Danieli
5 Pa nthawi imene Belisazara+ anali mfumu anakonzera nduna zake 1,000 phwando lalikulu ndipo iyeyo ankamwa vinyo atakhala patsogolo pawo.+ 2 Belisazara ataledzera ndi vinyoyo analamula kuti abweretse ziwiya zagolide ndi zasiliva zimene Nebukadinezara bambo ake anatenga mʼkachisi ku Yerusalemu.+ Anachita zimenezi kuti mfumuyo, nduna zake, adzakazi* ake ndi akazi ake ena amweremo. 3 Ndiyeno anabweretsa ziwiya zagolide zimene anazitenga mʼkachisi, mʼnyumba ya Mulungu ku Yerusalemu. Kenako mfumuyo, nduna zake, adzakazi ake ndi akazi ake ena anayamba kumwera mʼziwiyazo. 4 Iwo anamwa vinyo nʼkuyamba kutamanda milungu yagolide, yasiliva, yakopa,* yachitsulo, yamitengo ndi yamiyala.
5 Nthawi yomweyo, dzanja la munthu linaonekera ndipo linayamba kulemba pakhoma lapulasitala la nyumba ya mfumu, pafupi ndi choikapo nyale ndipo mfumuyo inaona dzanja limene linkalembalo. 6 Ndiyeno nkhope ya mfumuyo inasintha ndipo iye anachita mantha kwambiri. Miyendo komanso mawondo+ ake anayamba kunjenjemera.
7 Ndiye mfumuyo inaitana mofuula olankhula ndi mizimu, Akasidi* ndi okhulupirira nyenyezi.+ Mfumuyo inauza amuna anzeru a mʼBabulo amenewa kuti: “Aliyense amene angawerenge mawuwa nʼkundiuza kumasulira kwake, ndimuveka zovala zapepo ndi mkanda wagolide mʼkhosi+ ndipo akhala wolamulira wachitatu mu ufumuwu.”+
8 Amuna onse anzeru anabwera kwa mfumu koma sanathe kuwerenga mawu amene analembedwawo kapena kuuza mfumu kumasulira kwake.+ 9 Choncho Mfumu Belisazara inachita mantha kwambiri ndipo nkhope yake inasintha. Nduna zakenso zinathedwa nzeru.+
10 Mfumukazi itamva mawu a mfumu ndi a nduna zake, inalowa mʼchipinda chimene ankachitira phwandolo. Mfumukaziyo inati: “Inu mfumu, mukhale ndi moyo mpaka kalekale. Musachite mantha komanso nkhope yanu isasinthe. 11 Mu ufumu wanu muli munthu amene ali ndi mzimu wa milungu yoyera. Mʼmasiku a bambo anu, anthu anazindikira kuti munthuyu ndi wodziwa zinthu kwambiri, wozindikira ndiponso ali ndi nzeru zofanana ndi nzeru za milungu.+ Ndiyeno bambo anu, Mfumu Nebukadinezara, anamuika kuti akhale mkulu wa ansembe ochita zamatsenga, anthu okhulupirira mizimu, Akasidi* ndi anthu okhulupirira nyenyezi.+ Ndithudi mfumu, bambo anu anamupatsa udindo umenewu. 12 Anachita zimenezi chifukwa Danieli, amene mfumu inamupatsa dzina lakuti Belitesazara,+ anali ndi luso lodabwitsa, anali wodziwa zinthu ndi wozindikira pa nkhani yomasulira maloto, kumasulira mikuluwiko komanso kuthana ndi zinthu zovuta.*+ Tsopano itanani Danieli ndipo akuuzani kumasulira kwa mawu amenewa.”
