Khululukani Kuchokera Mumtima
“Chomwechonso Atate wanga adzachitira inu, ngati inu simukhululukira yense mbale wake ndi mitima yanu.”—MATEYU 18:35.
1, 2. (a) Kodi wochimwa winawake wodziŵika anasonyeza motani kuti anayamikira Yesu? (b) Kodi Yesu analongosola mfundo yotani poyankha?
MKAZIYO anali hule, osati munthu amene mungayembekezere kum’peza m’nyumba ya munthu wachipembedzo. Ngati ena anadabwa kumuona m’nyumbamo, zimene anachita zinali zodabwitsa koposa. Anapita kwa mwamuna wakhalidwe labwino koposa ndi kusonyeza kuti amayamikira ntchito yake mwa kum’sambitsa mapazi ake ndi misozi yake ndi kuwapukuta ndi tsitsi lake.
2 Mwamunayo, Yesu, sananyansidwe naye mkazi ameneyu, “wochimwa, amene anali m’mudzimo.” Koma mwininyumbayo, Simoni Mfarisi, anavutika mtima popeza kuti mkaziyo anali wochimwa. Yesu anayankha mwa kusimba za amuna aŵiri amene anali ndi ngongole kwa wobwereketsa ndalama. Wina ngongole yake inali yaikulu—pafupifupi malipiro a wantchito wamba a zaka ziŵiri. Winayo ngongole yake inali yochepa, ndalama zosakwanira malipiro a miyezi itatu. Atalephera kubweza ngongole zawo, wowakongozayo “anawakhululukira onse aŵiri.” Inde, amene anakhululukidwa ngongole yaikulu anali ndi chifukwanso chachikulu chokondera wom’kongoza ndalamayo. Atagwirizanitsa nkhaniyi ndi kukoma mtima kwa mkaziyo, Yesu anawonjezerapo pulinsipulo lakuti: “Munthu amene anam’khululukira pang’ono, iye akonda pang’ono.” Ndiyeno anauza mkaziyo kuti: “Machimo ako akhululukidwa.”—Luka 7:36-48.
3. Kodi tiyenera kupenda chiyani ponena za ife eni?
3 Dzifunseni kuti, ‘Ndikanakhala mkazi uja kapena nditakhala mumkhalidwe wofananawo ndiyeno ndikusonyezedwa chifundo, kodi ndikanakhala wouma mtima ndi wosakhululukira ena?’ Mungayankhe kuti, ‘Sindingachite zimenezo!’ Komabe, kodi ndinu wotsimikizadi mtima kuti m’mafuna kukhululuka? Kodi chimenecho n’chibadwa chanu? Kodi mwakhululukirapo ena mosanyinyirika, ndipo kodi ena anganene kuti ndinu munthu wokonda kukhululuka? Tiyeni tione chifukwa chimene aliyense wa ife ayenera kupenda nkhani imeneyi moona mtima ndiponso modzifufuza yekha.
Kukhululukira Ena N’kofunika—Ndipo Kumasonyezedwa kwa Ife
4. Kodi tiyenera kuvomereza chiyani ponena za ife eni?
4 Ndinu wopanda ungwiro, ndipo m’madziŵa bwino lomwe zimenezo. Mutafunsidwa, muthanso kuvomereza, mwinanso kukumbukira mawu a pa 1 Yohane 1:8 akuti: “Tikati kuti tilibe uchimo, tidzinyenga tokha, ndipo mwa ife mulibe choonadi.” (Aroma 3:23; 5:12) Kwa ena, uchimo wawo mwina unaonekera mwa machimo aakulu kwambiri oumitsa thupi. Koma ngakhale kuti mukudziŵa kuti simunachitepo machimo oterowo, pali nthaŵi zambiri, ndiponso njira zambiri, pamene mwalephera kufika pamiyezo ya Mulungu, kapena kuti pamene mwachimwa. Kodi si tero?
