Kodi Nkhosazo ndi Mbuzizo Zili ndi Mtsogolo Motani?
“Iye adzalekanitsa iwo wina ndi mnzake, monga mbusa alekanitsa nkhosa ndi mbuzi.”—MATEYU 25:32.
1, 2. Kodi nchifukwa ninji tiyenera kuchita chidwi ndi fanizo la nkhosa ndi mbuzi?
YESU KRISTU analidi Mphunzitsi wamkulu woposa onse pa dziko lapansi. (Yohane 7:46) Imodzi ya njira zake zophunzitsira inali kugwiritsira ntchito miyambi, kapena mafanizo. (Mateyu 13:34, 35) Ameneŵa anali osavuta koma amphamvu posonyeza choonadi chakuya chauzimu ndi chaulosi.
2 M’fanizo la nkhosa ndi mbuzi, Yesu anasonyeza nthaŵi pamene iye adzakhala ndi malo apadera: “Koma pamene Mwana wa munthu adzadza mu ulemerero wake, ndi . . . ” (Mateyu 25:31) Fanizo limeneli tiyenera kuchita nalo chidwi chifukwa ndilo limene Yesu akumaliza nalo yankho lake pa funsolo: “Chizindikiro cha [kukhalapo, NW] kwanu nchiyani, ndi cha mathedwe a nthaŵi ya pansi pano?” (Mateyu 24:3) Koma kodi zimenezi zikutanthauzanji kwa ife?
3. Poyambirira m’nkhani yake, kodi Yesu anati nchiyani chidzachitika chitangoyamba chisautso chachikulu?
3 Yesu ananeneratu za zochitika zodabwitsa zimene zidzachitika “pomwepo” chitaulika chisautso chachikulu, zochitika zomwe tikuziyembekezera. Anati pomwepo padzaoneka “chizindikiro cha Mwana wa munthu.” Chimenechi chidzakhudza kwambiri “mitundu yonse ya pa dziko lapansi” imene “idzapenya Mwana wa munthu alinkudza pa mitambo ya kumwamba, ndi mphamvu ndi ulemerero waukulu.” Mwana wa munthu adzatsagana ndi “angelo ake.” (Mateyu 24:21, 29-31)a Bwanji nanga za fanizo la nkhosa ndi mbuzi? Mabaibulo amakono amaliika m’chaputala 25, koma lili mbali ya yankho la Yesu, lomafotokoza zowonjezera ponena za kudza kwake ndi ulemerero ndipo lomasumika pa kuweruza kwake “mitundu yonse.”—Mateyu 25:32.
Anthu a m’Fanizolo
4. Kodi fanizo la nkhosa ndi mbuzi likuyamba ndi mawu otani ponena za Yesu, ndipo ndaninso amene akutchulidwa?
4 Yesu akuyamba fanizo lake mwakuti: “Koma pamene Mwana wa munthu adzadza.” Mwachionekere mukumdziŵa “Mwana wa munthu.” Kaŵirikaŵiri olemba Mauthenga Abwino anagwiritsira ntchito mawuwo kunena Yesu. Ngakhale Yesu mwiniyo anatero, mosakayika akumakumbuka masomphenya a Danieli a “wina ngati mwana wa munthu” akuyandikira kwa Nkhalamba ya Kale Lomwe kulandira “ulamuliro ndi ulemerero, ndi ufumu.” (Danieli 7:13, 14; Mateyu 26:63, 64; Marko 14:61, 62) Pamene Yesu ndiye munthu wamkulu m’fanizoli, iye saali yekha. Poyambirira m’nkhaniyo, monga momwe pakufotokozera pa Mateyu 24:30, 31, iye anati pamene Mwana wa munthu ‘alinkudza ndi mphamvu ndi ulemerero waukulu,’ angelo ake adzachita mbali yofunika kwambiri. Mofanana ndi zimenezo, fanizo la nkhosa ndi mbuzi likusonyeza angelo pamodzi ndi Yesu pamene iye ‘akukhala pa chimpando cha kuŵala kwake’ kuweruza. (Yerekezerani ndi Mateyu 16:27.) Koma Woweruzayo ndi angelo ake ali kumwamba, choncho kodi fanizolo likufotoza za anthu?
