Mboni Zachikristu Zochirikiza Ulamuliro wa Mulungu
“Mukalalikire zoposazo za iye amene anakuitanani mutuluke mumdima, muloŵe kuunika kwake kodabwitsa.”—1 PETRO 2:9.
1. Kodi ndi umboni wotani wogwira mtima umene unaperekedwa ponena za Yehova Chikristu chisanakhaleko?
CHIKRISTU chisanakhaleko, mpambo wautali wa mboni zinachitira umboni kuti Yehova ndiye Mulungu woona yekha. (Ahebri 11:4–12:1) Pokhala ndi chikhulupiriro cholimba, zinamvera malamulo a Yehova mopanda mantha nizikana kugonja pankhani za kulambira. Zinapereka umboni wamphamvu kuchirikiza ulamuliro wa Yehova wa chilengedwe chonse.—Salmo 18:21-23; 47:1, 2.
2. (a) Kodi Mboni yaikulu koposa ya Yehova ndani? (b) Kodi ndani anatenga malo a Israyeli monga mboni ya Yehova? Tidziŵa bwanji?
2 Mboni yomaliza ndi yaikulu koposa yokhalako Chikristu chisanakhaleko anali Yohane Mbatizi. (Mateyu 11:11) Anali ndi mwaŵi wa kulengeza kudza kwa Wosankhika, ndipo anadziŵikitsa Yesu monga Mesiya wolonjezedwayo. (Yohane 1:29-34) Yesu ndiye Mboni yaikulu koposa ya Yehova, “mboni yokhulupirika ndi yoona.” (Chivumbulutso 3:14) Popeza kuti Israyeli wakuthupi anakana Yesu, Yehova anawakana nasankha mtundu watsopano, Israyeli wa Mulungu wauzimu, kukhala mboni yake. (Yesaya 42:8-12; Yohane 1:11, 12; Agalatiya 6:16) Petro anagwira mawu ulosi wonena za Israyeli nasonyeza kuti unali kunena za “Israyeli wa Mulungu,” mpingo Wachikristu, pamene anati: “Inu ndinu mbadwa yosankhika, ansembe achifumu, mtundu woyera mtima, anthu a mwini wake, kotero kuti mukalalikire zoposazo za iye amene anakuitanani mutuluke mumdima, muloŵe kuunika kwake kodabwitsa.”—1 Petro 2:9; Eksodo 19:5, 6; Yesaya 43:21; 60:2.
3. Kodi thayo lalikulu la Israyeli wa Mulungu ndi “khamu lalikulu” nlotani?
3 Mawu a Petro amasonyeza kuti thayo lalikulu la Israyeli wa Mulungu ndilo kupereka umboni wapoyera wa ulemerero wa Yehova. Masiku ano “khamu lalikulu” la mboni zimenenso zimalemekeza Mulungu poyera ladziphatika kwa mtundu wauzimu umenewu. Limafuula ndi mawu aakulu kuti onse amve: “Chipulumutso kwa Mulungu wathu wakukhala pa mpando wachifumu, ndi kwa Mwanawankhosa.” (Chivumbulutso 7:9, 10; Yesaya 60:8-10) Kodi Israyeli wa Mulungu ndi atsamwali awo angauchite motani umboni wawo? Mwa chikhulupiriro chawo ndi kumvera.
Mboni Zonama
4. Kodi nchifukwa ninji Ayuda a m’tsiku la Yesu anali mboni zonama?
4 Chikhulupiriro ndi kumvera zimafuna kutsatira malamulo aumulungu. Zimene Yesu ananena pa atsogoleri achipembedzo Achiyuda a m’tsiku lake zimasonyeza kufunika kwake kwa zimenezo. Iwo ‘anakhala pa mpando wa Mose’ monga ophunzitsa Chilamulo. Anatumiza ndi amishonale kukatembenuza osakhulupirira. Komabe, Yesu anawauza kuti: “Mupitapita kunyanja ndi kumtunda kuyesa munthu mmodzi mtembenuki; ndipo mmene akhala wotere, mumsandutsa mwana wa Gehena woposa inu kaŵiri.” Achipembedzo amenewo anali mboni zonama—zodzikuza, zonyenga, ndi zopanda chikondi. (Mateyu 23:1-12, 15) Nthaŵi ina Yesu anauza Ayuda ena kuti: “Inu muli ochokera mwa atate wanu Mdyerekezi, ndipo zolakalaka zake za atate wanu mufuna kuchita.” Nchifukwa ninji ananena zimenezo kwa anthu a mtundu wosankhika wa Mulungu? Chifukwa chakuti sanalabadire mawu a Mboni yaikulu koposa ya Yehova.—Yohane 8:41, 44, 47.
