Kodi ndi Mapemphero Andani Amene Amayankhidwa?
“ZINTHU zambiri zimaikidwa mpemphero kuposa ndi mmene dziko limalingalira.” Adatero wolemba ndakatulo Wachingelezi wa m’zaka za zana la 19 Alfred Tennyson. Koma ambiri apemphera mwachabe kaamba ka thanzi laumoyo, chimwemwe, mtendere, ndi chitukuko. Ndithudi, ena amalingalira kuti Mulungu samamvetsera kwenikweni ku mapemphero. Komabe, Baibulo limamutcha iye “Wakumva pemphero.”—Salmo 65:2.
Ichi chingakupangitseni kufunsa kuti: ‘Kodi “Wakumva pemphero” ameneyu ndani? Kodi tiyenera kufikira ziyeneretso zapadera kuti mapemphero athu amvedwe? Kodi tiyenera kupemphera motani? Ndipo kodi ndi mapemphero andani amene amayankhidwa?’
Mapemphero Awo Anamvedwa
Pemphero n’lakale mofanana ndi mtundu wa anthu. Lingalirani Abele, mwana wamwamuna wa makolo athu oyambirira, Adamu ndi Hava. Pamene anapereka nsembe yolandirika kwa Mulungu, mosakaikira iyo inatsagana ndi mawu a pembedzero ndi chitamando.—Genesis 4:1-5.
M’zaka za zana lachisanu ndi chinayi Nyengo yathu Ino isanafike, Yona mneneri wa Mulungu “anapemphera kwa Yehova Mulungu wake ali m’mimba mwa nsombayo” imene inaikidwiratu kum’meza iye. Kodi pemphero limenelo linali logwira ntchito? Inde, popeza kuti “pamenepo Yehova analankhula ndi nsombayo, ndipo inam’sanzira Yona kumtunda.” Chotero Yona anapitiriza kukwaniritsa ntchito yake yopatsidwa ndi Mulungu kupita ku Nineve.—Yona 1:17; 2:1, 10; 3:1-5.
Pamene Davide wa Israyeli wakale anazingidwa ndi adani ake, anafuula kuti: “Imvani pemphero langa, Yehova; ndicherere khutu kupempha kwanga; ndiyankheni mwa chikhulupiriko chanu, mwa chilungamo chanu.” (Salmo 143:1) Mapemphero a Davide a kupulumutsidwa anayankhidwa, popeza kuti adani ake sanapambane konse m’kumupha iye. Chotero, iye anakhoza kunena kuti: “Yehova ali pafupi ndi onse akuitanira kwa iye, onse akuitanira kwa iye m’chowonadi.”—Salmo 145:18.
Kuzifikira Ziyeneretso Zazikulu
Chotero pamenepa, mapemphero a atumiki a Mulungu a nthaŵi zakale anayankhidwa. Ndithudi, iwo sanangopemphera monga mwambo kwa Mulungu wopanda dzina. Iwo anapemphera mwachikhulupiriro mwa Yehova, “Wam’mwambamwamba pa dziko lonse lapansi.” (Salmo 83:18) Chotero, kuti mapemphero athu akhale ogwira ntchito, ndi ziyeneretso zazikulu zotani zimene tiyenera kuzifikira?
Pempherani kokha kwa Yehova. M’chenicheni—kuli kopanda pake, kopanda malemba—kupemphera kwa milungu yonyenga, imene mafano awo opanda moyo ali ndi milomo yosalankhula, makutu ogontha, manja osagwira, mapazi osayenda, ndi mimero yosalankhula. (Salmo 115:5-7; 1 Yohane 5:21) Mosiyana ndi milungu yopanda pake yoteroyo, Yehova amachitapo kanthu mokomera awo omwe amkonda ndi ku’mtumikira. Mwachitsanzo, zaka mazana mazana zapitazo aneneri a mulungu wonyenga Bala anapemphera kwa iye kuti agwetse moto kuchokera kumwamba. Ngakhale kuti iwo anapemphera kuchokera m’mawa mpaka madzulo, Bala sanakhoze kuyankha. Kenaka Eliya anapempha Yehova, yemwe anayankha mwa kutumiza moto umene unatentha kotheratu nsembe yoikidwa pa guwa.—1 Mafumu, mutu 18.
