Pamene Yesu Afika mu Ulemerero wa Ufumu
“Ena a iwo aima pano sadzalaŵa ndithu imfa, kufikira adzaona Mwana wa munthu atadza mu ufumu wake.”—MATEYU 16:28.
1, 2. Kodi chinachitika nchiyani atangopita kumene Pentekoste wa 32 C.E., ndipo cholinga cha chochitikacho chinali chiyani?
ATANGOPITA Pentekoste wa 32 C.E., atatu mwa atumwi a Yesu Kristu anaona masomphenya osaiŵalika. Malinga ndi kunena kwa mbiri youziridwa, “Yesu anatenga Petro, ndi Yakobo, ndi Yohane mbale wake, napita nawo paokha paphiri lalitali; ndipo iye anasandulika pamaso pawo.”—Mateyu 17:1, 2.
2 Masomphenya a kusandulikako anafika panthaŵi yofunika kwambiri. Yesu anali atayamba kuuza otsatira ake kuti iyeyo adzazunzika ndi kufa m’Yerusalemu, koma iwo sanamvetse zimenezo. (Mateyu 16:21-23) Masomphenyawo analimbitsa chikhulupiriro cha atumwi a Yesu atatuwo pokonzekera imfa yake yoyandikirayo ndi ntchito yaikulu ndi ziyeso zomwe mpingo wachikristu ukayang’anizana nazo m’zaka zotsatira. Kodi ife lero tingaphunzirepo kanthu kena pa masomphenya ameneŵa? Inde, chifukwa zimene anaphiphiritsira zikuchitika m’nthaŵi yathu ino.
3, 4. (a) Kodi Yesu ananenanji kutatsala masiku asanu ndi limodzi kuti kusandulikako kuchitike? (b) Fotokozani zomwe zinachitika pakusandulikako.
3 Masiku asanu ndi limodzi kusanachitike kusandulikako, Yesu anauza otsatira ake kuti: “Mwana wa munthu adzabwera mu ulemerero wa Atate wake, pamodzi ndi angelo ake; ndipo pomwepo iye adzabwezera kwa anthu onse monga machitidwe awo.” Mawuŵa anali kudzakwaniritsidwa ku “mathedwe a nthaŵi ya pansi pano.” Yesu anatinso: “Ena a iwo aima pano sadzalaŵa ndithu imfa, kufikira adzaona Mwana wa munthu atadza mu ufumu wake.” (Mateyu 16:27, 28; 24:3; 25:31-34, 41; Danieli 12:4) Kusandulikako kunachitika kukwaniritsa mawu omalizaŵa.
4 Kodi atumwi atatuwo anaonanji kwenikweni? Nawa malongosoledwe a Luka a chochitikacho: “Ndipo m’kupemphera kwake [Yesu], maonekedwe a nkhope yake anasandulika, ndi chovala chake chinayera ndi kunyezimira. Ndipo onani, analikulankhulana naye amuna aŵiri, ndiwo Mose ndi Eliya; amene anaonekera mu ulemerero, nanena za kumuka kwake kumene Iye ati adzatsiriza ku Yerusalemu.” Pamenepo, “unadza mtambo, nuwaphimba iwo [atumwiwo]; ndipo anaopa pakuloŵa iwo mumtambo. Ndipo munatuluka mawu mumtambo nanena, Uyu ndiye Mwana wanga, wosankhidwayo; mverani Iye.”—Luka 9:29-31, 34, 35.
Chikhulupiriro Chimalimbitsidwa
5. Kodi kusandulikako kunamkhudza motani mtumwi Petro?
5 Mtumwi Petro anali atamdziŵikitsa kale Yesu monga “Kristu, Mwana wa Mulungu wamoyo.” (Mateyu 16:16) Mawu a Yehova ochokera kumwamba anachitira umboni zimenezo, ndipo masomphenya a kusandulika kwa Yesu anapereka chithunzi cha kufika kwa Kristu m’mphamvu ndi ulemerero wa Ufumu, ndipo potsirizira pake kuweruza mtundu wa munthu. Patapita zaka zoposa 30 kuchokera pa kusandulikako, Petro analemba kuti: “Pakuti sitinatsata miyambi yachabe, pamene tinakudziŵitsani mphamvu ndi maonekedwe a Ambuye wathu Yesu Kristu, koma tinapenya m’maso ukulu wake. Pakuti analandira kwa Mulungu Atate ulemu ndi ulemerero, pakumdzera Iye mawu otere ochokera ku ulemerero waukulu, Uyu ndi Mwana wanga wokondedwa, amene Ine ndikondwera naye; ndipo mawu awa ochokera Kumwamba tidawamva ife, pokhala pamodzi ndi Iye m’phiri lopatulika lija.”—2 Petro 1:16-18; 1 Petro 4:17.
