Lankhulani Ponena za Ulemerero wa Ufumu wa Mulungu
“Adzanenera ulemerero wa ufumu wanu, adzalankhulira mphamvu yanu.”—MASALMO 145:11.
1. Kwenikweni, nchifukwa ninji Yehova anatipatsa ife kulankhula?
YEHOVA anali ndi chifuno m’kutipatsa ife kulankhula. (Eksodo 4:11) Makamaka, chinali chakuti milomo yathu “itulutse chilemekezo” kwa iye. (Masalmo 119:171, 172) Monga mmene wamasalmo Davide ananenera: “Ntchito zanu zonse zidzakuyamikani, Yehova, ndi okondedwa anu adzakulemekezani. Adzanenera ulemerero wa ufumu wanu, adzalankhulira mphamvu yanu; kudziŵitsa ana a anthu zamphamvu zake, ndi ulemerero waukulu wa ufumu wake. Ufumu wanu ndiwo ufumu wonka muyaya, ndi kuweruza kwanu kufikira mibadwo yonse yonse.”—Masalmo 145:10-13.
2. Tiri ofulumizidwa “kutulutsa chilemekezo” kwa Mulungu m’njira ziti?
2 Atsatiri odzozedwa a Yesu Kristu ndi anzawo a “khamu lalikulu” ali ofunitsitsa kulemekeza Yehova, “Mfumu ya muyaya.” (Chivumbulutso 7:9; 15:3) Kupyolera mu phunziro losamalitsa la Baibulo ndi Nsanja ya Olonda ndi zofalitsidwa zina za Chikristu monga zothandizira, tingapeze chidziŵitso cholongosoka ponena za Mulungu kuti ali ngati mtsinje wa madzi oyera, wopatsa mpumulo, wopatsa moyo. Chotero, ku mbali yathu ‘kasupe wa moyo amakhala mtsinje wodzala.’ (Miyambo 18:4) Ife timafulumizidwa “kutulutsa chilemekezo” mu kuchitira umboni wa kunyumba ndi nyumba ndi mitundu ina ya utumiki wa m’munda. Koma palinso chifukwa cha m’Malemba cha kuchitira umboni wa mwamwaŵi.
Zochitika za m’Malemba
3. Chonde tchulani zitsanzo za umboni wa mwamwaŵi kumbali ya Yesu Kristu.
3 Ulaliki woyamba umene Yesu anachita pambuyo pa kudzozedwa ndi mzimu woyera unali pamalo ake ogona, kumene anaitana Yohane, Andreya, ndipo mwachiwonekere Petro. Iwo anathera tsikulo kumeneko, mwachiwonekere kulandira umboni mwa makhazikitsidwe a mwamwaŵi amenewo. (Yohane 1:35-42) Panalinso pansi pa makhalidwe a mwamwaŵi—“pamene anali kupita”—kuti Yesu anawona Mateyu pa ofesi ya a msonkho ndi kupeza zotulukapo zabwino pamene Iye ananena kuti: “Khala wonditsata.”—Mateyu 9:9.
4. Nchiyani chimene Yesu ananena pamene anachitira umboni kwa mkazi wa chiSamariya, ndipo ichi chinatsogolera ku chiyani?
4 Yesu anali chitsanzo chabwino koposa cha ‘mtsinje wanzeru zotumphuka.’ Ngakhale kuti anakhala wa njala ndi wotopa pa chitsime cha Yakobo pafupi ndi Sukari, iye anachitira umboni kwa mkazi wa chiSamariya yemwe anabwera kudzatunga madzi. “Iye wakumwa madzi amene ndidzampatsa sadzamva ludzu nthaŵi zonse,” Yesu anatero, “koma madzi amene ndidzampatsa adzakhala mwa iye kasupe wa madzi otumphukira ku moyo wosatha.” Kuchitira umboni kwa mwamwaŵi kumeneko kunatsogolera kulalikira kwa Yesu kwa gulu limene mkaziyo analikoka kubwera limodzi naye ndi kumva zimene iye ananena.—Yohane 4:6-42.