5. Kodi tidziŵa motani kuti Dziko Lachikristu lapereka umboni wonama ponena za Mulungu?
5 Momwemonso, mkati mwa zaka mazana ambiri chiyambire nthaŵi ya Yesu, miyandamiyanda m’Dziko Lachikristu adzitcha ophunzira ake. Komabe, sanachite chifuniro cha Mulungu ndipo chotero Yesu sanawadziŵe. (Mateyu 7:21-23; 1 Akorinto 13:1-3) Dziko Lachikristu latumiza amishonale, ndipo ambiri a iwo analidi odzipereka. Komabe, anaphunzitsa anthu kulambira mulungu wa Utatu amene amatentha ochimwa m’moto wa helo, ndipo ochuluka mwa anthu amene anatembenuza samasonyeza kwenikweni umboni wakuti ndi Akristu. Mwachitsanzo, dziko la m’Afirika la Rwanda lakhala munda wobala zipatso wa amishonale a Roma Katolika. Chikhalirechobe, Akatolika a ku Rwanda analoŵa ndi mtima wonse m’nkhondo ya mafuko yaposachedwa m’dzikolo. Zipatso za m’munda wa amishonale umenewo zikusonyeza kuti sunalandire umboni woona Wachikristu kuchokera ku Dziko Lachikristu.—Mateyu 7:15-20.
Kutsatira Malamulo Aumulungu
6. Kodi ndimotani mmene khalidwe labwino lilili mbali yofunika kwambiri pa kupereka umboni?
6 Khalidwe loipa la aja amene amati ndi Akristu limadzetsa chitonzo pa “njira ya choonadi.” (2 Petro 2:2) Mkristu weniweni amachita mogwirizana ndi malamulo aumulungu. Samaba, kunama, ngakhale kuchita chisembwere. (Aroma 2:22) Samapha mnansi wake ayi. Amuna Achikristu amayang’anira mabanja awo mwa chikondi. Akazi amachirikiza uyang’aniro umenewo mwa ulemu. Ana amaphunzitsidwa ndi makolo awo choncho amakhala okonzeka kudzakhala achikulire athayo Achikristu. (Aefeso 5:21–6:4) Zoona, ife tonse tili opanda ungwiro ndipo timalakwa. Koma Mkristu weniweni amalemekeza miyezo ya Baibulo ndipo amayesayesa kwambiri kuigwiritsira ntchito. Ena amaziona zimenezi ndipo zimapereka umboni wabwino. Nthaŵi zina, aja amene poyamba amatsutsa choonadi amaona khalidwe labwino la Mkristu ndipo amatembenuka.—1 Petro 2:12, 15; 3:1.
7. Kodi kukondana kwa Akristu nkofunika motani?
7 Yesu anasonyeza mbali yofunika kwambiri ya khalidwe Lachikristu pamene anati: “Mwa ichi adzazindikira onse kuti muli akuphunzira anga, ngati muli nacho chikondano wina ndi mnzake.” (Yohane 13:35) Dziko la Satana ladzala ndi “zosalungama . . . , kuipa, kusirira, dumbo; odzala ndi kaduka, mbanda, ndewu, chinyengo, udani; akazitape, osinjirira, akumuda Mulungu, achipongwe, odzitama, amatukutuku, oyamba zoipa, osamvera [makolo, NW] awo.” (Aroma 1:29, 30) M’mikhalidwe yotero, gulu la padziko lonse lodziŵika ndi chikondi lingakhale chisonyezero champhamvu cha ntchito ya mzimu wa Mulungu—umboni wogwira mtima. Amene apanga gulu lotero ndiwo Mboni za Yehova.—1 Petro 2:17.
