“Dzanja la Yehova Linali Nawo”
“Chotero mawu a [Yehova, “NW”] anatuluka mwamphamvu nalakika.”—MACHITIDWE 19:20.
1. (a) Ndi kudandaula kotani kumene adani a Chikristu anapanga m’zana loyamba C.E.? (b) Nchiyani chomwe chinatsatira kulikonse kumene m’mishonale Paulo analalikira mbiri yabwino ya Ufumu wa Mulungu, ndipo nchiyani chomwe nthaŵi zonse chinali ndi Akristu oyambirira?
ZOPOSA zaka 1,900 zapitazo, adani a uthenga Wachikristu ndi otsutsa a m’mishonale mtumwi Paulo anadandaula kuti: “Omwe aja asanduliza dziko lokhalamo anthu afika kunonso, . . . ndipo [iwo] achita zokana malamulo a Kaisara, nanena kuti pali mfumu ina, Yesu.” (Machitidwe 17:6, 7) Kulikonse kumene m’mishonale Wachikristu Paulo anadziŵitsa mbiri yabwino ya Ufumu wa Yehova, kunali kachitidwe ndi kavomerezedwe, ndipo kaŵirikaŵiri chizunzo. Akristu ena oyambirira anavutikanso ndi chizunzo. Koma nthaŵi zonse “dzanja la Yehova linali nawo.”—Machitidwe 11:21.
2. Ndani yemwe anayambitsa ntchito ya umishonale Yachikristu, ndipo motani?
2 Ndani yemwe anayambitsa ntchito ya umishonale Yachikristu yofunika koposayi? Anali Yesu, munthu wapadera wokhala ndi uthenga wochititsa nthumanzi ndi njira yachilendo yoyambitsira iwo. Kumbukirani kuti Yesu, Mwana wa Mulungu, anabwera kwa anthu Achiyuda ndi chilengezo chozizwitsa ponena za Ufumu wa Mulungu. Koma iwo anali okondweretsedwa kokha m’chipulumutso chawochawo mwa ntchito za Lamulo.—Mateyu 4:17; Luka 8:1; 11:45, 46.
“Kwa Mitundu Yonse”
3. Ndi ulosi wotani wa Yesu womwe ungakhale unadabwitsa ophunzira ake a Chiyuda, ndipo nchifukwa ninji?
3 Chotero, tingalingalire kudabwitsidwa kwa ophunzira a Yesu a Chiyuda pamene iye anawauza iwo masiku atatu isanafike imfa yake: “Ndipo mbiri imeneyi yabwino ya Ufumu idzalalikidwa pa dziko lonse lokhalidwa ndi anthu kaamba ka umboni kwa mitundu yonse; ndipo pomwepo chidzafika chimaliziro.” Ophunzira ake angakhale anadabwa mmene iwo akalalikirira mbiri yabwino “kwa mitundu yonse.” Ndimotani mmene gulu laling’ono loterolo lokhulupirira likanakwaniritsira gawo lalikulu koposa loterolo?—Mateyu 24:14; Marko 13:10.
4. Ndi lamulo lotani limene Yesu wowukitsidwayo anapereka kwa ophunzira ake?
4 Pambuyo pake, Yesu wowukitsidwayo anawonjezera lamulo, akumanena kuti: “Mphamvu zonse zapatsidwa kwa ine kumwamba ndi pa dziko lapansi. Chifukwa chake mukani phunzitsani anthu a mitundu yonse, ndi kuwaphunzitsa iwo m’dzina la Atate ndi la Mwana ndi la mzimu woyera, ndi kuwaphunzitsa asunge zinthu zonse zimene ndinakulamulirani inu.” Mwakutero iwo anapatsidwa ntchito kutenga uthenga wa Ambuye wawo kwa “anthu a mitundu yonse.”—Mateyu 28:18-20.
5, 6. (a) Ndimotani mmene kulalikira kwa mbiri yabwino ya Ufumu wa Mulungu kunafikira Akunja, ndipo ndi chotulukapo chotani? (b) Ndimotani mmene akulu mu Yerusalemu anavomerezera pamene Petro analongosola kwa iwo chokumana nacho chake ndi Korneliyo Wachikunja?
