Mutu 7
Mawu Anayi Amene Anasintha Dziko
1. Kodi mawu anayi olembedwa pakhoma kalekalelo anali amphamvu chotani?
MAWU anayi aafupi analembedwa pakhoma pomata bwino. Komabe, mawu anayiwo anachititsa mantha wolamulira wamphamvu moti anam’thetsa nzeru. Uthenga wake wa mawuwo unali kunena za kugwa kwa mafumu aŵiri, imfa ya mmodzi wa iwo, ndi kutha kwa ulamuliro wamphamvu padziko lonse. Zotsatira za mawuwo zinanyazitsa gulu la achipembedzo audindo wapadera olemekezedwa kwambiri. Koma chachikulu n’chakuti mawuwo anakweza kulambira koyera kwa Yehova ndi kutsimikizira za uchifumu wake panthaŵi imene anthu ambiri anali ataiŵala zonsezi. Eya, mawu amenewo anaunikanso zochitika za padziko lapansi lerolino! Kodi ndi motani mmene mawu anayi okhawo anachitira zonsezo? Tiyeni tione.
2. (a) Kodi chinachitika n’chiyani m’Babulo pambuyo pa imfa ya Nebukadinezara? (b) Kodi ndani tsopano anali wolamulira?
2 Panapita zaka zambiri chichitikireni zinthu zofotokozedwa m’chaputala 4 cha buku la Danieli. Ulamuliro wa zaka 43 wa Nebukadinezara, Mfumu ya Babulo yonyadayo, unathera pa imfa yake mu 582 B.C.E. Kenako panatsatira mndandanda wa mafumu om’lowa m’malo ochokera ku banja lake, koma ulamuliro wawo sunakhalitse chifukwa mmodzi ndi mmodzi wa iwo amamwalira msanga kapena kuphedwa. Potsirizira pake, munthu wina wotchedwa Nabonidasi anagalukira boma ndi kulanda mpando wachifumu. Monga mwana wa mkulu wa ansembe wachikazi wa mulungu wa mwezi wotchedwa Sini, zikuoneka kuti Nabonidasi sanachokere m’banja lachifumu la Babulo. Zolemba zina zanena kuti iye anakwatira mwana wa Nebukadinezara. Pofuna kuti ulamuliro wake ukhale wololeka, anasankha mwana wake Belisazara kukhala wom’thandiza, ndipo iye amachoka kwa zaka zingapo akumasiyira mwana wakeyo kulamulira Babulo. Ngati zinali choncho, ndiye kuti Belisazara anali mdzukulu wa Nebukadinezara. Kodi iye anaphunzirapo kanthu pa zimene zinaonekera agogo ake, kuti Yehova ndiye Mulungu Wamkulukulu, wokhoza kuchititsa manyazi mfumu iliyonse? Kutalitali!—Danieli 4:37.
MADYERERO APITIRIRA MUYESO
3. Kodi phwando la Belisazara linali motani?
3 Chaputala 5 cha buku la Danieli chimayamba ndi phwando. “Mfumu Belisazara anakonzera anthu ake akulu chikwi chimodzi madyerero aakulu, namwa vinyo pamaso pa chikwicho.” (Danieli 5:1) Tangoganizani ukulu wake wa holo imene inakwana kukhalamo amuna onsewo, limodzi ndi akazi aang’ono ndi akazi apambali a mfumuyo. Katswiri wina anati: “Mapwando achibabulo anali apamwamba kwambiri, ngakhale kuti kaŵirikaŵiri amathera m’maledzero. Pamagome odyera pamadzaza vinyo woitanitsa kunja ndi mitundumitundu yosaneneka ya zakudya zokoma. Fungo lokoma la zonunkhiritsa limamvekera paliponse m’holo; akatswiri oimba pakamwa komanso oimbira zipangizo ankasangalatsa alendo osonkhana.” Atakhala pamalo oonekera kwa onse, Belisazara anamwa vinyo wake ndipo anamwa, ndi kumwa.
4. (a) N’chifukwa chiyani zingaoneke zodabwitsa kuti Ababulo anali pamadyerero usiku wa pa October 5/6, mu 539 B.C.E.? (b) N’chiyani chinapatsa Ababulowo chidaliro poyang’anizana ndi adani oukirawo?
