Kodi Ano Ndiwodi Masiku Otsiriza?
MULI kumutu kwa bwato pamene likuyandikira pamadzi othamanga okokoma. Mukuona miyala yaikulu pamene madzi akugavira. Muyesa kuizemba. Munthu ali kumbuyo kwanuko bwenzi akukuthandizani kuwongolera bwatolo, koma sadziŵa. Kuipa kwake nkwakuti mulibenso mapu, ndiye simudziŵa kuti kaya mapeto a kugavira kwa madziko adzakhala dziŵe labata kapena mathithi.
Si chithunzi chabwino, eti? Ndiye tiyeni tichisinthetu. Yerekezerani kuti muli ndi wotsogoza waluso, yemwe amadziŵa thanthwe lililonse mumtsinjewu, ndi mokhota mwake momwe. Anadziŵiratu kuti madzi ogavirawo akuyandikira, akudziŵanso mmene adzathera ndipo akudziŵa mmene angapalasire powapyola. Kodi simungadzimve wosungika?
Ndithudi, tonsefe tili m’vuto lofananalo. Tili m’nyengo yovuta ya mbiri ya anthu, osati chifukwa cha kulakwa kwathu iyayi. Anthu ochuluka sadziŵa kuti zinthu zidzakhala motere kufikira liti, kaya mikhalidwe idzawongokera, kapena kuti angapirire bwanji tsopano lino. Koma sitifunikira kumva ngati otayika kapena ngati osoŵa chochita. Mlengi wathu watipatsa chotsogoza—chimene chinaneneratu za nyengo ino yoopsa ya m’mbiri, chimalosera mmene idzathera, ndipo chimatipatsa chitsogozo chimene timafuna kuti tipulumuke. Chotsogoza chimenecho ndi buku, Baibulo. Mlembi wake, Yehova Mulungu, amadzitcha yekha kuti Mlangizi Wamkulu, ndipo kupyolera mwa Yesaya ananena motonthoza kuti: “Makutu ako adzamva mawu kumbuyo kwa iwe akuti, Njira ndi iyi, yendani inu mmenemo: potembenukira inu kulamanja, ndi potembenukira kulamanzere.” (Yesaya 30:20, 21) Kodi mungakonde chitsogozo choterocho? Tiyenitu tione ngati Baibulo linaneneratu mmene masiku athu adzakhalira.
Atsatiri a Yesu Amfunsa Funso Lofunika
Atsatiri a Yesu ayenera kuti anadabwa. Yesu anali atangowauza kumene motsimikiza kuti nyumba zochititsa kaso za kachisi wa Yerusalemu zidzawonongedwa kotheratu! Kulosera koteroko kunali kodabwitsa. Patangopita nthaŵi pang’ono, ali khale pa Phiri la Azitona, ophunzira a Yesu anayi anamfunsa kuti: “Mutiuze ife zija zidzaoneka liti? Ndipo chizindikiro cha kufika [“kukhalapo,” NW] kwanu nchiyani, ndi cha mathedwe a nthaŵi ya pansi pano?” (Mateyu 24:3; Marko 13:1-4) Kaya anazindikira kapena sanatero, kukwaniritsidwa kwa yankho la Yesu kunayenera kukhala ndi mbali zingapo.
Chiwonongeko cha kachisi wa Yerusalemu ndi mapeto a dongosolo la zinthu lachiyuda sizinali zofanana ndi nthaŵi ya kukhalapo kwa Kristu ndi mapeto a dongosolo la zinthu la dziko lonse. Komabe, m’yankho lake lalitalilo, Yesu anafotokoza mwaluso mbali zonsezi za funsolo. Anawauza mmene zinthu zidzakhalira Yerusalemu asanawonongedwe; anawauzanso mmene dziko lidzakhalira pakukhalapo kwake, pamene adzakhala akulamulira kumwamba monga Mfumu ndi pamenenso adzakhala pafupi kuwononga dongosolo la zinthu la dziko lonse.