5 Ichi chanafikira pa kuphatikiza kulalikira kwa Akunja, chomwe chinatsimikizira kukhala chitokoso. Mkhalidwe wa Petro zoposa zaka zitatu pambuyo pake uli umboni wa chimenecho. Kupyolera mwa masomphenya, Petro anawuzidwa kudya zolengedwa zodetsedwa monga chakudya. Pamene Mulungu anasonyeza kwa iye kuti zinthu zomwe kalelo zinalingaliridwa kukhala zodetsedwa tsopano zinali kuwonedwa monga zoyera, Petro anazizwitsidwa. Kenaka Petro anatsogozedwa ndi mzimu wa Mulungu kuchezera nyumba ya munthu Wakunja Korneliyo, kentuliyo Wachiroma. Kumeneko, iye anazindikira kuti chinali chifuno cha Mulungu kwa iye kulalikira kwa Korneliyo, ngakhale kuti iye kalelo analingalira kuti kugwirizana ndi anthu a mafuko ena kukakhala kopanda lamulo. Pamene Petro anali kulankhula, mzimu woyera unagwa pa banja Lakunja limenelo, ndipo ichi chinasonyeza, m’chenicheni, kuti munda kaamba ka ntchito ya umishonale Yachikristu tsopano uyenera kufutukulidwa kuphatikizapo dziko losakhala la Chiyuda.—Machitidwe 10:9-16, 28, 34, 35, 44.
6 Pamene Petro analongosola chochitika chimenechi kwa akulu mu Yerusalemu, “anakhala du, nalemekeza Mulungu, ndi kunena: ‘Potero, Mulungu anapatsa kwa amitundunso kutembenukira mtima ku moyo.’” (Machitidwe 11:18) Tsopano mitundu Yakunja ikakhoza kulandira mwaufulu mbiri yabwino ya Kristu ndi Ufumu wake!
Amishonale kwa Amitundu
7. Ndimotani mmene ntchito yoyambirira ya umishonale Yachikristu inayambira kufutukukira m’maiko ozungulira Mediterranean, ndipo ndimotani mmene Yehova anawonera ichi?
7 Ntchito yolalikira, yomwe inawonjezera mphamvu pambuyo pa kuphedwa ka Stefano, tsopano inatenga mbali yosiyana. Kupatulapo atumwi, mpingo mu Yerusalemu unamwazikana. Choyamba, Ayuda okhulupirira ozunzidwawo analalikira kokha kwa Ayuda mu Fonike, Kupro, ndi Antiyokeya. “Koma, . . . amuna a ku Kupro ndi Kurene . . . analankhula ndi [anthu olankhula Chigriki, NW], ndi kulalikira uthenga wabwino wa Ambuye Yesu.” Ndimotani mmene Yehova anawonera ntchito ya umishonale imeneyi kwa amitundu? “Dzanja la [Yehova, NW] linali nawo, ndi unyinji wakukhulupira unatembenukira kwa Ambuye.” Chiyamikiro chipite ku kulimba mtima kwa Akristu oyambirira amenewa, ntchito ya umishonale yokhutiritsa inali kuyamba kufalikira m’maiko ozungulira Mediterranean. Koma zambiri zinalinkudza.—Machitidwe 4:31; 8:1; 11:19-21.
8. Ndimotani mmene Mulungu anasonyezera kachitidwe kosankha kaamba ka kufutukula kwa ntchito ya umishonale?
8 Chifupifupi 47-48 C.E., Mulungu, kupyolera mwa mzimu woyera, anasonyeza kachitidwe kosankha kaamba ka kufutukula ntchito ya umishonale. Cholembedwa cha pa Machitidwe 13:2-4 chimatiuza ife kuti: “Mzimu woyera unati: ‘Mundipatulire ine Barnaba ndi Saulo ku ntchito imene ndinawaitanirako.’ . . . Pomwepo iwo, otumidwa ndi mzimu woyera, anatsikira ku Selukeya [doko la pa nyanja la Antiyokeya wa ku Siriya], ndipo pochokerapo anapita m’ngalawa ku Kupro.” Chimenecho chinali chosangalatsa chotani nanga kwa Paulo ndi Barnaba—kuyenda pa madzi ku gawo lawo lachilendo loyamba! Mtumwi Paulo anali kupititsa patsogolo ntchito ya umishonale Yachikristu. Iye analinso kuika maziko kaamba ka ntchito yomwe ikatsirizidwa m’zana lathu la 20.