4 Zikuoneka zodabwitsa kuti Ababulowo anali pachisangalalo choterocho usiku umenewu—pa October 5/6, 539 B.C.E. Dziko lawo linali pankhondo, ndipo zinthu sizinali kuwayendera bwino. Posachedwa, Nabonidasi anali atagonjetsedwa ndi asilikali a Mediya ndi Perisiya ndipo anathaŵira ku Borisipa, kumwera chakumadzulo kwa Babulo. Ndipo tsopano asilikali a Koresi anamanga misasa kunja kwenikweniko kwa Babulo. Komabe, sizimaoneka kuti Belisazara ndi nduna zakezo anada nkhaŵa. Ndi iko komwe, mzinda wawo suja nanga wotchedwa Babulo wosagonjetseka! Linga lake lalikululo linali apo! Kutalika kwake pamwamba pa maenje a chemba akuya kwambiri odzaza madzi a mtsinje waukulu wa Firate umene unadutsa mumzindamo. Palibe mdani aliyense amene anazemberapo ndi kuloŵa m’Babulo pazaka zoposa chikwi chimodzi. Nanga chodera nkhaŵa n’chiyani? Mwinamwakenso Belisazara anaganiza kuti phokoso la chisangalalo chawo likaonetsa adani awo kunjako chidaliro chawo ndi kuwaziziritsa m’nkhongono.
5, 6. Kodi Belisazara anatani atadakwa ndi vinyo, ndipo n’chifukwa chiyani zimene anachitazo zinali kum’tukwana kwambiri Yehova?
5 Posakhalitsa, vinyo uja amene Belisazara anali kumwa mopitirira muyeso anam’dakwitsa. Malinga n’kunena kwa Miyambo 20:21, “vinyo achita chiphwete.” Koma pachochitikachi, vinyo anachititsa mfumuyi chinthu chopusa koposa. Inalamula kuti zotengera zopatulika zimene zinatengedwa m’kachisi wa Yehova zibwere pamadyereropo. Zotengerazo, zimene Nebukadinezara anafunkha pogonjetsa Yerusalemu, zinayenera kugwiritsidwa ntchito kokha pakulambira koyera. Ngakhale ansembe achiyuda amene ankaloledwa kuzigwiritsa ntchito m’kachisi ku Yerusalemu nthaŵi za m’mbuyomo, anali atachenjezedwa kuti anayenera kuzisunga zoyera.—Danieli 5:2; yerekezani ndi Yesaya 52:11.
6 Komabe, Belisazara anali kuganizabe kuchita chinthu china chamwano kwambiri. “Mfumu ndi akulu ake, akazi ake ndi akazi ake aang’ono, anamweramo. . . . nalemekeza milungu yagolidi, ndi yasiliva, yamkuwa, yachitsulo, yamtengo, ndi yamwala.” (Danieli 5:3, 4) Choncho Belisazara anafuna kukweza milungu yake pamwamba pa Yehova! Zikuoneka kuti maganizo amenewo anali ofala pakati pa Ababulo. Iwo anaona akaidi awo achiyudawo monga anthu onyozeka, ananyoza chipembedzo chawo ndi kusawapatsa chiyembekezo chilichonse chobwerera kudziko lakwawo lokondekalo. (Salmo 137:1-3; Yesaya 14:16, 17) Mwinamwake mfumu yodakwayi inaganiza kuti kunyazitsa andendewa ndi kutukwana Mulungu wawo kukasangalatsa akazi ake ndi nduna zakezo, kuti ioneke yamphamvu kwa iwo.a Koma ngati Belisazara panthaŵiyi anali atamva mangolomera, anali apakanthaŵi.
MAWU OLEMBEDWA PAKHOMA
7, 8. Kodi madyerero a Belisazara anasokonezedwa bwanji, ndipo zimenezo zinaikhudza motani mfumuyo?
7 Nkhani youziridwa imati: “Nthaŵi yomweyo zinabuka zala za dzanja la munthu, nizinalemba pandunji pa choikapo nyali, pomata pa khoma la chinyumba cha mfumu; ndipo mfumu inaona nsonga yake ya dzanja lidalembalo.” (Danieli 5:5) Zinali zoopsa bwanji! Dzanjalo linangoonekera lili lenga, m’malere pafupi ndi khoma lounikidwa bwino. Tangoganizani bata limene linagwa paphwandopo, pamene alendowo anangoti kukamwa yasa, podabwa ndi zimene anali kuonazo. Dzanjalo linayamba kulemba pakhoma mawu osazindikirika.b Chochitikachi chinali chododometsa kwambiri ndi chosaiŵalika, moti mpaka lero anthu amatchulabe mawu akuti “mawu olembedwa pakhoma” pochenjeza za tsoka linalake loyandikira.
