MUTU
Kodi Yesu Ankatanthauza Chiyani Pamene Ananena Kuti ‘Ukhale Wotsatira Wanga’?
1, 2. Kodi munthu angasangalale kwambiri ataitanidwa ndi ndani, nanga ndi funso liti limene tingadzifunse?
KODI ndi nthawi iti imene munasangalala kwambiri munthu wina atakuitanani kumwambo winawake? Mwina mungakumbukire nthawi imene munaitanidwa kumwambo winawake wapadera, monga ku ukwati wa mnzanu wa pamtima. Kapena mungakumbukire tsiku limene anakuitanani kuti mukayambe ntchito inayake yofunika kwambiri. Ngati munaitanidwapo ku zochitika ngati zimenezi, n’zosakayikitsa kuti munasangalala kwambiri ndiponso munamva kuti mwalemekezedwa. Komabe zoona zake n’zakuti aliyense wa ife, akuitanidwa kuti achite zinthu zinazake zofunika kwambiri kuposa zimenezi. Ndipotu zilizonse zimene tingasankhe pa nkhani imeneyi zingakhudze moyo wathu chifukwa ndi nkhani yofunika kwambiri.
2 Kodi amene akutiitana ndi ndani? Ndi Yesu Khristu, Mwana wobadwa yekha wa Yehova, Mulungu Wamphamvuyonse. Mawu amene iye ananena potiitana ali m’Baibulo palemba la Maliko 10:21. Iye anati: ‘Bwera ukhale wotsatira wanga.’ Ngakhale kuti Yesu ananena mawu amenewa kwa munthu mmodzi, mawuwa akugwiranso ntchito kwa aliyense wa ife. Choncho tingachite bwino kudzifunsa kuti, ‘Popeza Yesu akundiitana, kodi ineyo ndichite chiyani?’ Yankho la funso limeneli lingaoneke ngati losavuta chifukwa tingaganize kuti palibe amene angakane ataitanidwa ndi Yesu. Koma n’zodabwitsa kuti anthu ambiri amakana. N’chifukwa chiyani amakana?
3, 4. (a) Kodi munthu amene anapita kwa Yesu n’kufunsa zimene angachite kuti apeze moyo wosatha, anali ndi zinthu ziti zimene anthu ambiri amazisirira? (b) Kodi Yesu ayenera kuti anaona makhalidwe ati abwino mwa wolamulira wachinyamata amene anali wolemera?
3 Mwachitsanzo, taganizirani munthu amene anaitanidwa ndi Yesu pamasom’pamaso zaka pafupifupi 2,000 zapitazo. Munthu ameneyo anali wolemekezeka kwambiri. Iye anali ndi zinthu zitatu zimene anthu ambiri amazisirira ndiponso amaziona kuti n’zofunika kwambiri. Anali ndi zinthu monga chuma, udindo ndiponso anali wachinyamata. Ponena za munthuyu, Baibulo limanena kuti anali ‘mnyamata,’ anali “wolemera kwambiri” ndiponso anali “wolamulira.” (Mateyu 19:20; Luka 18:18, 23) Komatu panali chinthu china chofunika kwambiri chokhudza mnyamatayu. Iye anamva za Mphunzitsi Waluso, Yesu, ndipo anasangalala kwambiri ndi zimene anamvazo.
4 M’masiku amenewo, olamulira ambiri ankalephera kulemekeza Yesu. (Yohane 7:48; 12:42) Koma wolamulira wachinyamatayu anachita zinthu mosiyana ndi olamulira enawo. Baibulo limati: “Pamene [Yesu] ankachoka kumeneko, mwamuna wina anamuthamangira n’kugwada pamaso pake. Kenako anamufunsa kuti: ‘Mphunzitsi Wabwino, ndichite chiyani kuti ndikapeze moyo wosatha?’” (Maliko 10:17) Mungaone kuti munthuyu anali ndi chidwi chofuna kulankhula ndi Yesu. Iye anachita zinthu zimene munthu wosauka ndiponso wonyozeka angachite, chifukwa anathamangira Khristu anthu onse akuona. Komanso atamupeza, anagwada pamaso pake mwaulemu. Choncho, mungaone kuti wolamulira wachinyamatayu anali wodzichepetsa ndithu komanso ankazindikira zosowa zake zauzimu. Yesu anasangalala ndi makhalidwe abwinowa. (Mateyu 5:3; 18:4) Choncho n’zosadabwitsa kuti “Yesu anamuyang’ana ndipo anamukonda.” (Maliko 10:21) Kodi Yesu anayankha bwanji funso limene mnyamatayo anafunsa?