Mapeto a Yerusalemu
Choyamba talingalirani zimene Yesu ananena za Yerusalemu ndi kachisi wake. Zaka zoposa makumi atatu pasadakhale, ananeneratu za nthaŵi yovutitsitsa ya umodzi wa mizinda yaikulu padziko lapansi. Taonani makamaka mawu ake olembedwa pa Luka 21:20, 21: “Pamene paliponse mudzaona Yerusalemu atazingidwa ndi magulu a ankhondo, zindikirani pamenepo kuti chipululutso chake chayandikira. Pamenepo iwo ali m’Yudeya athaŵire kumapiri, ndi iwo ali mkati mwa uwo atuluke, ndi iwo ali kumiraga asaloŵemo.” Ngati magulu a ankhondo anali kudzazinga, kukweteza Yerusalemu, kodi nanga “iwo ali mkati mwa uwo” ‘akanatulukamo’ bwanji, monga momwe Yesu analamulira? Mwachionekere, Yesu anatanthauza kuti mpata udzatseguka. Kodi unatsegukadi?
Mu 66 C.E., magulu a nkhondo achiroma otsogozedwa ndi Cestius Gallus anawaingitsira ku Yerusalemu magulu opanduka achiyudawo nawatsekereza mumzinda mommo. Aromawo analoŵanso ngakhale mumzinda mwenimwenimo, nafika kukhoma la kachisi. Komano Gallus analamula magulu ake kuchita kanthu kena kodabwitsadi. Anawalamula kuchoka! Asilikali achiyudawo atakondwa anayamba kutsatira ndi kuwavulaza adani awo achiroma omathaŵawo. Chotero, mpata umene Yesu ananeneratu uja unatseguka. Akristu oona analabadira chenjezo lake ndipo anathaŵamo m’Yerusalemu. Anachitadi mwanzeru, pakuti pambuyo pa zaka zinayi chabe, magulu a nkhondo achiromawo anabweranso, Kazembe Titus akuwatsogolera. Ulendo uno kuthaŵa sikunatheke.
Magulu a nkhondo achiromawo anazinganso Yerusalemu; namanga linga la mitengo yosongoka momkweteza. Yesu anali atalosera za Yerusalemu kuti: “Masiku adzakudzera, ndipo adani ako adzakuzingira linga, nadzakuzungulira iwe kwete, nadzakutsekereza ponsepo.”a (Luka 19:43) Posakhalitsa, Yerusalemu anagonjetsedwa; kachisi wake waulemeleroyo anasanduka mabwinja ofuka utsi. Mawu a Yesu anakwaniritsidwa mwatsatanetsatane!
Komabe, Yesu anali kuganiza zambiri osati za chiwonongeko cha Yerusalemu basi. Ophunzira ake anali atamfunsanso za chizindikiro cha kukhalapo kwake. Nawonso sanadziŵe, koma funso lawolo linatanthauza nthaŵi pamene iye adzalongedwa kuti alamulire monga Mfumu kumwamba. Kodi analoseranji?
Nkhondo m’Masiku Otsiriza
Mutaŵerenga Mateyu machaputala 24 ndi 25, Marko chaputala 13, ndi Luka chaputala 21, mudzaona umboni wosakanika wakuti Yesu anali kunena za nyengo yathu yomwe ino. Ananeneratu za nthaŵi ya nkhondo—osati chabe “nkhondo ndi mbiri za nkhondo” zimene nthaŵi zonse zimaipitsa mbiri ya anthu koma nkhondo za ‘mtundu ndi mtundu wina ndi ufumu ndi ufumu wina’—inde, nkhondo zazikulu zapadziko lonse.—Mateyu 24:6-8.