8 Kodi zimenezi zinaikhudza motani mfumu yonyadayo imene inayesa kudzikweza ndi kukwezanso milungu yake pamwamba pa Yehova? “Pamenepo padasandulika pa nkhope pake pa mfumu, ndi maganizo ake anam’sautsa, ndi mfundo za m’chuuno mwake zinaguluka, ndi mawondo ake anawombana.” (Danieli 5:6) Cholinga cha Belisazara chinali choti aoneke wamkulu ndi wopambana kwa nduna zake. M’malo mwake, anaoneka wamantha womvetsa chisoni. Nkhope yake inasintha ndi mantha, mfundo za m’chiuno mwake zinaguluka, thupi lake lonse linanjenjemera kwambiri moti mawondo ake anali kuwombana. Mawu a Davide m’nyimbo yake kwa Yehova anakhaladi oona. Iye anati: “Maso anu ali pa odzikuza kuti muwachepetse.”—2 Samueli 22:1, 28; yerekezani ndi Miyambo 18:12.
9. (a) N’chifukwa chiyani mantha a Belisazara sanali aumulungu? (b) Kodi mfumuyo inawalonjeza chiyani amuna anzeru a Babulo?
9 Tiyenera kudziŵa kuti mantha a Belisazara sanali mantha aumulungu, mantha olemekeza Yehova, amene ali chiyambi cha nzeru. (Miyambo 9:10) M’malo mwake, anali mantha a kuopsezedwa, ndipo sanapereke nzeru iliyonse kwa mfumu yonjenjemerayo.c M’malo mopempha chikhululukiro kwa Mulungu amene anali atam’tukwana kumene, iye anafuula kuitana “openda, Akasidi, ndi alauli.” Mpaka analengeza kuti: “Aliyense amene adzaŵerenga lemba ili, nadzandifotokozera kumasulira kwake, adzavekedwa chibakuwa, ndi unyolo wagolidi m’khosi mwake, nadzakhala wolamulira wachitatu m’ufumuwu.” (Danieli 5:7) Wolamulira wachitatu mu ufumuwo akakhala wamkulu kwambiri, akaposedwa ndi mafumu olamulira aŵiri okha, Nabonidasi ndi Belisazara mwiniyo. Udindo umenewo anayenera kuusungira mwana wamkulu wa Belisazara. Mfumuyo inathedwa nzeru koopsa! Ikanachita chilichonse chotheka kuti uthenga wozizwitsawo aumasulire!
10. Kodi zinawayendera bwanji amuna anzeruwo poyesetsa kumasulira mawu olembedwa pakhoma?
10 Amuna anzeru anandandalikana m’holo yaikuluyo. Analipo ambiri kwabasi, popeza Babulo unali mzinda wozama m’chipembedzo chonyenga ndipo unali ndi akachisi ambirimbiri. Amuna odzinenera kuti amatha kutanthauzira malaulo ndi kuŵerenga zilembo zosazindikirika analiponso ochuluka. Amuna anzeru ameneŵa ayenera kuti anali atanyadira mpata wapadera umenewo. Anaona kuti unali mwayi wawo kuti aonetse ukatswiri wawo pamaso pa akuluakulu, kuti asangalatse mfumu, ndi kuti akwezedwe paudindo wapamwamba. Koma kulephera kwawo kunali kochititsa manyazi! “Sanakhoza kuŵerenga lembalo, kapena kudziŵitsa mfumu kumasulira kwake.”d—Danieli 5:8.
11. N’zifukwa zotani zimene zikanalepheretsa amuna anzeru a Babulo kuŵerenga mawu olembedwawo?
11 N’zosatsimikizika ngati amuna anzeru a Babulo analephera kuŵerenga zilembo zenizeni za mawu olembedwawo. Koma ngati analepheradi, amuna osaona mtima ameneŵa akanakhala ndi mpata wopereka tanthauzo lililonse lachinyengo, ngakhale lotamanda mfumuyo moigwira m’maso. Mwinanso zilembozo zinali zotheka kuŵerengeka. Komabe, popeza zinenero monga Chialamu ndi Chihebri zinkalembedwa zopanda mavawelo, liwu lililonse likanatha kukhala ndi matanthauzo angapo osiyanasiyana. Ngati zinali choncho, kukanakhala kovuta kuti amuna anzeruwo adziŵe mawu ofunikirawo. Ngakhale akanadziŵa mawuwo, iwo akanalepherabe kumvetsa tanthauzo la mawuwo kuti awamasulire. Mulimonse mmene zinalili, mfundo ndi yakuti: Amuna anzeru a Babulo analephera, zinawakanika mochititsa manyazi!