Fikirani Mulungu kupyolera mwa Yesu Kristu yekha. Yehova Mulungu anatumiza Mwana wake wobadwa yekha, Yesu Kristu, kudziko lapansi kudzatumikira monga dipo kuwombola mtundu wa anthu ku uchimo ndi imfa. (Yohane 3:16, 36; Aroma 5:12; 6:23) Chotero, kwa awo odzipereka ku makonzedwe amenewa, Mulungu anatsegula njira yatsopano yomufikira m’pemphero. Atumiki oyambirira a Mulungu oterowo onga wamasalmo Davide anapemphera mwachindunji kwa Yehova. (Salmo 4:1; 17:1; 55:1; 102:1) Koma kafikidwe katsopano kanali kupyolera mwa Yesu, yemwe anati: “Palibe munthu adza kwa Atate, koma mwa ine. Ngati mudzapempha kanthu m’dzina langa, ndidzachita.” (Yohane 14:6, 14) Palibe kulikonse kumene Malemba amapereka lingaliro lakuti mapemphero ayenera kuperekedwa kwa Mulungu kupyolera mwa wina aliyense.
Chotero, titaphunzira kuti tiyenera kupemphera kwa Mulungu m’dzina la Yesu, mapemphero athu sakayankhidwa pokhapo titapemphera kokha kwa Yehova kupyolera mwa Mwana wake. Koma palinso zifukwa zina zimene Yehova samayankhira mapemphero ambiri.
Chifukwa Chake Mulungu Samayankha
Mulungu sadzayankha mapemphero athu kokha chifukwa chakuti timatsatira kakhalidwe ka thupi kapadera pamene tikupemphera. Malemba samafuna kuti tipemphere kokha m’kaimidwe kamodzi ka thupi. Ndithudi, kugwada kungasonyeze kudzichepetsa pamaso pa Mulungu. Komabe n’kololedwa kupemphera pamene tiri oyimirira, okhala pa thebulo, tikupuma m’kama, kapena pochita ntchito za tsiku ndi tsiku. (Danieli 6:10, 11; Marko 11:25) Nkulekeranji, Yehova amayankha ngakhale mapemphero a kachetechete! Asanawuze mfumu ya ku Perisiya kuti anafuna kukamanganso malinga ogwetsedwa a Yerusalemu, Nehemiya “anapemphera [mwa kachetechete kwa] Mulungu wa Kumwamba,” ndipo Yehova anayankha pemphero limenelo. (Nehemiya 2:1-6) Chotero ngati kaimidwe ka thupi sindikodi chinthu chofunika, nanga nchifukwa ninji mapemphero ambiri chotero samayankhidwa ndi Mulungu?
Yehova samakondwera ndi mapemphero a oipa. Inde, “wopewetsa khutu lake kuti asamve chilamulo, ngakhale pemphero lake linyansa.” (Miyambo 28:9) Kupyolera mwa mneneri Yesaya, Mulungu anawuza anthu Ake opatuka kuti: “Ndipo pamene mutambasula manja anu, ndidzakubisirani inu maso anga; inde pochulukitsa mapemphero anu ine sindidzamva; manja anu adzala mwazi.” (Yesaya 1:15) Mwachibadwa, mapemphero a oipa samayankhidwa ngakhale ataperekedwa kwa Mulungu kupyolera mwa Kristu.
Mulungu samayankha mapemphero achinyengo. “Ndipo pamene mupemphera,” anatero Yesu Kristu, “musakhale monga onyengawo; chifukwa iwo akonda kuimirira ndi kupemphera m’masunagoge, ndi pa mphambano za makwalala, kuti aonekere kwa anthu. Indetu ndinena kwa inu, Iwo alandiriratu mphotho zawo.” Yesu anawonjezera kuti: “Koma iwe popemphera, loŵa m’chipinda chako, nutseke chitseko chako, nupemphere Atate wako ali m’tseri, ndipo Atate wako wakuwona m’tseri adzakubwezera iwe.” (Mateyu 6:5, 6) Mwa kunena zimenezi, Yesu sanatsutse mapemphero onse apoyera, popeza kuti iyemwini anapemphera momvekera pamaso pa ena. (Mateyu 14:19) Koma Kristu anali kusonyeza kuti n’kulakwa kupemphera poyera ndi cholinga chongofuna kuwonedwa ndi kumvedwa ndi ena ndi kulandira chitamando chawo.
