Moyo ndi Uminisitala za Yesu
Kumaliza Uminisitala Wapakachisi
YESU akuwonekera pa kachisi kwa nthaŵi yomalizira. Kwenikwenidi, iye akumaliza uminisitala wake wapoyera wa padziko lapansi kusiyapo zochitika za kuzengedwa mlandu kwake ndi kuphedwa masiku atatu pambuyo pake. Tsopano iye akupitiriza kudzudzula alembi ndi Afarisi.
Iye akufuulanso katatu kuti: “Tsoka inu, alembi ndi Afarisi, onyenga!” Choyamba, iye akulengeza tsoka pa iwo chifukwa chakuti iwo atsuka “kunja kwake kwa chikho ndi mbale, koma mkatimo iwo adzala ndi kulanda ndi kusadziletsa.” Chotero iye akulangiza kuti: “Yambotsuka mkati mwa chikho ndi mbale, kuti kunja kwake kukhalenso koyera.”
Chotsatira iye akulengeza tsoka pa alembi ndi Afarisi kaamba ka kuola kwawo kwa mkati ndi chinyengo zimene akuyesera kubisa mwa chikhulupiriko chakunja. “Mufanafana ndi manda opaka njereza,” iye akutero, “amene awonekera okoma kunja kwake, koma adzala mkatimo ndi mafupa a anthu akufa ndi zonyansa zonse.”
Chomalizira, chinyengo chawo chikuwonekera m’kufunitsitsa kwawo kumanga manda kaamba ka aneneri ndi kuwakometsera kuti akokere chisamaliro ku ntchito zawo zachifundo. Komabe, monga mmene Yesu akuvumbulira, iwo ali “ana a iwo amene anapha aneneri.” Ndithudi, aliyense amene avumbula chinyengo chawo akhala m’ngozi!
Mopitirizabe, Yesu akulankhula mawu ake a chidzudzulo amphamvu koposa. “Njoka inu, obadwa inu a mamba,” iye akutero, “mudzatha bwanji kuthaŵa kulanga kwake kwa gehena?” Gehena ali chigwa chimene chinagwiritsiridwa monga dzala lotayako zinyalala la Yerusalemu. Chotero Yesu akutanthauza kuti chifukwa cha kulondola njira yawo yoipa, alembi ndi Afarisi adzawonongedwa kosatha.
Ponena za awo amene akuwatumiza monga oimira ake, Yesu akunena kuti: “Ena a iwo mudzawapha, mudzawapachika; ndi ena a iwo mudzawakwapula m’masunagoge mwanu, ndi kuwazunza, kuchokera ku mudzi umodzi, kufikira ku mudzi wina; kotero kuti udzafika pa inu mwazi wonse wotayidwa pa dziko lapansi, kuyambira ku mwazi wa Abele wolungamayo, kufikira ku mwazi wa Zakariya mwana wa Barakiya [wotchedwa Yehoyada mu 2 Mbiri], amene munamupha pakati pa Kachisi ndi guwa la nsembe. Indetu ndinena kwa inu, Zinthu zonse izi zidzafika pa mbadwo uwu wamakono.”
Chifukwa chakuti Zekariya molimba mtima anatsutsa atsogoleri a Israyeli, iwo “anampangira chiwembu, namponya miyala, mwa lamulo la mfumu m’bwalo la nyumba ya Yehova.” Koma, monga mmene Yesu akuneneratu, Israyeli adzalipira kaamba ka mwazi wonse wolungama wokhetsedwa woterowo. Zaka 37 pambuyo pake iwo akulipira, mu 70 C.E., pamene magulu ankhondo Achiroma akuwononga Yerusalemu ndipo Ayuda oposa miliyoni imodzi akuphedwa.
Pamene Yesu akulingalira chochitika chowopsya chimenechi, akupsyinjika. “Ha, Yerusalemu, Yerusalemu,” iye akulengezanso, “Ine ndinafuna kangati kusonkhanitsa pamodzi ana ako, inde monga thadzi lisonkhanitsa anapiye ake m’mapiko ake, koma inu simunafuna ai! Onani, nyumba yanu yasiyidwa kwa inu yabwinja.”
Kenaka Yesu akuwonjezera kuti: “Simudzandiwonanso Ine, kuyambira tsopano, kufikira mudzanena, Wolemekezedwa Iye amene akudza m’dzina la [Yehova, NW].” Tsikulo lidzakhala pa kukhalapo kwa Kristu pamene adzabwera mu Ufumu wake wakumwamba ndipo anthu akumuwona ndi maso a chikhulupiriro.
Yesu tsopano akusunthira pamalo ena pamene akhoza kuwona zosungiramo ndalama namapenyerera makamu akuponyamo ndalama. Olemera akuponyamo ndalama zambiri. Koma mkazi wamasiye waumphawi adza naponyamo tindalama tiŵiri tamtengo wochepa.
Akumaitana ophunzira ake kuti abwere, Yesu akuti: “Ndithu ndinena ndi inu, Mkazi wamasiye amene waumphaŵi anaponya zambiri koposa onse akuponya mosungiramo.” Iwo ayenera kudabwa mmene zingakhalire choncho. Chotero Yesu akulongosola nati: “Pakuti anaponyamo onse mwa zochuluka zawo; koma iye anaponya mwa kusoŵa kwake zonse anali nazo, inde moyo wake wonse.” Atalankhula zinthu zimenezi, Yesu akuchoka pa kachisi kwa nthaŵi yomalizira.
Pozizwitsidwa ndi ukulu ndi kukongola kwa kachisiyo, ophunzira ake akudzuma nati: “Mphunzitsi, onani, miyala yotere ndi nyumba yotere.” Indedi, miyalayo ikusimbidwa kukhala inali yamamita 11 m’litali, kuposa pa mamita 5 m’lifupi, ndi msinkhu woposa pa mamita 3!
“Kodi waona nyumba izi zazikulu?” Yesu akuyankha. “Sudzasiyidwa pano mwala umodzi pamwamba pa unzake, umene sudzagwetsedwa.”
Atatha kulankhula zinthu zimenezi, Yesu ndi ophunzira ake akudutsa Chigwa cha Kedroni ndi kukwera Phiri la Azitona. Kuchokera pamenepo akhoza kuyang’ana pansi ku kachisi wokongolayo. Mateyu 23:25–24:3; Marko 12:41–13:3; Luka 21:1-6; 2 Mbiri 24:20-22.
◆ Kodi Yesu akuchitanji mkati mwa kuyendera kachisi kwake komalizira?
◆ Kodi ndimotani mmene chinyengo cha alembi ndi Afarisi chikuwonekera?
◆ Kodi nchiyani chikutanthauzidwa ndi “kulanga kwake kwa gehena”?
◆ Kodi Yesu akuneneranji kuti mkazi wamasiyeyo wapereka zambiri koposa olemera?