12. Kodi kulephera kwa amuna anzeruwo kunatsimikizira chiyani?
12 Pachifukwa chimenecho, amuna anzeruwo anaonekera poyera kukhala atambwali, ndi udindo wawo m’chipembedzo unavumbuluka kukhala wachinyengo. Anali ogwiritsa mwala bwanji! Belisazara ataona kuti chidaliro chake mwa achipembedzo ameneŵa chinali chogwiritsa fuwa lamoto, mantha ake anaŵirikiza, nkhope yake inasinthiratu, ndipo ngakhale nduna zakezo ‘zinathedwa nzeru.’e—Danieli 5:9.
MUNTHU WALUNTHA AITANIDWA
13. (a) N’chifukwa chiyani mfumukaziyo inapempha kuti Danieli aitanidwe? (b) Kodi Danieli anali ndi moyo wotani?
13 Panthaŵi yovuta imeneyi, mfumukazi yeniyeniyo, mwachionekere amayi ake a mfumuyo, analoŵa m’chipinda cha madyereromo. Anali atamva phokoso lochokera kuphwandoko, ndipo ankadziŵa munthu wina amene akanatha kuŵerenga mawu olembedwa pakhomawo. Zaka zambiri m’mbuyomo bambo wake wa mayiyu, Nebukadinezara, anali atasankha Danieli monga woyang’anira amuna ake onse anzeru. Mfumukaziyu anakumbukira kuti munthuyo anali ndi “mzimu wopambana, ndi chidziwitso, ndi luntha.” Popeza zikuoneka kuti Danieli sanali wodziŵika kwa Belisazara, mneneriyo ayenera kuti anali atachotsedwa paudindo wake wapamwamba m’boma pambuyo pa imfa ya Nebukadinezara. Koma malo apamwamba sanali kanthu kwa Danieli. Panthaŵiyi, zikuoneka kuti anali m’zaka za m’ma 90, koma wokhulupirikabe potumikira Yehova. Ngakhale kuti anali atakhala m’Babulo monga wandende kwa zaka pafupifupi 80, iye anadziŵikabe ndi dzina lake lachihebri. Ngakhale mfumukaziyo inamutcha Danieli, osati dzina lachibabulo limene anapatsidwa. Ndithudi, mfumukaziyo inalimbikitsa mfumu kuti: “Amuitane Danieli tsono, iye adzafotokozera kumasuliraku.”—Danieli 1:7; 5:10-12.
14. Kodi Danieli anakumana ndi chiyeso chotani ataona mawu olembedwa pakhoma?
14 Danieli anaitanidwa ndipo anadzaonekera pamaso pa Belisazara. Zinali zochititsa manyazi kuti mfumuyi ipemphe thandizo kwa Myuda ameneyu, amene Mulungu wake yangom’tukwana kumene. Komabe, Belisazara anayeserabe kum’nyengerera Danieli, akumam’lonjeza mfupo imodzimoziyo ya kukhala wolamulira wachitatu mu ufumuwo ngati angaŵerenge ndi kumasulira mawu achinsinsiwo. (Danieli 5:13-16) Danieli anakweza maso ake nayang’ana mawuwo pakhoma, ndipo mzimu woyera unam’zindikiritsa tanthauzo lake. Unali uthenga wa chiweruzo chochokera kwa Yehova Mulungu! Kodi Danieli akanalengeza bwanji pamasom’pamaso chiweruzo choopsacho kwa mfumu yonyada chotero komanso pamaso pa akazi ake ndi nduna zake? Tangoganizani chiyeso chimene Danieli anakumana nacho! Kodi anakopeka ndi mawu onyengerera a mfumuyo ndi lonjezo lake lom’patsa chuma ndi ulemerero? Kodi mneneriyo akafeŵetsa chilengezo cha chiweruzo cha Yehova?
15, 16. Kodi Belisazara analephera kuphunzira chiyani ku mbiri yakale, ndipo kulephera kofananako n’kofala motani lerolino?