Mwayi Wapadera Kwambiri
5. Kodi Yesu anamuyankha bwanji mnyamata wolemera uja, ndipo tikudziwa bwanji kuti “chinthu chimodzi” chimene chimasoweka mwa iye sichinali choti akhale wosauka? (Onaninso mawu a m’munsi.)
5 Poyankha, Yesu anasonyeza kuti Atate wake anali atapereka kale mfundo zofunika zothandiza anthu kuti adzalandire moyo wosatha. Yesu anauza mnyamatayo mfundo za m’Malemba zimene ankayenera kutsatira, koma iye ananena motsimikiza kuti amatsatira mfundo za m’Chilamulo cha Mose mokhulupirika. Komabe, chifukwa choti Yesu anali ndi nzeru zakuya, anaona zimene zinali mumtima mwa wolamulirayo. (Yohane 2:25) Iye anaona kuti wolamulirayo anali ndi vuto linalake lalikulu lokhudza ubwenzi wake ndi Mulungu. N’chifukwa chake Yesu anamuuza kuti: “Chinthu chimodzi chikusowekabe mwa iwe.” Kodi ‘chinthu chimodzicho’ chinali chiyani? Yesu anati: “Pita ukagulitse zinthu zimene uli nazo ndipo ndalama zake ukapatse osauka.” (Maliko 10:21) Kodi Yesu ankatanthauza kuti munthu ayenera kukhala wosauka kuti azitumikira bwino Mulungu? Ayi.a Apa, Khristu ankaphunzitsa munthuyu mfundo ina yofunika kwambiri.
6. Kodi Yesu anaitana wolamulira wachinyamata amene analinso wolemera, kuti achite chiyani, nanga zimene wachinyamatayo anachita zinasonyeza kuti anali ndi vuto lotani mumtima mwake?
6 Pofuna kusonyeza chimene chinkasowa mwa mnyamatayo, Yesu anam’patsa mwayi wapadera kwambiri pomuuza kuti: ‘Bwera ukhale wotsatira wanga.’ Wolamulirayo anali ndi mwayi waukulu chifukwa Mwana wa Mulungu Wam’mwambamwamba anamuitana pamasom’pamaso kuti azimutsatira. Kuwonjezera pamenepa, Yesu anamulonjeza madalitso osaneneka chifukwa anamuuza kuti: “Udzakhala ndi chuma kumwamba.” Kodi wolamulira wachinyamatayu, amene analinso wolemera, anavomera mwayi wapadera kwambiriwu? Nkhaniyi imati: “Iye atamva mawu amenewo anakhumudwa ndipo anachoka ali ndi chisoni, chifukwa anali ndi katundu wambiri.” (Maliko 10:21, 22) Choncho, zimene Yesu ananena zomwe mnyamatayo sankaziyembekezera, zinachititsa kuti vuto limene linali mumtima mwake lionekere. Iye ankakonda kwambiri chuma chake ndiponso ankasangalala ndi udindo umene anali nawo komanso ulemu umene anthu ankamupatsa chifukwa cha zimenezi. N’zomvetsa chisoni kuti ankakonda kwambiri zinthu zimenezi kuposa mmene ankakondera Khristu. Choncho “chinthu chimodzi” chimene chinkasowa mwa iye chinali chakuti iye sankakonda Yesu ndiponso Yehova ndi mtima wake wonse. Chifukwa chakuti wachinyamatayu analibe chikondi chimenechi, anakana mwayi wapadera wokhala wotsatira wa Yesu. Komano, kodi inuyo nkhaniyi ikukukhudzani bwanji?
