Mutu 10
Kodi Tsiku Lililonse Mumafunsa Kuti, “Ali Kuti Yehova?”
1, 2. (a) Kodi moyo wauzimu wa Ayuda a m’nthawi ya Yeremiya unali wotani? (b) Kodi Ayudawo anayenera kuchita chiyani poona mmene moyo wawo wauzimu unalili?
YEREMIYA anakhudzidwa kwambiri moti mpaka analira chifukwa choona mmene moyo wauzimu wa Ayuda anzake unalili pa nthawiyo, komanso chifukwa cha uthenga waulosi umene Mulungu anamuuza wokhudza tsogolo la anthuwo. Iye ankalakalaka mutu wake ukanakhala chitsime cha madzi ndiponso maso ake akanakhala kasupe kuti iye azingolira osalekeza. Yeremiya anali ndi zifukwa zomveka zolirira mtundu wa Yuda chifukwa cha mmene zinthu zinalili. (Yer. 9:1-3; werengani Yeremiya 8:20, 21.) Ayudawo anapitiriza kukana kumvera malamulo a Yehova ndipo sankamvera mawu ake, choncho ankayembekezera kukumana ndi tsoka.—Yer. 6:19; 9:13.
2 Komabe anthu a ku Yuda sankafuna kumva mmene Yehova ankaonera khalidwe lawolo. M’malomwake, iwo ankakonda kumva uthenga wochokera kwa atsogoleri awo achipembedzo, omwe ankangokhalira kuwauza kuti zonse zili bwino. (Yer. 5:31; 6:14) Ayudawo anali ngati anthu odwala amene ankafunafuna dokotala woti awauze zinthu zongowasangalatsa, osati za matenda aakulu omwe anali nawo. Inuyo mutakhala kuti mukudwala kwambiri, kodi simungafune kuti dokotala akuyezeni n’kupeza matenda enieni amene mukudwalawo, n’cholinga choti mulandire chithandizo choyenerera mwamsanga? Mofanana ndi zimenezi, Ayuda a m’nthawi ya Yeremiya anayenera kupempha kuti Mulungu awaunike n’kuwauza mmene moyo wawo wauzimu unalilidi. Iwo anayenera kufunsa kuti: “Ali kuti Yehova?”—Yer. 2:6, 8.
3. (a) Kodi Ayuda akanayankha bwanji funso lakuti, “Ali kuti Yehova?” (b) Kodi njira imodzi imene Ayudawo akanafunirafunira Yehova inali yotani?
3 Kuti Ayudawo afunse kuti, “Ali kuti Yehova?” anafunika kuti nthawi zonse akamasankha zochita, kaya pa nkhani zing’onozing’ono kapena zikuluzikulu, azifufuza kaye malangizo a Mulungu. Koma Ayuda a nthawi imeneyo sankachita zimenezi. Komabe, pambuyo poti mzinda wa Yerusalemu wawonongedwa ndipo Ayudawo abwerako ku Babulo, iwo anafunika ‘kufunafuna Yehova.’ Ngati akanachita zimenezi, akanamupeza ndi kudziwa njira zake. (Werengani Yeremiya 29:13, 14.) Koma kodi iwo akanamufunafuna bwanji? Njira imodzi ikanakhala kupemphera kwa Mulungu mochokera pansi pa mtima kuti awatsogolere. Izi n’zimene Mfumu Davide ankachita. Iye anapempha Mulungu kuti: “Ndidziwitseni njira zanu, inu Yehova. Ndiphunzitseni kuyenda m’njira zanu.” (Sal. 25:4) Taonani mawu olimbikitsa amene Yehova, yemwe ndi Wakumva pemphero, anauza anthuwo kudzera mwa Yeremiya m’chaka cha 10 cha ulamuliro wa Mfumu Zedekiya. Iye anati: “Mundiitane ndipo ndidzakuyankhani. Nthawi yomweyo ndidzakuuzani zinthu zazikulu ndi zovuta kuzimvetsa zimene simukuzidziwa.” (Yer. 33:3) Ngati mfumuyo pamodzi ndi mtundu wa anthu opandukawo akanaitana Mulungu, Mulunguyo akanawauza zinthu zimene kwa iwo zikanakhala “zovuta kuzimvetsa,” zokhudza kuwonongedwa kwa mzinda wa Yerusalemu ndiponso kumangidwa kwake pambuyo pa zaka 70.
4, 5. Kodi anthu a Mulungu akanafunafuna Yehova m’njira zina ziti?