15 Danieli analankhula molimba mtima, ndipo anati: “Mphatso zanu zikhale zanu, ndi mphotho zanu mupatse wina; koma ndidzaŵerengera mfumu lembalo, ndi kum’dziŵitsa kumasulira kwake.” (Danieli 5:17) Kenako, Danieli anavomereza ukulu wa Nebukadinezara, mfumu yamphamvu imene inakhoza kupha, kukantha, kukweza, kapena kunyazitsa aliyense amene inafuna. Komabe, Danieli anakumbutsa Belisazara kuti Yehova, “Mulungu Wam’mwambamwamba,” anakweza Nebukadinezara kukhala wamkulu. Analinso Yehova amene ananyazitsa mfumu yamphamvuyo pamene inakula mtima. Inde, Nebukadinezara anakakamizidwa kuphunzira kuti “Wam’mwambamwamba alamulira m’ufumu wa anthu, nauikira aliyense Iye afuna mwini.”—Danieli 5:18-21.
16 Koma Belisazara ‘anadziŵa izi zonse.’ Ngakhale ndi choncho, analephera kutengapo phunziro pa mbiri yakale. Ndi iko komwe, tchimo lake linali lalikulu kuposa la Nebukadinezara amene vuto lake makamaka linali kunyada. Iye anasonyeza mwano weniweni wotukwana Yehova. Danieli anavumbula poyera tchimo la mfumuyo. Komanso, pamaso pa osonkhana akunjawo, Danieli anauza Belisazara molimba mtima kuti milungu yonamayo “siiona, kapena kumva, kapena kudziŵa.” Mneneri wa Mulungu wolimba mtimayo anafotokozanso kuti mosiyana ndi milungu yopanda pakeyo, Yehova ndi Mulungu “amene m’dzanja mwake muli mpweya wanu.” Mpaka lero, anthu amapanga milungu ya zinthu zopanda moyo, amalambira ndalama, ntchito, ulemerero, ngakhale zosangalatsa. Koma zonsezo sizingapereke moyo. Yehova yekhayo ndiye akutikhalitsa moyo, amene timadalira kaamba ka mpweya uliwonse umene tipuma.—Danieli 5:22, 23; Machitidwe 17:24, 25.
KUMASULIRA MKULUWIKOWO
17, 18. Kodi mawu anayi amene analembedwa pakhoma anali otani, ndipo amatanthauzanji m’ganizo lenileni?
17 Mneneri wokalambayo anachita chinthu chimene chinawakanika amuna anzeru onse a Babulo. Anatha kuŵerenga ndi kumasulira mawu olembedwa pakhomawo. Mawuwo anali akuti: “MENE MENE TEKEL UFARSIN.” (Danieli 5:24, 25) Kodi amatanthauzanji?
18 M’ganizo lenileni, mawuwo amatanthauza kuti “mina imodzi, mina imodzi, sekeli, ndi theka la sekeli.” Liwu lililonse limatanthauza ndalama, kuyamba ndi yaikulu kumaliza ndi yaing’ono. Zosokoneza bwanji! Ngakhale ngati amuna anzeruwo a Babulo akanakhoza kuŵerenga zilembozo, n’kwachionekere kuti iwo sakanatha kudziŵa tanthauzo lake.
19. Kodi liwu lakuti “MENE” linatanthauza chiyani polimasulira?
19 Mothandizidwa ndi mzimu woyera wa Mulungu, Danieli anafotokoza kuti: “Kumasulira kwake kwa mawu awa ndi uku: MENE, Mulungu anaŵerenga ufumu wanu, nautha.” (Danieli 5:26) Makonsonanti a liwu loyambalo analola kuwaŵerenga kuti “mina,” komanso kuwaŵerenga monga liwu lachialamu lotanthauza kuti “kuŵerengera kochotsapo,” kapena kuti “kuŵerengedwa,” malinga ndi mavawelo oikidwamo ndi wowerengayo. Danieli anadziŵa bwino lomwe kuti ukaidi wa Ayuda unali pafupi kutha. Panyengo yoloseredwayo ya zaka 70, zaka 68 zinali zitapita kale. (Yeremiya 29:10) Wosunga Nthaŵi Wamkuluyo, Yehova, anali atawerenga masiku a ulamuliro wa Babulo monga ufumu wamphamvu padziko lonse. Ndipo mapeto ake anali atafika kale, zimene sanadziŵe aliyense amene anali paphwando la Belisazara. Nthaŵi inali itatha kale, osati kwa Belisazara yekha komanso kwa bambo wake, Nabonidasi. Chingakhale chifukwa chake liwu lakuti “MENE” linalembedwa kaŵiri—kulengeza mapeto a ulamuliro wa mafumu onse aŵiriwo.
