Danieli
9 Mʼchaka choyamba cha Dariyo+ mwana wa Ahasiwero, wa mtundu wa Amedi, amene anaikidwa kuti akhale mfumu ya ufumu wa Akasidi,+ 2 mʼchaka choyamba cha ulamuliro wake, ineyo Danieli ndinazindikira chiwerengero cha zaka zimene zinatchulidwa mʼmawu amene Yehova anauza mneneri Yeremiya, kuti Yerusalemu adzakhala bwinja+ kwa zaka 70.+ Ndinazindikira zimenezi nditawerenga mʼmabuku.* 3 Choncho ndinayangʼana kwa Yehova Mulungu woona ndipo ndinapemphera momuchonderera, ndinasala kudya,+ ndinavala ziguduli komanso kudzithira phulusa. 4 Ndinapemphera kwa Yehova Mulungu wanga nʼkuvomereza machimo athu kuti:
“Inu Yehova Mulungu woona, Mulungu wamkulu komanso wochititsa mantha. Inu mumakwaniritsa pangano lanu ndipo mumasonyeza chikondi chokhulupirika+ kwa anthu amene amakukondani ndi kusunga malamulo anu.+ 5 Ife tachimwa, tachita zinthu zolakwika komanso zoipa ndipo takupandukirani.+ Tapatuka nʼkusiya kutsatira malamulo ndi zigamulo zanu. 6 Sitinamvere atumiki anu aneneri,+ amene analankhula mʼdzina lanu kwa mafumu athu, akalonga athu, makolo athu ndi anthu onse amʼdziko lathu. 7 Inu Yehova ndinu wolungama, koma ifeyo tadzibweretsera manyazi* ngati mmene zilili lero. Manyazi agwira amuna a mu Yuda, anthu a ku Yerusalemu ndi anthu onse a ku Isiraeli, amene ali pafupi ndiponso amene ali kutali, kumayiko onse amene munawabalalitsirako chifukwa choti anakuchitirani zinthu zosakhulupirika.+
8 Inu Yehova, tachita zinthu zochititsa manyazi,* mofanana ndi mafumu athu, akalonga athu ndi makolo athu chifukwa takuchimwirani. 9 Inu Yehova Mulungu wathu, ndinu wachifundo ndi wokhululuka,+ koma ife takupandukirani.+ 10 Sitinamvere mawu anu, inu Yehova Mulungu wathu, chifukwa sitinatsatire malamulo anu amene munatipatsa kudzera mwa atumiki anu, aneneri.+ 11 Aisiraeli onse aphwanya Chilamulo chanu ndipo apatuka posamvera mawu anu. Choncho inu mwatitsanulira temberero ndi malumbiro amene analembedwa mʼChilamulo cha Mose, mtumiki wanu,+ chifukwa takuchimwirani. 12 Inu mwachitadi zimene munachenjeza kuti mudzachitira ifeyo+ ndi atsogoleri athu amene ankatilamulira.* Mwachita zimenezi potigwetsera tsoka lalikulu. Zimene zachitika mu Yerusalemu sizinayambe zachitikapo padziko lonse lapansi.+ 13 Mogwirizana ndi zimene zinalembedwa mʼChilamulo cha Mose, masoka onsewa atigwera.+ Koma sitinapemphe inu Yehova Mulungu wathu kuti mutikomere mtima.* Sitinachite zimenezi posiya zolakwa zathu+ komanso posonyeza kuti tikumvetsa choonadi chanu.*
14 Koma inu Yehova, munakhala tcheru ndipo munatigwetsera tsoka chifukwa inu Yehova Mulungu wathu ndinu wolungama pa ntchito zonse zimene mwachita, koma ife sitinamvere mawu anu.+