9. Nchiyani chimene mtumwi Paulo anakwaniritsa kupyolera mwa maulendo ake a umishonale?
9 Paulo anapitirizabe kupanga maulendo atatu a umishonale olembedwa kuphatikizapo ulendo wake wopita ku Roma monga wandende. Mkati mwa maulendowa, iye anatsegula ntchito m’mizinda yambiri mu Europe ndipo analalikira uthenga wa Ufumu m’maiko ndi zisumbu zomwe lerolino zimadziŵika monga Syria, Cyprus, Crete, Turkey, Greece, Malta, ndi Sicily. Iye angakhalenso anafika ku Spain. Iye anathandiza kukhazikitsa mipingo m’mizinda yambiri. Nchiyani chomwe chinali chinsinsi cha ntchito yake ya umishonale yokhutiritsa?
Kuphunzitsa Kokhutiritsa
10. Nchifukwa ninji Paulo anali wokhutiritsa chotero mu ntchito yake ya umishonale?
10 Paulo anatsanzira njira ya Kristu yophunzitsira. Chotero iye anadziŵa mmene angalankhulire kwa anthu. Iye anadziŵa mmene angaphunzitsire ndi mmene angalangizire ena monga aphunzitsi. Iye anazika kuphunzitsa kwake pa Malemba. Iye sanayesere kusangalatsa ena ndi nzeru yake koma, m’malomwake, analingalira kuchokera mu Malemba. (Machitidwe 17:2, 3) Paulo anadziŵanso mmene angasinthire ku gulu lake ndi mmene angagwiritsirire ntchito makhazikitsidwe a kumaloko monga chofutukulira uthenga wake. Monga mmene ananenera kuti: “Ndinadzilowetsa ndekha ukapolo kwa onse, kuti ndipindule ochuluka. Ndipo kwa Ayuda ndinakhala monga Myuda . . . Kwa iwo opanda lamulo monga wopanda lamulo . . . Kwa ofooka ndinakhala ngati wofooka, kuti ndipindule ofooka. Ndakhala zonse kwa anthu onse, kuti pali ponse ndikapulumutse ena.”—1 Akorinto 9:19-23; Machitidwe 17:22, 23.
11. Nchiyani chomwe chikusonyeza kuti Paulo ndi mabwenzi ake anali amishonale okhutiritsa, ndipo ndimotani mmene utumiki Wachikristu unafalikira?
11 Paulo ndi mabwenzi ake anali amishonale okhutiritsa. Mwa kulimbikira ndi chipiriro, iwo anakhazikitsa ndi kulimbikitsa mipingo Yachikristu kulikonse kumene anapita. (Machitidwe 13:14, 43, 48, 49; 14:19-28) Utumiki woyambirira Wachikristu unali wofalikira kotero kuti Paulo potsirizira pake anakhoza kulemba ponena za “chowonadi cha uthenga wabwino umene udafikira kwa inu, monganso m’dziko lonse lapansi lomabala zipatso . . . , wolalikidwa m’cholengedwa chonse cha pansi pa thambo.” Zowonadi, ntchito yoyambirira ya umishonale Yachikristu inayambukira anthu.—Akolose 1:5, 6, 23.