Kwa kanthaŵi talingalirani mmene nkhondo zasinthira m’zaka zathu za zana lino. Pamene nkhondo inatanthauza chabe kumenyana kwa magulu a nkhondo oimira mitundu iŵiri yotsutsana, namakanthana ndi malupanga kapena ngakhale kuomberana mfuti kubwalo la nkhondo, zinali zoopsadi. Koma mu 1914 Nkhondo Yaikulu inaulika. Mtundu unatsatira mtundu wina m’chipiyoyo chodzutsa kaligone—nkhondo yoyamba yadziko. Zida zaotomatiki zinapangidwa kuti ziphe anthu ambiri ali pamtunda wautali. Mfuti zachiwaya zinaomba zipolopolo paliŵiro loopsa; mustard gas inawotcha, kuzunza, kupundula, ndi kupha asilikali zikwizikwi; akasinja ndi mfuti zawo zazikulu zolilima anabangula mwankhanza pa adani awo. Ndege zankhondo ndi sitima zankhondo za pansi pa madzi nazonso anazigwiritsira ntchito—kalambula bwalo chabe wa zimene zinali kudzakhalapo.
Nkhondo Yadziko II inachita zoopsa—inaposeratu kutali ija yoyamba, kupha anthu mamiliyoni ochuluka. Zombo zazikulu zonyamula ndege, mizinda ndithu yoyandama, zinali kuyenda panyanja nizimatumiza ndege zankhondo kukayoyotsera adani mabomba zili m’mlengalenga. Sitima za pansi pa madzi zinaombera zombo za adani ndi kuzimiza. Ndipo mabomba a atomu anaponyedwa, napha anthu zikwizikwi pakuphulika kulikonse! Monga momwe Yesu analoserera, ‘kwakhaladi zoopsa’ zozindikiritsa nyengo ya nkhondoyi.—Luka 21:11.
Kodi nkhondo zachepako chiyambire Nkhondo Yoyamba II? Kutalitali. Nthaŵi zina nkhondo zambiri zimaulika chaka chimodzi—ngakhale m’zaka khumi za ma 1990 zino—ndi kupha anthu mamiliyoni ambiri. Ndipo pakhala kusintha ponena za oyambirira kuphedwa m’nkhondo. Tsopano si asilikali okha omwe amafa. Lero, ochuluka amene akufa pankhondo—kunena zoona, oposa 90 peresenti—ndi anthu wamba.
Mbali Zina za Chizindikiro
Nkhondo yangokhala mbali ina ya chizindikiro chimene Yesu anatchula. Anachenjezanso kuti “kudzakhala njala.” (Mateyu 24:7) Ndipo yakhalakodi, ngakhale dziko lapansi limatulutsa zakudya zochuluka kuposa zimene anthu angafunikire kudya, ngakhale sayansi ya zaulimi yatsogola kuposa ndi kalelonse m’mbiri ya anthu, ngakhale pali magalimoto aliŵiro ndi amphamvu opereka zakudya kulikonse padziko lapansi. Ngakhale zili choncho, pafupifupi limodzi mwa magawo asanu a anthu onse a padziko lapansi amagona ndi njala tsiku ndi tsiku.
Yesu analoseranso kuti “m’malo akutiakuti” mudzakhala “miliri.” (Luka 21:11) Ndiponso, m’nyengo yathu ino taona zosemphana ndi zimene tinali kuyembekeza—mankhwala amphamvu kuposa kale, kupambana kwa tekinoloji, akatemera oletsa matenda ambiri ofala; komabe miliri ya matenda nayonso yawonjezeka kuposa kale. Fuluwenza ya Spanya inatsatira itangotha Nkhondo Yadziko I ndi kupha anthu ochuluka kuposa omwe nkhondoyo inapha. Nthendayo inali yoyambukira kwambiri koti m’mizinda ngati New York, anthu anali kuwalipiritsa faindi kapena kuwatsekera m’ndende chifukwa choyetsemula basi! Lero, kansa ndi nthenda ya mtima zikupha anthu mamiliyoni ochuluka chaka chilichonse—miliri yeniyeni. AIDS ikukanthabe anthu, kwakuti sayansi ya zamankhwala ikulephera kuithetsa.
