Mutu 12
Alimbikitsidwa ndi Mthenga Wochokera kwa Mulungu
1. Kodi Danieli anadalitsidwa motani pokhala ndi chidwi chachikulu pa kukwaniritsidwa kwa chifuniro cha Yehova?
CHIDWI chachikulu cha Danieli pa kukwaniritsidwa kwa chifuniro cha Yehova chinam’dalitsa kwambiri. Iye anapatsidwa ulosi wosangalatsa kwambiri wa masabata 70 okhudzana ndi kuonekera kwa Mesiya. Danieli anadalitsikanso mwa kuona otsalira okhulupirika a anthu ake akubwerera kudziko lakwawo. Zimenezo zinachitika mu 537 B.C.E, chakumapeto kwa “chaka choyamba . . . cha Koresi mfumu ya ku Perisiya.”—Ezara 1:1-4.
2, 3. Kodi n’chiyani chingakhale chifukwa chimene Danieli sanabwererere kudziko la Yuda limodzi ndi Ayuda otsalawo?
2 Danieli sanapite nawo paulendo wobwerera kudziko la Yuda. Zikuoneka kuti kuyenda kukanam’vuta chifukwa cha ukalamba. Komabe, Mulungu anali ndi utumiki winanso umene anafuna kuti Danieli achite ku Babuloko. Zaka ziŵiri zapita. Kenako nkhaniyo ikutiuza kuti: “Chaka chachitatu cha Koresi mfumu ya Perisiya, chinavumbulutsidwa chinthu kwa Danieli, amene anamutcha Belitsazara; ndipo chinthucho n’choona, ndicho nkhondo yaikulu ndipo anazindikira chinthucho, nadziŵa masomphenyawo.”—Danieli 10:1.
3 “Chaka chachitatu cha Koresi,” chinayenera kukhala 536 kapena 535 B.C.E. Panapita zaka zoposa 80 kuchokera pamene Danieli anatengeredwa ku Babulo limodzi ndi achinyamata a mbewu ya mafumu ndi ya akalonga a Yuda. (Danieli 1:3) Ngati pofika ku Babulo anali m’zaka za m’ma 14 kapena 15, ndiye kuti tsopano anali ndi zaka pafupifupi 100. Ha, inali mbiri ya utumiki wokhulupirika bwanji!
4. Ngakhale kuti Danieli anali atakalamba, ndi mbali yofunika yotani imene anafunikirabe kuichita mu utumiki wake kwa Yehova?
4 Komabe, ngakhale kuti Danieli anali atakalamba, mbali yake inali isanathe mu utumiki wake kwa Yehova. Kudzera mwa iye, Mulungu anafunanso kupereka uthenga waulosi umene tanthauzo lake linali lofika patali kwambiri. Unali ulosi wodzafika mpaka m’nthaŵi yathu ino ndi kupitirira. Pofuna kum’konzekeretsa Danieli ntchito yowonjezereka imeneyi, Yehova anaona kuti kunali kofunika kuti am’thandize, mwa kum’patsa nyonga kaamba ka utumiki umene unali patsogolo.
CHIFUKWA CHODERA NKHAŴA
5. Kodi ndi malipoti otani omwe akuoneka kuti ndiwo anachititsa nkhaŵa Danieli?
5 Ngakhale kuti Danieli sanabwerere kudziko la Yuda limodzi ndi Ayuda otsalawo, anali ndi chidwi chachikulu pa zimene zinali kuchitika kudziko lakwawolo. Kuchokera m’malipoti amene anam’peza, Danieli anadziŵa kuti zinthu sizinali bwino kwenikweni kumeneko. Zoona, guwa lawo la nsembe linali litakhazikitsidwanso ndipo maziko a kachisi anali atamangidwa ku Yerusalemu. (Ezara, chaputala 3) Koma mitundu yoyandikana nayo imafuna kuletsa ntchito yomangayo, choncho imachitira mtopola Ayuda obwererawo. (Ezara 4:1-5) Ndithudi, Danieli anayenera kuda nkhaŵa chifukwa cha zinthu zambiri.