5. Mlaliki Filipo ndi mtumwi Paulo anapereka zitsanzo zotani za umboni wa mwamwaŵi?
5 Filipo mlaliki anaimitsa gareta lodutsa ndi kuchitira umboni wa mwamwaŵi kwa mwiniwake, amene anali kuŵerenga ulosi wa Yesaya. Ataitanidwa kukwera m’garetayo, Filipo analongosola “mbiri yabwino yonena za Yesu” kwa mdindo wa ku Aitiopiya ameneyo, amene chivomerezo chake choyamikira chinatulukamo mu ubatizo wake. (Machitidwe 8:26-38) Pamene zingwe za ndende za mtumwi Paulo zinamasulidwa ndi chivomezi chachikulu mu Filipi, iye anachitira umboni mwamwaŵi kwa osunga ndende. Chotulukapo chake? “Pomwepo, iye ndi apabanja pake anabatizidwa mosachedwetsa.”—Machitidwe 16:19-34.
6. Umboni wa mwamwaŵi moyenera unachita mbali yotani m’ntchito za ophunzira a Yesu pambuyo pa kuponyedwa miyala kwa Stefano?
6 Lerolino, kuchitira umboni mwamwaŵi iri njira imodzi ya kulengezera mbiri yabwino kumene ntchito yathu ya Chikristu iri pansi pa ziletso. Ngakhale kuti tikuzunzika, komabe, mitima yathu imatifulumiza ife kulankhula ponena za ulemerero wa ufumu wa Mulungu. Pambuyo pa kuphedwa ndi miyala kwa Stefano, ambiri a ophunzira ozunzidwawo anabalalitsidwa. Komabe, anapitirizabe kulalikira mbiri yabwino, ndipo mosakaikira kuchitira umboni mwamwaŵi kunaphatikizidwamo m’zoyesayesa zawo za kulalikira Ufumu.—Machitidwe 8:4-8; 11:19-21.
7. Pamene anabindikiritsidwa, nchiyani chimene Paulo anachita, ichi chinadzutsa funso lotani?
7 Kuchitira umboni mwamwaŵi iri njira imodzi ya kulankhula ponena za ulemerero wa ufumu wa Mulungu ngati tiri m’ndende kapena tiri otsekeredwa kunyumba zathu chifukwa cha matenda kapena kupunduka. Paulo anabindikiritsidwa kwa zaka ziŵiri pansi pa woyang’anira wa Aroma. Koma m’malo mothaŵa, iye anatumiza kaamba ka khamu ndipo “analandira onse akufika kwa iye, kulalikira Ufumu wa Mulungu, ndi kuphunzitsa kaamba ka Ambuye Yesu Kristu ndi kulimbikitsa konse, wosamuletsa munthu.” (Machitidwe 28:16-31) Ndi chitsanzo chabwino chotani nanga! Ngati inu muli mboni yotsekeredwa ya Yehova, kodi mungachite chinachake chofanana nacho?
8. Kodi umboni wa mwamwaŵi wa Paulo unali wokhutiritsa motani?
8 Pamene olindira a Paulo anasintha kwa nthaŵi ndi nthaŵi, osiyanasiyana anamumva iye akulankhula kwa ena ponena za ulemerero wa ufumu wa Mulungu. Tingakhale otsimikizira, ngakhale kuli tero, kuti iye anachitiranso umboni mwachindunji kwa olindira amenewo. Umboni wa mwamwaŵi umenewo unali wokhutiritsa kotero kuti Paulo analemba kuti: “Zija za kwa ine zidachita makamaka kuthandizira uthenga wabwino; kotero kuti zomangira zanga zinawonekera mwa Kristu m’bwalo lonse la alonda, ndi kwa onse ena; ndi kuti unyinji wa abale mwa Ambuye, pokhulupirira m’zomangira zanga, alimbika mtima koposa kulankhula mawu a Mulungu opanda mantha.” (Afilipi 1:12-14) Monga Paulo, ngati tidzaikidwa m’ndende ndi kumanidwa mwaŵi wa umboni wa nthaŵi zonse, tingalankhulebe ponena za ufumu wa Mulungu. Ndipo ndi chilimbikitso chotani nanga chimene ichi chidzaika mwa abale athu!
9, 10. Ndi chitsimikiziro cha kudziko chotani chimene chiripo chakuti Akristu oyambirira anachitira umboni mwamwaŵi?