Pamene kuli kwakuti Yesu anafotokoza masiku otsiriza makamaka pankhani yokhudza mikhalidwe ya m’mbiri ndi m’zandale, mtumwi Paulo anasumika maganizo kwambiri pa mavuto a anthu ndi mzimu wofala. Zina zimene analemba nzakuti: “Zindikira ichi, kuti masiku otsiriza zidzafika nthaŵi zoŵaŵitsa. Pakuti anthu adzakhala odzikonda okha, . . . osayera mtima, opanda chikondi chachibadwidwe, osayanjanitsika, . . . osakhoza kudziletsa, aukali, osakonda abwino, achiwembu, aliuma olimbirira, otukumuka mtima, okonda zokondweretsa munthu, osati okonda Mulungu.”—2 Timoteo 3:1-5.
Kodi mawu ameneŵa akumveka ozoloŵereka kwa inu? Talingalirani mbali imodzi yokha ya kunyonyotsoka kwa khalidwe m’dziko lero—kupasuka kwa banja. Unyinji wa mabanja opasuka, kumenya akazi, ana ochitidwa nkhanza, ndi kuchitira nkhanza makolo okalamba—zimenezi zikusonyeza kuti anthu alibedi “chikondi chachibadwidwe,” ‘ngaukali,’ ndipotu ‘ngachiwembu,’ “osakonda abwino”! Inde, tikuona kuti mikhalidwe imeneyi njofala lero.
Kodi Mbadwo Wathuwu ndi Umene Maulosi Analosera?
Komabe, mungafunse kuti, ‘Kodi mikhalidwe imeneyi sindiyo imene yasautsa anthu nthaŵi zonse? Kodi tingadziŵe bwanji kuti mbadwo wathu wamakonowu ndi umene maulosi analosera?’ Tiyeni tione maumboni atatu amene amasonyeza kuti Yesu anali kunena za nthaŵi yathu ino.
Woyamba, ngakhale chiwonongeko cha Yerusalemu ndi kachisi wake inali mbali yoyamba kukwaniritsidwa, ndithudi mawu a Yesu anasonya ku nthaŵi yamtsogolo. Zaka ngati 30 litapita tsoka limene linawononga Yerusalemu, Yesu anapatsa mtumwi Yohane wokalambayo masomphenya omwe anasonyeza kuti mikhalidwe yoloseredwayo—nkhondo, njala, miliri, ndi imfa yotsatirapo—idzakhalako padziko lonse mtsogolo. Inde, sikuti masautso ameneŵa adzakhala pamalo amodzi okha, koma adzakuta “dziko” lonse.—Chivumbulutso 6:2-8.
Wachiŵiri, m’zaka za zana lino mbali zina za chizindikiro cha Yesu zikukwaniritsidwa pa mlingo waukulu kwambiri. Mwachitsanzo, kodi kungatheke kuti nkhondo zifike pakuipa kwambiri kuposa mmene zakhalira chiyambire 1914? Kukanakhala Nkhondo Yadziko III, maiko onse amene ali ndi zida zanyukiliya nagwiritsira ntchito zida zawo, pambuyo pake dziko lapansi likanangokhala bwinja lopserera—ndipo anthu akanasoloka. Mofananamo, Chivumbulutso 11:18 chinaneneratu kuti m’masiku ameneŵa pamene mitundu ‘idzakwiya,’ anthu adzakhala ‘akuwononga dziko.’ Kwa nthaŵi yoyamba m’mbiri, kuipitsa ndi kuwononga malo okhala tsopano zikuwononga mphamvu ya pulaneti lino yochirikiza moyo! Chotero mbali imeneyinso ikukwaniritsidwa pamlingo wocheperapo kapena pafupifupi pamlingo waukulu. Kodi nkhondo ndi kuipitsa zingapitirizebe kuipiraipira mpaka munthu atadziwononga yekha limodzi ndi pulaneti lino? Ayi; pakuti Baibulo limalamula kuti dziko lapansi lidzakhalapo kosatha, anthu oongoka mtima namakhalapo.—Salmo 37:29; Mateyu 5:5.