15 Tsopano inu Yehova Mulungu wathu, amene munatulutsa anthu anu mʼdziko la Iguputo ndi dzanja lamphamvu+ nʼkuchititsa kuti dzina lanu lidziwike bwino mpaka lero,+ ife tachimwa ndipo tachita zinthu zoipa. 16 Inu Yehova, nthawi zonse mumachita zinthu zolungama.+ Chonde, chotsani mkwiyo wanu waukulu pa Yerusalemu, phiri lanu loyera. Chifukwa cha machimo athu ndi zolakwa za makolo athu, Yerusalemu komanso anthu anu, tikunyozedwa ndi anthu onse otizungulira.+ 17 Tsopano inu Mulungu wathu, imvani pemphero langa ine mtumiki wanu ndi kuchonderera kwanga. Malo anu opatulika+ amene awonongedwa+ akomereni mtima, inu Yehova, chifukwa cha dzina lanu. 18 Inu Mulungu wanga, tcherani khutu lanu kuti mumve. Tsegulani maso anu kuti muone zimene zatichitikira komanso mmene mzinda wodziwika ndi dzina lanu wawonongekera. Ifeyo sitikukuchondererani chifukwa choti tachita zinthu zolungama ayi, koma chifukwa cha chifundo chanu chachikulu.+ 19 Imvani, inu Yehova. Tikhululukireni,+ inu Yehova. Timvereni ndipo muchitepo kanthu, inu Yehova! Musazengereze inu Mulungu wanga, chifukwa cha dzina lanu. Chifukwa mzinda wanu ndi anthu anu amadziwika ndi dzina lanu.”+
20 Ndili mkati molankhula, kupemphera ndi kuvomereza machimo anga ndi machimo a anthu a mtundu wanga, Aisiraeli komanso kupempha Yehova Mulungu wanga kuti andikomere mtima pa nkhani yokhudza phiri loyera la Mulungu wanga,+ 21 inde, ndili mkati molankhula zimenezi mʼpemphero, munthu uja Gabirieli,+ amene ndinamuona mʼmasomphenya poyamba paja,+ anabwera kwa ine nditatopa kwambiri, pa nthawi yopereka nsembe yamadzulo imene imaperekedwa ngati mphatso. 22 Iye anandithandiza kuti ndimvetse, ndipo anandiuza kuti:
“Iwe Danieli, tsopano ndabwera kuti ndikupatse nzeru ndi kukuthandiza kumvetsa zinthu zonsezi. 23 Utangoyamba kupemphera Mulungu anandiuza uthenga, ndiye ndabwera kudzakufotokozera uthengawo chifukwa ndiwe munthu wokondedwa kwambiri.*+ Choncho mvetsera mwatcheru zimene ndikufuna kukuuza ndipo umvetse masomphenyawa.
24 Pali milungu* 70 imene yaikidwa yokhudza anthu a mtundu wako ndi mzinda wanu woyera+ ndi cholinga choti athetse kuphwanya malamulo, athetse machimo,+ aphimbe cholakwa,+ abweretse chilungamo kuti chikhalepo mpaka kalekale,+ adinde chidindo pamasomphenya ndi maulosi,*+ ndiponso kuti adzoze Malo Opatulika Koposa.* 25 Uyenera kudziwa ndi kuzindikira kuti kuchokera pamene lamulo lakuti Yerusalemu akonzedwe ndi kumangidwanso+ lidzaperekedwe kukafika pamene Mesiya*+ Mtsogoleri+ adzaonekere, padzadutsa milungu 7 komanso milungu 62.+ Yerusalemu adzakonzedwa ndi kumangidwanso ndipo adzakhala ndi bwalo ndi ngalande yachitetezo. Koma zimenezi zidzachitika pa nthawi ya mavuto.
26 Pambuyo pa milungu 62 imeneyi, Mesiya adzaphedwa+ ndipo sadzasiya kalikonse.+
Mtsogoleri adzabwera ndi gulu lake lankhondo ndipo adzawononga mzindawo ndi malo oyera.+ Malo oyerawo adzafafanizidwa ndi madzi osefukira ndipo padzakhala nkhondo mpaka kumapeto. Mogwirizana ndi zimene Mulungu wasankha, kudzakhala chiwonongeko.+
27 Iye* adzasungira anthu ambiri pangano kwa mlungu umodzi. Ndiye pakatikati pa mlunguwo adzathetsa nsembe zanyama ndi nsembe zina zoperekedwa ngati mphatso.+
Wowonongayo adzabwera pamapiko a zinthu zonyansa ndipo zimene Mulungu wasankha zija zidzakhuthulidwanso pachowonongedwacho+ kufikira chitafafanizidwa.”