6. N’chifukwa chiyani mikhalidwe ya ku Yerusalemu inali yom’sautsa mtima Danieli?
6 Danieli anali kudziŵa za ulosi wa Yeremiya. (Danieli 9:2) Iye anadziŵa kuti kumangidwanso kwa kachisi ku Yerusalemu ndi kubwezeretsedwa kwa kulambira koona zinali zokhudzana kwambiri ndi chifuniro cha Yehova ponena za anthu Ake, ndi kutinso zonsezo zikachitika asanaonekere Mesiya wolonjezedwayo. Kwenikweni, Danieli anapatsidwa mwayi wapadera kwambiri wolandira kwa Yehova ulosi wa “masabata makumi asanu ndi aŵiri.” Mwa ulosiwo anadziŵa kuti Mesiyayo akadza patapita “masabata” 69 kuchokera pa kuperekedwa kwa lamulo la kukonzanso ndi kumanganso Yerusalemu. (Danieli 9:24-27) Komabe, chifukwa cha kupasuka kwa Yerusalemu komanso kuchedwa komanga kachisiyo, m’posavuta kuona chifukwa chake Danieli anaguluka m’mawondo, kukhumudwa, ndi kugwa mphwayi.
7. Kodi Danieli anachitanji kwa masabata atatu?
7 “Masiku aja ine Danieli ndinali kulira masabata atatu amphumphu,” ikutero nkhaniyo. “Chakudya chofunika osachidya ine, nyama kapena vinyo zosapita pakamwa panga, osadzola ine konse, mpaka anakwaniridwa masabata atatu amphumphu.” (Danieli 10:2, 3) “Masabata atatu amphumphu,” kapena masiku 21, a kulira ndi kusala kudya inali nthaŵi yaitali kwambiri. Mwachionekere inatha pa “tsiku lamakumi aŵiri mphambu anayi la mwezi woyamba.” (Danieli 10:4) Choncho, nyengo imene Danieli anasala kudya inaphatikizapo Paskha, wochitika tsiku la 14 la mwezi woyamba wa Nisani, ndi chikondwerero chotsatira cha masiku asanu ndi aŵiri cha mkate wopanda chotupitsa.
8. Ndi pachochitika chanji m’mbuyomo pamene Danieli anachonderera chilangizo cha Yehova, ndipo chotsatirapo chinali chiyani?
8 Danieli anakhalanso ndi chochitika chofanana m’mbuyomo. Panthaŵiyo, anazunguzika maganizo posadziŵa za kukwaniritsidwa kwa ulosi wa Yehova wonena za zaka 70 za chipululutso cha Yerusalemu. Kodi Danieli anatani pamenepo? “Ndinaika nkhope yanga kwa Ambuye Mulungu,” anatero Danieli, “kum’funsa Iye m’pemphero, ndi mapembedzero ndi kusala, ndi ziguduli, ndi mapulusa.” Yehova anayankha pemphero la Danieli mwa kutumiza mngelo Gabrieli ndi uthenga umene unam’limbikitsa kwambiri. (Danieli 9:3, 21, 22) Kodi Yehova apanso adzachita m’njira yofanana, kum’patsa Danieli chilimbikitso chimene akufunikira kwambiricho?
MASOMPHENYA OCHITITSA MANTHA
9, 10. (a) Kodi masomphenyawo anam’peza ali kuti Danieli? (b) Fotokozani zimene Danieli anaona m’masomphenyawo.
9 Danieli sanataye mtima. Akupitiriza kutiuza chimeneno chinachitika, akumati: “Pokhala ine m’mphepete mwa mtsinje waukulu, ndiwo Hidikeli, ndinakweza maso anga, ndinapenya ndi kuona munthu wovala bafuta, womanga m’chuuno ndi golidi woona wa ku Ufazi. (Danieli 10:4, 5) Hidikeli unali mtsinje umodzi mwa inayi imene inali kuchokera m’munda wa Edene. (Genesis 2:10-14) M’Perisiya wakale, mtsinje wa Hidikeli unali kutchedwa Tigra, kumene kunachokera dzina lachigiriki lakuti Tigirisi. Chigawo chapakati pa mtsinje umenewu ndi mtsinje wa Firate chinatchedwa Mesopotamiya, kutanthauza “Dziko Lapakati pa Mitsinje.” Zimenezi zikutsimikizira kuti pamene Danieli analandira masomphenya ameneŵa, anali adakali m’dziko la Babuloniya, koma mwina osati mumzinda wotchedwa Babulo.