5. Kodi “abale” a Yesu tingawadziŵe motani?
5 Kupenda fanizolo kumasonyeza magulu atatu amene tiyenera kuwazindikira. Pa nkhosa ndi mbuzi, Mwana wa munthu akuwonjezapo gulu lina lachitatu limene kudziŵika kwake nkofunika kwambiri pa kuzindikira nkhosa ndi mbuzi. Yesu akutcha gulu lachitatulo abale ake auzimu. (Mateyu 25:40, 45) Iwo ayenera kukhala alambiri oona, pakuti Yesu anati: “Aliyense amene adzachita chifuniro cha Atate wanga . . . , yemweyo ndiye mbale wanga, ndi mlongo wanga, ndi amayi wanga.” (Mateyu 12:50; Yohane 20:17) Moyenerera kwambiri, Paulo analemba za Akristu omwe ali mbali ya “mbewu ya Abrahamu” ndi amenenso ali ana a Mulungu. Anatcha ameneŵa “abale” a Yesu ndi “olandirana nawo maitanidwe akumwamba.”—Ahebri 2:9–3:1; Agalatiya 3:26, 29.
6. Kodi “aang’onong’ono” a abale a Yesu ndani?
6 Kodi nchifukwa ninji Yesu anatchula “aang’onong’ono” a abale ake? Mawuwo amakumbutsa zimene atumwi anamumva akunena poyambirira. Posiyanitsa Yohane Mbatizi, yemwe anafa Yesu asanafe, motero nakhala ndi chiyembekezo cha pa dziko lapansi, ndi aja opeza moyo wakumwamba, Yesu anati: “Sanauke wakubadwa mwa akazi munthu wamkulu woposa Yohane Mbatizi; koma iye amene ali wochepa mu ufumu wakumwamba amkulira iye.” (Mateyu 11:11) Ena opita kumwamba angakhale anali omveka mumpingo, monga atumwi, ndi ena osamveka kwenikweni, koma onsewo ndi abale auzimu a Yesu. (Luka 16:10; 1 Akorinto 15:9; Aefeso 3:8; Ahebri 8:11) Chotero, ngakhale ngati ena anaoneka ochepa pa dziko lapansi, anali abale ake ndipo anayenera kuchitidwa monga otero.
Kodi Nkhosa ndi Mbuzi Ndani?
7, 8. Kodi Yesu anati bwanji ponena za nkhosa, choncho nchiyani chomwe tinganene za iwo?
7 Timaŵerenga zotere ponena za chiweruzo cha nkhosa: “[Yesu] [a]dzanena kwa iwo akudzanja lake lamanja, Idzani kuno inu odalitsika a Atate wanga, loŵani mu ufumu wokonzedwera kwa inu pa chikhazikiro chake cha dziko lapansi: pakuti ndinali ndi njala, ndipo munandipatsa ine kudya; ndinali ndi ludzu, ndipo munandimwetsa ine; ndinali mlendo, ndipo munachereza ine; wamaliseche ine, ndipo munandiveka; ndinadwala, ndipo munadza kucheza ndi ine; ndinali m’nyumba yandende, ndipo munadza kwa ine. Pomwepo olungama adzamyankha iye kuti, Ambuye, tinakuonani inu liti wanjala, ndi kukudyetsani? Kapena waludzu, ndi kukumwetsani? Ndipo tinaona inu liti mlendo, ndi kukucherezani? Kapena wamaliseche, ndi kukuvekani? Ndipo tinakuonani inu liti wodwala, kapena m’nyumba yandende, ndipo tinadza kwa inu? Ndipo mfumuyo idzayankha nidzati kwa iwo, Indetu ndinena kwa inu, Chifukwa munachitira ichi mmodzi wa abale anga, ngakhale aang’onong’ono aŵa, munandichitira ichi ine.”—Mateyu 25:34-40.
