MUTU 5
“Ife Tiyenera Kumvera Mulungu Monga Wolamulira”
Atumwi anachita zinthu zimene Akhristu onse oona ayenera kutsanzira
Nkhaniyi yachokera pa Machitidwe 5:12–6:7
1-3. (a) N’chifukwa chiyani atumwi anawapititsa ku Khoti Lalikulu la Ayuda, ndipo nkhani yaikulu inali yotani? (b) N’chifukwa chiyani timachita chidwi kwambiri ndi zimene atumwiwo anachita?
OWERUZA a Khoti Lalikulu la Ayuda anali atakwiya kwambiri. Atumwi a Yesu ankaimbidwa mlandu m’khoti lalikulu limeneli. Kodi iwo analakwa chiyani? Yosefe Kayafa, yemwe anali mkulu wa ansembe ndiponso mtsogoleri wa oweruza a Khoti Lalikulu la Ayuda, anawalankhula mwaukali kuti: “Tinakulamulani mwamphamvu kuti musaphunzitsenso m’dzina limeneli.” Kayafa yemwe anali atakwiya kwambiri sanayese n’komwe kutchula dzina la Yesu. Iye anapitiriza kulankhula kuti: “Koma mwadzaza Yerusalemu yense ndi mfundo zimene mukuphunzitsa, ndipo mwatsimikiza mtima kuti ife tikhale ndi mlandu wa magazi a munthu ameneyu.” (Mac. 5:28) Apatu mfundo yake inali yoonekeratu. Iye ankatanthauza kuti: Musiye kulalikira, mukapanda kusiya tikukhaulitsani.
2 Kodi atumwiwo akanatani? Yesu, amene anapatsidwa udindo ndi Mulungu, ndi amene anawalamula kuti azigwira ntchito yolalikira. (Mat. 28:18-20) Kodi atumwiwo akanasiya ntchito yawo yolalikirayo chifukwa choopa anthu? Kapena kodi akanalimba mtima n’kupitirizabe kugwira ntchitoyo? Apa nkhani yaikulu inali yakuti: Kodi iwo akanamvera Mulungu kapena munthu? Mosazengereza, mtumwi Petulo analankhula m’malo mwa atumwi ena onsewo. Iye analankhula mosapita m’mbali ndiponso molimba mtima.
3 Monga Akhristu oona, timachita chidwi kwambiri ndi mmene atumwiwo anachitira ataopsezedwa ndi oweruza a Khoti Lalikulu la Ayuda. Ifenso Mulungu anatipatsa ntchito yolalikira ndipo tikamagwira ntchito imeneyi anthu angamatitsutse. (Mat. 10:22) Koma kodi tingachite chiyani ngati anthu amene amatitsutsa akuyesetsa kutiletsa kulalikira? Tingapeze mfundo zothandiza kwambiri tikamaganizira zimene atumwi anachita pa nthawi imene ankatsutsidwa ndi kutengeredwa ku Khoti Lalikulu la Ayuda.a
“Mngelo wa Yehova Anatsegula Zitseko” (Machitidwe 5:12-21a)
4, 5. N’chifukwa chiyani Kayafa ndi Asaduki “anachita nsanje”?
4 Kumbukirani kuti atumwi atalamulidwa koyamba kuti asiye kulalikira, Petulo ndi Yohane anayankha kuti: “Ife sitingasiye kulankhula zinthu zimene tinaziona ndi kuzimva.” (Mac. 4:20) Atachoka ku Khoti Lalikulu la Ayuda, Petulo ndi Yohane limodzi ndi atumwi ena onse, anapitirizabe kulalikira m’kachisi. Atumwiwo ankachita zozizwitsa monga kuchiritsa odwala ndi kutulutsa ziwanda. Ankachita zozizwitsa zimenezo “Pakhonde la Zipilala la Solomo,” pamene Ayuda ambiri ankakonda kusonkhanapo. Khondeli linali ndi denga ndipo linali chakum’mawa kwa kachisi. Ndipotu zikuoneka kuti odwala ankachira chithunzithunzi cha Petulo chikafika pa iwo. Anthu ambiri amene anachiritsidwa matenda awo analandira mawu a Mulungu a choonadi. Choncho “okhulupirira Ambuye anapitiriza kuwonjezereka, chifukwa amuna ndi akazi ambirimbiri anakhala ophunzira.”—Mac. 5:12-15.