20. Kodi liwu lakuti “TEKEL” linatanthauza chiyani polimasulira, ndipo linakwaniritsidwa motani pa Belisazara?
20 Koma liwu lakuti “TEKEL” linalembedwa kamodzi ndipo limanena za chinthu chimodzi. Zimenezi zingasonyeze kuti limanena makamaka za Belisazara. Ndipo zimenezo n’zoyenerera, chifukwa iye payekha ananyoza Yehova kwambiri. Liwulo limatanthauza “sekeli,” koma makonsonanti akenso amalola kuwaŵerenga kuti “kuyesedwa pamuyeso.” N’chifukwa chake Danieli anati kwa Belisazara: “TEKEL, Mwayesedwa pamiyeso, nimupezeka mwapereŵera.” (Danieli 5:27) Kwa Yehova, mitundu yathunthu ya anthu ili yosanunkha kanthu pamiyeso yake mofanana ndi fumbi. (Yesaya 40:15) Iwo sali kanthu kuti angalepheretse zolinga zake. Nangano mfumu imodzi yamwano ingachite chiyani? Belisazara anali atayesa kudzikweza pamwamba pa Mfumu ya chilengedwe chonse. Munthu wamba ameneyu anali atayesa kutukwana Yehova ndi kunyoza kulambira koyera koma inapezeka kuti ‘yapereŵera.’ Inde, Belisazara anayenereradi chiweruzo chimene chinali kufika mofulumira!
21. Kodi liwu lakuti “UFARSIN” linatanthauza zinthu zitatu zotani, ndipo liwuli linasonyezanji za tsogolo la Babulo monga ulamuliro wamphamvu padziko lonse?
21 Liwu lomaliza pakhomapo linali “UFARSIN.” Danieli analiŵerenga monga liwu lonena chinthu chimodzi, “PERES,” mwinamwake chifukwa anali kulankhula kwa mfumu imodzi pamene inayo panalibe. Liwu limeneli linali chimake cha mkuluwiko waukuluwo wa Yehova ndipo limatanthauza zinthu zitatu. M’ganizo lenileni, “ufarsin” limatanthauza “theka la sekeli.” Koma zilembozi zimalolanso matanthauzo ena aŵiri—“kugawa” ndi “Aperisi.” Choncho Danieli ananenera kuti: “PERES, ufumu wanu wagaŵika, nuperekedwa kwa Amedi ndi Aperisi.”—Danieli 5:28.
22. Kodi Belisazara anatani atamva kumasulira kwa mkuluwikowo, ndipo zikuoneka kuti anali ndi chiyembekezo chotani?
22 Choncho mkuluwikowo unamasuliridwa. Babulo wamkuluyo anali pafupi kugwetsedwa ndi gulu la nkhondo la Mediya ndi Perisiya. Ngakhale kuti nkhope yake inali itagwa ndi chisoni chachikulu pakumva chiweruzocho, Belisazara anakwaniritsabe lonjezo lake. Anauza anyamata ake kuti aveke Danieli chibakuwa, ndi unyolo wagolidi m’khosi mwake, nam’lengeza monga wolamulira wachitatu mu ufumuwo. (Danieli 5:29) Danieli sanakane ulemu umenewo, pozindikira kuti unalemekeza Yehova. Inde, mwina Belisazara anaganiza kuti ngati alemekeza mneneri wa Yehova, n’kutheka kuti Yehova akafeŵetsa chiweruzo chake. Ngati anaganiza choncho, munali m’mbuyo mwa alendo.
KUGWA KWA BABULO
23. Kodi ndi ulosi wakale wotani umene unali kukwaniritsidwa pamene madyerero a Belisazara anali m’kati?
23 Ngakhale kuti Belisazara ndi nduna zakezo anali kumwa polemekeza milungu yawo ndi kunyodola Yehova, zimene zinali kuchitika mumdima kunja kwa nyumba ya mfumuyo zinali zoopsa. Ulosi umene unaperekedwa kupyolera mwa Yesaya zaka pafupifupi mazana aŵiri kalelo unali kukwaniritsidwa. Ponena za Babulo, Yehova ananeneratu kuti: “Kuusa moyo kwake konse ndakutonthoza.” Inde, nkhanza zonse za mzinda woipawo pa anthu osankhika a Mulungu zinali pafupi kutha. Mwa njira yotani? Ulosi umodzimodziwo unati: “Kwera Elamu iwe; zunguniza Media iwe.” Elamu anakhala mbali ya Perisiya pambuyo pa masiku a mneneri Yesaya. Pofika nthaŵi ya madyerero a Belisazara, zimene zinaloseredwanso mu ulosi womwewomwewo wa Yesaya, Perisiya ndi Mediya anagwirizana kuti ‘akwere’ ndi ‘kuzunguniza’ Babulo.—Yesaya 21:1, 2, 5, 6.