5. Kodi tiyenera kuthokoza Mulungu pachifukwa chiti?
5 Chotero, mwina kwa inu zinthu zikugwirizana ndi mafotokozedwe a mtumwi Paulo akuti: “Pokhala akufa m’zolakwa ndi kusadulidwa kwa thupi lanu, [Mulungu] anakupatsani moyo pamodzi ndi Iye [Yesu], mmene adatikhululukira ife zolakwa zonse.” (Akolose 2:13; Aefeso 2:1-3) Taonani mawuwo ‘adatikhululukira ife zolakwa zonse.’ Pamenepo pali nkhani. Aliyense wa ife ali ndi chifukwa chabwino chochonderera monga momwe Davide anachitira kuti: ‘Chifukwa cha dzina lanu, Yehova, ndikhululukireni kusakaza [“kulakwa,” NW] kwanga, pakuti ndiko kwakukulu.’—Salmo 25:11.
6. Kodi tingakhale otsimikiza za chiyani ponena za Yehova ndi chikhululukiro?
6 Kodi inuyo, kapena aliyense wa ife, mungakhululukidwe motani? Mfundo yaikulu ndiyakuti Yehova Mulungu amafunitsitsa kukhululuka. Ndi mmene umunthu wake wakhalira. (Eksodo 34:6, 7; Salmo 86:5) Ndiye m’pomveka kuti Mulungu amayembekeza kuti tipite kwa iye m’pemphero ndi kum’chonderera, kum’pempha kuti atikhululukire. (2 Mbiri 6:21; Salmo 103:3, 10, 14) Ndipo waikapo njira yalamulo yotisonyezera chikhululukiro chimenechi—nsembe ya dipo ya Yesu.—Aroma 3:24; 1 Petro 1:18, 19; 1 Yohane 4:9, 14.
7. Kodi muyenera kufuna kutsanzira Yehova m’njira yotani?
7 Mutayang’ana kufunitsitsa kwa Mulungu kuti akhululuke, mudzaona mmene muyenera kukhalira ndi anthu anzanu. Paulo anagogomezera zimenezi, ndipo analemba kuti: “Mukhalirane okoma wina ndi mnzake, a mtima wachifundo, akukhululukirana nokha, monganso Mulungu mwa Kristu anakhululukira inu.” (Aefeso 4:32) M’posakayikitsa kuti mfundo ya Paulo ikuphatikizapo kutengapo kwathu phunziro pachitsanzo cha Mulungu, popeza vesi lotsatira limapitiriza kuti: “Chifukwa chake khalani akutsanza a Mulungu, monga ana okondedwa.” (Aefeso 5:1) Kodi mukuona kugwirizana kwake? Yehova Mulungu anakukhululukirani, chotero muyenera kum’tsanzira ndi kukhala ‘a mtima wachifundo, akukhululukira’ ena, anagogomezera motero Paulo. Koma dzifunseni kuti, ‘Kodi ndikuchita zimenezo? Ngati sichibadwa changa, kodi ndikuyesetsa kukhala munthu wotero, kuyesetsa mwamphamvu kutsanzira Mulungu pankhani ya kukhala wokhululuka?’
Tiyenera Kuyesetsa Kukhala Okhululuka
8. Kodi tiyenera kuzindikira chiyani ponena za anthu a mumpingo wathu?
8 Zingakhale zosangalatsa kuganiza kuti mumpingo wachikristu, si nthaŵi zambiri kuti mumachitika zinthu zofuna kuti tisonyeze mkhalidwe waumulungu wa kukhululuka. Koma si mmene zilili. Zoonadi, abale ndi alongo athu akuyesetsa kutsatira njira yachikondi ya Yesu. (Yohane 13:35; 15:12, 13; Agalatiya 6:2) Ayesetsa kwanthaŵi yaitali, ndipo akuyesetsabe kusiyana ndi malingaliro, kalankhulidwe, ndi kachitidwe ka zinthu ka dziko loipali. Iwo akufunadi kusonyeza umunthu watsopano. (Akolose 3:9, 10) Koma, sitinganyalanyaze mfundo yakuti mpingo wapadziko lonse, komanso mpingo wakwathu uliwonse, ndi wopangidwa ndi anthu opanda ungwiro. Pazambiri, iwo ali bwino kwambiri kusiyana ndi mmene analili kale, koma adakali opanda ungwiro.
9, 10. N’chifukwa chiyani sitiyenera kudabwa ngati pakati pa abale pakubuka mavuto?