Yehova samayankha mapemphero obwerezabwereza, osawona mtima. Yesu ananena kuti: “Ndipo popemphera musabwerezebwereze chabe iai, monga amachita anthu akunja, chifukwa ayesa kuti adzamvedwa ndi kulankhulalankhula kwawo. Chifukwa chake inu musafanane nawo: Pakuti [Mulungu, NW] Atate wanu adziŵa zomwe mudzisowa, inu musanayambe kupempha iye.” (Mateyu 6:7, 8) Ambiri m’maiko Akum’mawa amaganiza kuti nthaŵi iriyonse pamene azungulitsa wilo yamapemphero (chidiramu momwe amaika mapemphero olembedwa), mapemphowo amabwerezedwa. Mamiliyoni ena amagwiritsira ntchito Kolona kapena kuloŵeza mapemphero kuchokera m’mabuku. Koma awo ofuna kumvedwa ndi Mulungu adzapewa mapemphero obwerezabwereza ndipo adzapereka chisamaliro ku malangizo owonjezereka a Yesu.
“Pempherani . . . Chomwechi”
Chotsatira Yesu anapereka limene ambiri amalitcha pemphero lachitsanzo. (Mateyu 6:9-13) Iye adati: “Chifukwa chake pempherani inu chomwechi: Atate wathu wa Kumwamba, dzina lanu liyeretsedwe.” Kuitana Mulungu kuti “Atate wathu” kumasonyeza kuti ena nawonso ali ndi unansi wathithithi ndi iye monga mbali ya banja la alambiri ake. Kuyeretsedwa kwa dzina la Mulungu, Yehova, nkofunika koposa, koma kodi ndimotani mmene iye adzaliyeretsera ilo? Mwa kuchotsapo oipa, iye adzachotsa chitonzo chonse chowunjikidwa pa dzinalo.—Ezekieli 38:23.
“Ufumu wanu udze. Kufuna kwanu kuchitidwe, monga kumwamba chomwecho pansi pano,” adawonjezera tero Yesu. Ulamuliro wa Mulungu monga wasonyezedwera mu Ufumu wakumwamba Waumesiya wa Mwana wake udzabwera posachedwapa molimbana ndi otsutsa onse a ulamuliro waumulungu, kuwachotsa iwo pa dziko lapansi. (Danieli 2:44) Koma kodi chitanthauzanji pamene timapempha kuti kufuna kwa Mulungu kuchitidwe pa dziko lapansi monga kumwamba? Iri liri pempho lakuti Yehova achite zifuno zake padziko lapansi, kuphatikizapo kuchotsedwa kwa otsutsa ake.—Chibvumbulutso 16:14-16; 19:11-21.
Ataika Mulungu, kuyeretsedwa Kwake, ndi zifuno Zake m’malo oyamba m’pemphero lachitsanzo, Yesu anapitiriza kuti: “Mutipatse ife lero chakudya chathu chalero.” Kumpempha Yehova kupereka zofunikira ‘zalero’ kumachirikiza chikhulupiriro m’mphamvu yake ya kusamalira zosoŵa za tsiku ndi tsiku za alambiri ake. Limeneli sirili pempho ladyera lofuna zopereka zopambanitsa.
Yesu anawonjezera kuti: “Ndipo mutikhululukire mangawa athu, monga ifenso takhululukira amangawa athu.” (Luka 11:4 imasonyeza kuti “mangawa” amenewa ali “machimo.”) Ife tingapeze chikhululukiro kuchokera kwa Mulungu kokha titakhululukira awo otichimwira. (Mateyu 6:14, 15) Pamenepa, moyenerera, mtumwi Paulo ananena kuti: “Monganso [Yehova] anakhululukira inu, teroni inunso.”—Akolose 3:13.
Kumaliza pemphero lachitsanzolo, Yesu adanena kuti: “Ndipo musatitengere kokatiyesa, koma mutipulumutse kwa woipayo.” Yehova samayesa anthu “ndi zoipa.” (Yakobo 1:13) Kuyesa kumachokera kwa woipayo, Satana Mdyerekezi, koma Baibulo nthaŵi zina limanena kuti kulola kwa Mulungu zinthu zina kumafikira pa mlingo wa kuzichita iyemwini. (Rute 1:20, 21; Mlaliki 7:13) Kuyankha pempho lakuti, “musatitengere kokatiyesa,” Yehova samasiya atumiki ake okhulupirika, ngakhale kuti amawalola iwo kuyesedwa. Ndithudi, “Mulungu ali wokhulupirika, amene sadzalola inu kuyesedwa koposa kumene mukhoza; koma pamodzi ndi chiyeso adzaikanso populumukirapo, kuti mudzakhoze kupirirako.”—1 Akorinto 10:13.