4 Njira ina imene Ayudawo akanafunirafunira Yehova inali kufufuza mbiri yakale n’kuona mmene Yehova ankachitira zinthu ndi anthu ake. Ngati akanachita zimenezi, akanakumbukira zinthu zimene Mulungu anasangalala nazo komanso zimene zinamukwiyitsa. Iwo anali ndi mabuku amene Mose analemba komanso mabuku angapo a mbiri yakale ouziridwa ndi Mulungu, ndiponso anali ndi mabuku ofotokoza mbiri ya mafumu a Isiraeli ndi Yuda. Ngati Ayuda a m’nthawi ya Yeremiya akanaganizira mozama zinthu zimene zinali m’mabuku amenewa komanso ngati akanamvera zonena za aneneri oona a Mulungu, akanatha kupeza yankho la funso lakuti, “Ali Kuti Yehova?”
5 Njira yachitatu imene Ayudawo akanafunirafunira Yehova inali kuphunzira pa zinthu zimene zinachitikira iwowo komanso anthu ena. Sikuti iwo anafunika kuphunzira chilichonse pambuyo pokumana kaye ndi mavuto, koma akanaganizira zimene iwo anachita m’mbuyomo ndi mmene Yehova anazionera, zikanawathandiza kwambiri. Iwo akanati aziganizira zinthu mofatsa, akanatha kudziwa mmene Yehova ankaonera zinthu zomwe iwo anali kuchita pa nthawiyo.—Miy. 17:10.
6. Kodi chitsanzo cha Yobu chingakulimbikitseni bwanji?
6 Koma tsopano tiyeni tibweretse nkhani imeneyi kwa ife masiku ano. Kodi inuyo mukamasankha zochita ndiponso mukamaganizira zimene mukufuna kuchita pa moyo wanu, nthawi zonse mumafunsa kuti, “Ali kuti Yehova?” Ena angavomereze kuti akhala asakuchita zimenezi mokwanira. Ngati inunso mukuona kuti penapake muli ndi vuto limeneli, musakhumudwe. Ngakhale Yobu, amene anali munthu wokhulupirika, analinso ndi vuto limeneli pa nthawi ina. Atakumana ndi mavuto oopsa, iye anayamba kumangoganizira kwambiri za iye yekha. Moti Elihu anachita kukumbutsa Yobu za vuto limene anthu ambiri amakhala nalo, pomuuza kuti: “Palibe wanena kuti, ‘Kodi Mulungu, Wondipanga Wamkulu, ali kuti?’” (Yobu 35:10) Kenako Elihu analimbikitsa Yobu kuti: ‘Ganizirani mozama ntchito zodabwitsa za Mulungu.’ (Yobu 37:14) Yobu ankafunika kuti aganizire mofatsa ntchito zamphamvu za Yehova zimene zili paliponse m’chilengedwe, komanso aganizire mmene Mulungu wakhala akuchitira zinthu ndi anthu. Kudzera m’zinthu zimene Yobu anakumana nazo, anafika pomvetsa bwino njira za Yehova. Yobu atapirira mavuto oopsa amene anakumana nawo ndiponso ataona mmene Yehova anayendetsera zinthu, anati: “Ine ndinalankhula, koma sindinali kuzindikira zinthu zodabwitsa kwambiri kwa ine, zimene sindikuzidziwa. Ndinkangomva za inu, koma tsopano diso langa lakuonani.”—Yobu 42:3, 5.
7. Monga mmene chithunzi cha patsamba 116 chikusonyezera, kodi tikambirana chiyani m’ndime zotsatirazi?
7 Koma mneneri Yeremiya anapitiriza kufunafuna Yehova, ndipo anamupeza. Mosiyana ndi Ayuda anzake, pa zaka zambirimbiri zimene Yeremiya ankagwira mokhulupirika ntchito yake monga mneneri, anapitiriza kufunsa kuti: “Ali kuti Yehova?” M’ndime zotsatira za mutu uno, tiona kudzera m’chitsanzo cha Yeremiya momwe nafenso tingafunirefunire Yehova. Chitsanzo cha Yeremiya chitithandiza kuona kuti tingafunefune Yehova kudzera m’pemphero, kuphunzira mawu ake, ndiponso kudzera mu zinthu zimene zatichitikira pa moyo wathu.—1 Mbiri 28:9.
Kodi kufunsa kuti “Ali kuti Yehova,” kumatanthauza chiyani? Kodi Ayuda a m’nthawi ya Yeremiya akanafunsa funso limeneli pochita zinthu zotani?
YEREMIYA ANKAPEMPHERA KWA YEHOVA NTHAWI ZONSE
8. Kodi Yeremiya ankapemphera kwa Mulungu pa nthawi ziti?
8 Pa zaka zonse zimene Yeremiya anali mneneri wa Mulungu kwa anthu a fuko la Yuda, ankafunafuna Yehova popemphera kwa iye mochokera pansi pa mtima. Mwachitsanzo, iye anapemphera kwa Yehova pamene ankafunika kulengeza uthenga umene anthu ambiri ankadana nawo, pa nthawi imene ankaona kuti sangathe kupitiriza utumiki wake, ndiponso pa nthawi imene sankamvetsa chifukwa chimene zinthu zinazake zinkachitikira. Ndipo Mulungu anamuyankha n’kumupatsa malangizo omuthandiza kudziwa chochita. Tiyeni tione zitsanzo zingapo za zimenezi.