7. N’chifukwa chiyani tingatsimikize kuti mawu amene Yesu ananena poitana wolamulira uja akukhudzanso ifeyo masiku ano?
7 Mawu amene Yesu ananena poitana munthu uja, sakukhudza wolamulira yekhayo kapenanso anthu ochepa chabe. Yesu anati: “Ngati munthu akufuna kunditsatira, . . . apitirize kunditsatira.” (Luka 9:23) Palembali, mawu akuti “munthu” akutanthauza kuti aliyense angakhale wotsatira wa Khristu ngati “akufuna.” Mulungu amakokera kwa Mwana wake anthu oona mtima ngati amenewo. (Yohane 6:44) Aliyense ali ndi mwayi woti angakhale wotsatira wa Yesu, kaya ndi wolemera, wosauka ngakhalenso wochokera mu fuko kapena mtundu uliwonse wa anthu. Choncho, mawu amene Yesu ananenawa sakukhudza anthu okhawo amene analipo pa nthawi imene iye ananena zimenezi. Mawu a Yesu onena kuti, ‘bwera ukhale wotsatira wanga’ akukhudzanso inuyo. N’chifukwa chiyani muyenera kutsatira Khristu? Nanga munthu ayenera kuchita chiyani kuti asonyeze kuti ndi wotsatira wa Khristu?
N’chifukwa Chiyani Tiyenera Kukhala Otsatira a Khristu?
8. Kodi anthu onse amafunikira chiyani, nanga n’chifukwa chiyani?
8 Pali mfundo inayake yoona imene tonse tiyenera kuidziwa. Mfundo yake ndi yakuti anthufe timafunikira kukhala ndi mtsogoleri wabwino. Zimenezi ndi zoona ngakhale kuti si anthu onse amene amavomereza mfundoyi. Yeremiya, yemwe anali mneneri wa Yehova, anauziridwa kulemba mfundo yosatsutsika yakuti: “Ine ndikudziwa bwino, inu Yehova, kuti munthu alibe ulamuliro wosankha yekha njira ya moyo wake. Munthu amene akuyenda alibe ulamuliro wowongolera mapazi ake.” (Yeremiya 10:23) Anthu alibe mphamvu ndiponso ufulu wodzilamulira okha. N’zoonadi, zinthu zonse zimene zakhala zikuchitika pa moyo wa anthu kuyambira kale zikusonyeza kuti ulamuliro wa anthu ndi woipa. (Mlaliki 8:9) M’nthawi ya Yesu, atsogoleri ankapondereza, kuzunza komanso kusocheretsa anthu awo. Ndipo Yesu anaona kuti anthu wamba anali “ngati nkhosa zimene zilibe m’busa.” (Maliko 6:34) Ndi mmene zililinso masiku ano. Tonsefe monga gulu, komanso aliyense payekha, timafunika kukhala ndi atsogoleri amene tingawakhulupirire ndiponso kuwalemekeza. Kodi Yesu ndi munthu wodalirika amene anthu angamulemekeze? Inde. Onani zifukwa zotsatirazi zimene zikutichititsa kuyankha choncho.
9. Kodi Yesu akusiyana bwanji ndi olamulira ena?
9 Choyamba, Yesu anasankhidwa ndi Yehova Mulungu. Atsogoleri ambiri amasankhidwa ndi anthu anzawo omwe si angwiro. Atsogoleriwa nthawi zambiri amagwiritsa fuwa la moto anthu amene anawasankhawo chifukwa salamulira bwino. Koma Yesu ndi wosiyana ndi atsogoleri amenewa. Ngakhale dzina lake lenilenilo likutsimikizira zimenezi. Mawu akuti “Khristu,” omwe ndi ofanana ndi mawu akuti “Mesiya,” amatanthauza “Wodzozedwa.” Ndipotu Yesu anachita kudzozedwa, kapena kuti kusankhidwa ndi Ambuye Wamkulu Koposa, amenenso ndi wolamulira wa chilengedwe chonse, kuti agwire ntchito yopatulikayi. Ponena za Mwana wakeyu, Yehova Mulungu anati: “Taonani mtumiki wanga amene ndamusankha, wokondedwa wanga, amene amandisangalatsa kwambiri. Ndidzaika mzimu wanga pa iye.” (Mateyu 12:18) Palibe aliyense amene angadziwe bwino mtsogoleri amene anthufe tingafunikire kuposa Mlengi wathu. Yehova ali ndi nzeru zozama, choncho tili ndi zifukwa zomveka zokhulupirira munthu amene iye anamusankha.—Miyambo 3:5, 6.