5 Kayafa anali m’gulu la chipembedzo la Asaduki, ndipo iye pamodzi ndi Asaduki anzakewo “anachita nsanje” ndi atumwi ndipo analamula kuti awaponye m’ndende. (Mac. 5:17, 18) N’chifukwa chiyani Asaduki anakwiya kwambiri chonchi? Atumwi ankaphunzitsa kuti Yesu anaukitsidwa, pomwe Asaduki sankakhulupirira kuti akufa adzauka. Atumwi ankanena kuti munthu angapulumutsidwe pokhapokha ngati angakhulupirire Yesu, pomwe Asaduki ankaopa kuti Aroma adzawapatsa chilango ngati anthu atayamba kukhulupirira kuti Yesu ndi Mtsogoleri wawo. (Yoh. 11:48) N’chifukwa chake Asaduki anatsimikiza mtima kuletsa atumwi kuti asamalalikire.
6. Kodi masiku ano ndi ndani amene amayambitsa kuti atumiki a Yehova azizunzidwa, ndipo n’chifukwa chiyani sitiyenera kudabwa ndi zimenezi?
6 Masiku anonso, zipembedzo zabodza ndi zimene zimayambitsa kuti atumiki a Yehova azizunzidwa. Nthawi zambiri, zipembedzo zimenezi zimayesetsa kunyengerera olamulira a boma komanso kugwiritsa ntchito mabungwe ofalitsa nkhani kuti aletse ntchito yathu yolalikira. Kodi tiyenera kudabwa zimenezi zikamachitika? Ayi. Uthenga wathu umathandiza anthu kudziwa chipembedzo chonyenga. Anthu amtima wabwino akaphunzira choonadi cha m’Baibulo, amasiya zikhulupiriro ndi makhalidwe osagwirizana ndi Baibulo. (Yoh. 8:32) Ndiyetu n’zosadabwitsa kuti uthenga wathu nthawi zambiri umachititsa kuti atsogoleri achipembedzo azidana nafe chifukwa cha nsanje.
7, 8. Kodi atumwi anamva bwanji mngelo atawalamula kuti apite m’kachisi, nanga ndi funso liti limene ifeyo tingadzifunse?
7 Pamene atumwi anali m’ndende kudikira kuwaimba mlandu, mwina ankaganiza kuti aphedwa ndi adani awo. (Mat. 24:9) Koma usiku watsiku limenelo kunachitika zinthu zodabwitsa chifukwa “mngelo wa Yehova anatsegula zitseko za ndendeyo.”b (Mac. 5:19) Kenako mngeloyo anawapatsa malangizo omveka bwino akuti: “Pitani mukaime m’kachisi ndipo mukapitirize kuuza anthu.” (Mac. 5:20) N’zosakayikitsa kuti lamulo limenelo linatsimikizira atumwiwo kuti akuchita zoyenera. Mawu a mngeloyo ayenera kuti analimbikitsa atumwiwo kuti akhalebe olimba mtima ngakhale atazunzidwa koopsa. Atumwiwo “analowa m’kachisi n’kuyamba kuphunzitsa” molimba mtima komanso ali ndi chikhulupiriro cholimba.—Mac. 5:21.
8 Choncho aliyense payekha ayenera kudzifunsa kuti, ‘Kodi ndingalimbe mtima komanso kukhalabe ndi chikhulupiriro cholimba kuti ndipitirize kulalikira nditakumana ndi mavuto ngati amenewa?’ Tingalimbikitsidwe kudziwa kuti angelo amatithandiza ndi kutitsogolera tikamagwira ntchito yofunika imeneyi ‘yochitira umboni mokwanira za ufumu wa Mulungu.’—Mac. 28:23; Chiv. 14:6, 7.
“Ife Tiyenera Kumvera Mulungu Monga Wolamulira, Osati Anthu” (Machitidwe 5:21b-33)
9-11. Kodi atumwi anayankha bwanji oweruza a Khoti Lalikulu la Ayuda atawalamula kuti asiye kulalikira, ndipo zimenezi zikupereka chitsanzo chotani kwa Akhristu oona?