9. (a) Kodi Yeremiya anafotokoza zotani pa Yeremiya 15:15, 16, ndipo Yehova anamuyankha bwanji? (b) Kodi n’chifukwa chiyani mukuona kuti kufotokoza maganizo anu kwa Mulungu m’pemphero n’kofunika?
9 Pa nthawi ina Yeremiya atauzidwa kuti alengeze uthenga wodzudzula Ayuda mwamphamvu, iye ankaona kuti aliyense akumufunira zoipa. Choncho mneneriyu anapemphera kwa Mulungu kuti amukumbukire. Taganizirani zimene ananena m’pemphero lake, limene timalipeza pa Yeremiya 15:15, 16. (Werengani.) M’pempheroli, Yeremiya anafotokoza mavuto amene ankakumana nawo, komanso momwe anamvera atalandira thandizo lochokera kwa Yehova. Koma iye atapeza mawu a Mulungu n’kuwadya mophiphiritsira, anakhalanso wosangalala. Yehova anamuthandiza kuti aziyamikira mwayi umene anali nawo wotchedwa ndi dzina la Mulungu komanso kulengeza uthenga wochokera kwa Mulungu. Yeremiya anatha kuona bwinobwino maganizo a Yehova pa nkhani imeneyi. Kodi ifeyo tingaphunzirepo chiyani pamenepa?
10. Kodi Mulungu anathandiza bwanji Yeremiya atanena m’pemphero kuti sadzalankhulanso m’dzina la Yehova?
10 Pa nthawi inanso, Yeremiya atamenyedwa ndi wansembe Pasuri, mwana wa Imeri, ananena kuti sadzalankhulanso m’dzina la Yehova. Kodi Mulungu anamuyankha bwanji Yeremiya, atafotokoza maganizo akewa m’pemphero? (Werengani Yeremiya 20:8, 9.) Baibulo silimatiuza kuti Mulungu anayankha pemphero la Yeremiyali polankhula naye kuchokera kumwamba. Koma mawu a Mulungu anakhala ngati moto woyaka umene anautsekera m’mafupa ake, ndipo sakanachitira mwina koma kuwalengeza basi. Chifukwa chakuti Yeremiya analankhula moona mtima kwa Mulungu m’pemphero komanso analola kuti akhudzidwe mtima ndi zinthu zimene ankadziwa zokhudza chifuniro cha Mulungu, iye analimbikitsidwa ndipo anachita zinthu zimene Mulungu ankafuna kuti iye achite.
11, 12. Kodi Yeremiya anayankhidwa bwanji funso lake lokhudza anthu oipa amene ankaoneka ngati zinthu zikuwayendera bwino?
11 Yeremiya anavutika mumtima ataona kuti anthu oipa zinthu zikuwayendera bwino. (Werengani Yeremiya 12:1, 3.) Mneneriyu sankakayikira zoti Yehova ndi wolungama, komabe ankafuna kuti Mulungu amuyankhe pa “dandaulo” lake. Iye analankhula mosapita m’mbali, zimene zikusonyeza kuti anali pa ubwenzi wabwino ndi Mulungu, ngati umene umakhalapo pakati pa mwana ndi bambo ake achikondi. Chimene chinachititsa Yeremiya kudandaula n’chakuti sankamvetsa chifukwa chake Ayuda ambiri zinthu zinkawayendera bwino ngakhale kuti anali oipa. Kodi Yeremiya anapeza yankho logwira mtima? Inde, chifukwa Yehova anamutsimikizira kuti adzazula anthu oipa. (Yer. 12:14) Yeremiya ataona mmene nkhani zimene anauza Mulungu m’pemphero zinayendera, ayenera kuti anayamba kukhulupirira kwambiri kuti Mulungu ndi wachilungamo. Poona zimenezi, Yeremiya ayenera kuti anayamba kulankhula ndi Mulungu pafupipafupi m’pemphero, n’kumauza Atate wake wakumwambayo nkhawa zake.