6. Kodi zinthu zinayenda motani pambuyo pa kusandulikako?
6 Angakhale lero, zimene atumwi atatuwo anaona zimalimbitsa chikhulupiriro chathu. Nzoona kuti pachitika zinthu zambiri chiyambire 32 C.E. Chaka chotsatira, Yesu anafa naukitsidwa, nakwera kumwamba kudzanja lamanja la Atate wake. (Machitidwe 2:29-36) Pa Pentekoste wa chakacho, “Israyeli wa Mulungu” watsopano anabadwa, ndipo mkupiti wolalikira unayamba, kuyambira mu Yerusalemu mpaka kumalekezero a dziko lapansi. (Agalatiya 6:16; Machitidwe 1:8) Posapita nthaŵi, chikhulupiriro cha otsatira a Yesu chinayesedwa. Atumwiwo anamangidwa ndi kumenyedwa koopsa chifukwa anakana kuleka kulalikira. Posapita nthaŵi, Stefano anaphedwa. Kenako, Yakobo yemwe anaona ndi maso kusandulikako, anaphedwanso. (Machitidwe 5:17-40; 6:8-7:60; 12:1, 2) Komabe, Petro ndi Yohane anapulumuka natumikira Yehova mokhulupirika zaka zina zambiri. Ndipo chakumapeto kwa zaka za zana loyamba C.E., Yohane analemba masomphenya ena osonyeza Yesu mu ulemerero wake wakumwamba.—Chivumbulutso 1:12-20; 14:14; 19:11-16.
7. (a) Kodi masomphenya a kusandulika anayamba liti kukwaniritsidwa? (b) Kodi Yesu anabwezera liti kwa ena monga mwa machitidwe awo?
7 Kuchokera kuchiyambi kwa “tsiku la Ambuye” mu 1914, masomphenya ambiri omwe Yohane anaona akwaniritsidwa. (Chivumbulutso 1:10) Nanga bwanji za ‘kubwera kwa Yesu mu ulemerero wa Atate wake,’ kochitiridwa chithunzi ndi kusandulikako? Masomphenyawa anayamba kukwaniritsidwa pakubadwa kwa Ufumu wakumwamba wa Mulungu mu 1914. Pamene Yesu anauka, monga nthanda, kukhala Mfumu yatsopano m’chilengedwe chonse, chinali chiyambi cha tsiku latsopano, kunena kwake titero. (2 Petro 1:19; Chivumbulutso 11:15; 22:16) Kodi Yesu panthaŵiyo anabwezera kwa anthu ena molingana ndi machitidwe awo? Inde. Pali umboni wamphamvu wakuti, posapita nthaŵi, chiukiriro chopita kumwamba cha Akristu odzozedwa chinayamba.—2 Timoteo 4:8; Chivumbulutso 14:13.
8. Kodi ndi zochitika zotani zimene zidzakhala mapeto aakulu a kukwaniritsidwa kwa masomphenya a kusandulika?
8 Komabe, posachedwapa Yesu adzafika “mu ulemerero wake, ndi angelo onse pamodzi naye” kudzaweruza mtundu wonse wa munthu. (Mateyu 25:31) Panthaŵiyo, adzaonekera mu ulemerero wake wonse nadzabwezera mwachilungamo kwa “anthu onse” monga mwa machitidwe awo. Onga nkhosa adzalandira moyo wosatha mu Ufumu umene anawakonzera, ndipo onga mbuzi “adzadulidwa kwamuyaya.” (NW) Amenewo adzakhaladi mapeto aakulu a kukwaniritsidwa kwaulemerero kwa masomphenya a kusandulikako!—Mateyu 25:34, 41, 46; Marko 8:38; 2 Atesalonika 1:6-10.