10. N’chifukwa chiyani Yesu ndi chitsanzo chabwino kwambiri chofunika kutsanzira?
10 Chachiwiri, Yesu anapereka chitsanzo chabwino kwambiri choti titsanzire. Mtsogoleri wabwino amayenera kukhala ndi makhalidwe amene anthu omwe akuwatsogolera angawasirire ndiponso kuwatsanzira. Iye ayenera kupereka chitsanzo chabwino kwa anthu ena, zimene zingathandize kuti moyo wawo usinthe n’kukhala wabwino kwambiri. Kodi inuyo mungalemekeze kwambiri mtsogoleri amene ali ndi makhalidwe ati? Wolimba mtima, wanzeru ndiponso wachifundo? Kodi simungalemekezenso mtsogoleri amene amapirira akakumana ndi mavuto? Mukamaphunzira nkhani yonena za moyo wa Yesu ali padziko lapansi, muona kuti iye anali ndi makhalidwe amenewa ndi enanso ambiri. Yesu anasonyeza kwambiri makhalidwe a Mulungu amenewa chifukwa choti ankatsanzira Atate wake wakumwamba. Zochita zake zonse zinatsimikizira kuti analidi munthu wangwiro. Choncho pa chilichonse chimene anachita, m’mawu aliwonse amene analankhula ndiponso pa khalidwe lililonse limene anasonyeza, tingapezepo zofunika kutsanzira. Baibulo limati iye anatipatsa ‘chitsanzo kuti titsatire mapazi ake mosamala kwambiri.’—1 Petulo 2:21.
11. Kodi Yesu anasonyeza bwanji kuti ndi “m’busa wabwino”?
11 Chachitatu, Khristu ankachita zinthu zogwirizana ndi zomwe ananena zakuti: “Ine ndine m’busa wabwino.” (Yohane 10:14) Kwa anthu a m’nthawi imeneyo, fanizo limeneli linali lodziwika bwino. Abusa ankasamalira nkhosa zawo mwakhama. “M’busa wabwino” ankalolera kuika moyo wake pangozi pofuna kuteteza nkhosa zake. Mwachitsanzo, Davide yemwe anali kholo la Yesu, ali mnyamata anali m’busa. Ndipo kangapo konse, iye anaika moyo wake pangozi pofuna kuteteza nkhosa zake zimene zinkafuna kugwidwa ndi chilombo cholusa. (1 Samueli 17:34-36) Koma Yesu anachitira otsatira ake zinthu zoposa zimenezi chifukwa iye anawafera. (Yohane 10:15) Kodi masiku ano pangapezeke mtsogoleri amene ali ndi mtima wololera kuvutikira ena ngati umene Yesu anasonyezawu?
12, 13. (a) Kodi m’busa amasonyeza bwanji kuti amazidziwa bwino nkhosa zake, nanga nkhosazo zimasonyeza bwanji kuti zimamudziwa m’busayo? (b) N’chifukwa chiyani mukufuna kuti M’busa Wabwino azikutsogolerani?
12 Yesu anali “m’busa wabwino” m’njira inanso. Iye anati: “Nkhosa zanga ndimazidziwa ndipo nazonso zimandidziwa.” (Yohane 10:14) Taganizirani mfundo imene Yesu ankafuna kuti anthu aimvetse. Kwa munthu yemwe si m’busa, akaona gulu la nkhosa, amangoona ngati zonse n’zofanana. Koma m’busa amadziwa bwino nkhosa iliyonse payokha. Iye amadziwa nkhosa zazikazi zimene angafunikire kuzithandiza mwapadera zikabereka. Amadziwanso ana a nkhosa amene angafunikire kuwanyamula chifukwa choti sangathe kuyenda okha ulendo wautali, komanso amadziwa nkhosa zimene zikudwala kapena zimene zavulala. Nazonso nkhosa zimadziwa bwino m’busa wawo ndipo zimadziwa ngakhale mawu ake moti sizingawasokoneze ndi mawu a m’busa wina. M’busayo akaziitana mosonyeza kuti kuli chinachake choopsa, nthawi yomweyo nkhosazo zimabwera pafupi ndi iye. Komanso zimam’tsatira kulikonse kumene iye akuzitsogolera. M’busayo amadziwa malo amene kuli msipu wobiriwira, kumene kuli madzi abwino ndiponso amadziwa malo odyetserako nkhosazo amene ali otetezeka. M’busayo akamaziyang’anira, nkhosazo zimadziwa kuti n’zotetezeka.—Salimo 23.