8 Ndithudi, nkhosa zoweruzidwa kukhala kulamanja kwa Yesu kolemekezeka ndi kwachiyanjo zimaimira kagulu ka anthu. (Aefeso 1:20; Ahebri 1:3) Kodi anachitanji ndipo liti? Yesu akuti iwo mokoma mtima, mwaulemu, ndi mowoloŵa manja anampatsa chakudya, madzi, ndi zovala, kumthandiza pamene anadwala kapena pamene anali m’ndende. Pamene nkhosazo zikuti sizinachite zimenezo kwa Yesu mwachindunji, iye akuti zinachirikizadi abale ake auzimu, otsalira a Akristu odzozedwa, choncho m’lingaliro limenelo anamchitira iye zimenezo.
9. Kodi nchifukwa ninji fanizolo silikunena za mu Zaka Chikwi?
9 Fanizolo silikunena za mu Zaka Chikwi, pakuti nthaŵiyo odzozedwa sadzakhala anthu omavutika ndi njala, ludzu, kudwala, kapena sadzakhala m’ndende. Komabe, ambiri a iwo zinthu zotero zawachitikira m’nthaŵi ino ya chimaliziro cha dongosolo ili la zinthu. Chiyambire pamene Satana anagwetseredwa pa dziko lapansi, walunjikitsa mkwiyo wake pa otsalira monga chandamale chake chapadera, akumawatonzetsa, kuwazunza, ndi kuwapha.—Chivumbulutso 12:17.
10, 11. (a) Kodi nchifukwa ninji kuli kosayenera kulingalira kuti nkhosazo zikuphatikizapo aliyense wokomera mtima abale a Yesu? (b) Moyenerera, kodi nkhosa zimaimira yani?
10 Kodi Yesu akunena kuti yense wosonyeza kukoma mtima pang’ono kwa abale ake, monga mwa kuwapatsa buledi kapena madzi akumwa, amakhala mmodzi wa nkhosazo? Zoona, kuchita mokoma mtimako kungasonyeze kukoma mtima kwa munthu, komatu, zikuoneka kuti pali zochuluka zimene zikufunika kwa nkhosa za m’fanizoli. Mwachitsanzo, Yesu sanali konse kunena za okana Mulungu kapena atsogoleri achipembedzo amene angakomere mtima mmodzi wa abale akeŵa. Mosiyana ndi zimenezo, Yesu kaŵiri anatcha nkhosazo “olungama.” (Mateyu 25:37, 46) Chotero nkhosazo ziyenera kukhala aja omwe nthaŵi yaitali athandiza—kuchirikiza mwachangu—abale a Kristu ndipo asonyeza chikhulupiriro kufikira pa kukhala ndi kaimidwe kolungama pamaso pa Mulungu.
11 M’zaka mazanamazana, anthu ambiri monga Abrahamu akhala ndi kaimidwe kolungama. (Yakobo 2:21-23) Nowa, Abrahamu, ndi okhulupirika ena akuphatikizidwa pa “nkhosa zina” amene adzalandira moyo m’Paradaiso mu Ufumu wa Mulungu. Posachedwapa enanso mamiliyoni ambiri alandira kulambira koona monga nkhosa zina ndipo akhala “gulu limodzi” ndi odzozedwa. (Yohane 10:16; Chivumbulutso 7:9) Aŵa oyembekezera kukhala pa dziko lapansi amazindikira kuti abale a Yesu ndiwo akazembe a Ufumu choncho awathandiza—kuthupi ndi mwauzimu. Zimene nkhosa zina zimachitira abale ake pa dziko lapansi Yesu amaona kuti zimachitira iye. Anthu otero amene adzakhala ndi moyo pamene iye adzadza kudzaweruza mitundu adzaweruzidwa monga nkhosa.
