyenyeziyo unafika kumapeto. Itamanidwa zoichirikiza za nyonga, inagwa ndi kulemera kwake, ndipo pambuyo pa kugwa kumeneko kuphulika kunachitika, ikumamwazira m’mlengalenga zinthu zonse zomwe zinalengedwa mkati mwa nyenyeziyo m’nthaŵi ya moyo wake.”
Kukuyerekezeredwa kuti nyenyezi zina, zimagwiritsira ntchito hydrogen yawo, zimasintha kukhala red giants ndipo kenaka kukhala white dwarfs kapena supernovas, zina pomalizira zimathera monga nyenyezi za neutron kapena, mwa nthanthi, black holes.
Pamene kuli kwakuti malongosoledwe oterowo akulandiridwa mofala, liwu lomalizira lingakhale lisanamvedwe; zochulukira zingaphunziridwe. Mwachitsanzo, lingalirani nsonga zonenedwa mu The New York Times ya January 24, 1989: “Asayansi amakhulupirira kuti iwo ali pafupi kutulukira zambiri zonena za ‘nyengo yamdima’ ya chilengedwe chonse, nyengo yofunika kwambiri kuchokera pa mphindi zitatu pambuyo pa kuphulika kwa chilengedwe kufikira pa kuwonekera kwa milalang’amba yaikulu. . . . Pokhala ndi umboni wachindunji wochepera woterowo, chiyambi cha zinthu chachititsa asayansi kuthedwa nzeru kotheratu. James S. Trefil, katswiri wa sayansi yachilengedwe pa Yunivesite ya George Mason mu Fairfax, Va., analemba kuti: ‘Vuto la kulongosola kukhalapo kwa milalang’amba latsimikizira kukhala limodzi la mavuto othetsa nzeru koposa m’sayansi yachilengedwe. Mwakuyenera konse, iyo siyeneradi kukhala kumeneko, komabe iripo.’”
Nkhaniyo inanena zimene zingachitike mkati mwa “mphindi zitatu zoyambirira,” monga momwe Dr. John Mather, katswiri wa sayansi yachilengedwe yopenda zakuthambo walongosolera. Komabe, timaŵerenga kuti: “Dr. Mather, atawona kusokonezeka maganizo komakulakula kwa wofunsayo, anadodometsa kulongosola kwake lingaliro lovomerezeka la zochitika za chilengedwe nanena kuti, ‘Ndithudi, zonsezi nzongoyerekezera,’ kutanthauza kuti ali malongosoledwe atsatanetsatane a nthanthi ozikidwa pa kuyerekezera.”
Inde, asayansi aumunthu ali ochepekedwa kwambiri ponena za zimene iwo kwenikweni amadziŵa ndi zimene angadziŵe. Komabe, nkosiyana chotani nanga, ndi Mlengiyo. Nzeru zake ndi nyonga yake yamphamvu ziridi zoyenera kutidabwitsa. Wamasalmo molondola ananena kuti: “Aŵerenga nyenyezi momwe ziri; azitcha maina zonsezi. Ambuye wathu ndi wamkulu ndi wa mphamvu zambiri; nzeru yake njosatha. . . . Haleluya.”—Salmo 147:4, 5, 20.
[Mawu a Chithunzi patsamba 31]
Chithunzi cha NASA