Mboni Zili Ophunzira Baibulo
8, 9. (a) Kodi wamasalmo analimbikitsidwa motani mwa kuphunzira Chilamulo cha Mulungu ndi kuchisinkhasinkha? (b) Kodi phunziro la Baibulo ndi kusinkhasinkha zidzatilimbikitsa motani kupitiriza kupereka umboni?
8 Kuti Mkristu akhoze kupereka umboni wabwino, ayenera kudziŵa ndi kukonda malamulo olungama a Yehova ndi kudadi kuipa kwa dzikoli. (Salmo 97:10) Dzikoli limanyengerera pochirikiza kalingaliridwe kake, ndipo mzimu wake ungakhale wovuta kuukaniza. (Aefeso 2:1-3; 1 Yohane 2:15, 16) Kodi nchiyani chimene chingatithandize kukhala ndi mkhalidwe woyenera wa maganizo? Phunziro la Baibulo la nthaŵi zonse ndi latanthauzo. Wolemba Salmo 119 anabwereza nthaŵi zambiri kutchula chikondi chake pa Chilamulo cha Yehova. Anachiŵerenga ndi kuchisinkhasinkha nthaŵi zonse, “tsiku lonse.” (Salmo 119:92, 93, 97-105) Chotero, anakhoza kulemba kuti: “Ndidana nalo bodza ndi kunyansidwa nalo; koma ndikonda chilamulo chanu.” Ndiponso, chikondi chake chachikulu chinamsonkhezera kuchitapo kanthu. Iye akuti: “Ndikulemekezani kasanu ndi kaŵiri, tsiku limodzi, chifukwa maweruzo anu alungama.”—Salmo 119:163, 164.
9 Momwemonso, phunziro lathu la nthaŵi zonse la Mawu a Mulungu ndi kuwasinkhasinkha zidzakhudza mitima yathu ndi kutisonkhezera ‘kumlemekeza’—kuchitira umboni za Yehova—nthaŵi zambiri, ngakhale “kasanu ndi kaŵiri, tsiku limodzi.” (Aroma 10:10) Mogwirizana ndi zimenezi, wolemba salmo loyamba akuti amene alingirira mawu a Yehova nthaŵi zonse ‘adzanga mtengo wooka pa mitsinje ya madzi; wakupatsa chipatso chake pa nyengo yake, tsamba lake lomwe losafota; ndipo zonse azichita apindula nazo.’ (Salmo 1:3) Nayenso mtumwi Paulo anasonyeza mphamvu ya Mawu a Mulungu pamene analemba kuti: “Lemba lililonse adaliuzira Mulungu, ndipo lipindulitsa pa chiphunzitso, chitsutsano, chikonzero, chilangizo cha m’chilungamo: kuti munthu wa Mulungu akhale woyenera, wokonzeka kuchita ntchito iliyonse yabwino.”—2 Timoteo 3:16, 17.
10. Kodi chimene chili choonekeratu ponena za anthu a Yehova lerolino nchiyani?
10 Kuwonjezeka kofulumira kwa chiŵerengero cha alambiri oona m’zaka za zana lino la 20 kumasonyeza dalitso la Yehova. Mosakayikira, mboni zamakono zimenezi za ulamuliro wa Mulungu, monga gulu, zakulitsa kukonda chilamulo cha Yehova m’mitima mwawo. Monga wamasalmo, zimasonkhezereka kumvera chilamulo Chake ndi kuchitira umboni mokhulupirika za ulemerero wa Yehova “usana ndi usiku.”—Chivumbulutso 7:15.
Ntchito Zamphamvu za Yehova
11, 12. Kodi zozizwitsa zochitidwa ndi Yesu ndi otsatira ake zinakwaniritsa chiyani?