9 Tsopano Kayafa limodzi ndi oweruza ena a Khoti Lalikulu la Ayuda anali okonzeka kuti athane ndi atumwi. Oweruzawo sankadziwa zimene zinachitika kundendeko, choncho anatuma alonda kuti akatenge akaidiwo. Tangoganizani mmene alondawo anadabwira atapeza kuti akaidiwo kulibe, ngakhale kuti ndende inali “yokhoma ndiponso yotetezedwa bwino, alonda ataima m’makomo.” (Mac. 5:23) Pasanapite nthawi, woyang’anira kachisi anamva kuti atumwiwo apitanso kukachisi ndipo akugwira ntchito yochitira umboni za Yesu Khristu imene inawachititsa kuti aponyedwe m’ndende. Mwamsanga, woyang’anirayo ndi alonda ake anapita kukachisiko kuti akagwire atumwiwo n’kupita nawo kukhoti.
10 Monga mmene tafotokozera kumayambiriro kwa mutu uno, atsogoleri achipembedzo amene anali okwiyawo, anauza atumwiwo momveka bwino kuti asiye kulalikira. Kodi atumwiwo anayankha kuti chiyani? Poimira atumwi enawo, Petulo anayankha molimba mtima kuti: “Ife tiyenera kumvera Mulungu monga wolamulira, osati anthu.” (Mac. 5:29) Pamenepa atumwiwo anapereka chitsanzo kwa Akhristu onse oona. Mulungu amatiuza kuti tizimvera olamulira, koma ngati anthu olamulira atiuza kuti tichite zinthu zimene Mulungu amaletsa, kapena ngati akutiletsa kuchita zinthu zimene Mulungu amafuna, tikuyenera kumvera Mulungu osati iwowo. Choncho masiku anonso ngati “olamulira akuluakulu” aletsa ntchito yathu yolalikira uthenga wabwino, ife sitingasiye kugwira ntchito imene Mulungu anatipatsayi. (Aroma 13:1) M’malomwake, mwanzeru pogwiritsa ntchito njira zina, tidzapitiriza kuchitira umboni mokwanira za Ufumu wa Mulungu.
11 N’zosadabwitsa kuti kulimba mtima kwa atumwiwo kunawonjezera mkwiyo wa oweruzawo. Iwo anatsimikiza mumtima mwawo kuti ‘angopha’ atumwiwo basi. (Mac. 5:33) Zinaoneka ngati atumwi, omwe ankachitira umboni mwakhamawo, aphedwadi. Koma iwo anali atatsala pang’ono kupulumutsidwa mozizwitsa.
“Simungathe Kuwaletsa” (Machitidwe 5:34-42)
12, 13. (a) Kodi Gamaliyeli anapereka malangizo otani kwa oweruza anzake, ndipo iwo anachita chiyani? (b) Kodi Yehova angathandize bwanji anthu ake masiku ano, ndipo ifeyo tingakhale otsimikiza za chiyani ngati ‘tikuvutika chifukwa cha chilungamo’?
12 Kenako Gamaliyeli, “mphunzitsi wa Chilamulo wolemekezedwa ndi anthu onse,” analankhula.c Woweruza ameneyu ayenera kuti ankalemekezedwa kwambiri ndi anzake, chifukwa iye “analamula kuti anthuwo awatulutse kwakanthawi.” (Mac. 5:34) Popereka zitsanzo za anthu amene anayambitsa timagulu tawo koma timaguluto sitinapite patali atsogoleri awo atamwalira, Gamaliyeli anapempha oweruza a khotilo kuti asalimbane ndi atumwiwo, amene Mtsogoleri wawo Yesu, anali atangomwalira chakumene. Gamaliyeli analankhula mogwira mtima kuti: “Asiyeni anthu amenewa musalimbane nawo. Chifukwa ngati zolinga zawo kapena ntchito iyi ikuchokera kwa anthu, sipita patali. Koma ngati ikuchokera kwa Mulungu, simungathe kuwaletsa. Ndipo mukaumirira mukhoza kupezeka kuti mukulimbana ndi Mulungu.” (Mac. 5:38, 39) Oweruzawo anamvera malangizowo, komabe analamula kuti atumwiwo akwapulidwe ndiponso kuti “asiye kulankhula m’dzina la Yesu.”—Mac. 5:40.
