Chivumbulutso Chimene Yohane Analandira
16 Kenako ndinamva mawu ofuula kuchokera mʼmalo opatulika+ akuuza angelo 7 aja kuti: “Pitani, kathireni mbale 7 za mkwiyo wa Mulunguzo padziko lapansi.”+
2 Mngelo woyamba anapita nʼkukathira mbale yake padziko lapansi.+ Atatero, anthu amene anali ndi chizindikiro cha chilombo+ komanso amene ankalambira chifaniziro chake,+ anagwidwa ndi mliri wa zilonda zopweteka+ komanso zoopsa.
3 Mngelo wachiwiri anathira mbale yake mʼnyanja.+ Nyanjayo inasanduka magazi+ ngati a munthu wakufa, moti chamoyo chilichonse mʼnyanjamo chinafa.+
4 Mngelo wachitatu anathira mbale yake pamitsinje ndi pa akasupe amadzi+ ndipo zonse zinasanduka magazi.+ 5 Ndiye ndinamva mngelo amene ali ndi ulamuliro pa madzi akunena kuti: “Inu Mulungu amene mulipo ndi amene munalipo,+ inu Wokhulupirika,+ ndinu wolungama chifukwa mwapereka ziweruzo zimenezi,+ 6 chifukwa iwo anakhetsa magazi a oyera ndi a aneneri+ ndipo inu mwawapatsa magazi kuti amwe.+ Iwo akuyeneradi kulandira chiweruzo chimenechi.”+ 7 Kenako ndinamva guwa lansembe likunena kuti: “Inde, Yehova* Mulungu, inu Wamphamvuyonse,+ ziweruzo* zanu ndi zoona komanso zolungama.”+
8 Mngelo wa 4 anathira mbale yake padzuwa+ ndipo dzuwalo linaloledwa kuwotcha anthu ndi moto. 9 Anthu anapsa ndi kutentha kwakukulu. Koma iwo ananyoza dzina la Mulungu, amene ali ndi ulamuliro pa miliri imeneyi ndipo sanalape nʼkumupatsa ulemerero.
10 Mngelo wa 5 anathira mbale yake pampando wachifumu wa chilombo. Ufumu wa chilombocho unachita mdima+ ndipo anthu anayamba kudziluma malilime chifukwa cha ululu. 11 Koma iwo ananyoza Mulungu wakumwamba chifukwa cha ululu umene ankamva komanso chifukwa cha zilonda zawo ndipo sanalape ntchito zawo.
12 Mngelo wa 6 anathira mbale yake pamtsinje waukulu wa Firate+ ndipo madzi ake anauma,+ kuti njira ya mafumu+ ochokera kotulukira dzuwa* ikonzedwe.
13 Kenako ndinaona mauthenga atatu onyansa ouziridwa,* amene ankaoneka ngati achule. Mauthengawo ankatuluka mʼkamwa mwa chinjoka,+ mʼkamwa mwa chilombo ndi mʼkamwa mwa mneneri wabodza. 14 Kwenikweni amenewa ndi mauthenga ouziridwa ndi ziwanda ndipo amachita zizindikiro.+ Mauthengawo akupita kwa mafumu a dziko lonse lapansi kumene kuli anthu, kuti awasonkhanitse pamodzi kunkhondo+ ya tsiku lalikulu la Mulungu Wamphamvuyonse.+
15 “Taona! Ndikubwera ngati wakuba.+ Wosangalala ndi amene akukhalabe maso+ ndiponso amene wavalabe malaya ake akunja, kuti asayende wosavala anthu nʼkuona maliseche ake.”+
16 Ndipo anawasonkhanitsa pamodzi, kumalo amene mʼChiheberi amatchulidwa kuti Aramagedo.*+
17 Mngelo wa 7 anakhuthulira mbale yake pampweya. Atatero, kunamveka mawu ofuula kuchokera mʼmalo opatulika,+ kuchokera kumpando wachifumu, akuti: “Zachitika!” 18 Ndiyeno kunachita mphezi, kunamveka mawu, kunagunda mabingu komanso kunachita chivomerezi chachikulu chimene sichinachitikepo kuyambira pamene munthu analengedwa padziko lapansi.+ Chivomerezicho chinali champhamvu kwambiri komanso chachikulu. 19 Mzinda waukulu+ unagawika zigawo zitatu ndipo mizinda ya mitundu ya anthu inagwa. Ndiyeno Mulungu anakumbukira Babulo Wamkulu,+ kuti amupatse kapu imene inali ndi vinyo wa mkwiyo wake waukulu.+ 20 Komanso chilumba chilichonse chinamira ndipo mapiri sanapezeke.+ 21 Kenako matalala aakulu, lililonse lolemera pafupifupi makilogalamu 20,* anagwera anthu kuchokera kumwamba.+ Anthuwo ananyoza Mulungu chifukwa cha mliri wa matalalawo,+ chifukwa mliriwo unali waukulu modabwitsa.