11 M’zaka za zana loyamba, mzimu woyera unapatsa mboni zokhulupirika Zachikristu mphamvu yochitira zozizwitsa, zimene zinapereka chisonyezero champhamvu chakuti umboni wawo unali woona. Pamene Yohane Mbatizi anali m’ndende, anatuma ophunzira kukafunsa Yesu kuti: “Inu ndinu Wakudza kodi, kapena tiyembekezere wina?” Yesu sanayankhe kuti inde kapena iyayi. M’malo mwake, anati: “Mukani mubwezere mawu kwa Yohane zimene muzimva ndi kuziona: akhungu alandira kuona kwawo, ndi opunduka miyendo ayenda, akhate akonzedwa, ndi ogontha akumva, ndi akufa aukitsidwa, ndi kwa aumphaŵi ulalikidwa uthenga wabwino. Ndipo wodala iye amene sakhumudwa chifukwa cha ine.” (Mateyu 11:3-6) Ntchito zamphamvu zimenezi zinakhala umboni kwa Yohane wakuti Yesu analidi “Wakudza.”—Machitidwe 2:22.
12 Momwemonso, ena a otsatira a Yesu anachiritsa odwala ngakhale kuukitsa akufa. (Machitidwe 5:15, 16; 20:9-12) Zozizwitsa zimenezi zinali monga umboni wochokera kwa Mulungu mwini kaamba ka iwo. (Ahebri 2:4) Ndipo ntchito zimenezo zinasonyeza mphamvu yaikulu ya Yehova. Mwachitsanzo, ndi zoona kuti Satana “mkulu wa dziko lapansi,” ali ndi mphamvu ya kuchititsa imfa. (Yohane 14:30; Ahebri 2:14) Koma pamene Petro anaukitsa Dorika, mkazi wokhulupirika kwa akufa, sakanachita zimenezo mwa mphamvu ina kusiyapo ya Yehova yokha, pakuti ndi Iye yekha amene atha kubwezeretsa moyo.—Salmo 16:10; 36:9; Machitidwe 2:25-27; 9:36-43.
13. (a) Kodi zozizwitsa za m’Baibulo zimachitirabe motani umboni za mphamvu ya Yehova? (b) Kodi kukwaniritsidwa kwa ulosi kumathandizira kwambiri motani kusonyeza Umulungu wa Yehova?
13 Lerolino, ntchito zozizwitsa zimenezo sizimachitikanso. Zinakwaniritsa chifuno chake. (1 Akorinto 13:8) Komabe, tikali ndi mbiri yake m’Baibulo, imene openyerera ambiri anakhalira mboni. Pamene Akristu lerolino afotokoza nkhani za m’mbiri zimenezi, ntchitozo zimaperekabe umboni wogwira mtima wa mphamvu ya Yehova. (1 Akorinto 15:3-6) Ndiponso, m’tsiku la Yesaya, Yehova anasonyeza ulosi wolondola kukhala umboni wapadera wakuti Iye ndiye Mulungu woona. (Yesaya 46:8-11) Maulosi ambiri ouziridwa a Baibulo akukwaniritsidwa lerolino—ambiri a iwo pa mpingo Wachikristu. (Yesaya 60:8-10; Danieli 12:6-12; Malaki 3:17, 18; Mateyu 24:9; Chivumbulutso 11:1-13) Kuwonjezera pa kusonyeza kuti tikukhala mu “masiku otsiriza,” kukwaniritsidwa kwa maulosi ameneŵa kumatsimikizira kuti Yehova ndiye Mulungu woona yekha.—2 Timoteo 3:1.
14. Kodi mbiri yamakono ya Mboni za Yehova yakhala motani umboni wamphamvu wakuti Yehova ndiye Ambuye Mfumu?
14 Potsiriza, Yehova akali kuchitira anthu ake zinthu zazikulu, zinthu zodabwitsa. Kuunika komawonjezeka kwa choonadi cha Baibulo kumatsogozedwa ndi mzimu wa Yehova. (Salmo 86:10; Chivumbulutso 4:5, 6) Ziwonjezeko zazikulu zomveka padziko lonse zili umboni wakuti Yehova ‘akufulumiza ichi m’nthaŵi yake.’ (Yesaya 60:22) Pamene kwabuka chizunzo chowopsa m’maiko osiyanasiyana m’nthaŵi yonseyi ya masiku otsiriza, kupirira kolimba mtima kwa anthu a Yehova kwatheka chifukwa cha mphamvu yolimbikitsa ya mzimu woyera. (Salmo 18:1, 2, 17, 18; 2 Akorinto 1:8-10) Inde, mbiri yokha yamakono ya Mboni za Yehova ili umboni wamphamvu wakuti Yehova ndiye Ambuye Mfumu.—Zekariya 4:6.