13 Masiku anonso, Yehova angagwiritsire ntchito anthu audindo ngati Gamaliyeli kuti athandize anthu ake. (Miy. 21:1) Yehova angagwiritsenso ntchito mzimu wake woyera kuti uchititse olamulira amphamvu, oweruza kapena opanga malamulo kuti achite zinthu zogwirizana ndi chifuniro chake. (Neh. 2:4-8) Koma ngati atalola kuti ‘tivutike chifukwa chochita zinthu mwachilungamo,’ tingakhale otsimikizira za zinthu ziwiri. (1 Pet. 3:14) Choyamba, Mulungu angatipatse mphamvu kuti tithe kupirira. (1 Akor. 10:13) Chachiwiri, anthu amene akutitsutsa ‘sangathe kuletsa’ ntchito ya Mulungu.—Yes. 54:17.
14, 15. (a) Kodi atumwi anatani atakwapulidwa, ndipo n’chifukwa chiyani? (b) Perekani chitsanzo chosonyeza kuti anthu a Yehova amapirira mosangalala.
14 Kodi atumwiwo anakhumudwa kapena kufooka chifukwa chokwapulidwa? Ayi ndithu. Iwo ‘anachoka pamaso pa Khoti Lalikulu la Ayuda, ali osangalala.’ (Mac. 5:41) Kodi n’chifukwa chiyani “anali osangalala”? N’zodziwikiratu kuti iwo sankasangalala ndi ululu umene ankamva atakwapulidwa. Koma ankasangalala popeza ankadziwa kuti akuzunzidwa chifukwa chotumikira Yehova mokhulupirika komanso chifukwa choti ankatsanzira Yesu.—Mat. 5:11, 12.
15 Mofanana ndi abale athu a m’nthawi ya atumwi, ifenso timapirira mosangalala tikamazunzidwa chifukwa cha uthenga wabwino. (1 Pet. 4:12-14) Sitisangalala adani akamatiopseza, akamatizunza kapena kutitsekera m’ndende. Koma timasangalala kwambiri chifukwa timadziwa kuti tikupitirizabe kutumikira Mulungu mokhulupirika. Mwachitsanzo, taganizirani za Henryk Dornik, amene anapirira kwa zaka zambiri pamene ankazunzidwa ndi olamulira ankhanza kwambiri. Iye amakumbukira kuti mu August 1944, akuluakulu a boma anaganiza zomutumiza iyeyo ndi mchimwene wake kundende yozunzirako anthu. Akuluakulu a bomawo anati: “Sizingatheke kukakamiza anthu amenewa kuti achite zimene tikufuna. Iwo amasangalalabe ngakhale mutawauza kuti muwapha.” M’bale Dornik anafotokoza kuti: “Ngakhale kuti sindinkafuna kuphedwa, ndinkasangalalabe chifukwa chakuti ndikupirira komanso ndikupitirizabe kutumikira Yehova mokhulupirika.”—Yak. 1:2-4.
16. Kodi atumwi anasonyeza bwanji kuti ndi otsimikiza mtima kuchitira umboni mokwanira, ndipo ifeyo timatsanzira bwanji njira imene iwo ankagwiritsa ntchito polalikira?
16 Atumwi sanachedwe kuyambiranso ntchito yawo yolalikira. Mopanda mantha, iwo “tsiku lililonse anapitiriza kuphunzitsa mwakhama m’kachisi ndiponso kunyumba ndi nyumba komanso ankalengeza uthenga wabwino wonena za Khristu Yesu.”d (Mac. 5:42) Atumwi amenewa, omwe ankalalikira mwakhama, anatsimikiza mtima kuchitira umboni mokwanira. Onani kuti iwo ankapita m’makomo a anthu kukalalikira uthenga wabwino potsatira zimene Yesu Khristu anawauza. (Mat. 10:7, 11-14) N’chifukwa chake anakwanitsa kudzaza Yerusalemu ndi mfundo zimene ankaphunzitsa. Masiku ano, Mboni za Yehova zimadziwika chifukwa chotsatira njira ya atumwi imeneyi polalikira. Tikamalalikira kunyumba ndi nyumba m’gawo lathu, timasonyeza kuti ifenso tikufuna kuonetsetsa kuti wina aliyense ali ndi mwayi woti amve uthenga wabwino. Kodi Yehova wadalitsa utumiki wathu wa kunyumba ndi nyumba? Inde. M’nthawi ya mapeto ino, anthu ambirimbiri akhala atumiki a Mulungu ndipo ambiri anamva koyamba za uthenga wabwino umenewu a Mboni atafika panyumba pawo.