9 Kuchitira umboni wa mwamwaŵi kunali kofala pakati pa Akristu oyambirira chakuti ngakhale mu zaka zotsatirapo chikananenedwa kuti: “Kuchokera kwa mlembi wa Chikristu, mwinamwake mu Carthage chifupifupi 200, timapeza chithunzithunzi . . . [chimene] chimakhudza anthu omwe anali ophunzira koposa. Maloya atatu achichepere, mabwenzi athithithi, anathera tchuthi cha tsiku limodzi m’mphepete mwa nyanja. Aŵiri ali Akristu, wachitatu ndi wakunja. Nkhani yawo kenaka inatembenukira ku chipembedzo . . . Mbiri ya kukangana kwakutali itha, ‘Tinapita kunyumba achimwemwe, tonse atatu. Mmodzi anali wachimwemwe chifukwa chakuti anafika ku chikhulupiriro cha Chikristu, ndipo enawo chifukwa anamtsogoza iye ku icho.’ Zolembedwazo sizikunyengezera kukhala mbiri yeniyeni; izo ziri chodzikhululukira cha Minucius Felix. Koma chikuimira mtundu wa chinthu chomwe chinachitika pakati pa anthu okhala ndi mwaŵi wokulira.” (Church History 1—The First Advance: AD 29—500, yolembedwa ndi John Foster, masamba 46, 48) Inde, ndipo mbiri imeneyo ikusonyeza kuti umboni wa mwamwaŵi sunafe pakati pa wodzinenera kukhala Akristu a m’nthaŵi imeneyo.
10 Poneza za Akristu oyambirira, chanenedwanso kuti: “Kunali kokha chiŵerengero chokhazikika chomakulakulabe cha akhulupiriri Achikristu, amene, kulikonse kumene anapita, kaya ku malo awo a nthaŵi zonse a malonda kapena kuperekedwako ndi chizunzo, analalikira Kristu . . . Za awo amene anapanga malonda awo, ntchito yawo, ntchito yawo ya tsiku ndi tsiku, kapena mtundu uliwonse, njira ya kufutukulira chikhulupiriro chawo, panali khamu lalikulu.” (The Missionary Enterprise, yolembedwa ndi Edwin Munsell Bliss, tsamba 14) Inde, olengeza Ufumu oyambirira anachitira umboni mwa nthaŵi zonse ndi mwamwaŵi.
Kulingalira Pasadakhale ndi Kukonzekera
11. Nchiyani chimene tingaphunzire kuchokera kwa Yesu ponena za kulunjikitsa chidwi pa chowonadi cha Mulungu?
11 Mofanana ndi Yesu ndi atsatiri ake oyambirira, tiyenera kuchitira umboni ponse paŵiri mwa nthaŵi zonse ndi mwamwaŵi. Kuchita tero mokhutiritsa kumafunikira kulingalira kwa pasadakhale ndi kukonzekera. Kuchitira umboni mwamwaŵi kapena kupereka langizo, Yesu analozera kwa ana, chakudya, zovala, mbalame, maluŵa, mkhalidwe wa nyengo, ndi ntchito. (Mateyu 4:18, 19; 6:25-34; 11:16-19; 13:3-8; 16:1-4) Ife nafenso tingagwiritsire ntchito chifupifupi nkhani iriyonse monga maziko akulunjikitsira chidwi chathu ku chowonadi cha Mulungu.
12. Pamene tikukonzekera ulendo, ndimotani mmene tingakonzekere kaamba ka umboni wa mwamwaŵi?
12 Tingachitire umboni mwamwaŵi kwa anthu okhala mu parki, oimirira pa mizere pa malo ogula zinthu, ndi zina zotero. Mu Athens, Paulo analingalira “bwalo la malonda masiku onse ndi iwo anakomana nawo.” (Machitidwe 17:17) Koma timafunikira kukonzekera kaamba ka umboni wa mwamwaŵi. Mwachitsanzo, kodi mukukonzekera kupanga ulendo pa ndege, pa sitima, kapena pa basi? Chotero tengani limodzi nanu Baibulo ndi matrakiti ena, magazini, kapena timabroshuwa. Kuŵerenga zofalitsidwa za Chikristu pamene muli paulendo waunyinji kapena kwina kulikonse kaŵirikaŵiri kumayambitsa kukambitsirana.