13 Kodi simungafune kukhala ndi mtsogoleri wotere? Yesu yemwe ndi M’busa Wabwino wasonyeza kuti amasamalira otsatira ake m’njira yabwino kwambiri ngati imeneyo. Iye akukulonjezani kuti adzakutsogolerani kuti mukhale ndi moyo wosangalala komanso watanthauzo panopa ndiponso kuti mudzapeze moyo wosatha m’tsogolo. (Yohane 10:10, 11; Chivumbulutso 7:16, 17) Komabe, m’pofunika kuti mudziwe zinthu zimene muyenera kuchita kuti muzitsatira Khristu.
N’chiyani Chimafunika Kuti Munthu Akhale Wotsatira wa Khristu?
14, 15. Kodi munthu angakhaledi wotsatira wa Khristu ngati wangonena kuti iye ndi Mkhristu kapena kuti amakonda Yesu basi?
14 Masiku ano, anthu ambiri amaganiza kuti akutsatira Khristu. Ndipo iwo amasankha kudzitchula kuti ndi Akhristu. Mwina amapita kutchalitchi chinachake chifukwa choti makolo awo anawabatizitsa kutchalitchi chimenecho. Kapena iwo amanena kuti amakonda kwambiri Yesu ndipo anamulandira kukhala Mpulumutsi wawo. Koma kodi zimenezi zimawapangitsa kuti akhale otsatira a Khristu enieni? Kodi Yesu ankatanthauza zimenezi pamene anatiitana kuti tikhale otsatira ake? Pali zinthu zina zambiri zimene munthu ayenera kuchita kuti akhaledi wotsatira wa Khristu.
15 Taganizirani zimene zimachitika m’mayiko amene amati ndi a Chikhristu. Anthu ambiri m’mayiko amenewa amanena kuti ndi otsatira a Khristu. Kodi zinthu zimene zimachitika m’mayiko amenewo n’zogwirizana ndi zimene Yesu Khristu ankaphunzitsa? Ayi, chifukwa m’mayikowa muli chidani, kuponderezana, chiwawa ndiponso mumachitika zinthu zambiri zopanda chilungamo, mofanana ndi zimene zimachitika m’mayiko ena onse.
16, 17. Kodi nthawi zambiri chimasowa n’chiyani mwa anthu amene amati ndi Akhristu, nanga otsatira enieni a Khristu tingawadziwe bwanji?
16 Yesu ananena kuti otsatira ake enieni adzadziwika ndi zochita zawo, osati ndi zolankhula zawo kapena dzina lawo lokha. Mwachitsanzo, iye ananena kuti: “Sikuti aliyense amene amanditchula kuti, ‘Ambuye, Ambuye,’ adzalowa Ufumu wakumwamba, koma yekhayo amene akuchita zimene Atate wanga wakumwamba amafuna.” (Mateyu 7:21) N’chifukwa chiyani anthu ambiri amene amanena kuti Yesu ndi Ambuye wawo, amalephera kuchita zimene Atate wake amafuna? Kumbukirani wolamulira wachinyamata uja, yemwenso anali wolemera. Nthawi zambiri, ‘chinthu chimodzi chimene chimasoweka’ mwa anthu amene amati ndi Akhristu n’chakuti iwo sakonda Yesu ndi mtima wawo wonse ndiponso Yehova amene anatuma Yesuyo.
