1 Samueli
16 Patapita nthawi, Yehova anauza Samueli kuti: “Kodi ulirira Sauli mpaka liti,+ munthu woti ine ndamukana kuti akhale mfumu ya Isiraeli?+ Thira mafuta mʼnyanga* yako+ ndipo unyamuke. Ndikutumiza kwa Jese+ wa ku Betelehemu, chifukwa ndasankha mmodzi wa ana ake aamuna kuti akhale mfumu yanga.”+ 2 Koma Samueli anati: “Ndipita bwanji? Sauli akamva andipha ndithu.”+ Atatero, Yehova anamuuza kuti: “Popita utenge ngʼombe yaikazi yaingʼono ndipo ukanene kuti, ‘Ndabwera kudzapereka nsembe kwa Yehova.’ 3 Ndiyeno ukaitanire Jese kopereka nsembeko, ndipo ine ndidzakuuza zochita. Ukandidzozere munthu amene ndidzakusonyeza.”+
4 Samueli anachita zimene Yehova anamuuza. Atafika ku Betelehemu,+ akulu a mzindawo anayamba kunjenjemera atakumana naye ndipo anamufunsa kuti: “Kodi nʼkwabwino?” 5 Iye anayankha kuti: “Inde, nʼkwabwino. Ndabwera kudzapereka nsembe kwa Yehova. Dziyeretseni, ndipo tipite limodzi kopereka nsembe.” Kenako iye anayeretsa Jese ndi ana ake ndipo anawaitanira kopereka nsembe. 6 Pamene iwo ankalowa, Samueli anaona Eliyabu+ ndipo anati: “Sindikukayikira, Yehova wasankha ameneyu.”* 7 Koma Yehova anauza Samueli kuti: “Usaganizire mmene akuonekera komanso kutalika kwake+ chifukwa ine ndamukana ameneyu. Chifukwatu mmene munthu amaonera si mmene Mulungu amaonera. Munthu amaona zooneka ndi maso, koma Yehova amaona mumtima.”+ 8 Kenako Jese anaitana Abinadabu+ kuti Samueli amuone, koma Samueli anati: “Yehova sanasankhenso ameneyu.” 9 Kenako Jese anaitana Shama,+ koma Samueli anati: “Ameneyunso Yehova sanamusankhe.” 10 Choncho Jese anaitana ana ake 7 kuti Samueli awaone. Koma Samueli anauza Jese kuti: “Yehova sanasankhe aliyense wa amenewa.”
11 Kenako Samueli anafunsa Jese kuti: “Kodi anyamata anu onse ndi omwewa basi?” Iye anayankha kuti: “Wamngʼono kwambiri+ wachokapo. Wapita koweta nkhosa.”+ Zitatero Samueli anauza Jese kuti: “Tumizani munthu akamutenge, chifukwa sitikhala pansi kuti tidye mpaka iye atabwera.” 12 Iye anatumadi munthu kukamʼtenga. Mnyamatayo anali wa maso okongola ndiponso wooneka bwino.+ Ndiyeno Yehova anati: “Ndi ameneyu! Nyamuka umudzoze.”+ 13 Samueli anatenga nyanga ya mafuta+ nʼkumudzoza azichimwene ake akuona. Kuyambira tsiku limenelo, mzimu wa Yehova unayamba kuthandiza Davide.+ Kenako Samueli anabwerera ku Rama.+
14 Ndiyeno mzimu wa Yehova unamʼchokera Sauli,+ ndipo Yehova analola kuti maganizo oipa* azimuvutitsa Sauli.+ 15 Atumiki a Sauli anamuuza kuti: “Tikuona kuti mzimu woipa wochokera kwa Mulungu ukukuvutitsani. 16 Mbuye wathu, uzani atumiki anu kuti akupezereni katswiri woimba zeze.+ Mzimu woipa wochokera kwa Mulungu ukakubwererani, iye azikuimbirani zeze ndipo inu muzimva bwino.” 17 Choncho Sauli anauza atumiki ake kuti: “Ndipezereni munthu wodziwa kuimba, ndipo mubwere naye kuno.”
18 Mmodzi wa atumikiwo ananena kuti: “Ine ndinaona mwana wa Jese wa ku Betelehemu akuimba, ndipo amaimba mwaluso. Iye ndi mwamuna wolimba mtima ndiponso msilikali wamphamvu.+ Ndiwodziwa kulankhula, wooneka bwino+ komanso Yehova ali naye.”+ 19 Sauli atamva zimenezi, anatumiza uthenga kwa Jese wakuti: “Nditumizire mwana wako Davide amene amaweta nkhosa.”+ 20 Choncho Jese anatenga mkate, thumba lachikopa la vinyo ndi mwana wa mbuzi nʼkuziika pa bulu kuti mwana wake Davide apite nazo kwa Sauli. 21 Davide anapita kwa Sauli nʼkuyamba kumutumikira.+ Sauli anamʼkonda kwambiri Davide, moti anakhala womunyamulira zida. 22 Zitatero, Sauli anatumiza uthenga kwa Jese, wakuti: “Ndikupempha kuti Davide apitirize kunditumikira chifukwa ndamʼkonda.” 23 Ndiyeno maganizo oipa* akamubwerera Sauli, Davide ankatenga zeze nʼkumuimbira. Akatero, Sauli ankamva bwino ndipo maganizo oipawo ankamuchokera.+