12. Kodi nkhosa zingafunsirenji mmene zinamkomera mtima Yesu?
12 Ngati nkhosa zina tsopano zikulalikira uthenga wabwino limodzi ndi odzozedwa ndipo zikuwathandiza, chifukwa ninji akufunsa kuti: “Ambuye, tinakuonani inu liti wanjala, ndi kukudyetsani? Kapena waludzu, ndi kukumwetsani?” (Mateyu 25:37) Pangakhale zifukwa zingapo. Limeneli ndi fanizo. Mwa ilo, Yesu akusonyeza kudera nkhaŵa kwambiri abale ake auzimu; amalingalira za iwo, amavutika nawo. Poyamba Yesu anati: “Iye wakulandira inu, andilandira ine, ndi wakulandira ine, amlandira iye amene ananditumiza ine.” (Mateyu 10:40) M’fanizo limeneli, Yesu akupitiriza ndi mfundo imeneyo, kusonyeza kuti (zabwino kapena zoipa) zochitidwa kwa abale ake zimafika ndi kumwamba komwe; zili monga ngati zimachitidwa kwa iye kumwamba. Ndiponso, Yesu panopa akugogomezera muyezo wa Yehova woweruzira, kumveketsa bwino kuti chiweruzo cha Mulungu kaya choyanja kapena chotsutsa, nchoyenera ndi cholungama. Mbuzizo sizingapereke chodzikhululukira chakuti, ‘Koma tikanakuonani inu mwini.’
13. Kodi nchiyani chimene onga mbuzi angatchere Yesu “Ambuye”?
13 Titangomvetsa pamene chiweruzo chosonyezedwa m’fanizoli chidzaperekedwa, timakhala ndi chithunzi chabwino cha amene ali mbuzi. Lidzakwaniritsidwa pamene “padzaoneka m’thambo chizindikiro cha Mwana wa munthu; ndipo mitundu yonse ya pa dziko lapansi idzadziguguda pachifuŵa, nidzapenya Mwana wa munthu alinkudza . . . ndi mphamvu ndi ulemerero waukulu.” (Mateyu 24:29, 30) Opulumuka chisautso cha Baibulo Wamkulu amene anyozera abale a Mfumu mwina tsopano adzatcha Woweruzayo “Ambuye,” pokhulupirira kuti adzapulumutsa miyoyo yawo.—Mateyu 7:22, 23; yerekezerani ndi Chivumbulutso 6:15-17.
14. Kodi Yesu adzaweruza nkhosa ndi mbuzi pazifukwa zotani?
14 Komabe, chiweruzo cha Yesu sichidzazikidwa pa kuyesayesa kudzilungamitsa kwa omwe kale anali atchalitchi, okana Mulungu, ndi ena. (2 Atesalonika 1:8) M’malo mwake, woweruzayo adzapenda mitima yawo ndi zochita zakale za anthuwo kulinga kwa “aang’onong’ono aŵa [a abale ake].” Zoona, Akristu odzozedwa otsalira pa dziko lapansi chiŵerengero chawo chikuchepa. Komabe, malinga ngati odzozedwa, opanga “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru,” apitiriza kugaŵira chakudya chauzimu ndi chitsogozo, oyembekeza kukhala nkhosa ali ndi mwaŵi wakuchitira chabwino kagulu ka kapolo, monga momwedi lachitira ‘khamu lalikulu ochokera mwa mtundu uliwonse, ndi mafuko ndi anthu.’—Chivumbulutso 7:9, 14.
15. (a) Kodi ambiri asonyeza motani kuti ali ngati mbuzi? (b) Kodi nchifukwa ninji tiyenera kupeŵa kunena kuti kaya wina ndi nkhosa kapena mbuzi?
15 Kodi abale a Kristu ndi mamiliyoni a nkhosa zina ogwirizana nawo kukhala gulu limodzi achitiridwa motani? Anthu ambiri angakhale sanaukire oimira Kristu, komanso sanachitire anthu ake mwachikondi. Pokonda dziko loipa, onga mbuzi amakana uthenga wa Ufumu, kaya adzimverere iwo eni kaya aumve mwa njira ina. (1 Yohane 2:15-17) Ndithudi, Yesu makamaka ndiye waikidwa kupereka chiweruzo. Sizili kwa ife kunena amene ali nkhosa ndi amene ali mbuzi.—Marko 2:8; Luka 5:22; Yohane 2:24, 25; Aroma 14:10-12; 1 Akorinto 4:5.
