Moyo ndi Uminisitala za Yesu
Zoyesera Zowonjezereka za Kupha Yesu
POPEZA iri nthaŵi yachisanu, Yesu akuyenda m’malo ofoleredwa odziŵika monga khumbi la Solomo. Ilo liri m’phepete mwa kachisi. Pano Ayuda amuzinga iye ndi kuyamba kunena kuti: “Kufikira liti musinkhitsasinkhitsa moyo wathu? Ngati inu ndinu Kristu, tiwuzeni momveka.”
“Ndakuwuzani,” Yesu akuyankha tero, “ndipo simukhulupirira.” Yesu sanawauze iwo mwachindunji kuti iye anali Kristu, monga mmene anauzira mkazi wa chiSamariya pa chitsime. Komabe iye, m’chenicheni, anavumbula chizindikiritso chake pamene analongosola kwa iwo kuti iye anali wochokera kumwamba ndipo kuti anakhalako asanakhaleko Abrahamu.
Yesu, ngakhale kuli tero, akufuna anthu kufikira mapetowo iwo eni kuti iye ali Kristu mwa kuyerekeza ntchito zake ndi zimene Baibulo linaneneratu kuti Kristu akakwaniritsa. Chimenecho ndicho chifukwa chake kumayambiriro iye analamula ophunzira ake kuti asauze aliyense kuti iye anali Kristu. Ndipo chimenecho ndicho chifukwa chake iye tsopano akupitiriza kunena kwa ayuda ankhalwe amenewa: “Ntchito izi ndizichita ine m’dzina la Atate wanga, zimenezi zindichitira umboni. Koma inu simukhulupirira.”
Nchifukwa ninji sakukhulupirira? Chifukwa cha kusoweka kwa umboni wakuti Yesu ali Kristu? Ayi, koma kaamba ka chifukwa chimene Yesu akukpereka pamene akuwauza iwo kuti: “Simuli a mwa nkhosa zanga. Nkhosa zanga zimva mawu anga, ndipo ine ndizizindikira, ndipo zinditsata ine. Ndipo ine ndizipatsa moyo wosatha, ndipo sizidzawonongeka ku nthaŵi yonse, ndipo palibe munthu adzazikwatula m’dzanja langa. Atate wanga amene anandipatsa izo ali wamkulu ndi onse, ndipo palibe wina angathe kuzikwatula m’dzanja la Atate.”
Yesu kenaka akulongosola unansi wake wathithithi ndi Atate wake, akumalongosola kuti: “Ine ndi Atate ndife amodzi.” Popeza kuti Yesu ali padziko lapansi ndipo Atate wake ali kumwamba, mwachiwonekere iye sakunena kuti iye ndi atate wake ali m’chenicheni, kapena mwakuthupi, amodzi. M’malomwake, iye akutanthauza kuti iwo ali amodzi m’chifuno kapena ali pa umodzi.
Okwiyitsidwa ndi mawu a Yesu, Ayuda atola miyala kuti amuphe, mongadi mmene anachitira miyezi ingapo kumayambiriro, mkati mwa Madyerero a Misasa. Molimba mtima akumayang’anizana ndi omwe akakhala omupha ake, Yesu akunena kuti: “Ndakuwonetsani inu ntchito zabwino za kwa Atate. Chifukwa cha ntchito iti ya izo mundiponya miyala?”
“Chifukwa cha ntchito yabwino, sitikuponyani miyala,” iwo akuyankha tero, “koma chifukwa cha mwano, ndi kuti inu, muli munthu, mudziyesera nokha mulungu.” Popeza kuti Yesu sanadzinenerepo kukhala mulungu, nchifukwa ninji Ayuda akunena ichi?
Mwachiwonekere chiri chifukwa chakuti Yesu akupereka chitamando kwa iyemwini ponena za mphamvu zomwe iwo akukhulupirira kuti ziri kotheratu za Mulungu. Mwachitsanzo, iye wangonena za “nkhosa,” “ndizipatsa moyo wosatha,” chomwe chiri chinachake chomwe munthu sangachite. Ayuda, ngakhale kuli tero, akunyalanyaza chenicheni chakuti Yesu akuvomereza kulandira ulamuliro kuchokera kwa Atate wake.
Kuti Yesu akudzinenera kukhala wocheperako pa Mulungu, iye kenaka akusonyeza mwa kufunsa kuti: “Kodi sikunalembedwe m’Chilamulo [pa Salmo 82:6], ‘Ndinati: “Muli milungu”’? Ngati anawatcha ‘milungu’ iwo amene mawu a Mulungu anadzera, ndipo Cholemba sichingathe kuthyoka, kodi inu munena za ine amene Atate anamupatula namutuma kudziko lapansi, ‘Uchita mwano,’ chifukwa ndinati, ndiri Mwana wa Mulungu?”
Inde, popeza kuti Malemba amatcha ngakhale oŵeruza aumunthu opanda chilungamo “milungu,” ndi cholakwa chotani chimene Ayuda amenewa akupeza ndi Yesu kaamba ka kunena kuti, “ndiri Mwana wa Mulungu”? Yesu akuwonjezera: “Ngati sindichita ntchito za Atate wanga, musakhulupirira ine. Koma ngati ndichita, mungakhale simukhulupirira ine, khulupirirani ntchitozo, kuti mukadziŵe ndi kuzindikira kuti Atate ali mwa ine ndi ine mwa Atate.”
Pamene Yesu anena ichi, Ayuda ayesera kumugwira iye. Koma iye athaŵa, mongadi mmene anachitira kumayambiriro pa Madyerero a Misasa. Iye achoka m’Yerusalemu ndi kuyenda kudutsa Mtsinje wa Yordani kumene Yohane anayamba kubatiza chifupifupi zaka zinayi kumayambiriro. Malo amenewa mwachidziŵikire sali kutali kuchokera ku gombe la kum’mwera kwa Nyanja ya Galileya, ulendo wa masiku aŵiri kapena kuposerapo kuchokera ku Yerusalemu.
Anthu ambiri adza kwa Yesu pa malo amenewa ndi kuyamba kunena kuti: “Sanachita chizindikiro, Yohane, koma zinthu zirizonse Yohane ananena za iye zinali zowona.” Chotero ambiri aika chikhulupiriro mwa Yesu pano. Yohane 10:22-42; 4:26; 8:23, 58; Mateyu 16:20.
◆ Ndi kupyolera mwachiyani mmene Yesu akufuna anthu kuzindikira iye monga Kristu?
◆ Ndimotani mmene Yesu ndi Atate ake aliri amodzi?
◆ Nchifukwa ninji, mwachiwonekere, Ayuda akunena kuti Yesu akudzipanga iyemwini kukhala mulungu?
◆ Ndimotani mmene kugwira mawu kwa Yesu kuchokera ku Masalmo kukusonyezera kuti iye sakudzinenera kukhala wofanana ndi Mulungu?