13. Chitirani chitsanzo mmene mungayambire umboni kwa munthu wa chikulire pamene mukuyenda.
13 Malonje aubwenzi kaŵirikaŵiri amabwera choyamba. Bukhu lam’manja la Reasoning From the Scriptures limalingalira malonje oyenera kugwiritsira ntchito mu utumiki wa m’munda, koma ena a iwo ayenera kukonzedwa kugwiritsiridwa ntchito pamene mukuchitira umboni wa mwamwaŵi. Mwachitsanzo, ngati pamene mukuyenda mwakhala pafupi ndi munthu wachikulire, inu munganene kuti: “Dzina langa ndine——. Ndakhala ndikulingalira kwambiri ponena za chifuno cha moyo. Anthu ambiri ali otanganitsidwa kupeza zowathandiza m’moyo kotero kuti sakhala ndi nthaŵi ya kulingalira ponena za chifuno cha moyo. Pamene tikukula mu zaka, ngakhale kuli tero, timazindikira kuti moyo uli waufupidi ndipo timadabwa: ‘Kodi ichi ndicho chokha chimene moyo unatanthauzidwa kukhala?’ Kodi mukuganiza kuti Mulungu ali ndi chifuno kaamba ka kukhalapo kwathu?” Lolani kaamba ka yankho. Kenaka mungalankhule ponena za chifuno cha Mulungu kaamba ka mtundu wa anthu ndi kuchitira ndemanga pa zinthu zambiri zolonjezedwa pa Chivumbulutso 21:3, 4. Kaamba ka kuchitira umboni mwamwaŵi kokhutiritsa, mungagwiritsirenso ntchito nsonga zina zabwino zophunziridwa pa misonkhano ya mpingo ndi m’zofalitsidwa za Chikristu.
Zotulukapo Zabwino Zingayembekezeredwe
14. Ndi chipambano chotani chimene mbale mmodzi anali nacho m’kuchitira umboni mwamwaŵi mkati mwa ulendo?
14 Monga Yesu ndi atsatiri ake oyambirira, tingakhale ndi chipambano pamene tichitira umboni mwamwaŵi. Kuchitira chitsanzo: Mkati mwa ulendo wa pa ndege, Mboni imodzi inalankhula kwa nduna ya nkhondo yomwe inali yokwatira kwa zaka 20. Mkazi wa mwamuna ameneyo anali kumwa anamgoneka, ndipo anayesera kudzipha nthaŵi zambiri, ndipo anali pafupi kumusiya iye kutenga mwamuna wachicheperepo. Pamene Mboniyo inalankhula ponena za thandizo la m’Malemba limene iye anali kulandira kuchokera mu Nsanja ya Olonda ndi magazini inzake ya Galamukani!, ndunayo inalembetsa ndipo inafuna kuti magaziniwo adzitumizidwa kwa mkazi wake. Apaulendo enawo anamva chimene Mboniyo inanena. Chotulukapo chake? Nkulekelanji, popeza kuti chifukwa chochitira umboni pa chochitika chimenecho, anapeza kulembetsa 22 ndi kugawira magazini 45 ndi mabukhu 21!
15, 16. (a) Perekani zitsanzo za chipambano cha umboni wa mwamwaŵi kwa antchito anzathu. (b) Ndi chiyani chimene zotulukapo zimenezi zikulingalira kwa inu?
15 Bwanji ponena za kuchitira umboni mwamwaŵi kwa ogwira nawo ntchito? Mbale mmodzi anasiya kope imodzi ya magazini yathu m’chipinda chosambira ku malo ake antchito. Ogwira naye ntchito anaŵerenga magaziniwo, kumufunsa mbaleyo, ndipo analembetsa kaamba ka iwo. Mwamunayo anavomerezanso phunziro la Baibulo ndi kusiya moyo wake woipa, koma mkazi wake anachoka kunyumba panthaŵi iriyonse pamene dzina la Mulungu linatchulidwa. Pamene mwamunayo anafuna kuchoka ku tchalitchi cha kumaloko, minisitala wa tchalitchi anabwera kudzakambitsirana za ichi, kungopeza kokha mkazi wa mwamunayo kunyumba. Kusoweka kwa chikhulupiriro kwa minisitalayo ndi mabodza ake ponena za Mboni za Yehova zinamudabwitsa iye, popeza iye anali atawona kusintha kwa mwamuna wake ku mkhalidwe wabwinopo. Iye anauza minisitalayo kuti: “Mungalembe chikalata cha kuleka tchalitchi kaamba ka ine ndiponso ana!” M’kupita kwanthaŵi, mwamuna ameneyu ndi mkazi wake anakhala Mboni zobatizidwa.