24. Kodi ndi mbali ziti zonena za kugwa kwa Babulo zimene ulosi wa Yesaya unali utaneneratu?
24 Ndipo ngakhale dzina lenileni la mtsogoleri wa gulu la asilikali amenewo linanenedweratu, chimodzimodzinso njira imene akamenyera nkhondo yake. Zaka pafupifupi 200 m’mbuyomo, Yesaya anali ataneneratu kuti Yehova akadzoza munthu wina, dzina lake Koresi, kuti akathire nkhondo Babulo. Pomenya nkhondo yakeyo, akam’chotsera zopinga zonse panjira yake. Madzi a Babulo ‘akauma,’ ndipo zitseko zake zamphamvuzo zikasiyidwa chitsegukire. (Yesaya 44:27–45:3) Ndipo zinaterodi. Asilikali a Koresi anapatutsa mtsinje wa Firate, kotero kuti madziwo anatsika pansi moti iwo anatha kuyenda khuvukhuvu pamadzipo. Alonda osasamala anasiya zitseko za linga la Babulo zili chitsegukire. Malinga n’kunena kwa olemba mbiri yakale, adani analoŵa mumzindawo pamene anthu ake anali pachisangalalo. Babulo analandidwa ngati maseŵera. (Yeremiya 51:30) Komabe, imfa yodziŵika inali ya munthu mmodzi basi. Danieli anasimba kuti: “Usiku womwewo Belisazara mfumu ya Akasidi anaphedwa. Ndipo Dariyo Mmedi analandira ufumuwo ali wa zaka makumi asanu ndi limodzi mphambu ziŵiri.”—Danieli 5:30, 31.
KUTENGERA PHUNZIRO PA MAWU OLEMBEDWA PAKHOMA
25. (a) N’chifukwa chiyani Babulo wakale ali chizindikiro choyenerera cha dongosolo la padziko lonse la zipembedzo zonyenga? (b) Kodi atumiki a Mulungu amakono anali andende m’Babulo m’lingaliro lotani?
25 Nkhani youziridwa ya m’Danieli chaputala 5 ndi yofunika kwambiri kwa ife. Monga chimake cha mapembedzedwe onyenga, Babulo wakaleyo ali chizindikiro choyenerera cha ufumu wa dziko lonse wa chipembedzo chonyenga. Dongosolo lonse la zipembedzo zonyenga limeneli, losonyezedwa m’buku la Chivumbulutso monga mkazi wachigololo wodzala magazi m’manja mwake, limatchedwa ‘Babulo Wamkulu.’ (Chivumbulutso 17:5) Posamvera machenjezo onena za ziphunzitso zake zonyenga ndi machitachita onyoza Mulungu, mkazi ameneyu wakhala akuzunza alaliki a choonadi cha Mawu a Mulungu. Mofanana ndi anthu a Yerusalemu ndi Yuda wakale, otsalira okhulupirika a Akristu odzozedwa anali ngati andende mu “Babulo Wamkulu,” pamene chizunzo cholimbikitsidwa ndi atsogoleri achipembedzo chinaimitsa ntchito yolalikira Ufumu mu 1918.
26. (a) Kodi “Babulo Wamkulu” anagwa motani mu 1919? (b) Ndi chenjezo lotani limene ife enife tiyenera kulabadira ndi kuchenjezanso ena?
26 Koma mwadzidzidzi, “Babulo Wamkulu” anagwa! Ndipo kugwa kwake kunali kwakachetechete monga mmene Babulo wakale anagwera popanda phokoso kwenikweni mu 539 B.C.E. Komabe kugwa kophiphiritsa kumeneku kunali kosakaza. Kunachitika mu 1919 C.E. pamene anthu a Yehova anamasulidwa ku ukaidi wachibabulo ndipo anadalitsidwa ndi chiyanjo cha Mulungu. Zimenezi zinathetsa ulamuliro wa “Babulo Wamkulu” pa anthu a Mulungu ndipo chinali chiyambi cha kum’vumbula poyera monga wonyenga wosadalirika. Kugwa kumeneko kwakhala kosatheka kunyamukanso, ndipo chiwonongeko chom’maliziratu chili pafupi. Chifukwa chake atumiki a Yehova akhala akulengeza chenjezo lakuti: “Tulukani mmenemo, anthu anga; kuti mungayanjane ndi machimo ake.” (Chivumbulutso 18:4) Kodi mwalabadira chenjezo limenelo? Kodi mumachenjezanso ena?f
27, 28. (a) Ndi mfundo yofunika yotani imene Danieli sanaiŵale? (b) Pali umboni wotani wosonyeza kuti posachedwapa Yehova adzawononga dziko loipa lilipoli?