12 Ulamuliro wa Zedekiya utatsala pang’ono kutha, pa nthawi imene Ababulo anazungulira mzinda wa Yerusalemu, Yeremiya analemba mawu ofotokoza za Yehova. Iye anati: “Maso anu amaona njira zonse za ana a anthu kuti munthu aliyense mumuchitire zinthu mogwirizana ndi njira zake komanso zipatso za ntchito zake.” (Yer. 32:19) Yeremiya anatha kuona bwinobwino kuti Yehova amakondadi chilungamo. Iye anazindikira kuti Mulungu amaona zinthu zonse zimene aliyense akuchita, ndipo amamvetsera mapemphero ochokera pansi pa mtima a atumiki ake. M’kupita kwa nthawi, atumiki a Mulungu anaona umboni winanso wochuluka wosonyeza kuti iye ‘amachitira munthu aliyense zinthu mogwirizana ndi njira zake komanso zipatso za ntchito zake.’
13. N’chifukwa chiyani muli wotsimikiza kuti Mulungu adzachita chifuniro chake?
13 N’zoona kuti ifeyo mwina sitikayikira zoti Mulungu ndi wachilungamo komanso sitikayikira zoti iye amachita zinthu mwanzeru pokwaniritsa chifuniro chake panopa ngakhalenso m’tsogolo. Komabe, kuganizira mozama zinthu zimene Yeremiya anakumana nazo, n’kumafotokoza m’mapemphero athu mmene tikumveradi mumtima mwathu, kungatithandize. Tikamachita zimenezi, chikhulupiriro chathu mwa Yehova chidzakula ndipo sitidzakayikira zoti iye adzakwaniritsadi chifuniro chake. Mwina panopa sitikumvetsetsa bwinobwino chifukwa chimene zinthu zikuchitikira mwanjira inayake padzikoli. Mwinanso sitikumvetsetsa chifukwa chimene zinthu zokhudzana ndi chifuniro cha Mulungu zikuyendera pang’onopang’ono. Ngakhale zili choncho, tikhoza kuuza Mulungu m’pemphero kuti tikudziwa kuti iye ndi amene akuyendetsa zinthu zonse. Chifuniro chake chidzachitika m’njira imene iyeyo akuona kuti ndi yabwino kwambiri ndiponso pa nthawi yake. Zimenezi n’zotsimikizirika, ndipo tilibe chifukwa chilichonse chozikayikirira. Tipitirizabe kufunsa kuti “Ali kuti Yehova?” popemphera kwa iye nthawi zonse kuti atithandize kumvetsa chifuniro chake ndiponso kuona umboni woti chifuniro chakecho chikukwaniritsidwa.—Yobu 36:5-7, 26.
Mukaona zimene zinachitikira Yeremiya pambuyo popemphera kwa Yehova, kodi zikukulimbikitsani bwanji?
YEREMIYA ANKAPHUNZITSA MTIMA WAKE MAWU A MULUNGU
14. Kodi tikudziwa bwanji kuti Yeremiya ankafufuza mbiri ya anthu a Mulungu?
14 Kuti apeze yankho la funso lakuti, “Ali kuti Yehova?” Yeremiya ankadziwa bwino kufunika ‘kodziwa Yehova.’ (Yer. 9:24) Pamene Yeremiya ankalemba mabuku amene panopa amadziwika kuti Mafumu Woyamba ndi Wachiwiri, ayenera kuti anafufuza bwino mbiri ya anthu a Mulungu. Iye anatchula mwachindunji ‘buku lonena za Solomo,’ ‘buku la zochitika za m’masiku a mafumu a Isiraeli’ ndiponso ‘buku la zochitika za m’masiku a mafumu a Yuda.’ (1 Maf. 11:41; 14:19; 15:7) Chifukwa chofufuza mbiri ya anthu a Mulungu, iye anamvetsa bwino mmene Yehova anachitira zinthu pa nkhani zosiyanasiyana. Yeremiya anatha kuona zinthu zimene zinkasangalatsa Yehova ndiponso mmene Yehovayo ankaonera zinthu zimene anthu ankasankha kuchita. Iye ayenera kuti ankawerenganso mabuku ouziridwa ndi Mulungu amene analipo pa nthawiyo, monga mabuku olembedwa ndi Mose, Yoswa, Samueli, Davide, ndi Solomo. Mosakayikira, mneneriyu ayenera kuti ankadziwa bwino zonena za aneneri a m’mbuyo mwake, komanso a m’nthawi yake. Kodi kuphunzira zinthu zonsezi kunamuthandiza bwanji Yeremiya?