Kodi Gulu Lililonse Lili ndi Mtsogolo Motani?
16, 17. Kodi nkhosa zidzakhala ndi mtsogolo motani?
16 Yesu anapereka chiweruzo chake pa nkhosa kuti: “Idzani kuno inu odalitsika a Atate wanga, loŵani mu ufumu wokonzedwera kwa inu pa chikhazikiro chake cha dziko lapansi.” Ndi chiitano chabwino chotani nanga chimenecho—“Idzani”! Kuti? Ku moyo wosatha, malinga ndi zimene anafotokoza mwachidule kuti: “Olungama [adzaloŵa] ku moyo wa nthaŵi zonse.”—Mateyu 25:34, 46.
17 M’fanizo la matalente, Yesu anasonyeza zofunika kwa aja amene adzalamulira naye kumwamba, koma m’fanizo ili akusonyeza zofunika kwa nzika za Ufumuwo. (Mateyu 25:14-23) Mosapita m’mbali, chifukwa cha kuthandiza kwawo abale a Yesu ndi mtima wonse, nkhosazo zilandira malo m’chigawo cha pa dziko lapansi cha Ufumu wake. Adzasangalala ndi moyo m’paradaiso pa dziko lapansi—mtsogolo mmene Mulungu anawakonzera “pa chikhazikiro chake cha dziko lapansi” la anthu oomboleka.—Luka 11:50, 51.
18, 19. (a) Kodi Yesu adzapereka chiweruzo chotani pa mbuzi? (b) Kodi titsimikiza bwanji kuti mbuzi sizidzazunzika kwa muyaya?
18 Ha, chiweruzo choperekedwa pa mbuzi nchosiyana chotani nanga ndi zimenezo! “Pomwepo iye adzanena kwa iwo akudzanja lamanzere, Chokani kwa ine otembereredwa inu, kumoto wa nthaŵi zonse wokolezedwera Mdyerekezi ndi amithenga ake: pakuti ndinali ndi njala, ndipo simunandipatsa ine kudya: ndinali ndi ludzu, ndipo simunandimwetsa ine: ndinali mlendo, ndipo simunandilandira ine; wamaliseche ndipo simunandiveka ine; wodwala, ndi m’nyumba yandende, ndipo simunadza kundiona ine. Pomwepo iwonso adzayankha kuti, Ambuye, tinakuonani liti wanjala, kapena waludzu, kapena mlendo, kapena wamaliseche, kapena m’nyumba yandende, ndipo ife sitinakutumikirani inu? Pomwepo iye adzayankha iwo kuti, Indetu ndinena kwa inu, Chifukwa munalibe kuchitira ichi mmodzi wa aŵa aang’onong’ono, munalibe kundichitira ichi ine.”—Mateyu 25:41-45.
19 Ophunzira Baibulo akudziŵa kuti zimenezi sizikutanthauza kuti miyoyo yosafa ya onga mbuzi idzazunzika m’moto wamuyaya ayi. Pakuti anthu ndiwo miyoyo; alibe moyo wosafa. (Genesis 2:7; Mlaliki 9:5, 10; Ezekieli 18:4) Mwa kuweruzira mbuzi ku “moto wa nthaŵi zonse,” Woweruzayo akutanthauza chiwonongeko chopanda chiyembekezo cha mtsogolo, chimenenso chidzakhala mapeto achikhalire a Mdyerekezi ndi ziŵanda zake. (Chivumbulutso 20:10, 14) Chotero, Woweruza wa Yehova akupereka ziweruzo zosiyana. Akuuza nkhosa kuti, “Idzani”; mbuzi, “Chokani kwa ine.” Nkhosazo zidzalandira “moyo wa nthaŵi zonse.” Mbuzi zidzalandira “chilango cha nthaŵi zonse.”—Mateyu 25:46.b
Kodi Zikutanthauzanji kwa Ife?