10 Ha, Danieli analandira masomphenya ochititsa chidwi bwanji! Mwachionekere, amene iye anamuona pokweza maso ake sanali munthu wamba. Danieli anafotokoza chithunzi chooneka bwino ichi: “Thupi lake lomwe linanga berulo, ndi nkhope yake ngati maonekedwe a mphezi, ndi maso ake ngati nyali zamoto, ndi manja ake ndi mapazi ake akunga mkuwa wonyezimira, ndi kumveka kwa mawu ake kunanga phokoso la aunyinji.”—Danieli 10:6.
11. Kodi masomphenyawo anam’khudza motani Danieli komanso amuna amene anali nawo limodzi?
11 Ngakhale kuti masomphenyawo anali kuwala kwambiri, “anthu anali nane sanaona masomphenyawo,” anatero Danieli. Pachifukwa chosatchulidwa, ‘kunawagwera kunjenjemera kwakukulu, nathaŵa kukabisala.’ N’chifukwa chake Danieli anatsala yekha m’mphepete mwa mtsinje. Maonekedwe a “masomphenya aakuluŵa” anali ochititsa mantha kwambiri moti iye anavomereza kuti: ‘Ndinatsala wosakhala ndi mphamvu ine; pakuti kukoma kwanga kunasandulika chivundi mwa ine, wosakhalanso ndi mphamvu ine.’—Danieli 10:7, 8.
12, 13. Ponena za mthengayo kodi (a) chovala chake chikusonyeza chiyani? (b) Nanga maonekedwe ake?
12 Tiyeni tim’pende mosamalitsa mthenga wochititsa chidwi ameneyu amene anaopsa Danieli chomwecho. Iye anali “wovala bafuta, womanga m’chuuno ndi golidi woona wa ku Ufazi.” Mu Israyeli wakale, chovala cha mkulu wa ansembe, efodi, ndi chapachifuŵa, komanso mikanjo ya ansembe ena, zimasokedwa ndi nsalu ya bafuta yoombedwa bwino ndipo zimakongoletsedwa ndi golidi. (Eksodo 28:4-8; 39:27-29) Choncho, chovala cha mthengayo chimasonyeza chiyero ndi ulemu wa malo ake antchito.
13 Danieli anachitanso mantha ndi maonekedwe a mthengayo. Kunyezimira kwa thupi lake longa mwala wa mtengo wapatali, kuwala kothobwa m’maso kwa nkhope yake, mphamvu yopyoza ya maso ake onga moto, ndi kunyezimira kwa mikono yake yamphamvuyo ndi mapazi ake. Ngakhale mawu ake amphamvuwo anali ochititsa mantha. Zonsezi zikusonyeza bwino lomwe kuti anali munthu waungelo. “Munthu wovala bafuta” ameneyu anali mngelo waudindo wapamwamba, amene anatumikira pamalo oyera pamaso pa Yehova, kumene anachokera ndi uthenga umene anafika nawo.a
‘MUNTHU WOKONDEDWA’ KWAMBIRI ALIMBIKITSIDWA
14. Kodi Danieli anafunikira chithandizo chotani kuti alandire uthenga wochokera kwa mngelo?
14 Uthenga umene mngelo wa Yehova anadza nawo kwa Danieli unali wolemera ndi wovuta. Danieli asanaulandire uthengawo, anafunikira achire kaye kupsinjika kwake m’thupi ndi m’maganizo. Mngeloyo podziŵa chimenecho, anapereka chithandizo ndi chilimbikitso chachikondi kwa Danieli. Tiyeni tim’tsatire Danieli mwiniyo pamene akufotokoza zimene zinachitika.
