Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga
Kodi Zakariya, atate wake wa Yohane Mbatizi, anachititsidwa kukhala ponse paŵiri wosalankhula ndi wogontha, monga momwe zikuwonekera pa Luka 1:62?
Ena agamula kuti Zakariya anakhalanso wogontha. Baibulo limanena kuti: ‘Ndipo akati amutche [mwanayo] dzina la atate wake Zakariya. Ndipo amake anayankha, kuti, Iyayi; koma adzatchedwa Yohane. Ndipo iwo anati kwa iye, Palibe wina wa abale ako amene atchedwa dzina ili. Ndipo anakodola atate wake, afuna amutche dzina liti? Ndipo iye anafunsa cholemberapo, nalemba, kuti, Dzina lake ndi Yohane.’—Luka 1:59-63.
M’cholembedwa chimenechi, palibe mawu amene amanena mwachindunji kuti Zakariya sanathe kumva kwa nyengo yakutiyakuti.
Poyambirira mngelo Gabrieli adalengeza kwa Zakariya kubadwa kwa mwana wamwamuna yemwe akatchedwa Yohane. Zakariya wokalambayo kudamkhalira kovuta kukhulupirira zimenezo. Mngeloyo anayankha kuti: ‘Udzakhala wotonthola ndi wosakhoza kulankhula, kufikira tsiku limene zidzachitika izi, popeza kuti sunakhulupirira mawu anga, amene adzakwanitsidwa panyengo yake.’ (Luka 1:13, 18-20) Mngeloyo anati kulankhula kwa Zakariya, osati kumva kwake, kudzayambukiridwa.
Cholembedwacho chimapitiriza kuti: ‘Koma m’mene iye anatulukamo [m’malo opatulika akachisi], sanatha kulankhula nawo [anthu odikirirawo], ndipo anazindikira kuti iye adawona masomphenya m’kachisimo. Ndipo iye analinkukodola iwo, nakhalabe wosalankhula.’ (Luka 1:22) Liwu Lachigiriki lotembenuzidwa “wosalankhula” panopa limapereka lingaliro lakulephera, m’kulankhula, kumva, kapena zonse ziŵiri. (Luka 7:22) Nanga bwanji ponena za Zakariya? Eya, talingalirani zimene zinachitika pamene anachira. ‘Pomwepo panatseguka pakamwa pake, ndi lirime lake linamasuka, ndipo iye analankhula, nalemekeza Mulungu.’ (Luka 1:64) Zimenezi zimapereka lingaliro lakuti luso lakulankhula la Zakariya ndilo lokha linalepheretsedwa.
Pamenepa, nanga nchifukwa ninji ena anafunsa Zakariya ‘mwakukodola, afuna amutche dzina liti [mwanayo]’? Otembenuza ena amamasulira zimenezi kuti “m’chinenero chamanja” kapena “kulankhula ndi manja.”
Zakariya, yemwe anakhala wosalankhula kuchokera pachilengezo cha mngelo, kaŵirikaŵiri analankhula ndi majesichala, mtundu wa chinenero cha kukodola. Mwachitsanzo, “analinkukodola” kwa iwo pakachisi. (Luka 1:21, 22) Pamene iye pambuyo pake anapempha cholemberapo, ayenera kuti analankhula ndi manja kapena majesichala. (Luka 1:63) Chotero, nkotheka kuti awo okhala naye m’nyengo ya kusalankhula kwake nawonso anazoloŵera kulankhula ndi majesichala.
Komabe, pali malongosoledwe omvekera bwinopo a kukodola kotchulidwa pa Luka 1:62. Elisabeti anali atangomaliza kuwauza zimene iye anadziŵa ponena za dzina la mwanayo. Chotero, popanda kumtsutsa, mwina anangotenga sitepe lotsatira ndi loyenera lakufunsira chosankha cha mwamuna wake. Iwo akachita zimenezo mwakungogwedeza mutu kapena kuchita jesichala. Chenicheni chakuti sanalembe funso lawo kotero kuti Zakariya aliŵerenge chingakhale umboni wakuti iye anamva mawu a mkazi wake. Chifukwa chake, kungomkodola ndi mutu kapena kuchita jesichala kunali kokwanira kunena kuti, ‘Eya, tonsefe (kuphatikizapo inuyo, Zakariya) tamva chonena cha mkazi wanu, koma kodi chosankha chanu nchotani ponena za dzina la mwanayo?’
Ndipo mwamsanga pambuyo pake panachitika chozizwitsa china, kutembenuza mkhalidwewo. ‘Ndipo pomwepo panatseguka pakamwa pake, ndi lirime lake linamasuka, ndipo iye analankhula.’ (Luka 1:64) Inde, sipakutchulidwadi za kumva kwake chifukwa chakuti sikudayambukiridwe.