Yesaya
37 Mfumu Hezekiya itangomva zimenezi, inangʼamba zovala zake nʼkuvala chiguduli. Itatero inapita mʼnyumba ya Yehova.+ 2 Kenako inatuma Eliyakimu amene ankayangʼanira banja lachifumu,* Sebina mlembi ndi akuluakulu a ansembe, onse atavala ziguduli, kuti apite kwa mneneri Yesaya,+ mwana wa Amozi. 3 Iwo anamuuza kuti: “Hezekiya wanena kuti, ‘Lero ndi tsiku la zowawa,* lonyozedwa ndi lochititsidwa manyazi. Chifukwa tili ngati akazi amene atsala pangʼono kubereka,* koma alibe mphamvu zoti aberekere.+ 4 Mwina Yehova Mulungu wanu amva mawu a Rabisake, amene mbuye wake mfumu ya Asuri yamutuma kuti adzanyoze Mulungu wamoyo.+ Ndipo amulanga chifukwa cha mawu amene Yehova Mulungu wanu wamva. Choncho inuyo mupemphere+ mʼmalo mwa anthu amene atsala.’”+
5 Choncho atumiki a Mfumu Hezekiya anapita kwa Yesaya.+ 6 Ndiyeno Yesaya anawauza kuti: “Mukauze mbuye wanu kuti, ‘Yehova wanena kuti: “Usachite mantha+ chifukwa cha mawu amene wamva, amene atumiki a mfumu ya Asuri+ alankhula pondinyoza. 7 Ndiika maganizo* mwa iye ndipo adzamva nkhani inayake nʼkubwerera kudziko lake.+ Ndidzachititsa kuti akaphedwe ndi lupanga mʼdziko lakelo.”’”+
8 Rabisake atamva kuti mfumu ya Asuri yachoka ku Lakisi anabwerera kwa mfumuyo ndipo anaipeza ikumenyana ndi Libina.+ 9 Tsopano mfumuyo inamva zokhudza Mfumu Tirihaka ya Itiyopiya kuti: “Wabwera kudzamenyana nanu.” Itangomva zimenezo, inatumizanso uthenga kwa Hezekiya+ wakuti: 10 “Mukauze Hezekiya mfumu ya Yuda kuti, ‘Mulungu wako amene ukumudalira asakunamize, ponena kuti: “Yerusalemu saperekedwa mʼmanja mwa mfumu ya Asuri.”+ 11 Iweyo wamva zimene mafumu a Asuri anachitira mayiko onse, kuti anawawononga.+ Ndiye iweyo ukuona ngati upulumuka? 12 Kodi milungu ya mitundu imene makolo anga anaiwononga inawapulumutsa?+ Kodi inapulumutsa Gozani, Harana,+ Rezefi ndi anthu a ku Edeni amene anali ku Tela-sara? 13 Ili kuti mfumu ya Hamati, mfumu ya Aripadi ndiponso mfumu ya mzinda wa Sefaravaimu,+ wa Hena ndi wa Iva?’”
14 Hezekiya anatenga makalatawo mʼmanja mwa anthuwo nʼkuwawerenga. Kenako iye anapita nawo kunyumba ya Yehova nʼkuwatambasula pamaso pa Yehova.+ 15 Ndiyeno Hezekiya anayamba kupemphera kwa Yehova+ kuti: 16 “Inu Yehova wa magulu ankhondo akumwamba,+ Mulungu wa Isiraeli, wokhala pamwamba* pa akerubi, inu nokha ndinu Mulungu woona wa maufumu onse apadziko lapansi. Inuyo munapanga kumwamba ndi dziko lapansi. 17 Tcherani khutu lanu, inu Yehova, mumve.+ Tsegulani maso anu, inu Yehova, muone.+ Imvani mawu onse amene Senakeribu watumiza onyoza Mulungu wamoyo.+ 18 Nʼzoonadi Yehova, kuti mafumu a Asuri awononga mayiko onse,+ ndi dziko lawo lomwe. 19 Aponya milungu yawo pamoto,+ chifukwa sinali milungu, koma ntchito ya manja a anthu,+ mitengo ndi miyala. Nʼchifukwa chake anatha kuiwononga. 20 Tsopano inu Yehova Mulungu wathu, tipulumutseni mʼmanja mwake, kuti maufumu onse apadziko lapansi adziwe kuti inu nokha Yehova, ndinu Mulungu.”+
21 Ndiyeno Yesaya mwana wa Amozi anatumiza uthenga kwa Hezekiya wakuti: “Yehova Mulungu wa Isiraeli wanena kuti, ‘Chifukwa chakuti wapemphera kwa ine za Senakeribu mfumu ya Asuri,+ 22 awa ndi mawu otsutsana naye amene Yehova wanena:
“Namwali, mwana wamkazi wa Ziyoni,* wakunyoza ndipo wakunyodola.