Pamene tipempha kupulumutsidwa kwa woipayo, tikupempha kuti Mdyerekeziyo asaloledwe kutilaka monga alambiri a Yehova okhulupirika. Ngati ndife atumiki okhulupirika a Mulungu, tingakhale achidaliro kuti iye adzayankha pempho loterolo, popeza kuti mtumwi Petro analemba kuti: “[Yehova] adziŵa kupulumutsa opembedza poyesedwa iwo.” (2 Petro 2:9) Ndipo njofunika chotani nanga mbali iyi ya pemphero lachitsanzolo, popeza kuti Satana Mdyerekezi “monga mkango wobuma, ayendayenda ndi kufunafuna wina akamlikwire”!—1 Petro 5:8.
Chifukwa Chake Mapemphero Awo Amayankhidwa
Mulungu amayankha mapemphero a alambiri ake okhulupirika. Chifukwa ninji? Kumbali ina, Yehova amatero chifukwa chakuti iwo amapemphera kwa iye yekha, kumfikira iye kupyolera mwa Yesu Kristu. Iwo amada choipa ndi kupeŵa mapemphero achinyengo ndi obwerezabwereza. M’malo mwakungobwereza pemphero lachitsanzolo mwa kuliloŵeza, Mboni za Yehova zimagwiritsira ntchito zitsogozo zake zabwinozo kulongosola kwa Mulungu malingaliro awo a kumtima. Komabe pali zifukwa zinanso zimene mapemphero awo amayankhidwira.
Awo amene mapemphero awo ayankhidwa adazifikira ziyeneretso zazikulu. Kusonyeza zimenezi, Paulo adalemba kuti: “Pakuti iye wakudza kwa Mulungu ayenera kukhulupirira kuti alipo, ndi kuti ali wobwezera mphotho iwo akumfuna iye.” (Ahebri 11:6) Onani mfundo zazikulu ziŵiri izi: Yehova amayankha mapemphero a (1) awo amene amakhulupirira kuti Mulungu ndiyedi, kapena aliko, ndi (2) awo ‘om’funafuna iye mowona mtima.’
Munthu mmodzi wa m’zaka za zana loyamba woteroyo anali Wakunja Korneliyo wokhulupirika. Iye anakhulupirira kuti Mulungu alikodi, ndipo anali kumfunafuna iye mowona mtima. Kodi nchiyani chimene Korneliyo anachita atapeza chidziŵitso cholongosoka? Nkulekeranji, iye anadzipereka kwa Yehova Mulungu mwa mtima wonse ndipo anabatizidwa kuchitira chizindikiro kudziperekako. Pambuyo pake, Korneliyo mwachiwonekere anali ndi unansi wathithithi ndi Mulungu, ndipo zimenezi ziyenera kukhala zidali ndi chiyambukiro chabwino pa mapemphero ake.—Machitidwe 10:1-44.
Korneliyo asanabatizidwe, mapemphero ake ‘anakwera nakhala chikumbutso pamaso pa Mulungu.’ (Machitidwe 10:4) Komabe, mwa kudzipereka kwa Mulungu pa maziko a kukhulupirira kwake mu nsembe ya dipo ya Yesu, ndi kubatizidwa, Korneliyo anadzipereka mosasiyako kwa Yehova. Izi zinakhazikitsa kuyandikana kwabwino kwenikweni pakati pa Mulungu ndi munthu wokhulupirika ameneyu—unansi umene unapatsa Korneliyo mwaŵi wopanda polekezera wa pemphero. (Yakobo 4:8) Iye akafikira Atate wake wakumwamba kupyolera mwa Yesu Kristu ndi chiyembekezo cha kumvedwa. Ndicho chimene chimachitika kwa onse odzipereka kwa Mulungu kupyolera mwa Kristu nabatizidwa. Iwo nawonso ali ndi mwaŵi wopanda polekezera wa pemphero.
Motsimikizirika, inu mufunadi kuti mapemphero anu adziyankhidwa. Chotero, ngati tsopano simum’tumikira Yehova monga mmodzi wa alambiri ake odzipereka, n’kwanzeru chotani nanga kumfunafuna iye mowona mtima! Tsatirani njira yofanana ndi ija ya Korneliyo, ndipo Mulungu adzayankha mapemphero anu.
[Chithunzi patsamba 6]
Kodi ndimotani mmene mapemphero a Korneliyo anayambukiridwira ndi kudzipereka ndi ubatizo wake kwa Mulungu?