13 Choncho anabweretsa Danieli kwa mfumu ndipo mfumuyo inamufunsa kuti: “Kodi iwe ndiwe Danieli, mmodzi wa anthu amene anatengedwa ukapolo ku Yuda ndi bambo anga mfumu?+ 14 Ndamva kuti mwa iwe muli mzimu wa milungu+ ndiponso kuti uli ndi luso lodabwitsa, ndiwe wozindikira komanso kuti uli ndi nzeru zodabwitsa.+ 15 Ineyo anandibweretsera amuna anzeru ndi anthu okhulupirira mizimu kuti awerenge mawu amene alembedwawa nʼkundiuza kumasulira kwake, koma iwo alephera kumasulira uthenga wake.+ 16 Koma ndamva kuti iweyo umatha kumasulira zinthu+ komanso kuthana ndi zinthu zovuta.* Ndiye ngati ungathe kuwerenga mawuwa nʼkundiuza kumasulira kwake, ndikuveka zovala zapepo ndi mkanda wagolide mʼkhosi mwako ndipo ukhala wolamulira wachitatu mu ufumuwu.”+
17 Ndiyeno Danieli anayankha mfumuyo kuti: “Mphatso zanuzo mukhoza kusunga ndipo mphoto zanuzo mupatse ena. Komabe, inu mfumu, ndikuwerengerani mawu amene alembedwawa ndipo ndikuuzani kumasulira kwake. 18 Inu mfumu, Mulungu Wamʼmwambamwamba anapatsa bambo anu Nebukadinezara ufumu, ukulu, ulemu ndi ulemerero.+ 19 Chifukwa chakuti Mulungu anamupatsa ukulu umenewu, anthu a mitundu yonse komanso anthu olankhula zinenero zosiyanasiyana ankanjenjemera chifukwa cha mantha pamaso pake.+ Aliyense amene ankafuna kumupha ankamupha, amene ankafuna kumusiya ndi moyo ankamusiya ndipo aliyense amene ankafuna kumukweza ankamukweza, amene ankafuna kumutsitsa ankamutsitsa.+ 20 Koma pamene mtima wake unayamba kudzikuza ndiponso pamene anaumitsa mtima wake nʼkuchita zinthu modzikweza,+ anatsitsidwa pampando wake wachifumu ndipo ulemerero wake unachotsedwa. 21 Iye anathamangitsidwa pakati pa anthu ndipo mtima wake unasinthidwa nʼkukhala ngati wa nyama moti anayamba kukhala limodzi ndi abulu akutchire. Iye ankadya udzu ngati ngʼombe ndipo thupi lake linkanyowa ndi mame akumwamba, mpaka pamene anadziwa kuti Mulungu Wamʼmwambamwamba ndi Wolamulira wa maufumu a anthu ndiponso kuti amapereka ulamuliro kwa munthu aliyense amene akufuna kumupatsa.+
22 Koma inuyo a Belisazara, amene ndinu mwana wake, simunadzichepetse mumtima mwanu ngakhale kuti mukudziwa zonsezi. 23 Mʼmalomwake mwadzikweza pamaso pa Ambuye wakumwamba+ ndipo munalamula anthu kuti akubweretsereni ziwiya zamʼnyumba yake.+ Ndiyeno inuyo, nduna zanu, adzakazi anu ndi akazi anu ena mwamwera vinyo mʼziwiya zimenezi ndipo mwatamanda milungu yasiliva, yagolide, yakopa, yachitsulo, yamitengo ndi yamiyala imene siona, kumva kapena kudziwa chilichonse.+ Koma Mulungu amene amakupatsani mpweya komanso amene ali ndi mphamvu zolamulira moyo wanu, simunamulemekeze.+ 24 Choncho Mulungu watumiza dzanja limene lalemba mawu amenewa.+ 25 Mawu amene alembedwa ndi awa: MENE, MENE, TEKELI ndi PARASINI.
26 Kumasulira kwa mawuwa ndi uku: MENE, Mulungu wawerenga masiku a ufumu wanu ndipo wauthetsa.+
27 TEKELI, mwayezedwa pasikelo ndipo mwapezeka kuti mukuperewera.
28 PERESI, ufumu wanu wagawidwa ndipo waperekedwa kwa Amedi ndi Aperisiya.”+
29 Ndiyeno Belisazara analamula kuti Danieli avekedwe zovala zapepo ndi mkanda wagolide mʼkhosi mwake. Ndipo analengeza kuti Danieli akhala wolamulira wachitatu mu ufumuwo.+
30 Usiku womwewo, Belisazara mfumu ya Akasidi anaphedwa.+ 31 Dariyo+ Mmedi anapatsidwa ufumuwo ndipo anali ndi zaka pafupifupi 62.