15. Kodi mngelo anachitanji pothandiza Danieli?
15 “Pamene ndinamva kunena kwa mawu ake ndinagwidwa ndi tulo tatikulu pankhope panga, nkhope yanga pansi.” Mwachionekere, mantha aakulu anam’gwira Danieli moti anachita ngati wakomoka. Kodi mngeloyo anachitanji pom’thandiza? “Taonani,” anatero Danieli, “linandikhudza dzanja ndi kundikhalitsa ndi maondo anga, ndi zikhato za manja anga.” Ndiponso, mngeloyo analimbikitsa mneneriyo ndi mawu aŵa: “Danieli, munthu wokondedwatu iwe, tazindikira mawu ndilikunena ndi iwe, nukhale chilili; pakuti ndatumidwa kwa iwe tsopano.” Dzanja lothandiza ndi mawu otonthoza anam’limbikitsa Danieli. Ngakhale kuti anali “kunjenjemera,” Danieli ‘anaimirira.’—Danieli 10:9-11.
16. (a) N’chifukwa chiyani tinganene kuti Yehova sazengereza kuyankha mapemphero a atumiki ake? (b) N’chifukwa chiyani mngeloyo anachedwa kufika kwa Danieli kuti akam’thandize? (Phatikizanipo bokosi.) (c) Kodi mngeloyo amakamuuza uthenga wotani Danieli?
16 Mngeloyo anatchula kuti ulendo wake unali wodzalimbikitsa Danieli. “Usaope Danieli,” anatero mngeloyo, “pakuti kuyambira tsiku loyamba lija unaika mtima wako kuzindikira ndi kudzichepetsa pamaso pa Mulungu wako, mawu ako anamveka; ndipo ndadzera mawu ako.” Ndiyeno mngeloyo anafotokoza chifukwa chake anachedwa. Iye anati: “Koma kalonga wa ufumu wa Perisiya ananditsekerezera njira masiku makumi aŵiri ndi limodzi; ndipo taonani, Mikaeli, wina wa akalonga omveka, anadza kundithandiza; ndipo ndinakhala komweko ndi mafumu a Perisiya.” Ndi chithandizo cha Mikaeli, mngeloyo anatha kukwaniritsa ntchito yake, yokauza Danieli uthenga wofulumira kwambiri wakuti: “Ndadzera tsono kukuzindikiritsa chodzagwera anthu amtundu wako masiku otsiriza; pakuti masomphenyawo ndiwo a masiku a m’tsogolo.”—Danieli 10:12-14.
17, 18. Kodi Danieli anathandizidwa motani kachiŵiri, ndipo zimenezo zinam’theketsa kuchitanji?
17 M’malo mwakuti Danieli atengeke maganizo kuti adzalandira uthenga wochititsa chidwi, kukuoneka kuti zinthu zimene anamva zinam’patsa mantha. Nkhaniyo imati: “Ndipo atanena ndi ine monga mwa mawu aŵa, ndinaŵeramitsa nkhope yanga pansi ndi kukhala du.” Koma mngeloyo monga mthenga anali wokonzeka kupereka chithandizo chachikondi kachiŵiri. Danieli anati: “Taonani, wina wakunga ana a anthu anakhudza milomo yanga; pamenepo ndinatsegula pakamwa panga ndi kunena.”b—Danieli 10:15, 16a.
18 Danieli analimbikitsidwa pamene mngeloyo anakhudza milomo yake. (Yerekezani ndi Yesaya 6:7.) Pokhala atayambanso kulankhula, Danieli anatha kufotokozera mthenga waungeloyo zovuta zimene anali kulimbana nazo. Danieli anati: “Mbuye wanga, chifukwa cha masomphenyawo zoŵaŵa zanga zandibwerera, ndipo ndilibenso mphamvu. Pakuti mnyamata wa mbuye wanga inu akhoza bwanji kulankhula ndi mbuye wanga inu? Pakuti ine tsopano apa mulibenso mphamvu mwa ine, osanditsaliranso mpweya.”—Danieli 10:16b, 17.