9 M’Baibulo, Mulungu amatiuziratu kuti mumpingo mwathu tingayembekezere zophophonya pakati pa abale ndi alongo athu. Mwachitsanzo, talingalirani mawu a Paulo olembedwa pa Akolose 3:13 akuti: “[Pitirizani, NW] kulolerana wina ndi mnzake, ndi kukhululukirana eni okha, ngati wina ali nacho chifukwa pa mnzake; monganso Ambuye anakhululukira inu.”
10 N’zochititsa chidwi kuti Baibulo panopo likutikumbutsa za kugwirizana kwapakati pa kutikhululukira kwa Mulungu ndi kukhululukira ena kumene tiyenera kuchita kumenenso kuli kofunika. N’chifukwa chiyani zimenezi zimavuta? Chifukwa chakuti Paulo anavomereza kuti wina angakhale nacho “chifukwa pa mnzake.” Iye anadziŵa kuti zifukwa zotere zidzakhalapo. Ziyenera kuti zinalipo m’zaka za zana loyamba, ngakhale pakati pa Akristu “oyera mtima,” amene anali ndi ‘chiyembekezo chosungikira iwo m’Mwamba.’ (Akolose 1:2, 5) Chotero kodi tingalingalire kuti lero zifukwazo padzakhala palibe pamene Akristu oona ochuluka alibe umboni wa mzimu wakuti ndi “osankhika a Mulungu, oyera mtima ndi okondedwa”? (Akolose 3:12) Ndiye chifukwa chake sitiyenera kuganiza kuti pali kenakake kolakwika kwambiri ngati mumpingo mwathu muli zifukwa zoterozo—kukhumudwa chifukwa cha kulakwiridwa kwenikweni kapena kongoganizira.
11. Kodi wophunzira Yakobo anatichenjeza za chiyani?
11 Mawunso a Yakobo mbale wa Yesu mwa atate wina amasonyeza kuti tiyenera kuyembekezera kuti nthaŵi zina tidzakumanabe ndi mikhalidwe ina imene idzafuna kuti tikhululukire abale athu. “Ndani ali wanzeru, ndi waluso mwa inu? Aonetsere ndi mayendedwe ake abwino ntchito zake munzeru yofatsa. Koma mukakhala nako kaduka koŵaŵa, ndi chotetana m’mtima mwanu, musadzitamandira, ndipo musamanama potsutsana nacho choonadi.” (Yakobo 3:13, 14) “Kaduka koŵaŵa, ndi chotetana” m’mitima ya Akristu oona? Inde, mawu a Yakobo akusonyeza bwino lomwe kuti zimenezo zinachitika mumpingo wa m’zaka za zana loyamba ndipo zidzachitikanso lerolino.
12. Kodi mumpingo wakale wa ku Filipi munabuka vuto lotani?
12 Chitsanzo chabwino kwambiri ndi cha Akristu aŵiri odzozedwa amene anali ndi mbiri yabwino ya kugwira ntchito mwakhama ndi Paulo. Mungakumbukire kuŵerenga za Euodiya ndi Suntuke, alongo a mumpingo wa ku Filipi. Ngakhale kuti Afilipi 4:2, 3, safotokoza nkhaniyo mwatsatanetsatane, amasonyeza kuti panali vuto pakati pawo. Kodi linayamba chifukwa cha kusayankhula bwino, kulalata, kuchitira chipongwe wachibale, kapena chifukwa cha kupikisana mwansanje koonekera? Kaya nkhani yake inali yotani, inadzakula kwambiri moti Paulo anaimva ali kutali kwambiri ku Roma. Alongo auzimu aŵiriwo ayenera kuti anali kungoonerana m’madzi, osafuna kukumana pamisonkhano kapena aliyense anali kuyankhula zonyoza ponena za wina pocheza ndi anzake.
13. Kodi n’chiyani chimene chiyenera kuti chinathandiza Euodiya ndi Suntuke, chimene chikutiphunzitsa chiyani?
13 Kodi zimenezo zikumveka ngati zimene zinachitikapo kwa ena mumpingo wanu kapena zimene zinakuchitikirani? Mwinanso pano tikunena pali vuto ngati limenelo. Kodi tingachitenji? Pachochitika chakalecho, Paulo analimbikitsa alongo aŵiri odzipatulirawo kuti “alingirire ndi mtima umodzi mwa Ambuye.” Ayenera kuti anavomera kukambirana nkhaniyo, kuthetsa vutolo, kusonyezana mtima wofuna kukhululukirana, ndiyeno kwenikweni kutsanzira mzimu wokhululuka wa Yehova. Palibe chifukwa choganizira mwa njira ina, koma kuti Euodiya ndi Suntuke anathetsa vuto lawo, ndipo ifenso tingathetse mavuto athu. Mzimu wokhululuka umenewo tingausonyeze lerolino mwachipambano.