Olandira Ulemerero Pamodzi ndi Yesu
9. Kodi tiyenera kuyembekezera kuti Mose ndi Eliya adzakhala pamodzi ndi Yesu pokwaniritsa masomphenya a kusandulikako? Fotokozani.
9 Yesu sanali yekha m’kusandulikako. Mose ndi Eliya anaoneka pamodzi naye. (Mateyu 17:2, 3) Kodi iwo analipodi pamenepo? Ayi, pakuti onse aŵiriwo anali atafa kalekale ndipo anali m’tulo m’fumbi akumayembekezera chiukiriro. (Mlaliki 9:5, 10; Ahebri 11:35) Kodi adzaonekera pamodzi ndi Yesu pamene afika mu ulemerero wakumwamba? Ayi, chifukwa Mose ndi Eliya anakhala ndi moyo panthaŵi imene chiyembekezo chakumwamba chinali chisanatseguke kwa anthu. Adzakhala pakati pa oukitsidwa pa “kuuka kwa olungama” kwa padziko lapansi. (Machitidwe 24:15) Choncho kuonekera kwawo m’masomphenya a kusandulika kunali kophiphiritsa. Kuphiphiritsira chiyani?
10, 11. Kodi Eliya ndi Mose akuphiphiritsira yani m’zochitika zosiyanasiyana?
10 M’zochitika zina, Mose ndi Eliya amaphiphiritsira zamtsogolo. Pokhala nkhoswe ya pangano la Chilamulo, Mose anaphiphiritsira Yesu, Nkhoswe ya pangano latsopano. (Deuteronomo 18:18; Agalatiya 3:19; Ahebri 8:6) Eliya anaphiphiritsira Yohane Mbatizi, kalambula bwalo wa Mesiya. (Mateyu 17:11-13) Ndiponso, m’nkhani ya Chivumbulutso chaputala 11, Mose ndi Eliya anaphiphiritsira otsalira odzozedwa m’nthaŵi yamapeto. Kodi timadziŵa bwanji zimenezi?
11 Chabwino, tsegulani pa Chivumbulutso 11:1-6. M’vesi 3 timaŵerenga kuti: “Ndidzalamulira mboni zanga ziŵiri, ndipo zidzanenera masiku chikwi chimodzi ndi mazana aŵiri mphambu makumi asanu ndi limodzi, zovala chiguduli.” Ulosi umenewu unakwaniritsidwa pa otsalira a Akristu odzozedwa mkati mwa Nkhondo Yadziko I.a Chifukwa ninji mboni ziŵiri? Chifukwa otsalira odzozedwa amachita ntchito zofanana ndi za Mose ndi Eliya, m’lingaliro lauzimu. Mavesi 5 ndi 6 amati: “Wina akafuna kuipsa izo [mboni ziŵirizo], moto utuluka m’kamwa mwawo, nuwononga adani awo; ndipo wina akafuna kuipsa izo, maphedwe ake ayenera kutero. Izo zili nawo ulamuliro wakutseka m’mwamba, isagwe mvula masiku a chinenero chawo; ndipo ulamuliro zili nawo pamadzi kuwasandutsa mwazi, ndi kupanda dziko ndi mliri uliwonse nthaŵi iliyonse zikafuna.” Zimenezi zimatikumbutsa zozizwitsa zimene Eliya ndi Mose anachita.—Numeri 16:31-34; 1 Mafumu 17:1; 2 Mafumu 1:9-12.
12. Kodi Mose ndi Eliya akuphiphiritsira yani m’chochitika cha kusandulika?
12 Tsono ndani nanga amene Mose ndi Eliya akuphiphiritsira m’kusandulikako? Luka amati iwo anaonekera kumbali kwa Yesu “mu ulemerero.” (Luka 9:31) Mwachionekere, akuphiphiritsira Akristu omwe ali odzozedwa ndi mzimu woyera kukhala “oloŵa anzake” a Yesu amene analandira chiyembekezo chodabwitsa cha ‘kulandira ulemerero pamodzi ndi iye.’ (Aroma 8:17) Odzozedwa oukitsidwawo adzakhala pamodzi ndi Yesu pamene afika mu ulemerero wa Atate wake ‘kudzabwezera kwa onse monga mwa machitidwe awo.’—Mateyu 16:27.
Mboni Zonga Mose ndi Eliya
13. Kodi ndi zinthu ziti zomwe zimasonyeza kuti Mose ndi Eliya alidi oyenerera kuphiphiritsira oloŵa nyumba anzake odzozedwa a Yesu olandira naye ulemerero?