Amuna Oyenerera Amene Angayang’anire “Ntchito Yofunikayi” (Machitidwe 6:1-6)
17-19. Kodi ndi vuto lotani limene likanagawanitsa mpingo, ndipo atumwi anapereka malangizo otani pofuna kuthetsa vuto limeneli?
17 Mumpingo wa Chikhristu umene unali utangoyamba kumenewo, munayambika vuto lina limene likanausokoneza. Kodi vuto lake linali lotani? Ophunzira ambiri amene ankabatizidwa anali ochokera kumadera ena osati ku Yerusalemu ndipo anatsalira kwa kanthawi kuti aphunzire zambiri asanabwerere kwawo. Ophunzira a ku Yerusalemu anapereka ndalama mwakufuna kwawo kuti athandize alendowo kupeza chakudya ndiponso zinthu zina zofunika. (Mac. 2:44-46; 4:34-37) Pa nthawiyi, mumpingowo munayamba vuto lina limene linafunika kulithetsa mosamala kwambiri. Vutoli linayamba chifukwa “akazi amasiye a Chigiriki ankanyalanyazidwa pa nkhani yogawa chakudya cha tsiku ndi tsiku.” (Mac. 6:1) Koma akazi amasiye a Chiheberi sankanyalanyazidwa. Apa zikuoneka kuti vuto linali tsankho. Vuto limeneli lingagawanitse mpingo mosavuta poyerekezera ndi mavuto ena.
18 Atumwi, amene anali ngati bungwe lolamulira la mpingo umene unkakula kwambiriwo, anaona kuti sichinali chinthu chanzeru kuti iwowo ‘asiye ntchito yophunzitsa mawu a Mulungu n’kuyamba kugawa chakudya.’ (Mac. 6:2) Choncho, pofuna kuthetsa vutoli, iwo anauza ophunzira kuti afufuze amuna okwana 7 “amene ali ndi mzimu komanso nzeru,” omwe atumwiwo angawaike kuti ayang’anire “ntchito yofunikayi.” (Mac. 6:3) Panafunikadi amuna oyenerera chifukwa ntchito yake sinali yongogawa chakudya yokha koma ankafunikanso kuti azisunga ndalama, azigula zinthu ndiponso azilemba chilichonse chokhudza ndalamazo. Amuna onse amene anasankhidwawo anali ndi mayina a Chigiriki, ndipo zimenezi mwina zinathandiza kuti akazi amasiye odandaula aja asangalale. Ataona ngati anthu amene anasankhawo angayenerere pa udindowo komanso atapempherera nkhaniyo, atumwiwo anaika amuna 7 pa udindo woyang’anira “ntchito yofunikayi.”e
19 Kodi kugwira ntchito yogawa chakudya kunachititsa amuna 7 amene anaikidwa pa udindo aja kuti asamagwire nawo ntchito yolalikira uthenga wabwino? Ayi ndithu. Sitefano anali m’gulu la amuna amene anasankhidwawo, ndipo patapita nthawi anasonyeza kuti ankachitira umboni molimba mtima ndiponso mwamphamvu. (Mac. 6:8-10) Nayenso Filipo anali m’gulu lomweli, ndipo iye amatchedwa “mlaliki.” (Mac. 21:8) Choncho n’zoonekeratu kuti amuna 7 amenewa anapitirizabe kulalikira mwakhama za Ufumu.