20, 21. (a) Kodi ndi ntchito iti yofunika imene Akristu ayenera kuchita? (b) Kodi ndi kugaŵanika kotani kumene kukuchitika tsopano? (c) Kodi anthu adzakhala mumkhalidwe wotani pamene fanizo la nkhosa ndi mbuzi liyamba kukwaniritsidwa?
20 Atumwi anayi amene anamva yankho la Yesu lonena za chizindikiro cha kukhalapo kwake ndi cha chimaliziro cha dongosololi anali ndi zochuluka zozilingalira. Anafunika kukhala ogalamuka ndi odikira. (Mateyu 24:42) Anafunikanso kuchita ntchito ya umboni yotchulidwa pa Marko 13:10. Lerolino Mboni za Yehova zikuchita ntchitoyo mwachangu.
21 Koma, kodi kamvedwe katsopano kameneka ka fanizo la nkhosa ndi mbuzi kamatanthauzanji kwa ife? Eya, anthu ayamba kale kusankha mbali yoimako. Ena ali ‘panjira yaikulu yakumuka nayo kukuonongeka,’ pamenenso ena akuyesa kukhalabe ‘panjirayo yochepetsa yakumuka nayo kumoyo.’ (Mateyu 7:13, 14) Koma nthaŵi imene Yesu adzapereka chiweruzo chomaliza pa nkhosa ndi mbuzi zosonyezedwa m’fanizoli ikali kutsogolo. Pamene Mwana wa munthu adzadza monga Woweruza, adzatsimikiza kuti Akristu oona ambiri—kwenikweni “khamu lalikulu” la nkhosa zodzipatulira—ayeneretsedwa kupyola mbali yomaliza ya “chisautso chachikulu” kuloŵa m’dziko latsopano. Chiyembekezocho chiyenera kutipatsa chimwemwe tsopano. (Chivumbulutso 7:9, 14) Komabe, unyinji wa “mitundu yonse” adzakhala atasonyeza kuti ali ngati mbuzi zouma khosi. “Adzachoka kumka ku chilango cha nthaŵi zonse.” Dziko lapansi lidzakhala pampumulo wotani nanga!
22, 23. Popeza kukwaniritsidwa kwa fanizolo kukali mtsogolo, kodi nchifukwa ninji ntchito yathu yolalikira ili yofunika kwambiri lerolino?
22 Pamene chiweruzo chofotokozedwa m’fanizolo chili patsogolopa, ngakhale tsopano kanthu kena kofunika kwambiri kakuchitika. Ife Akristu tikuchita ntchito yopulumutsa miyoyo ya kulengeza uthenga wogaŵanitsa anthu. (Mateyu 10:32-39) Paulo analemba kuti: “Pakuti, amene aliyense adzaitana pa dzina la [Yehova, NW] adzapulumuka. Ndipo iwo adzaitana bwanji pa iye amene sanamkhulupirira? Ndipo adzakhulupirira bwanji iye amene sanamva za iye? Ndipo adzamva bwanji wopanda wolalikira?” (Aroma 10:13, 14) Utumiki wathu wapoyera ukufika anthu m’maiko oposa 230 ndi dzina la Mulungu ndi uthenga wake wa chipulumutso. Abale odzozedwa a Kristu akali kutsogolera ntchitoyi. Pafupifupi mamiliyoni asanu a nkhosa zina agwirizana nawo tsopano. Ndipo anthu padziko lonse akulabadira uthenga wolengezedwa ndi abale a Yesu.
