2 Mafumu
21 Manase+ anayamba kulamulira ali ndi zaka 12 ndipo analamulira zaka 55 ku Yerusalemu.+ Mayi ake anali Hefiziba. 2 Iye ankachita zoipa pamaso pa Yehova ndipo ankatsatira zinthu zonyansa zomwe ankachita anthu a mitundu+ imene Yehova anaithamangitsa pamaso pa Aisiraeli.+ 3 Iye anamanganso malo okwezeka amene Hezekiya bambo ake anachotsa.+ Komanso anamanga maguwa ansembe a Baala ndi mzati wopatulika,*+ ngati mmene Ahabu mfumu ya Isiraeli anachitira.+ Manase ankalambira ndiponso kutumikira gulu lonse la zinthu zakuthambo.+ 4 Anamanganso maguwa ansembe mʼnyumba ya Yehova,+ imene Yehova ananena kuti: “Ku Yerusalemu ndidzaikako dzina langa.”+ 5 Iye anamanga maguwa ansembe a gulu lonse la zinthu zakumwamba+ mʼmabwalo awiri a nyumba ya Yehova.+ 6 Manase anatentha* mwana wake wamwamuna pamoto, ankachita zamatsenga, ankawombeza+ ndiponso anaika anthu olankhula ndi mizimu komanso olosera zamʼtsogolo.+ Iye anachita zinthu zambiri zoipa pamaso pa Yehova ndiponso zomukwiyitsa.
7 Komanso iye anaika mʼnyumbayo chifaniziro cha mzati wopatulika+ chimene anapanga. Koma ponena za nyumbayo, Yehova anauza Davide ndi mwana wake Solomo kuti: “Mʼnyumba iyi ndiponso mu Yerusalemu, mzinda umene ndausankha pa mafuko onse a Isiraeli, ndidzaikamo dzina langa mpaka kalekale.+ 8 Sindidzachititsanso mapazi a Aisiraeli kuchoka mʼdziko limene ndinapatsa makolo awo,+ ngati atayesetsa kuchita zinthu mogwirizana ndi zonse zimene ndinawalamula,+ mogwirizana ndi Chilamulo chonse chimene Mose mtumiki wanga anawauza kuti azitsatira.” 9 Koma sanamvere ndipo Manase anapitiriza kusocheretsa anthu ndiponso kuwachititsa zinthu zoipa kuposa zimene mitundu yomwe Yehova anaiwononga pamaso pa Aisiraeli inkachita.+
10 Yehova anapitiriza kulankhula kudzera mwa atumiki ake, aneneri,+ kuti: 11 “Manase mfumu ya Yuda wachita zinthu zonyansa zonsezi. Wachita zinthu zoipa kwambiri kuposa zonse zimene anachita Aamori+ amene analiko iye asanakhale mfumu.+ Iye wachititsa Yuda kuchimwa ndi mafano ake onyansa.* 12 Choncho Yehova Mulungu wa Isiraeli wanena kuti, ‘Ndibweretsera tsoka Yerusalemu+ ndi Yuda loti aliyense akamva, mʼmakutu ake onse mudzalira.+ 13 Ndidzayeza Yerusalemu ndi chingwe chimene ndinayezera+ Samariya+ ndiponso ndidzamuyeza ndi levulo imene ndinayezera nyumba ya Ahabu.+ Yerusalemu ndidzamʼpukuta mpaka kuyera ngati mmene munthu amapukutira mbale yolowa mpaka kuyera, nʼkuitembenuza.+ 14 Anthu otsala pa cholowa changa+ ndidzawasiya ndipo ndidzawapereka mʼmanja mwa adani awo. Iwo pamodzi ndi katundu wawo adzatengedwa ndi adani awo onse.+ 15 Ndidzachita zimenezi chifukwa chakuti iwo anachita zoipa pamaso panga ndipo akhala akundikwiyitsa kuyambira tsiku limene makolo awo anatuluka ku Iguputo mpaka lero.’”+
16 Manase anaphanso anthu ambiri osalakwa mpaka magazi awo anadzaza Yerusalemu kuyambira koyambirira mpaka kumapeto,+ kuwonjezera pa tchimo lake lochititsa kuti Ayuda achimwe pochita zoipa pamaso pa Yehova. 17 Nkhani zina zokhudza Manase, zonse zimene anachita ndiponso machimo ake, zinalembedwa mʼbuku la mbiri ya mafumu a Yuda. 18 Kenako Manase, mofanana ndi makolo ake, anamwalira ndipo anaikidwa mʼmanda mʼmunda wapanyumba pake, mʼmunda wa Uziza.+ Ndiyeno mwana wake Amoni anakhala mfumu mʼmalo mwake.
19 Amoni+ anayamba kulamulira ali ndi zaka 22 ndipo analamulira zaka ziwiri ku Yerusalemu.+ Mayi ake anali a ku Yotiba ndipo dzina lawo linali Mesulemeti mwana wa Haruzi. 20 Amoni ankachita zoipa pamaso pa Yehova ngati mmene anachitira Manase bambo ake.+ 21 Iye ankayenda mʼnjira zonse zimene bambo ake anayendamo ndipo anapitiriza kutumikira mafano onyansa amene bambo ake ankawatumikira komanso kuwagwadira.+ 22 Choncho anasiya Yehova, Mulungu wa makolo ake ndipo sanayende mʼnjira ya Yehova.+ 23 Patapita nthawi, atumiki a Mfumu Amoni anamukonzera chiwembu nʼkumupha mʼnyumba mwake momwe. 24 Koma anthu a mʼdzikolo anapha anthu onse amene anakonzera chiwembu Mfumu Amoni. Kenako anthu amʼdzikolo anaika mwana wake Yosiya kuti akhale mfumu mʼmalo mwake.+ 25 Nkhani zina zokhudza Amoni ndiponso zimene anachita, zinalembedwa mʼbuku la mbiri ya mafumu a Yuda. 26 Choncho anamuika mʼmanda ake mʼmunda wa Uziza+ ndipo mwana wake Yosiya+ anakhala mfumu mʼmalo mwake.