Uthenga Wabwino Woyenera Kulalikidwa
15. Kodi mpingo Wachikristu unali kudzapereka umboni wotani wokulirapo?
15 Yehova anasankha Israyeli monga mboni yake kwa amitundu. (Yesaya 43:10) Komabe, ndi Aisrayeli oŵerengeka chabe amene Mulungu analamula kupita kukalalikira kwa osakhala Aisrayeli, ndipo nthaŵi zambiri chifuno chake chinali chakuti akalengeze ziweruzo za Yehova. (Yeremiya 1:5; Yona 1:1, 2) Chikhalirechobe, maulosi a m’Malemba Achihebri amasonyeza kuti Yehova tsiku lina adzatembenukira kwa amitundu, ndipo wazichita zimenezi kupyolera mwa Israyeli wauzimu wa Mulungu. (Yesaya 2:2-4; 62:2) Asanakwere kumwamba, Yesu analamula otsatira ake kuti: “Chifukwa chake mukani, phunzitsani anthu a mitundu yonse.” (Mateyu 28:19) Pamene kuli kwakuti Yesu anasumika maganizo pa “nkhosa zotayika za banja la Israyeli,” otsatira ake anawatuma ku “mitundu yonse,” ngakhale “kufikira malekezero ake a dziko.” (Mateyu 15:24; Machitidwe 1:8) Anthu onse anayenera kumva umboni Wachikristu.
16. Kodi mpingo Wachikristu wa m’zaka za zana loyamba unakwaniritsa ntchito yotani, ndipo pamlingo wotani?
16 Paulo anasonyeza kuti anamvetsetsa zimenezi. Pofika chaka cha 61 C.E., anakhoza kunena kuti uthenga wabwino unali ‘kubala zipatso m’dziko lonse lapansi.’ Uthenga wabwino sunangolalikidwa kwa mtundu umodzi kapena kagulu kamodzi chabe, monga kaja ‘kanagwadira angelo.’ M’malo mwake, ‘unalalikidwa poyera cholengedwa chonse cha pansi pa thambo.’ (Akolose 1:6, 23; 2:13, 14, 16-18) Chotero, Israyeli wa Mulungu m’zaka za zana loyamba anakwaniritsa ntchito yake ya ‘kulalikira zoposazo za iye amene anawaitana atuluke mumdima kuloŵa kuunika kwake kodabwitsa.’
17. Kodi Mateyu 24:14 akupitiriza motani kukwaniritsidwa mwa njira yokulira?
17 Chikhalirechobe, ntchito yolalikira ya m’zaka za zana loyamba imeneyo inali chabe chithunzi cha imene inali kudzachitidwa m’masiku otsiriza. Poyang’ana mtsogolo makamaka ku nthaŵi yathu, Yesu anati: “Uthenga uwu wabwino wa ufumu udzalalikidwa pa dziko lonse lapansi, ukhale mboni kwa anthu amitundu yonse; ndipo pomwepo chidzafika chimaliziro.” (Mateyu 24:14; Marko 13:10) Kodi ulosi umenewu wakwaniritsidwa? Inde, watero. Kuchokera pa chiyambi chochepa mu 1919, kulalikira uthenga wabwino tsopano kwafalikira kumaiko oposa 230. Umboni akuumva Kumpoto kozizira ndi kumadera otentha. Ukukuta makontinenti aakulu, ndipo zisumbu zakutali akuzifunafuna kuti nzika zake zilandire umboni. Ngakhale kumene chipolowe chowopsa chili mkati, ngati nkhondo ya ku Bosnia ndi Herzegovina, uthenga wabwino ukulalikidwabe. Monga m’zaka za zana loyamba, umboni ukubala chipatso “m’dziko lonse lapansi.” Uthenga wabwino ukulengezedwa poyera ku “cholengedwa chonse cha pansi pa thambo.” Chotulukapo chake? Choyamba, otsalira a Israyeli wa Mulungu asonkhanitsidwa mwa “mafuko onse, ndi manenedwe onse, ndi mitundu yonse.” Chachiŵiri, anayamba kubweretsa mamiliyoni a “khamu lalikulu” kuchokera mwa “mtundu uliwonse, ndi mafuko ndi anthu ndi manenedwe.” (Chivumbulutso 5:9; 7:9) Mateyu 24:14 akupitiriza kukwaniritsidwa mwa njira yokulira.