17 Kodi zimenezi zingatheke bwanji? Kodi anthu ambiri amene amati ndi Akhristu samanenanso kuti amakonda Khristu? Inde amatero, koma anthu amene amakonda Yesu ndi Yehova amafunika kuchita zinthu zambiri osati kungonena ndi pakamwa pokha. Yesu anati: “Ngati munthu amandikonda, adzasunga mawu anga.” (Yohane 14:23) Ndipo pamene ankalankhula monga m’busa, iye anati: “Nkhosa zanga zimamva mawu anga. Ine ndimazidziwa ndipo nkhosazo zimanditsatira.” (Yohane 10:27) N’zoonadi, zochita zathu n’zimene zimasonyeza kuti timakonda Khristu osati chabe zolankhula zathu kapena kungoganiza kuti timamukonda.
18, 19. (a) Kodi kuphunzira za Yesu kuyenera kutikhudza bwanji? (b) Kodi cholinga cha buku lino n’chiyani, nanga lithandiza bwanji anthu amene amadziona kuti ndi otsatira a Khristu?
18 Komatu zimene timachita zimachokera mumtima ndipo zimasonyeza kuti ndife anthu otani. Choncho kuti tikhaledi wotsatira wa Khristu tikuyenera kusintha umunthu wathu. Yesu anati: “Moyo wosatha adzaupeza akamaphunzira ndi kudziwa za inu, Mulungu yekhayo amene ndi woona, komanso za Yesu Khristu, amene inu munamutuma.” (Yohane 17:3) Tikamaphunzira komanso kuganizira mozama nkhani zoona zokhudza Yesu, mumtima mwathu mudzakhala zinthu zabwino. Kenako tidzayamba kukonda kwambiri Yesu ndipo tidzakhala ndi mtima wofunitsitsa kumutsatira tsiku ndi tsiku.
19 Choncho cholinga cha bukuli si kufotokoza mwachidule nkhani yonse ya moyo ndi utumiki wa Yesu, koma kutithandiza kudziwa bwino zimene tingachite kuti tizimutsatira.b Bukuli lapangidwa kuti litithandize kudzifufuza pogwiritsa ntchito Malemba, n’kumadzifunsa kuti, ‘Kodi ine ndikutsatiradi Yesu?’ (Yakobo 1:23-25) Mwina inuyo munayamba kale kudziona kuti ndinu nkhosa imene ikutsogoleredwa ndi M’busa Wabwino. Komabe, kodi simukuvomereza kuti mungafunikebe kusintha zina ndi zina pa moyo wanu? Baibulo limatilimbikitsa kuti: “Pitirizani kudziyesa kuti muone ngati mukadali ndi chikhulupiriro. Pitirizani kudziyesa kuti mudziwe kuti ndinu munthu wotani.” (2 Akorinto 13:5) Tikuyenera kuchita zonse zimene tingathe kuti tizitsogoleredwa ndi Yesu, M’busa wathu wabwino ndiponso wachikondi, amene Yehova anamusankha kuti azititsogolera.
20. Kodi tikambirana chiyani m’mutu wachiwiri?
20 Kuphunzira buku lino kukuthandizani kuti muyambe kukonda kwambiri Yesu ndiponso Yehova. Mukamakonda kwambiri Yesu ndi Mulungu mudzakhala ndi mtendere wa mumtima ndipo mudzakhala osangalala ngakhale kuti muli m’dziko loipali. Komanso mudzapitiriza kuyamikira Yehova chifukwa chotipatsa M’busa Wabwino. Komabe, tiyenera kukhala ndi cholinga chabwino tikamaphunzira za Khristu. Choncho, m’mutu wachiwiri wa bukuli tiona udindo umene Yesu ali nawo pokwaniritsa chifuniro cha Yehova.
a Yesu sanauze aliyense amene ankamutsatira kuti asiye chuma chake chonse. Ngakhale kuti iye ananenapo kuti n’zovuta kwambiri kuti munthu wachuma akalowe mu Ufumu wa Mulungu, ananenanso kuti: “Zinthu zonse n’zotheka kwa Mulungu.” (Maliko 10:23, 27) Ndipotu anthu angapo olemera anakhala otsatira a Khristu. Iwo anapatsidwa malangizo apadera mumpingo wa Chikhristu okhudza chumacho koma sanauzidwe kuti apereke chuma chawo chonse kwa anthu osauka.—1 Timoteyo 6:17.
b Kuti mumve za moyo ndiponso utumiki wa Yesu mwatsatanetsatane, onani buku lakuti Yesu Ndi Njira Choonadi ndi Moyo, lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.