16 Zaka zingapo zapita, mbale amene tsopano akukhala mu United States anachitira umboni wa mwamwaŵi kwa wogwira naye ntchito mu England ndipo anamutenga mwamuna wachichepereyo ku kanema yosonyezedwa ndi Mboni za Yehova. Zaka makumi atatu mphambu chimodzi pambuyo pake, mbaleyo analandira kalata iyi: “Ndingakonde kukuuza tsopano kuti umboni umene unapereka [kwa mwamuna wachichepere] unalipira, popeza kwa chifupifupi zaka ziŵiri pambuyo pake mbale wina analankhula kwa iye, anapereka magazini, ndi kumtenga iye limodzi ku Nyumba ya Ufumu ya kumaloko . . . Anakhala Mboni, anabatizidwa mu 1959, ndipo tsopano ali mkulu mu mpingo wake . . . Pambuyo pa zaka 14 mkazi wake anakhalanso Mboni ndipo anabatizidwanso. Zaka ziŵiri pambuyo pake mwana wake wamkazi anabatizidwa ndipo tsopano ali mpainiya wokhazikika mu North Derbyshire . . . Kuchokera pa umboni wochepera umenewo umene unachita kale kwambiri mu Ashford, mnyamata amene uja, mkazi wake ndi mwana wake wamkazi, msuweni wake ndi mwana wake wamkazinso, mwamuna wake ndi ana asanu, ndi mwana mmodzi wa mwana wamkazi wa msuweni wake onse anakhala Mboni. . . . Ndingakonde kukuthokoza, Ted, kwambiri ndithu, popeza ndine mchirikizi wa chitsulo, ndipo nkhani imene ndangokuuzayo iri nkhani yanga ya umboni wako kwa ine ndi mmene zonse zinatembenukira.”
17. Ndi mwaŵi wotani umene atumiki achichepere a Yehova ali nawo wochitira umboni mwa-mwaŵi?
17 Inu atumiki achichepere a Yehova mulinso ndi gawo lochitira umboni labwino—anzanu a ku sukulu ndi aphunzitsi. Kodi mumawapatsa umboni wa mwamwaŵi m’nkhani zolembedwa, kubwereramo kwa pakamwa, ndi zina zotero? Monga magwero a nkhani kaamba ka nkhani yolembedwa, wophunzira wa pa sukulu ya pamwamba ya ku Ecuador amene phunziro la Baibulo linali kutsogozedwa kwa iye anagwiritsira ntchito Galamukani! ya June 8, 1986 yokhala ndi nkhani yakuti: “Hiroshima—Kodi Phunziro Lake Lataika?” Kalembedwe ka nkhani yake kanapeza chiyamikiro cha oweruza mu mpikisano wa mitundu yonse ndipo chinatulukapo mu ulendo waulere ku Japan. Ndithudi, kupambana kwa mpikisano sikuli chifuno cha zofalitsidwa za Chikristu. Koma ichi chikuchitira chitsanzo mtengo wa mabukhu oterowo ndi kukhutiritsa kwa kupereka umboni kulemekeza Mulungu m’sukulu.
18. Nchiyani chimene chinatulukapo kuchokera ku kupereka umboni wachidule kwa munthu wofuna kuchita renti chipinda?
18 Kaamba ka zifukwa za ndalama, mlongo anafunikira kuchita renti chipinda. Pamene analandira lamya yofunsa ponena za icho, iye anauza mkazi woitanayo kuti iye anali mmodzi wa Mboni za Yehova ndipo sakanalola mkhalidwe woipa wa chisembwere m’nyumba yake. Alendo akafunikira kuchoka kusanade, ndipo alendo a amuna akayenera kukhala powonekera nthaŵi zonse. Wotuma lamyayo anadodoma, ndipo kenaka ananena kuti: “Ndinaphunzira pamene ndinali wachichepere, koma sichinandisangalatse ine, chotero ndinapita ku koleji.” Atafunsidwa ngati afuna kupitiriza phunziro lake la Baibulo, iye anayankha, “Inde.” M’kupita kwanthaŵi, wotuma lamyayo, mayi wake, ndi mng’ono wake anakhala atumiki odzipereka a Yehova—zonse chifukwa chakuti mlongo anachitira umboni mwamwaŵi.