Khazikitsani Mtendere—Khululukani
14. N’chifukwa chiyani nthaŵi zambiri kumakhala kotheka ndiponso n’kwabwino kwambiri kunyalanyaza zimene ena atilakwira?
14 Kodi kwenikweni kukhululuka kumafuna chiyani ukakhala kuti sukumvana ndi Mkristu wina? Kunena zoona, palibe njira yosavuta, koma Baibulo limapereka zitsanzo zothandiza ndi uphungu wothandiza. Njira yaikulu yabwino, ngakhale kuti ndi yovuta kuivomereza ndi kuigwiritsa ntchito, ndiyo kungoiiŵala nkhaniyo, kuchita ngati simunamve kalikonse. Nthaŵi zambiri pamene pali vuto, monga lomwe linali pakati pa Euodiya ndi Suntuke, aliyense payekha amaona kuti winayo ndi amene ali ndi mlandu kapena ndiye wayambitsa vutolo. Choncho pamkhalidwe ngati umenewo, mungalingalire kuti Mkristu winayo ndiye woyenera kuimbidwa mlandu kwenikweni kapena kuti ndiye walakwa kwambiri. Komano kodi mungaithetse nkhaniyo mwa kungokhululuka? Zindikirani kuti ngati, tikutitu ngati, Mkristu winayo ndiye wolakwa kwambiri kapena mlandu wonse ndi wake, inuyo ndinu amene muyenera kuinyalanyaza nkhaniyo kuti mwakhululuka ndipo yatha.
15, 16. (a) Kodi Mika anam’fotokoza motani Yehova? (b) Kodi kunena kuti Mulungu ‘amapitirira zolakwa’ kumatanthauza chiyani?
15 Tisaiŵale kuti Mulungu ndiye chitsanzo chathu cha kukhululuka. (Aefeso 4:32–5:1) Ponena za mmene Iye amanyalanyazira zolakwa, mneneri Mika analemba kuti: “Ndani Mulungu wofanana ndi Inu, wakukhululukira mphulupulu, wakupitirira zolakwa za otsala a choloŵa chake? Sasunga mkwiyo wake ku nthaŵi yonse popeza akondwera nacho chifundo.”—Mika 7:18.
16 Pofotokoza Yehova kuti ali “wakupitirira zolakwa,” Baibulo silikunena kuti iye satha kukumbukira zolakwa, ngati kuti amadwala matenda ena oiŵalaiŵala. Talingalirani za Samsoni ndi Davide, amene onse anachita machimo aakulu. Mulungu anatha kukumbukira machimo amenewo ngakhale patapita nthaŵi yaitali; ngakhalenso ifeyo timadziŵa ena mwa machimo awo chifukwa chakuti Yehova anawalemba m’Baibulo. Komabe, Mulungu wathu wokhululukayo anawachitira chifundo anthu aŵiriwo, kuwasonyeza kwa ife monga zitsanzo zachikhulupiriro zoti titsanzire.—Ahebri 11:32; 12:1.
17. (a) Kodi ndi malingaliro otani amene angatithandize kupitirira zophophonya, kapena zolakwa, za ena? (b) Ngati tiyesetsa kuchita zimenezo, kodi tidzakhala tikum’tsanzira motani Yehova? (Onani mawu a m’tsinde.)