13 Pali zinthu zapadera zimene zikusonyeza kuti Mose ndi Eliya ali oyenereradi kuphiphiritsira oloŵa nyumba ndi Yesu odzozedwawo. Onse aŵiri Mose ndi Eliya anali olankhulira Yehova zaka zambiri. Onse anayang’anizana ndi mkwiyo wa wolamulira. Pamene anali osoŵa, aliyense anasamalidwa ndi banja lachilendo. Onse analosera molimba mtima kwa mafumu nachirimika polimbana ndi aneneri onyenga. Mose ndi Eliya anaona zochitika zosonyeza mphamvu ya Yehova pa phiri la Sinai (lotchedwanso Horebe). Onse anasankha owaloŵa m’malo kutsidya la kummaŵa kwa Yordano. Ndipo m’nthaŵi yawo aŵiriwo Mose (ndi Yoswa) ndi Eliya (ndi Elisa) kunali zozizwitsa zochuluka kopambana, kupatulapo zija zochitika m’nthaŵi ya moyo wa Yesu.b
14. Kodi odzozedwa akhala motani olankhulira Yehova, mofanana ndi Mose ndi Eliya?
14 Kodi zonsezo sizikutikumbutsa za Israyeli wa Mulungu? Zimaterodi. Yesu anauza otsatira ake okhulupirika kuti: “Chifukwa chake mukani, phunzitsani anthu a mitundu yonse, ndi kuwabatiza iwo m’dzina la Atate, ndi la Mwana, ndi la Mzimu Woyera: ndi kuwaphunzitsa, asunge zinthu zonse zimene ndinakulamulirani inu; ndipo onani, Ine ndili pamodzi ndi inu masiku onse, kufikira chimaliziro cha nthaŵi ya pansi pano.” (Mateyu 28:19, 20) Pomvera mawuŵa, Akristu odzozedwa akhala olankhulira Yehova kuyambira pa Pentekoste wa 33 C.E. mpaka lero. Monga Mose ndi Eliya, ayang’anizana ndi mkwiyo wa olamulira nachitira umboni kwa iwo. Yesu anauza atumwi ake 12 kuti: “Adzamuka nanu kwa akazembe ndi mafumu chifukwa cha Ine, kukhala mboni ya kwa iwo, ndi kwa anthu akunja.” (Mateyu 10:18) Mawu ake akwaniritsidwa nthaŵi zambiri m’mbiri ya mpingo wa Akristu.—Machitidwe 25:6, 11, 12, 24-27; 26:3.
15, 16. Kodi pali kufanana kotani pakati pa odzozedwa kumbali iyi, kenako Mose ndi Eliya kumbali ina, ponena za (a) kuchirikiza kwawo choonadi mopanda mantha? (b) kulandira chithandizo kwa anthu osakhala Aisrayeli?
15 Ndiponso, Akristu odzozedwa akhala opanda mantha monga Mose ndi Eliya pochirikiza choonadi ndi kutsutsa mabodza a zipembedzo. Kumbukirani mmene Paulo anatsutsira mneneri wonyenga wachiyuda Baryesu, ndipo mwaluso komanso molimba mtima mmene anavumbulira chinyengo cha milungu ya Atene. (Machitidwe 13:6-12; 17:16, 22-31) Kumbukiraninso kuti lerolino, otsalira odzozedwa avumbula molimba mtima Dziko Lachikristu ndipo kuchitira umboni kumeneko kwalisakaza dzikolo.—Chivumbulutso 8:7-12.c
16 Mose atathaŵa mkwiyo wa Farao, anakabisala m’nyumba ya munthu wosakhala Mwisrayeli, Rehueli, wotchedwanso Yetero. Patapita nthaŵi, Mose analandira uphungu wabwino wa uyang’aniro kwa Rehueli, amene mwana wake Hobabu anatsogolera Israyeli m’chipululu.d (Eksodo 2:15-22; 18:5-27; Numeri 10:29) Kodi Israyeli wa Mulungu wathandizidwa mwauzimu ndi anthu amene sali odzozedwa a Israyeli wa Mulungu? Inde, wachirikizidwa ndi a “khamu lalikulu” a “nkhosa zina,” amene akhalapo mkati mwa masiku otsiriza ano. (Chivumbulutso 7:9; Yohane 10:16; Yesaya 61:5) Yesu poneneratu za chichirikizo chachikondi chimene “nkhosa” zimenezi zidzapereka kwa abale ake odzozedwa, anati kwa iwo mwaulosi: “Ndinali ndi njala, ndipo munandipatsa Ine kudya; ndinali ndi ludzu, ndipo munandimwetsa Ine; ndinali mlendo, ndipo munachereza Ine; wamaliseche Ine, ndipo munandiveka; ndinadwala, ndipo munadza kucheza ndi Ine; ndinali m’nyumba yandende, ndipo munadza kwa Ine. . . . Indetu ndinena kwa inu, Chifukwa munachitira ichi mmodzi wa abale anga, ngakhale ang’onong’ono awa, munandichitira ichi Ine.”—Mateyu 25:35-40.