19. Kodi Danieli anathandizidwa motani kachitatu, ndi chotsatirapo chotani?
19 Danieli sanali kudandaula kapena kupereka chodzikhululukira ayi. Anali kungofotokoza chothetsa nzeru chake, ndipo mngeloyo anamva chidandaulo chake. Choncho, kachitatu, Danieli anathandizidwa ndi mthenga waungelo. “Anandikhudzanso wina, maonekedwe ake ngati munthu, nandilimbikitsa ine,” anatero mneneriyo. Atam’limbikitsa mwa kum’khudza, mthengayo ananena mawu otonthoza aŵa: “Munthu wokondedwatu iwe, usaope, mtendere ukhale nawe; limbika, etu limbika.” Zikuoneka kuti kum’khudza kwachikondiko ndi mawu olimbikitsawo n’zimene Danieli anangofunikira. Zotsatira zake? Danieli anati: “Pamene ananena ndi ine ndinalimbikitsidwa, ndinati, Anene mbuye wanga; pakuti mwandilimbikitsa.” Tsopano Danieli anali wokonzeka kuchita ntchito inanso yovuta.—Danieli 10:18, 19.
20. N’chifukwa chiyani mthenga waungeloyo anafunikira kulimbikira kuti achite ntchito yake?
20 Pokhala atalimbikitsa Danieli ndi kum’thandiza kuchira zofooka zake za m’thupi ndi maganizo, mngeloyo anabwerezanso kutchula cholinga cha ulendo wakewo. Iye anati: “Kodi udziŵa chifukwa choti ndakudzera? Ndipo tsopano ndibwerera kulimbana ndi kalonga wa Perisiya; ndipo pomuka ine, taonani, adzadza kalonga wa Helene. Koma ndidzakufotokozera cholembedwa pa lemba la choonadi; ndipo palibe wina wakudzilimbikitsa pamodzi ndi ine, kutsutsana ndi aja, koma Mikaeli kalonga wanu.”—Danieli 10:20, 21.
21, 22. (a) Malinga ndi chokumana nacho cha Danieli, kodi tingaphunzirenji ponena za njira ya Yehova yochitira ndi atumiki ake? (b) Kodi Danieli tsopano analimbikitsidwa kuti achitenji?
21 Yehova alidi wachikondi ndi woganizira ena! Nthaŵi zonse amachita ndi atumiki ake molingana ndi maluso awo ndi zopereŵeza zawo. Kumbali ina, amawapatsa ntchito malinga ndi zimene adziŵa kuti adzakwanitsa, ngakhale kuti iwowo nthaŵi zina angaone ngati zosatheka. Komanso, amakhala ndi mtima wofuna kumvetsera kwa iwo ndi kuwapatsa zofunikira kuti ziwathandize pochita ntchito zimene amawagaŵira. Choncho, tiyeni nthaŵi zonse titsanzire Atate wathu wakumwamba, Yehova, mwa kumalimbikitsa alambiri anzathu mwachikondi.—Ahebri 10:24.
22 Uthenga wotonthoza wa mngeloyo unam’limbikitsa kwambiri Danieli. Mosasamala kanthu za ukalamba wake, Danieli tsopano analimbikitsidwa nakhala wokonzeka kulandira ndi kulemba ulosi wina wochititsa chidwi kaamba ka phindu lathu.
[Mawu a M’munsi]
a Ngakhale kuti mngeloyu sakutchulidwa dzina, zikuoneka kuti ndi mmodzimodziyo amene mawu ake anamveka akulangiza Gabrieli kuti athandize Danieli pom’fotokozera masomphenya amene anaona. (Yerekezani Danieli 8:2, 15, 16 ndi 12:7, 8.) Ndiponso, Danieli 10:13 amasonyeza kuti Mikaeli, “wina wa akalonga omveka,” anafika kudzathandiza mngelo ameneyu. Choncho, mngelo wosatchulidwa dzina ameneyu ayenera kuti ali ndi mwayi wogwira ntchito limodzi ndi Gabrieli komanso ndi Mikaeli.
b Ngakhale kuti mngelo mmodzimodziyo amene analankhula ndi Danieli angakhale atagwira milomo yake ndi kum’galamutsa, n’kutheka kuti mmene mawuwo akunenera, mngelo wina mwina Gabrieli, ndiye anachita zimenezo. Mulimonsemo, Danieli analimbikitsidwa ndi mthenga waungelo.
KODI MWAZINDIKIRA CHIYANI?
• N’chifukwa chiyani mngelo wa Yehova anachedwa kufika kwa Danieli kuti akam’thandize mu 536 kapena 535 B.C.E.?