19. Ndimotani mmene umboni wa mwamwaŵi unatembenukira m’nkhani ya mkazi wa mu Bahamas?
19 Mu Bahamas chikumbumtima cha mkazi wina wa Chikatolika chinamuvutitsa chifukwa anali asanapite ku tchalitchi kwa zaka zisanu. Chotero m’mawa mwina pa Sande la mvula, ananyamuka kumapita ku tchalitchi. M’njira anakumana ndi Mboni zitatu, zomwe zinamutenga iye m’galimoto lawo—ndi kumpatsa umboni. Pamene anafika ku tchalitchiko, iye anafunsa kumva zowonjezereka ndi kukhala ndi iwo pamene anayenda kukanyamula wophunzira Baibulo. Iwo kachiŵirinso anadutsa pa tchalitchi, koma iye anafunabe kumva zowonjezereka chotero anapita ku Nyumba ya Ufumu. Nkhani ya poyera inali nkhani imodzimodziyo imene anali kukambitsirana m’galimoto. Phunziro la Baibulo linayambidwa ndi mkaziyo, amene anamuchotsa mwamuna amene anali kukhala naye (tate wa ana ake anayi), ndipo iye anabatizidwa mkati mwa msonkhano wa mu Nassau mu 1986. Anali wachimwemwe chotani nanga kuti winawake anachitira umboni kwa iye mwamwaŵi!
Pitirizani Kulankhula za Ufumu wa Mulungu
20. (a) Ndimotani mmene umboni wa mwamwaŵi uyenera kuwonedwera m’chigwirizano ndi utumiki wa m’munda? (b) Nchiyani chimene chalingaliridwa ngati wina ali wa manyazi kuchitira umboni mwamwaŵi?
20 Kuchitira umboni mwamwaŵi sikuli cholowa m’malo cha utumiki wa m’munda wokhazikika wa Mboni za Yehova. Kulalikira kunyumba ndi nyumba mwachiwonekere kuli ponse paŵiri kwa m’Malemba ndi kokhutiritsa. (Machitidwe 5:42; 20:20, 21) Mosasamala kanthu za chimenecho, kuchitira umboni mwamwaŵi kuli kopindulitsa, ndipo atumiki a Yehova ayenera kugawana mu iko. Kulikonse kumene kuli anthu—anansi, ophunzira nawo anzathu, ogwira nawo ntchito, ndi ena—pali mwaŵi wa kulankhula ponena za ulemerero wa ufumu wa Mulungu. Chotero lolani kuti mantha kapena manyazi asakuletseni inu. (Miyambo 29:25; 2 Timoteo 1:6-8) Ngati inu muli wochita mantha kuchitira umboni mwamwaŵi, bwanji osapemphera monga mmene anachitira atumiki ozunzidwa a Yesu? Iwo anadandaula kuti: “Yehova, . . . patsani kwa akapolo anu alankhule mawu anu ndi kulimbika mtima konse.” Kodi pemphero lawo linayankhidwa? Inde, popeza “padagwedezeka pamalo pamene adasonkhanirapo, ndipo adadzazidwa onse ndi mzimu woyera, nalankhula mawu a Mulungu molimbika mtima.”—Machitidwe 4:23-31.
21. Nchiyani chimene chidzafulumiza munthu kupereka umboni pansi pa mikhalidwe yonse?
21 Chotero, kenaka, kulitsani kawonedwe kanu kabwino kulinga ku kuchitira umboni mwamwaŵi. Lolani kuti chikondi kaamba ka Mulungu chikufulumizeni inu kupereka umboni pansi pa mtundu uliwonse wa mikhalidwe. Khalani otenthedwa maganizo, moyenera m’kumatumpha ndi chowonadi pa mwaŵi uliwonse. Ndithudi, pitirizani kulankhula ponena za ulemerero wa ufumu wa Mulungu.
Ndi Ati Omwe Ali Mayankho Anu?
◻ Umboni wa mwamwaŵi uli ndi maziko otani a m’Malemba?
◻ Ndi ziti zomwe ziri njira zina za kukonzekera kaamba ka umboni wa mwamwaŵi?
◻ Ngati tichitira umboni mwamwaŵi, ndi zotulukapo zotani zimene tingayembekezere?
◻ Ndimotani mmene tiyenera kuwonera umboni wa mwamwaŵi m’chigwirizano ndi utumiki wa m’munda wa nthaŵi zonse?
[Chithunzi patsamba 23]
Ngati inu muli wobindikiritsidwa, kodi mumachitira umboni monga mmene anachitira Paulo pamene anali wobindikiritsidwa?
[Chithunzi patsamba 25]
Kukonzekera pasadakhale kudzatitheketsa ife kuchitira umboni mwamwaŵi m’njira yokhutiritsa