15. Kodi kuphunzira mozama ulosi wa Eliya kunamuthandiza bwanji Yeremiya?
15 Yeremiya analemba nkhani ya Yezebeli, mkazi woipa wa Mfumu Ahabu ya ku Samariya. M’nkhaniyi, iye analembanso zimene Eliya ananena zoti agalu adzadya Yezebeli m’munda wa ku Yezereeli. (1 Maf. 21:23) Ndipo mogwirizana ndi zimene Yeremiya analemba, mukudziwa kuti patapita zaka 18, Yezebeli anagwetsedwa pansi kuchokera pawindo kenako anapondedwapondedwa ndi mahatchi a Yehu, n’kudyedwa ndi agalu. (2 Maf. 9:31-37) Chikhulupiriro cha Yeremiya m’mawu a Mulungu chiyenera kuti chinalimba pamene ankaphunzira za ulosi umene Eliya ananena, komanso mmene unakwaniritsidwira wonse ndendende. Zoonadi, chimene chinathandiza Yeremiya kuti apirire pa ntchito yake monga mneneri, ndi chikhulupiriro chimene anali nacho chifukwa chophunzira mozama zinthu zimene Yehova anachitira anthu ake kalelo.
16, 17. Kodi mukuona kuti n’chifukwa chiyani Yeremiya anapirira pa ntchito yake yochenjeza mafumu oipa a m’nthawi yake?
16 Tsopano tiyeni tione chitsanzo china. Kodi mukuganiza kuti n’chiyani chinathandiza Yeremiya kuti apitirizebe kuchenjeza mafumu oipa monga Yehoyakimu ndi Zedekiya, ngakhale kuti iye ankazunzidwa? Chifukwa chachikulu chinali choti Yehova anachititsa Yeremiya kukhala ngati “mzinda wokhala ndi mpanda wolimba kwambiri, mzati wachitsulo ndi makoma amkuwa” kwa mafumu a Yuda. (Yer. 1:18, 19) Komabe tisaiwale mfundo yakuti Yeremiya anafufuza kwambiri nkhani zokhudza zinthu zimene mafumu akale a Yuda ndi Isiraeli anachita pa nthawi ya ulamuliro wawo. Iye analemba zoti Manase “anamangira maguwa ansembe khamu lonse la zinthu zakuthambo, m’mabwalo awiri a nyumba ya Yehova,” komanso zoti anatentha mwana wake pamoto pomupereka nsembe, ndiponso anakhetsa magazi ochuluka zedi a anthu osalakwa. (2 Maf. 21:1-7, 16; werengani Yeremiya 15:4.) Koma Yeremiya ayenera kuti ankadziwa kuti Manase atadzichepetsa n’kuyamba kupemphera kwa Yehova, “iye anamva kupembedzera kwake,” ndipo anabwezeretsa mfumuyo pampando wake wachifumu.—Werengani 2 Mbiri 33:12, 13.
17 M’mabuku amene Yeremiya analemba, sanatchulemo za chifundo chimene Yehova anachitira Manase. Komatu Manase anamwalira patangotsala zaka pafupifupi 15 kuti Yeremiya ayambe ntchito yake monga mneneri. Choncho mneneriyu ayenera kuti anamva zimene zinachitika Manase atalapa n’kusiya zoipa zimene ankachita kale. Yeremiya anafufuza za khalidwe loipa la Manase komanso zimene zinadzachitika pambuyo pake. Zimenezi ziyenera kuti zinamuthandiza kuona ubwino wolimbikitsa mafumu, monga Zedekiya, kuti apemphe Yehova kuti awachitire chifundo ndi kuwasonyeza kukoma mtima kosatha. Iye anazindikira zimenezi chifukwa ngakhale mfumu imene inali ndi mbiri yoipa kwambiri chifukwa cha kupembedza mafano ndi kukhetsa magazi a anthu osalakwa, inalapa n’kukhululukidwa. Inuyo mukanakhala kuti ndinu Yeremiya, kodi zimene zinachitikira Manase zikanakulimbikitsani, n’kukuthandizani kuti mupirire pa nthawi ya ulamuliro wa mafumu ena oipa?
ANATENGERAPO PHUNZIRO PA ZINTHU ZINA ZIMENE ZINACHITIKA
18. Kodi Yeremiya ayenera kuti anaphunzira chiyani pa chitsanzo cha Uliya, ndipo n’chifukwa chiyani mukuyankha choncho?
18 Pa nthawi yonse imene Yeremiya anali mneneri, ayenera kuti anaphunzirapo kanthu poona mmene Ayuda anzake ankachitira zinthu pa nkhani zosiyanasiyana. Mmodzi mwa anthu amenewa anali mneneri Uliya, amene analosera pa nthawi ya ulamuliro wa Yehoyakimu, za tsoka limene linali litatsala pang’ono kugwera Yerusalemu ndi Yuda. Koma Uliya anathawira ku Iguputo chifukwa choopa Mfumu Yehoyakimu. Ndiyeno mfumuyo inatuma anthu kuti akatenge Uliya ku Iguputo n’kubwera naye ku Yuda, ndipo kenako anamupha. (Yer. 26:20-23) Kodi mukuganiza kuti Yeremiya anaphunzirapo kanthu pa zimene zinachitikira Uliya? Mfundo yakuti Yeremiya anapitiriza kuchenjeza Ayuda za tsoka limene linali litatsala pang’ono kuwagwera, mpaka kufika powauza zimenezi pakachisi, ikusonyeza kuti iye anaphunzirapo kanthu. Yeremiya anapitiriza kukhala wolimba mtima, ndipo Yehova sanamutaye. Mulungu ayenera kuti ndi amene anachititsa Ahikamu, mwana wa Safani, kuti ateteze moyo wa mneneri wolimba mtimayu.—Yer. 26:24.