Wachitatu, chizindikiro cha masiku otsiriza chimakhala chokhutiritsa makamaka pamene tichitenga chonse. Zonse pamodzi, pamene tilingalira mbali zimene Yesu anatchula m’Mauthenga Abwino atatu, makalata a Paulo, ndi za m’Chivumbulutso, chizindikiro chimenechi chili ndi mbali zambiri. Koma munthu wina angazitsutse chimodzichimodzi, kuti mibadwo ina yaonapo mavuto oterowo, koma pamene tizilingalira zonse pamodzi, zimasonya pambadwo umodzi basi—wathu uno.
Koma kodi zonsezi zikutanthauzanji? Kuti Baibulo likungofotokoza kuti nyengo yathuyi njothetsa nzeru ndi yopanda chiyembekezo? Kutalitali!
Uthenga Wabwino
Mbali ina yapadera ya chizindikiro cha masiku otsiriza yalembedwa pa Mateyu 24:14: “Uthenga uwu wabwino wa Ufumu udzalalikidwa padziko lonse lapansi, ukhale mboni kwa anthu a mitundu yonse; ndipo pomwepo chidzafika chimaliziro.” M’zaka za zana lino, Mboni za Yehova zachita ntchito yapadera m’mbiri ya anthu. Zalandira uthenga wa Baibulo wonena za Ufumu wa Yehova Mulungu—chimene uli, mmene umalamulirira, ndi zimene udzachita—ndipo zalengeza uthengawo padziko lonse. Zafalitsa mabuku onena za nkhani imeneyi m’zinenero zoposa 300 ndipo zamka nawo kwa anthu m’nyumba zawo kapena m’makwalala kapena kuntchito kwawo pafupifupi m’dziko lililonse padziko lapansi.
Mwakutero, zakhala zikukwaniritsa ulosi umenewu. Koma zakhala zikufalitsanso chiyembekezo. Taonani kuti Yesu anachitcha “uthenga wabwino,” osati uthenga woipa. Kodi zimenezo zingatheke bwanji m’nthaŵi zovuta zino? Chifukwa nchakuti uthenga waukulu wa Baibulo si wonena za mmene zinthu zidzaipira kumapeto a dzikoli. Uthenga wake waukulu umanena za Ufumu wa Mulungu, ndi kuti Ufumu umenewo ukulonjeza kanthu kena kamene mtima wa munthu aliyense umafuna kwambiri—chilanditso.
Kodi chilanditso chimenecho nchiyani, ndipo mungachipeze bwanji? Chonde ŵerengani nkhani zotsatira pamfundo imeneyi.
[Mawu a M’munsi]
a Pano Titus anali kudzapambana basi. Komabe, pazinthu ziŵiri zazikulu, sanakwaniritse cholinga chake. Anawapatsa mwaŵi woti angogonja nadzipereke mwamtendere, koma atsogoleri a mzindawo anakana kwa mtu wa galu. Ndipo pamene makoma a mzindawo anagumulidwa potsirizira pake, analamula kuti kachisi atsale. Koma anatenthedwa yense! Ulosi wa Yesu unasonyeza bwino lomwe kuti Yerusalemu adzasakazidwa ndi kuti kachisi wake adzawonongedwa kotheratu.—Marko 13:1, 2.
[Mawu Otsindika patsamba 5]
Anthu akufunafuna mayankho a mafunso ovutitsa maganizo onga, Kodi zinthu zaipiranji chonchi? Kodi anthu akupita kuti?
[Mawu Otsindika patsamba 6]
Lero, oposa 90 peresenti amene amafa pankhondo ndi anthu wamba
[Chithunzi patsamba 7]
Ulosi wa Yesu wonena za chiwonongeko cha Yerusalemu unakwaniritsidwa mwatsatanetsatane