17 Inde, Yehova anatha ‘kupitirira’a zolakwa, monganso momwe Davide anam’pemphera mobwerezabwereza. (2 Samueli 12:13; 24:10) Kodi tingatsanzire Mulungu pazimenezi, kukhala wofunitsitsa kupitirira zimene atumiki anzathu, pokhala anthu opanda ungwiro, amatilakwira ngakhalenso chipongwe chimene amatichitira? Yerekezani kuti muli m’ndege imene ikuthamanga mumsewu wake kuti iyambe kuuluka. Mutasunzumira panja, mukuona mkazi, yemwenso ndi mnzanu pafupi ndi msewuwo akupanga gesichala yonyogodola. Mukudziŵa kuti anali wokhumudwa ndipo mwina gesichalayo akupangira inu. Komanso mwina sakupangira inu. Ndiye pamene ndegeyo iyamba kuuluka ndipo itembenuka m’mwamba, mukudutsa pamwamba pa mkaziyo, amene tsopano akungooneka ngati kadontho. Potha ola limodzi muli makilomita mazana ambiri kutali ndi iye, ndipo gesichala yake yonyogodolayo mwaisiya kutali kalekale. Mofananamo, nthaŵi zambiri zidzatithandiza kukhululuka ngati tiyesa kukhala ngati Yehova ndi kupitirira cholakwacho. (Miyambo 19:11) Kodi chipongwecho chidzaonekanso ngati nkhani patapita zaka khumi kuyambira lero kapena patapita zaka mazana aŵiri m’Zaka Chikwi? Bwanji osangochipitirira?
18. Ngati tikuona kuti tikulephera kukhululukira cholakwa cha winawake, kodi tingatsatire uphungu uti?
18 Koma mwina nthaŵi inayake munayesa kupemphera za nkhaniyo ndi kuyesa kukhululuka, koma mukuona kuti mukulephera. Kodi muyenera kutani tsopano? Yesu anati ndi bwino kupita kwa munthu winayo ndi kuyesa kuithetsa nkhaniyo kuti mukhazikitse mtendere. “Chifukwa chake ngati ulikupereka mtulo wako pa guwa la nsembe, ndipo pomwepo ukakumbukira kuti mbale wako ali ndi kanthu pa iwe, usiye pomwepo mtulo wako kuguwako, nuchoke, nuyambe kuyanjana ndi mbale wako, ndipo pamenepo idza nupereke mtulo wako.”—Mateyu 5:23, 24.
19. Ndi malingaliro otani amene tiyenera kukhala nawo ndiponso ndi malingaliro otani amene tiyenera kupeŵa pamene tikufuna kukhazikitsa mtendere ndi mbale wathu?
19 Chochititsa chidwi n’chakuti Yesu sananene kuti mupite kwa mbale wanu kukam’tsimikizira kuti inuyo simunalakwe koma kuti iyeyo ndiye wolakwa. Mwinadi anali wolakwa. Koma nonse aŵiri muyenera kuti munali olakwa m’njira ina. Mulimonse mmene zingakhalire, cholinga sichiyenera kukhala choti mupangitse winayo kuvomereza mlandu, kum’chititsa manyazi, titero kunena kwake. Ngati ndi mmene mukufunira kuchitira makambirano anu, zingakhale pafupifupi zotsimikizirika kuti zidzalephereka. Komanso cholinga sichiyenera kukhala kukalongosola mwatsatanetsatane kulakwa kwa winayo kumene anakuchitadi kapena kumene mukukuganizira. Pamene kukambirana moleza mtima kumeneko mumzimu wa chikondi chachikristu kusonyeza kuti kumvana molakwa n’kumene kunayambitsa vutolo, nonse aŵiri mungayese kuthetsa kumvana molakwa kumeneko. Kodi muyenera kulingalira kuti nthaŵi zonse m’pofunika kugwirizana pamfundo zonse pamene mukukambirana? Kodi sizingakhale bwino kwambiri malinga ngati mukuvomerezana kuti nonse aŵiri mukufunadi kutumikira Mulungu wathu wokhululukayo? Mutazindikira mfundo yofunika imeneyi, zidzakhala zosavuta kwa nonse aŵiri kunena mochokera pansi pa mtima kuti, “Pepani kuti chifukwa cha kupanda kwathu ungwiro tinasiyana maganizo. Chonde, tiyeni tiziiŵale.”