23 Ambiri amafikidwa ndi uthenga wathu pamene tilalikira kunyumba ndi nyumba kapena mwamwaŵi. Ena angamve za Mboni za Yehova ndi zimene timaimira mwa njira zosadziŵika kwa ife. Nthaŵi ya chiweruzo ikafika, kodi Yesu adzalingalira za thayo la anthu monga gulu ndi mikhalidwe ya banja kufika pamlingo wotani? Sititha kunena, ndipo kuyesa kulotera nkosathandiza. (Yerekezerani ndi 1 Akorinto 7:14.) Ambiri tsopano amanyalanyaza dala anthu a Mulungu, kuwatonza, kapena kutengamo mbali kuwazunza. Nchifukwa chake, nthaŵi ino njowopsa; oterowo angakhale akusanduka aja amene Yesu adzawaweruza monga mbuzi.—Mateyu 10:22; Yohane 15:20; 16:2, 3; Aroma 2:5, 6.
24. (a) Kodi nchifukwa ninji munthu yense afunika kuchitapo kanthu pa ulaliki wathu? (b) Kodi phunziroli lakuthandizani kuona motani utumiki wanu?
24 Koma chosangalatsa nchakuti ambiri amamva, amaphunzira Mawu a Mulungu, nakhala Mboni za Yehova. Ena amene tsopano akuoneka ngati mbuzi angasinthe ndi kukhala ngati nkhosa. Mfundo yake njakuti aja amene akumva ndi kuchirikiza mwachangu otsalira a abale a Kristu akupereka umboni tsopano mwa njira imeneyo umene udzapereka chifukwa chowaikira kudzanja lamanja la Yesu pamene iye, patsogolopa, adzakhala pa mpando wake wachifumu kuweruza. Ameneŵa akudalitsidwa ndipo adzadalitsidwabe. Chotero, fanizo limeneli liyenera kutisonkhezera kugwira ntchito ndi changu chonse mu utumiki Wachikristu. Tisanachedwe, tiyenera kuchita zonse zomwe tingathe kulengeza uthenga wabwino wa Ufumu ndipo mwa njirayo kupatsa ena mwaŵi wa kuchitapo kanthu. Ndiyeno zili kwa Yesu kupereka chiweruzo, chotsutsa kapena choyanja.—Mateyu 25:46.
[Mawu a M’munsi]
b El Evangelio de Mateo imati: “Moyo wa nthaŵi zonse uli moyo wotsimikizirika; chosiyana nawo ndicho chilango chotsimikizirika. Ajekitivi Yachigirikiyo aionios kwenikweni simatanthauza utali wa nyengo yake, koma mkhalidwe wake. Chilango chotsimikizirika ndicho imfa yosatha.”—Profesa Juan Mateos wopuma pantchito (Pontifical Biblical Institute, Rome) ndi Profesa Fernando Camacho, (Theological Center, Sevile), Madrid, Spain, 1981.
Kodi Mukukumbukira?
◻ Kodi ndi kufanana kotani kwa Mateyu 24:29-31 ndi Mateyu 25:31-33 kumene kumasonyeza kuti fanizo la nkhosa ndi mbuzi lidzakwaniritsidwa mtsogolo, ndipo ndiliti?
◻ Kodi “aang’onong’ono” a abale a Yesu ndani?
◻ Kodi kugwiritsira ntchito kwa Yesu mawu akutiwo “olungama” kumatithandiza motani kudziŵa amene iwo akuimira ndi amene sakuimira?
◻ Ngakhale kuti fanizolo lidzakwaniritsidwa mtsogolo, kodi nchifukwa ninji ulaliki wathu tsopano uli wofunika ndi wofulumiza?
[Bokosi/Chithunzi patsamba 24]
ONANI MBALI ZOFANANA
Mateyu 24:29-31 Mateyu 25:31-33
Chitayamba chisautso chachikulu, Mwana wa munthu afika
Mwana wa munthu adza
Adza ndi ulemerero waukulu Afika mu ulemerero ndi kukhala
pa chimpando choŵala
Angelo ali pamodzi naye Angelo afika limodzi naye
Mitundu yonse pa dziko Mitundu yonse isonkhanidwa;
lapansi ipenya mbuzi ziweruzidwa pomalizira
pake (chisautso chachikulu chitha)
[Mawu a Chithunzi]
Garo Nalbandian