17. Kodi nchiyani chinachitika kwa odzozedwa chofanana ndi chimene chinachitika kwa Eliya m’phiri la Horebe?
17 Ndiponso, Israyeli wa Mulungu anakumana ndi zofanana ndi zimene zinachitikira Eliya m’phiri la Horebe.e Monga Eliya panthaŵi yomwe anali kuthaŵa Mfumukazi Yezebeli, otsalira odzozedwa pochita mantha anaganiza kuti ntchito yawo inatha kumapeto kwa Nkhondo Yadziko I. Ndiyeno, monganso Eliya, anayang’anizana ndi Yehova, yemwe anafika kudzaweruza magulu odzitcha “nyumba ya Mulungu.” (1 Petro 4:17; Malaki 3:1-3) Pamene kuli kwakuti Dziko Lachikristu linapezedwa lopereŵera, otsalira odzozedwa anavomerezedwa kukhala “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru” ndipo anasankhidwa kukhala woyang’anira chuma chonse cha Yesu padziko lapansi. (Mateyu 24:45-47) M’phiri la Horebe, Eliya anamva “liwu lofeŵa ndi lotsika.” (NW) lomwe linali la Yehova, akumpatsa ntchito ina. M’zaka za bata nkhondo itapita, atumiki odzozedwa okhulupirika a Yehova anamva liwu lake mwa kuŵerenga Baibulo. Iwonso anazindikira kuti anali ndi ntchito yoti aitsirize—1 Mafumu 19:4, 9-18; Chivumbulutso 11:7-13.
18. Kodi zinthu zapadera zosonyeza mphamvu ya Yehova zachitika motani kupyolera mwa Israyeli wa Mulungu?
18 Pomaliza, kodi pakhala zochitika zapadera zosonyeza mphamvu ya Yehova zimene zachitika kupyolera mwa Israyeli wa Mulungu? Itapita imfa ya Yesu, atumwi anachita zozizwitsa zambiri, koma m’kupita kwa nthaŵi zimenezo zinalekeka. (1 Akorinto 13:8-13) Lerolino, sitimaona zozizwitsa m’lingaliro lakuthupi. Komabe, Yesu anati kwa otsatira ake: “Indetu, indetu, ndinena kwa inu, Wokhulupirira Ine, ntchito zimene ndichita Ine adzazichitanso iyeyu; ndipo adzachita zoposa izi.” (Yohane 14:12) Kukwaniritsidwa koyamba kwa zimenezi kunali pamene ophunzira a Yesu analalikira uthenga wabwino mu Ufumu wonse wa Roma m’zaka za zana loyamba. (Aroma 10:18) Ndipo ntchito zoposa zimenezo zachitikadi lero mmene otsalira odzozedwa apititsa patsogolo kulalikira uthenga wabwino “padziko lonse lapansi, ukhale mboni kwa anthu a mitundu yonse.” (Mateyu 24:14) Chotulukapo? Zaka za zana la 20 zaona kusonkhanitsidwa kwa chiŵerengero choposa ndi kale lonse cha atumiki okhulupirika odzipereka a Yehova. (Chivumbulutso 5:9, 10; 7:9, 10) Ha, ndi umboni wodabwitsa bwanji wa mphamvu ya Yehova!—Yesaya 60:22.