19. Kodi Yeremiya ayenera kuti anazindikira mfundo yotani poona kuti Yehova ankatumiza aneneri mobwerezabwereza kwa anthu ake?
19 Yeremiya anaphunziranso pa zimene iyeyo anakumana nazo pogwiritsidwa ntchito ndi Yehova kuti achenjeze anthu ake. M’chaka chachinayi cha ulamuliro wa Mfumu Yehoyakimu, Yehova anauza Yeremiya kuti alembe mawu onse amene Yehovayo anali atanena kuchokera m’nthawi ya Yosiya mpaka nthawi imeneyo. Kodi n’chifukwa chiyani Mulungu anauza Yeremiya kuti achite zimenezi? Chifukwa chakuti ankafuna kulimbikitsa anthu kuti asiye kuchita zoipa n’kukhululukidwa. (Werengani Yeremiya 36:1-3.) Yeremiya, amene ankadzuka m’mawa kwambiri kuti auze anthuwo mauthenga ochenjeza ochokera kwa Mulungu, anafika mpaka pochonderera anthuwo kuti asiye khalidwe lawo lonyansa. (Yer. 44:4) Apatu zikuonekeratu kuti Yeremiya anazindikira kuchokera pa zinthu zimene zinam’chitikira, kuti Mulungu ankatumiza aneneri kwa anthu akewo chifukwa chowamvera chisoni. Ndipo zimenezi ziyenera kuti zinathandiza Yeremiya kuwamveranso chisoni anthuwo. (2 Mbiri 36:15) Choncho m’pomveka kuti Yeremiya atapulumuka pa nthawi imene mzinda wa Yerusalemu unawonongedwa, ananena kuti: “Chifukwa cha kukoma mtima kosatha kwa Yehova, ife sitinafafanizidwe, ndipo chifundo chake sichidzatha. Chifundocho chimakhala chatsopano m’mawa uliwonse.”—Maliro 3:22, 23.
Kodi Yeremiya ayenera kuti anakhudzidwa bwanji atafufuza zimene Mulungu anachitira anthu ake, komanso ataganizira mozama zimene zinachitikira iyeyo ndi anthu ena? Kodi ifeyo tikuphunzirapo chiyani pamenepa? (Onaninso chithunzi patsamba 123.)
KODI INUYO TSIKU LILILONSE MUMAFUNSA KUTI, “ALI KUTI YEHOVA?”
20. Kodi mungatsanzire bwanji Yeremiya pa nkhani yofufuza chifuniro cha Yehova?
20 Mukamasankha zochita tsiku lililonse, kodi mumayesetsa kufufuza chifuniro cha Mulungu pa nkhaniyo, kumene kuli ngati kufunsa kuti, “Ali kuti Yehova?” (Yer. 2:6-8) Mosiyana ndi Ayuda a m’nthawi yake, Yeremiya nthawi zonse ankapempha Wamphamvuyonse kuti amuthandize kusankha zinthu mwanzeru. Choncho, n’chinthu chanzeru kuti aliyense wa ife akamasankha zochita tsiku lililonse, azitengera chitsanzo cha Yeremiya n’kumapempha Yehova kuti amuthandize kusankha zinthu mwanzeru.
21. Kodi ndi pemphero lotani limene lingakuthandizeni pa utumiki wanu? Nanga kodi pemphero lingakuthandizeni bwanji ngati munthu wina atakulankhulani mwachipongwe mu utumiki?