20. Kodi tingaphunzireponji pachitsanzo cha atumwi?
20 Kumbukirani kuti atumwi nawonso ankasiyana maganizo, monga pamene ena anafuna kukhala ndi ulemerero waukulu. (Marko 10:35-39; Luka 9:46; 22:24-26) Zimenezo zinayambitsa mavuto, mwinanso kupweteketsa ena mtima, kapena ngakhale kuwakhumudwitsa kwambiri. Koma anatha kupitirira kusiyana maganizo kumeneko ndi kupitirizabe kugwirira ntchito pamodzi. Mmodzi wa iwo anadzalemba kuti: “Iye wofuna kukonda moyo, ndi kuona masiku abwino, aletse lilime lake lisanene choipa, ndi milomo yake isalankhule chinyengo; ndipo apatuke pachoipa, nachite chabwino; afunefune mtendere ndi kuulondola.”—1 Petro 3:10, 11.
21. Yesu anapereka uphungu wofunika kwambiri wotani ponena za kukhululuka?
21 Poyambapo tinaona mbali imodzi ya chifukwa chokhululukira ena: Mulungu anatikhululukira machimo ambiri amene tinachita kumbuyoku, chotero tiyenera kum’tsanzira ndi kukhululukira abale athu. (Salmo 103:12; Yesaya 43:25) Koma chifukwa chimene tiyenera kukhululukira ena chimenechi chilinso ndi mbali ina. Atapereka chitsanzo cha pemphero, Yesu anati: “Ngati mukhululukira anthu zolakwa zawo adzakhululukira inunso Atate wanu wa Kumwamba.” Kuposa chaka chimodzi pambuyo pake, anatchulanso mfundo yaikuluyo pophunzitsa ophunzira ake kupemphera kuti: “Mutikhululukire ife machimo athu; pakuti ifenso tikhululukira munthu yense wa mangaŵa athu.” (Mateyu 6:12, 14; Luka 11:4) Kenako, kutatsala masiku ochepa kuti afe, Yesu anawonjezera kuti: “Pamene muimirira ndi kupemphera, khululukirani, ngati munthu wakulakwirani kanthu; kuti Atate wanunso ali Kumwamba akhululukire inu zolakwa zanu.”—Marko 11:25.
22, 23. Kodi kufunitsitsa kwathu kukhululuka kungakhudze motani tsogolo lathu?
22 Inde, chiyembekezo chathu cha kupitirizabe kukhululukidwa ndi Mulungu chimadalira kwambiri pa kufunitsitsa kwathu kukhululukira abale athu. Pakakhala vuto pakati pa Akristu, dzifunseni kuti, ‘Kodi kupeza chikhululukiro cha Mulungu sindiko kofunika kwambiri kuposa kuti nditsimikizire mbale kapena mlongo kuti anandichitira kanthu kena kachipongwe, kundilakwira pakanthu kena, kapena anasonyeza kupanda ungwiro kwa anthu?’ Yankho lake mukulidziŵa.
23 Komano bwanji ngati nkhaniyo ili yaikulu yoposa kungosiyana maganizo kapena vuto wamba? Nanga uphungu wa Yesu wolembedwa pa Mateyu 18:15-18 umagwira ntchito pankhani zotani? Tiyeni tidzakambirane mfundo zimenezi.
[Mawu a M’munsi]
a Katswiri wina ananena kuti phiphiritso lachihebrilo logwiritsidwa ntchito pa Mika 7:18 “linatengedwa pa zimene woyenda ulendo amachita pamene angodutsa molambalala chinthu chinachake chimene sakufuna kuchiyang’anitsitsa. Lingaliro limene phiphiritsolo likupereka si lakuti Mulungu saona tchimo, kapena kuti saliona ngati nkhani yaikulu, koma kuti saliyang’ana n’cholinga chopereka chilango; kuti sapereka chilango patchimolo, koma amalikhululukira.”—Oweruza 3:26; 1 Samueli 16:8.
Kodi Mukukumbukira?
◻ Kodi Yehova akutipatsa motani chitsanzo choti titsanzire ponena za kukhululuka?
◻ Kodi tiyenera kukumbukira chiyani ponena za anthu a mumpingo?
◻ Nthaŵi zambiri, kodi n’zotheka kuchita chiyani wina akatichitira chipongwe kapena kutilakwira?
◻ Ngati n’kofunika, kodi tingachitenji kuti tikhazikitse mtendere ndi mbale wathu?
[Chithunzi patsamba 15]
Pamene mwasiyana maganizo ndi Mkristu wina, yesani kuziiŵala; m’kupita kwa nthaŵi nkhaniyo sidzaonekanso ngati yaikulu