18. Kodi kulalikira uthenga wabwino padziko lonse kukukwaniritsa zinthu zina zotani?
18 Kulalikira uthenga wabwino padziko lonse kumathandizira kusonyeza kuti kukhalapo kwa Yesu kwachifumu kunayamba. (Mateyu 24:3) Ndiponso, ndiyo njira yaikulu yotutira “dzinthu za dziko,” pakuti imasonyeza anthu chiyembekezo chawo chokha, Ufumu wa Yehova. (Chivumbulutso 14:15, 16) Popeza kuti ndi Akristu enieni okha amene akulalikira uthenga wabwino, ntchito yofunika imeneyi imathandizira kusiyanitsa Akristu oona ndi onama. (Malaki 3:18) Mwa njira imeneyi, imadzetsa chipulumutso kwa olalikirawo ndi kwa omvera. (1 Timoteo 4:16) Chofunika koposa, kulalikira uthenga wabwino kumapereka chitamando ndi ulemu kwa Yehova Mulungu, amene analamula kuti kuchitidwe, amene amachirikiza aja amene akukuchita, ndi amene amakubalitsa zipatso.—2 Akorinto 4:7.
19. Kodi ndi kutsimikiza mtima kotani kumene Akristu onse akulimbikitsidwa kukhala nako pamene akuloŵa chaka chautumiki chatsopano?
19 Nchifukwa chake mtumwi Paulo anasonkhezereka kunena kuti: “Tsoka ine ngati sindilalikira uthenga wabwino.” (1 Akorinto 9:16) Ndi mmene Akristu lerolino amamvera. Kukhala “antchito anzake a Mulungu,” oŵalitsa kuunika kwa choonadi m’dziko lamdimali kuli mwaŵi waukulu ndipo ndi thayo lalikulu. (1 Akorinto 3:9; Yesaya 60:2, 3) Ntchito imene inali yaing’ono pachiyambi mu 1919 yakhala yaikulu kwambiri tsopano. Pafupifupi Akristu mamiliyoni asanu akuchitira umboni ulamuliro wa Mulungu pamene awonongera maola oposa mamiliyoni chikwi chimodzi pachaka pa kupereka uthenga wa chipulumutso kwa ena. Ha, nkosangalatsa chotani nanga kukhala ndi mbali m’ntchito imeneyi yoyeretsa dzina la Yehova! Pamene tikuloŵa chaka chautumiki cha 1996, tiyeni titsimikize mtima kuti sitidzabwerera m’mbuyo. M’malo mwake, koposa ndi kale lonse tidzalabadira mawu a Paulo kwa Timoteo: “Lalikira mawu, chita nawo panthaŵi yake.” (2 Timoteo 4:2) Pamene tikuchita zimenezo, tipemphere ndi mtima wonse kuti Yehova apitirize kudalitsa zoyesayesa zathu.
Kodi Mukukumbukira?
◻ Kodi ndani anatenga malo a Israyeli monga “mboni” ya Yehova kwa amitundu?
◻ Kodi khalidwe Lachikristu limathandizira motani kuperekedwa kwa umboni?
◻ Kodi nchifukwa ninji kuphunzira Baibulo ndi kulisinkhasinkha kuli kofunika kwa Mboni Yachikristu?
◻ Kodi mbiri yamakono ya Mboni za Yehova yakhala motani chisonyezero chakuti Yehova ndiye Mulungu woona?
◻ Kodi kulalikira uthenga wabwino kumakwaniritsa chiyani?
[Zithunzi patsamba 15]
M’malo mwa kulalikidwa kwa anthu ochepa, uthenga wabwino ukulengezedwa tsopano kwa “cholengedwa chonse cha pansi pa thambo”