21 Sikuti nkhani imene mukufunika kusankhapo chochitayo nthawi zonse iyenera kukhala yaikulu kapena yomwe ingasinthe moyo wanu. Mwachitsanzo, nkhani yake ikhoza kukhala yokhudza kupita mu utumiki wa kumunda pa tsiku limene munakonzekera kuchita zimenezi. Mwina mutadzuka pa tsikulo, mwaona kuti kumwamba kwachita mitambo, ndipo zimenezi zakugwetsani ulesi. Mwinanso gawo limene lasankhidwa kuti mukalalikire khomo ndi khomo tsiku limenelo, ndi loti mumalalikirako pafupipafupi. N’kuthekanso kuti mwakumbukira kuti ena mwa anthu a m’gawo limenelo anakukaniranipo uthenga wanu mwaulemu, kapenanso anakukanirani mwachipongwe kwambiri. Kodi mungapemphere m’mawa womwewo n’kufunsa kuti “Ali kuti Yehova?” Kupemphera mwanjira imeneyi kungakuthandizeni kuti mukumbukire kuti uthenga umene mukalalikire tsiku limenelo ndi wosangalatsa kwambiri komanso kungakuthandizeni kwambiri kukumbukira mfundo yakuti Mulungu akufuna kuti mukalengeze uthenga umenewo. Mukatero, mawu a Yehova angakuchititseni kuti mukhale wosangalala kwambiri mumtima mwanu, ngati momwe zinachitikira ndi Yeremiya. (Yer. 15:16, 20) Kenako pamene mukulalikira, ngati mutakumana ndi munthu wina amene akukuyankhani mwamwano kapenanso mokuopsezani, kachiwirinso mukhoza kupemphera kwa Mulungu. Kodi mudzachita zimenezi? Musaiwale kuti Mulungu akhoza kukupatsani mzimu woyera kuti ukuthandizeni kuyankha moyenerera, ndipo mtima wanu wofunitsitsa kulengeza uthenga wa Mulungu ungakuthandizeni kuti musakhumudwe.—Luka 12:11, 12.
22. N’chifukwa chiyani Mulungu angasiye kumvetsera mapemphero ena?
22 Ndi bwino kukumbukira kuti mapemphero ena akhoza kutsekerezedwa, kapena kusamvedwa. (Werengani Maliro 3:44.) Yehova sanamvere mapemphero a Ayuda opanduka chifukwa iwo ‘ankathawitsa makutu awo kuti asamumvere’ komanso ankangopitirizabe kuchita zinthu zosamvera malamulo. (Miy. 28:9) Apa panali phunziro loonekeratu kwa Yeremiya, lomwe liyeneranso kukhala loonekeratu kwa ife, lakuti: Ngati munthu sakuchita zinthu zogwirizana ndi mapemphero ake, Mulungu amakhumudwa ndipo akhoza kusiya kumvetsera mapemphero a munthuyo. Choncho, tiyenera kuyesetsa ndi mtima wonse kupewa zimenezi.
23, 24. (a) Kodi tiyenera kuchita chiyani kuti tidziwe chifuniro cha Yehova? (b) Kodi mungatani kuti muzipindula kwambiri mukamaphunzira Baibulo panokha?
23 Kuwonjezera pa kupemphera kwa Yehova mochokera pansi pa mtima kuti atitsogolere, tiyeneranso kupitiriza kuphunzira Baibulo patokha. Imeneyi ndi njira yofunika kwambiri yodziwira chifuniro cha Yehova. Pa nkhani imeneyi, ifeyo tili ndi mwayi waukulu kuposa Yeremiya, chifukwa tili ndi Baibulo lonse lathunthu. Mofanana ndi Yeremiya, amene anafufuza zinthu mwakhama kuti athe kulemba mabuku ouziridwa ndi Mulungu ofotokoza mbiri ya anthu ake, inunso mukhoza kufufuza m’Mawu a Mulungu kuti iye akutsogolereni, zomwe zingakhale ngati kufunsa kuti, “Ali kuti Yehova?” Mukamayesetsa kuphunzira Mawu a Mulungu kuti mudziwe chifuniro chake, mudzayamba kumudalira kwambiri ndipo mudzakhala “ngati mtengo wobzalidwa m’mphepete mwa madzi, umene mizu yake imakafika m’ngalande za madzi.”—Werengani Yeremiya 17:5-8.
24 Mukamawerenga Malemba Opatulika n’kumaganizira mozama zimene mukuwerengazo, muziyesetsa kuzindikira zimene Yehova akufuna kuti muchite pa nkhani zosiyanasiyana. Mukhoza kumafufuza mfundo zimene mukufuna kuti muzizikumbukira n’kumazigwiritsa ntchito pa moyo wanu. Mukamawerenga mabuku ofotokoza mbiri yakale, malamulo ndi mfundo za Mulungu, komanso miyambi yanzeru imene ili m’Mawu a Mulungu, muziganizira momwe zinthu zimenezi zingakuthandizireni pamene mukusankha zochita tsiku lililonse. Mukamafunsa kuti “Ali kuti Yehova?” iye akhoza kugwiritsira ntchito Mawu ake olembedwa kuti akutsogolereni pamene mukukumana ndi mavuto osiyanasiyana pa moyo wanu, ngakhalenso mavuto osowetsa mtendere kwambiri. Mukamachita zimenezi, mukhoza kuyamba kumvetsetsa zinthu za m’Baibulo ‘zovuta kuzimvetsa zimene simunali kuzidziwa,’ kapena zimene munali musanaziganizirepo mwanjira inayake.—Yer. 33:3.