Mwana wamkazi wa Yerusalemu* wakupukusira mutu.
23 Kodi ndi ndani amene iwe wamutonza+ ndi kumunyoza?
Ndi ndani amene iwe wamulankhula mokweza,+
Ndiponso kumukwezera maso ako onyada?
Ndi Woyera wa Isiraeli!+
24 Kudzera mwa atumiki ako, wanyoza Yehova+ ndipo wanena kuti,
‘Ndi magaleta anga ankhondo ambiri,
Ndidzakwera pamwamba pa mapiri,+
Ndidzafika kumadera akutali kwambiri a Lebanoni.
Ndidzadula mitengo yake ya mkungudza italiitali, ndi mitengo yake yabwino kwambiri ya junipa.*
Ndidzalowa kumalo ake amene ali pamwamba kwambiri, kunkhalango yowirira.
26 Kodi sunamve? Ndinakonza kalekale zimene ndidzachite.
Ndinakonza zimenezi mʼmasiku amakedzana.+
Tsopano ndizichita.+
Iweyo udzasandutsa mizinda yokhala ndi mipanda yolimba kwambiri kukhala milu ya mabwinja.+
27 Anthu okhala mʼmizindayo adzafooka.
Adzachita mantha ndiponso adzachititsidwa manyazi.
Adzakhala ngati zomera zakutchire komanso ngati udzu wanthete wobiriwira,
Ngati udzu womera padenga umene wawauka ndi mphepo yotentha yakumʼmawa.
28 Koma ine ndimadziwa ukakhala pansi, ukamatuluka ndiponso ukamalowa.+
Ndimadziwanso ukandipsera mtima,+
29 Chifukwa kundipsera mtima kwako+ ndi kufuula kwako zafika mʼmakutu mwanga.+
Choncho ndidzakola mphuno yako ndi ngowe yanga ndipo ndidzamanga zingwe zanga+ pakamwa pako.
Kenako ndidzakukoka nʼkukubweza kudzera njira imene unadutsa pobwera.”
30 Ichi chidzakhala chizindikiro chanu:* Chaka chino mudya mbewu zimene zamera zokha. Mʼchaka chachiwiri mudzadya mbewu zophuka kuchokera ku mbewu zimenezi. Koma mʼchaka chachitatu, mudzadzala mbewu nʼkukolola ndipo mudzalima minda ya mpesa nʼkudya zipatso zake.+ 31 Anthu amʼnyumba ya Yuda amene adzapulumuke, amene adzatsale,+ adzakhala ngati mitengo imene yazika mizu pansi nʼkubereka zipatso zambiri. 32 Chifukwa anthu otsala adzachokera ku Yerusalemu ndipo opulumuka adzachokera kuphiri la Ziyoni.+ Yehova wa magulu ankhondo akumwamba adzachita zimenezi modzipereka kwambiri.+
33 Choncho Yehova wanena izi zokhudza mfumu ya Asuri:+
“Sadzalowa mumzindawu+
Kapena kuponyamo muvi
Kapena kufikamo ndi chishango
Kapenanso kumanga malo okwera omenyerapo nkhondo atauzungulira.”’+
34 ‘Adzabwerera kudzera njira imene anadutsa pobwera,
Ndipo sadzalowa mumzindawu,’ watero Yehova.
35 ‘Ndidzateteza mzindawu+ ndipo ndidzaupulumutsa chifukwa cha ineyo+
Ndiponso chifukwa cha mtumiki wanga Davide.’”+
36 Ndiyeno mngelo wa Yehova anapita kumsasa wa Asuri nʼkukapha asilikali 185,000. Anthu podzuka mʼmawa, anangoona kuti onse ndi mitembo yokhayokha.+ 37 Choncho Senakeribu mfumu ya Asuri anachoka nʼkubwerera kukakhala ku Nineve.+ 38 Pamene Senakeribu ankaweramira mulungu wake Nisiroki mʼkachisi, ana ake Adarameleki ndi Sarezere anamupha ndi lupanga+ nʼkuthawira kudziko la Ararati.+ Kenako mwana wake Esari-hadoni+ anakhala mfumu mʼmalo mwake.