27 Choncho mawu olembedwa pakhoma akuonekera leronso koma osati kaamba ka “Babulo Wamkulu” yekha ayi. Kumbukirani mfundo yaikulu ya buku la Danieli: Yehova ndi Mfumu Yachilengedwe Chonse. Iye, ndipo iye yekhayo, ndiye ali ndi ufulu wokhazikitsa mfumu yolamulira mtundu wonse wa anthu. (Danieli 4:17, 25; 5:21) Chilichonse chopinga zolinga za Yehova chidzachotsedwa. Yehova adzachitapo kanthu posachedwa pom’pa, nthaŵi ikadzakwana. (Habakuku 2:3) Kwa Danieli, nthaŵiyo potsirizira pake inadzafika m’zaka za ma 90 za moyo wake. Iye anadzionera yekha mmene Yehova anachotsera ulamuliro wamphamvu padziko lonse umene unapondereza anthu a Mulungu chiyambire Danieli ali mnyamata wochepa.
28 Pali umboni wosakanika wakuti Yehova Mulungu wakhazika pampando wachifumu wakumwamba Mfumu yolamulira anthu onse. Kunyalanyaza kwa dziko Mfumu imeneyo ndi kutsutsa ulamuliro wake, kuli umboni wotsimikizika wakuti posachedwapa, Yehova adzawononga onse otsutsa ulamuliro wa Ufumuwo. (Salmo 2:1-11; 2 Petro 3:3-7) Kodi mukuchita changu malinga ndi kufulumira kwa nthaŵi zimene tikukhala, ndi kuika chidaliro chanu pa Ufumu wa Mulungu? Ngati mukutero, ndiye kuti mwatengapodi phunziro pa mawu olembedwa pakhoma!
[Mawu a M’munsi]
a M’zolemba zina zamakedzana, Mfumu Koresi inati za Belisazara: “Aika kanjipiti kuti kakhale [kolamulira] dziko lake.”
b Ngakhale mfundo yaing’ono imeneyi ya Danieli yapezeka kukhala yolondola. Akatswiri a mbiri ya zinthu zakale zokumbidwa pansi apeza kuti makoma a nyumba ya mfumu ya ku Babulo wakale anamangidwa ndi njerwa zomata pulasitala.
c Zikuoneka kuti zikhulupiriro za Ababulo zinawonjezera kuopsa kwa chozizwitsacho. Buku lakuti Babylonian Life and History limati: “Kuwonjezera pa milungu yambiri imene Ababulo anailambira, tikuona kuti anakhulupiriranso kwambiri mizimu, mwakuti mapemphero awo oitsutsa ndi matemberero zimapanga gawo lalikulu kwambiri la mabuku awo achipembedzo.”
d Magazini yotchedwa Biblical Archaeology Review inati: “Akatswiri a Babulo anaika m’magulu osiyanasiyana zikwizikwi za zizindikiro za malaulo. . . . Pamene Belisazara analamula kuti auzidwe tanthauzo la mawu olembedwa pakhomawo, amuna anzeru a Babulo, mosakayikira, anakafufuza m’mabuku ameneŵa a malaulo. Koma anapezeka kukhala opanda pake.”
e Olemba madikishonale anena kuti liwu limene linatembenuzidwa kuti “anathedwa nzeru” limatanthauza chipwirikiti chadzaoneni, monga kuti paphwandopo panabuka chisokonezo chachikulu.
f Onani masamba 205-71 m’buku lakuti Revelation—Its Grand Climax At Hand!, lofalitsidwa ndi Watchtower Bible and Tract Society of New York, Inc.
KODI MWAZINDIKIRA CHIYANI?
• Kodi madyerero a Belisazara anasokonezedwa motani usiku wa pa October 5/6, 539 B.C.E.?
• Kodi kumasulira mawu olembedwa pakhoma kunali kotani?
• Ndi ulosi wotani wonena za kugwa kwa Babulo umene unali kukwaniritsidwa pamene madyerero a Belisazara anali m’kati?
• Kodi nkhani ya mawu olembedwa pakhoma ndi yofunika motani lerolino?
[Chithunzi Chachikulu patsamba 98]
[Chithunzi Chachikulu patsamba 103]