25, 26. Kodi kuganizira zimene zinachitikira anthu ena komanso zimene zinachitikira ifeyo kungatithandize bwanji?
25 Komanso, mungaganizire zinthu zimene zakuchitikirani inuyo ndiponso zimene zachitikira anthu ena. Mwachitsanzo, mukhoza kuona kuti anthu ena amasiya kudalira Yehova, ngati mmene anachitira Uliya. (2 Tim. 4:10) Inuyo mungaphunzirepo kanthu kuchokera pa zimene anachitazo, n’kupewa kukumana ndi mavuto ofanana ndi amene iwo anakumana nawo. Muzikumbukira nthawi zonse zinthu zimene Yehova wakuchitirani chifukwa cha kukoma mtima kwake kosatha, ndipo musamaiwale kuti nayenso Yeremiya ankayamikira chifundo chimene Mulungu ankamusonyeza. Kaya zinthu zivute bwanji, musamaganize kuti Wam’mwambamwamba sakuganizirani. Iye amakuganizirani, mofanana ndi mmene anachitira ndi Yeremiya.
26 Mukamaganizira zinthu zimene Yehova akuchitira anthu osiyanasiyana masiku ano, mungathe kuona kuti iye akutitsogolera tsiku lililonse m’njira zosiyanasiyana. Mwachitsanzo, mlongo wina wachitsikana ku Japan, dzina lake Aki, ankadziona kuti si woyenera kukhala Mkhristu. Tsiku lina Aki ali mu utumiki wa kumunda ndi mkazi wa woyang’anira dera, anamuuza nkhawa zake. Aki anati ankaona kuti Yehova sasangalala ndi utumiki wake ndipo wangotsala pang’ono kumutaya ngakhale kuti iye ankayesetsa kuti apitirizebe kumutumikira. Pogwiritsa ntchito mawu a Yesu amene ali m’buku la Chivumbulutso, Aki anati: “Ndikuona kuti Yehova watsala pang’ono kundilavula m’kamwa mwake, koma ndikumuchonderera kuti andipatseko kanthawi.” Mkazi wa woyang’anira derayo anayang’anitsitsa Aki n’kumulimbikitsa ndi mawu akuti: “Ine sindinayambe ndaganizapo kuti iweyo ndiwe mlongo wofooka.” Aki anaganizira mozama mawu olimbikitsa amenewo. Ndipotu panalibe chinthu chilichonse chosonyeza kuti Yehova anayamba wamuonapo ngati wofooka. Kenako, Aki anapemphera kwa Yehova n’kumuuza kuti: “Nditumizeni kulikonse komwe mukufuna. Ndidzachita chilichonse chimene mukufuna kuti ndichite.” Chapanthawi yomweyo, Aki anapita kukacheza kudziko lina kumene kunali gulu laling’ono la chilankhulo cha Chijapani. Anthu a m’gululi ankafunika thandizo la munthu wolankhula chinenerochi yemwe akanatha kukhala m’dzikolo n’kumatumikira nawo limodzi. Mwamwayi, Aki anabadwira m’dziko limenelo, ndipo zinali zosavuta kuti iye asamukire m’dzikolo n’kumathandiza gulu lija. Koma vuto linali loti Aki analibe kokhala. Ndiyeno mlongo wina amene mwana wake wamkazi anali atangosamuka kumene, anauza Aki kuti akhoza kumakhala m’chipinda china m’nyumba yake. Aki anati: “Zonse zinkangoyenda bwinobwino, popanda chovuta chilichonse, ndipo zinkachita kuonekeratu kuti Yehova akunditsegulira njira.”
27. N’chifukwa chiyani funso lakuti, “Ali kuti Yehova?” liyenera kukulimbikitsani?
27 Abale ndi alongo ambiri angafotokoze kuti pa nthawi inayake anaona kuti Mulungu akuwatsogolera mwapadera, mwina pamene ankawerenga Baibulo kapena kuphunzira paokha mabuku ofotokoza Baibulo. Mwina inunso zimenezi zinakuchitikiranipo. Zinthu zimenezi ziyenera kulimbitsa ubwenzi wanu ndi Yehova n’kukulimbikitsani kuti muzipemphera kwa iye pafupipafupi ndiponso mochokera pansi pa mtima. Musakayikire kuti tsiku lililonse tikamafunsa kuti, “Ali kuti Yehova?” iye adzatisonyeza njira yake.—Yes. 30:21.
Kodi mungapeze bwanji yankho la funso lakuti, “Ali kuti Yehova?” Nanga mungachite zinthu zotani kuti mulole Yehova kukutsogolerani?