Machitidwe a Atumwi
25 Patatha masiku atatu kuchokera pamene Fesito+ anafika mʼchigawocho nʼkuyamba kulamulira, anapita ku Yerusalemu kuchokera ku Kaisareya. 2 Kumeneko ansembe aakulu ndi amuna olemekezeka pakati pa Ayuda anamuuza zinthu zoipa zokhudza Paulo.+ Ndiyeno anayamba kumuchonderera 3 kuti awakomere mtima nʼkuitanitsa Paulo kuti abwere ku Yerusalemu. Koma anakonza zoti amudikirire panjira nʼkumupha.+ 4 Koma Fesito anawayankha kuti Paulo akuyenera kusungidwa ku Kaisareya ndiponso kuti iyeyo watsala pangʼono kubwerera komweko. 5 Ndiyeno anati: “Amene ali ndi maudindo pakati panu, tipitire limodzi kuti ngati pali chilichonse chimene munthu ameneyu walakwa akamuimbe mlandu.”+
6 Choncho iye atakhala nawo kumeneko kwa masiku osapitirira 8 kapena 10, anabwerera ku Kaisareya. Ndipo tsiku lotsatira anakhala pampando woweruzira milandu nʼkuuza anthu kuti abweretse Paulo. 7 Paulo atafika, Ayuda amene anabwera kuchokera ku Yerusalemu, anaima momuzungulira nʼkumamuneneza milandu yambiri yoopsa, imene sanathe kupereka umboni wake.+
8 Koma Paulo podziteteza anati: “Ine sindinachimwire Chilamulo cha Ayuda kapena kachisi kapenanso Kaisara.”+ 9 Koma pofuna kuti Ayudawo amukonde,+ Fesito anafunsa Paulo kuti: “Kodi ukufuna kupita ku Yerusalemu kuti nkhaniyi ikaweruzidwe kumeneko pamaso panga?” 10 Koma Paulo anayankha kuti: “Ine ndaima kutsogolo kwa mpando woweruzira milandu wa Kaisara, kumene ndiyenera kuweruzidwa. Ayuda sindinawalakwire chilichonse ngati mmene inunso mukuonera. 11 Ngati ndilidi wolakwa, ndipo ndikuyenera kuphedwa chifukwa cha zimene ndachita,+ sindikukana kufa. Koma ngati zimene akundinenezazi ndi zosamveka, palibe munthu amene angandipereke kwa iwo kuti awasangalatse. Ndikuchita apilo kuti ndikaonekere kwa Kaisara.”+ 12 Ndiyeno Fesito atakambirana ndi aphungu, anayankha kuti: “Popeza wachita apilo kuti ukaonekere kwa Kaisara, udzapitadi kwa Kaisara.”
13 Patatha masiku angapo, Mfumu Agiripa ndi Berenike anafika ku Kaisareya pa ulendo wa boma wokapereka ulemu kwa Fesito. 14 Popeza anakhala kumeneko masiku angapo, Fesito anafotokozera mfumuyo nkhani yokhudza Paulo. Iye anati:
“Pali munthu wina amene Felike anamusiya mʼndende. 15 Pamene ndinali ku Yerusalemu, ansembe aakulu komanso akulu a Ayuda anabwera kudzandiuza zoipa zokhudza iyeyu+ ndipo anapempha chiweruzo choti aphedwe. 16 Koma ine ndinawayankha kuti Aroma sachita zinthu mʼnjira imeneyo. Iwo sapereka munthu kwa anthu omuneneza pongofuna kuwasangalatsa, munthu wonenezedwayo asanapatsidwe mwayi woonana pamasomʼpamaso ndi omunenezawo kuti adziteteze pa mlanduwo.+ 17 Choncho atafika kuno, sindinachedwe, koma tsiku lotsatira ndinakhala pampando woweruzira milandu nʼkuitanitsa munthuyo kuti abwere naye. 18 Omunenezawo ataima nʼkuyamba kufotokoza, sanatchule zoipa zilizonse zimene ndinkaganiza kuti munthuyu anachita.+ 19 Iwo ankangotsutsana naye nkhani zokhudza mmene amalambirira mulungu*+ komanso za munthu wina dzina lake Yesu amene anafa, koma Paulo akunenabe motsimikiza kuti ali moyo.+ 20 Nditalephera kuthetsa mkangano wa nkhani zimenezi, ndinamufunsa ngati akufuna kupita ku Yerusalemu kuti akaweruzidwe kumeneko.+ 21 Koma Paulo anapempha kuti timusunge kuti akamve chigamulo cha Wolemekezeka.+ Choncho ndinalamula kuti asungidwe mpaka pamene ndidzamutumize kwa Kaisara.”
22 Agiripa anauza Fesito kuti: “Inenso ndikufuna ndimve ndekha munthu ameneyu akulankhula.”+ Iye anati: “Mawa mudzamumvetsera.” 23 Tsiku lotsatira, Agiripa ndi Berenike anabwera ndi ulemu waukulu wachifumu nʼkulowa mʼchipinda chimene anthu ankasonkhana. Anali ndi akuluakulu a asilikali komanso anthu otchuka amumzindawo ndipo Fesito atalamula, anabweretsa Paulo. 24 Ndiyeno Fesito ananena kuti: “Mfumu Agiripa ndi anthu nonse amene muli nafe pano, mwamuona munthuyu? Ayuda onse ku Yerusalemu komanso kuno, anandipempha kuti iyeyu sakuyeneranso kukhala ndi moyo ndipo analankhula zimenezi mofuula.+ 25 Koma ine ndinaona kuti sanachite chilichonse choyenera kuphedwa.+ Choncho iyeyu atapempha kuti akaonekere kwa Wolemekezeka, ndinaganiza zomutumiza. 26 Koma ndilibe mfundo iliyonse imene ndingalembere Mbuyanga yokhudza munthuyu. Choncho ndamubweretsa kwa nonsenu, makamaka inu Mfumu Agiripa, kuti mukamufunsa za nkhaniyi, ndipeze cholemba. 27 Chifukwa ine ndikuona kuti si nzeru kutumiza mkaidi, koma osatchula milandu yake.”