Abale a Yesu Afika mu Ulemerero
19. Kodi ndi liti pamene abale odzozedwa a Yesu akuonekera mu ulemerero limodzi naye?
19 Pamene otsalira a abale a Yesu odzozedwawo amaliza moyo wawo wapadziko lapansi, amalandira ulemerero pamodzi naye. (Aroma 2:6, 7; 1 Akorinto 15:53; 1 Atesalonika 4:14, 17) Motero amakhala mafumu ndi ansembe osafa mu Ufumu wakumwamba. Limodzi ndi Yesu, pamenepo “adzawalamulira ndi ndodo yachitsulo, monga zotengera za woumba mbiya ziphwanyika mapale.” (Chivumbulutso 2:27; 20:4-6; Salmo 110:2, 5, 6) Adzakhala pamipando yachifumu pamodzi ndi Yesu ndi kuweruza “mafuko khumi ndi aŵiri a Israyeli.” (Mateyu 19:28) Chilengedwe chimene chikubuula chadikira mwachidwi zochitika zimenezi, zimene zili mbali ya “vumbulutso la ana a Mulungu.”—Aroma 8:19-21; 2 Atesalonika 1:6-8.
20. (a) Kodi kusandulikako kunalimbitsa chikhulupiriro cha Petro pachiyembekezo chotani? (b) Kodi kusandulikako kumawalimbitsa motani Akristu lerolino?
20 Paulo ananena za vumbulutso la Yesu mkati mwa “masauko aakulu” pamene analemba kuti: “Adzadza kudzalemekezedwa mwa oyera mtima ake, ndi kukhala wodabwizitsa mwa onse akukhulupirira . . . m’tsiku lija.” (Mateyu 24:21; 2 Atesalonika 1:10) Nchiyembekezo chaulemerero bwanji kwa Petro, Yakobo, Yohane, ndi Akristu onse odzozedwa ndi mzimu! Kusandulikako kunalimbitsa chikhulupiriro cha Petro. Ndithudi, kuŵerenga za kusandulikako kumalimbitsanso chikhulupiriro ndi chidaliro chathu chakuti posachedwapa Yesu ‘adzabwezera kwa aliyense monga mwa machitidwe ake.’ Akristu odzozedwa okhulupirika omwe akhalabe ndi moyo mpaka lero akhala ndi chidaliro chotsimikizika chakuti adzalemekezedwa limodzi ndi Yesu. A nkhosa zina chikhulupiriro chawo chalimbitsidwa podziŵa kuti Yesuyo adzawapulumutsa pamapeto a dongosolo loipali la zinthu kuloŵa m’dziko latsopano laulemerero. (Chivumbulutso 7:14) Nchilimbikitso chotani nanga chochirimika nacho kufikira mapeto! Ndipo masomphenya ameneŵa angatiphunzitse zambiri, monga tidzaonera m’nkhani yotsatira.
[Mawu a M’munsi]
a Onani mabuku akuti “Let Your Name Be Sanctified,” masamba 313-14, ndi Revelation—Its Grand Climax At Hand!, masamba 164-5, ofalitsidwa ndi Watchtower Bible and Tract Society of New York, Inc.
b Eksodo 2:15-22; 3:1-6; 5:2; 7:8-13; 8:18; 19:16-19; Deuteronomo 31:23; 1 Mafumu 17:8-16; 18:21-40; 19:1, 2, 8-18; 2 Mafumu 2:1-14.
c Onani masamba 133-41 m’buku la Revelation—Its Grand Climax At Hand!
d Onani buku lakuti You May Survive Armageddon Into God’s New World, lofalitsidwa ndi Watchtower Bible and Tract Society of New York, Inc., masamba 281-3.
e Onani buku lakuti “Let Your Name Be Sanctified,” masamba 317-20.
Kodi Mukukumbukira?
◻ Kodi ndani anaonekera pamodzi ndi Yesu m’kusandulika kwake?
◻ Kodi kusandulikako kunalimbitsa motani chikhulupiriro cha atumwi?
◻ Pamene Mose ndi Eliya anaonekera “mu ulemerero” pamodzi ndi Yesu m’kusandulikako, kodi anaphiphiritsira yani?
◻ Kodi pali kufanana kotani pakati pa Mose ndi Eliya kumbali iyi, ndi Israyeli wa Mulungu kumbali ina?
[Chithunzi patsamba 10]
Kusandulika kwalimbitsa chikhulupiriro cha Akristu akale ndi alero