20. Kodi anthu a Mulungu masiku ano amatsatira bwanji chitsanzo cha atumwi?
20 Anthu a Yehova masiku ano amatsatira chitsanzo cha atumwi. Amuna amene amaikidwa pa udindo mumpingo amayenera kusonyeza kuti amayendera nzeru za Mulungu ndipo amayeneranso kusonyeza kuti mzimu woyera ukugwira ntchito pa iwo. Motsogoleredwa ndi Bungwe Lolamulira, amuna amene amakwanitsa mfundo za m’Malemba zowayeneretsa kukhala pa udindo amaikidwa kuti akhale akulu kapena atumiki othandiza m’mipingo.f (1 Tim. 3:1-9, 12, 13) Tinganene kuti anthu amene amayenerera pa maudindo amenewa amaikidwa ndi mzimu woyera. Amuna amenewa, omwe amagwira ntchito mwakhama, amayang’anira ntchito zambiri zofunika. Mwachitsanzo, akulu angakonze zoti mpingo uzithandiza Akhristu achikulire okhulupirika amene akufunikiradi thandizo. (Yak. 1:27) Akulu ena amatanganidwa ndi ntchito yomanga Nyumba za Ufumu, yokonzekera misonkhano ikuluikulu kapena kukhala m’Makomiti Olankhulana ndi Achipatala. Atumiki othandiza amagwira ntchito zambiri zimene sizikhudzana kwenikweni ndi ubusa kapena kuphunzitsa. Komabe amuna osankhidwawa amayenera kugawa bwino nthawi yawo kuti azikwanitsa maudindo awo a mumpingo komanso maudindo ena owonjezera omwe angakhale nawo m’gulu la Yehova kwinaku akugwira ntchito imene Mulungu anatipatsa yolalikira uthenga wabwino wa Ufumu.—1 Akor. 9:16.
“Mawu a Mulungu Anapitiriza Kufalikira” (Machitidwe 6:7)
21, 22. Kodi n’chiyani chikusonyeza kuti Yehova anathandiza mpingo umene unali utangoyamba kumene?
21 Yehova anathandiza mpingo umene unali utangoyamba kumenewo kuti usathe pamene Akhristu ankazunzidwa ndiponso anauteteza utakumana ndi vuto limene likanatha kuugawanitsa. N’zoonekeratu kuti Yehova anadalitsa mpingowo, chifukwa timawerenga kuti: “Mawu a Mulungu anapitiriza kufalikira. Chiwerengero cha ophunzira chinkawonjezeka kwambiri mu Yerusalemu. Ndipo ansembe ambiri anakhala okhulupirira.” (Mac. 6:7) Chimenechi ndi chitsanzo chimodzi mwa zitsanzo zambiri zimene zili m’buku la Machitidwe zosonyeza kuti ntchito yolalikira inkapita patsogolo. (Mac. 9:31; 12:24; 16:5; 19:20; 28:31) Masiku anonso, timalimbikitsidwa kwambiri kumva mmene ntchito yolalikira za Ufumu wa Mulungu ikupitira patsogolo m’madera ena padziko lapansi.
22 M’nthawi ya atumwi, atsogoleri achipembedzo aja sanasiyiretu kuzunza Akhristu. Iwo anali atatsala pang’ono kuti ayambirenso kuzunza kwambiri Akhristu. Pasanapite nthawi, iwo anayamba kuzunza kwambiri Sitefano, ndipo tiona zimenezi m’mutu wotsatira.
a Onani bokosi lakuti “Khoti Lalikulu la Ayuda.”
b Iyi ndi nthawi yoyamba pa maulendo pafupifupi 20 pamene angelo akutchulidwa mwachindunji m’buku la Machitidwe. Palemba la Machitidwe 1:10, angelo sanatchulidwe mwachindunji koma anangowatchula kuti “azibambo . . . ovala zoyera.”
c Onani bokosi lakuti “Gamaliyeli Anali Rabi Wolemekezeka Kwambiri.”
d Onani bokosi lakuti “Kulalikira ‘Kunyumba ndi Nyumba.’”
e Amuna amenewa ayenera kuti ankafunika kusonyeza mfundo za makhalidwe abwino zimene akulu amafunika kusonyeza chifukwa kugwira “ntchito yofunikayi” unali udindo waukulu kwambiri. Komabe, Malemba sasonyeza nthawi imene amuna anayamba kuikidwa pa udindo wokhala akulu kapena oyang’anira mumpingo wa Chikhristu.
f M’nthawi ya atumwi, amuna oyenerera ankapatsidwa udindo woika akulu. (Mac. 14:23; 1 Tim. 5:22; Tito 1:5) Masiku anonso, Bungwe Lolamulira limasankha oyang’anira madera ndipo iwo amakhala ndi udindo wosankha akulu ndi atumiki othandiza.