• Kodi chovala ndi maonekedwe a mthenga waungelo wa Mulungu zinasonyeza chiyani ponena za iye?
• Kodi Danieli anafunikira chithandizo chotani, ndipo mngeloyo anachipereka motani katatu konse?
• Ndi uthenga wotani umene mngeloyo amakamuuza Danieli?
[Bokosi pamasamba 204, 205]
Angelo Oyang’anira Kapena Ziŵanda Zolamulira?
TIKHOZA kuphunzira zambiri pa zimene buku la Danieli limanena za angelo. Limatiuza za mbali imene amachita pokwaniritsa mawu a Yehova ndi khama limene amaikirapo pochita utumiki wawo.
Mngelo wa Mulungu anati pamene anali paulendo wokalankhula ndi Danieli, anatsekerezedwa ndi “kalonga wa ufumu wa Perisiya.” Atalimbana naye kwa masiku 21, mthenga waungeloyo sanathe kupitiriza ulendo wake kufikira atathandizidwa ndi “Mikaeli, wina wa akalonga omveka.” Mngeloyo anatinso akamenyananso ndi mdaniyo, mwinanso ndi “kalonga wa Helene.” (Danieli 10:13, 20) Sizinali zamaseŵera ayi, ngakhale kwa mngelo weniweniyo! Nangano akalonga a Perisiya ndi Helene anali ayani?
Choyamba, tikuona kuti Mikaeli anatchedwa “wina wa akalonga omveka” ndi “kalonga wanu.” Pambuyo pake, anati Mikaeli anali “kalonga wamkulu wakutumikira ana a anthu a [Danieli].” (Danieli 10:21; 12:1) Zimenezi zikusonyeza kuti Mikaeli ndiye mngelo amenenso anatumidwa ndi Yehova kuti akatsogolere Aisrayeli m’chipululu.—Eksodo 23:20-23; 32:34; 33:2.
Ganizo limeneli likuchirikizidwa ndi mawu a wophunzira Yuda akuti “Mikaeli mkulu wa angelo, pakuchita makani ndi Mdyerekezi anatsutsana za thupi la Mose.” (Yuda 9) Udindo wa Mikaeli, mphamvu yake, ndi ulamuliro wake zikum’tsimikiziradi kukhala “mkulu wa angelo,” kutanthauza “mngelo wamkulu.” Malo apamwamba ameneŵa sangayenerere wina aliyense kupatulapo Yesu Kristu, Mwana wa Mulungu, asanabwere padziko lapansi ndi pambuyo pake.—1 Atesalonika 4:16; Chivumbulutso 12:7-9.
Kodi zimenezi zikutanthauza kuti Yehova anasankhanso angelo oyang’anira mayiko monga Perisiya ndi Helene kuti aziwatsogolera m’nkhani zawo? Yesu Kristu, Mwana wa Mulungu, ananena poyera kuti: “Mkulu wa dziko lapansi alibe . . . kanthu mwa Ine.” Yesu anatinso: “Ufumu wanga suli wa dziko lino lapansi . . . ufumu wanga suli wochokera konkuno.” (Yohane 14:30; 18:36) Mtumwi Yohane analengeza kuti “dziko lonse lapansi ligona mwa woipayo.” (1 Yohane 5:19) N’zoonekeratu kuti mitundu ya padziko sinakhalepo, ndipo siilinso pansi pa utsogoleri kapena ulamuliro wa Mulungu kapena Kristu. Pamene Yehova walola “maulamuliro aakulu” kukhalapo ndi kuyendetsa maboma a padziko lapansi, sindiye kuti amasankha angelo kuti aziwayang’anira. (Aroma 13:1-7) “Akalonga” kapena “olamulira” alionse amene akuwayang’anira anaikidwa ndi mmodzi yekha, “mkulu wa dziko lapansi,” Satana Mdyerekezi. Amenewo ndi ziŵanda zolamulira osati angelo oyang’anira. Pamenepo, ndiye kuti zilipo ziŵanda zosaoneka, kapena “akalonga,” kuseri kwa olamulira oonekawo, ndipo nkhondo za pakati pa mayiko zimaphatikizapo ziŵandazo.
[Chithunzi chachikulu patsamba 199]
[Chithunzi chachikulu patsamba 207]