12. Chiyani chomwe chinapangitsa ntchito yowona ya umishonale Yachikristu kulekeka kwa kanthaŵi?
12 Ngakhale kuli tero, pofika ku chiyambi cha zana lachiŵiri C.E., mpatuko unali kulowerera mu mpingo Wachikristu, mongadi mmene Yesu ndi atumwi anali atachenjezera. (Mateyu 7:15, 21-23; Machitidwe 20:29, 30; 1 Yohane 2:18, 19) M’mazana omwe anatsatira, nthanthi ya za maphunziro a umulungu ndi chiphunzitso cha chikunja chinamiza uthenga wa Ufumu. Chikristu cha Dziko chinatumiza amishonale, osati kukalalikira Ufumu wowona wa Mulungu, koma kukalamulira kwa anthu opanda chinjirizo a kumaloko—kaŵirikaŵiri ndi lupanga—ufumu wa ambuye awo a ndale zadziko ndi achirikizi. Ntchito yowona Yachikristu ya umishonale inalekeka koma osati kosatha.
13. Ndimotani mmene ndawala ya umishonale inayambitsidwira m’nthaŵi zamakono, ndipo nchiyani chomwe chinakwaniritsidwa pofika kumapeto kwa 1916?
13 Kulinga kumapeto kwa zana la 19, Charles T. Russell, prezidenti woyamba wa Watch Tower Society, anawona chifuno kaamba ka ntchito ya umishonale. Iye chotero analinganiza ndawala yolalikira yokulira, ndipo iyemwini anachezera mizinda yambiri mu United States, limodzinso ndi kuyenda m’dziko ndi sitima ya pa madzi kuchezera maiko ambiri monga mmene kunathekera. Zolembedwa zake zozikidwa pa Baibulo zinafalitsidwa m’zinenero 35. Chikunenedwa kuti iye anayenda mtunda woposa mamailosi miliyoni imodzi monga mlankhuli wapoyera ndi kulalikira maulaliki oposa 30,000 isanafike imfa yake mu 1916.
14. Nchiyani chimene Joseph F. Rutherford anachita kupititsa patsogolo ntchito ya umishonale?
14 M’lowa m’malo wake, Joseph F. Rutherford, nayenso anazindikira chifuno chokulira kaamba ka ntchito ya umishonale. Kumayambiriro kwa ma 1920, iye anatumiza amuna ofikapo ku maiko osiyanasiyana kukathandiza kukhazikitsa ntchito yolalikira. Amishonale anachitira upainiya ntchito ya Ufumu imeneyi mu Spain, Kum’mwera kwa America, ndi Kumadzulo kwa Africa. Mu 1931 chifunsiro chinapangidwa kaamba ka odzipereka aufulu kulimbikitsa ntchito mu Spain. Amuna atatu achichepere ochokera ku England anavomereza ndi kutumikira kumeneko pansi pa mikhalidwe yovuta ndi yowopsya kwambiri kwa zaka zinayi kufikira kuwulika kwa Nkhondo ya Chiweniweni ya chiSpanish mu 1936. Kenaka iwo anayenera kuthaŵa kaamba ka miyoyo yawo.
15. Nchiyani chomwe chinachitika mu ma 1940 kufutukula ntchito ya umishonale mowonekera?
15 Mkati mwa zaka khumi za ma 1940, zinthu zabwinopo zinayenera kubwera mu ntchito ya umishonale. Prezidenti wachitatu wa Watch Tower Society, Nathan H. Knorr, anali ndi gulu la amuna achangu m’kugwira ntchito limodzi naye. Mwachiwonekere pansi pa chitsogozo cha mzimu woyera, mu 1942 iye anawona chifuno cha kutsegula sukulu ya umishonale m’kukonzekera kaamba ka chitokoso cha pamapeto pa Nkhondo ya Dziko ya II. Mkati mwa nkhondo imeneyo, iye anatenga kachitidwe koyamba, ndipo Sukulu ya Gileadi ya Watchtower inatsegulidwa kumpoto kwa Boma la New York mu February 1943. Ndi alangizi anayi, iyo inapereka maphunziro ozikidwa pa Baibulo kaamba ka utumiki wa umishonale kwa atumiki achipainiya okangalika oposa zana limodzi, amuna ndi akazi, miyezi isanu ndi iŵiri iriyonse. Kodi ntchito yawo yotulukapo yakhala yokhutiritsa?
16. (a) Ndi Mboni zingati zomwe zinali kulalikira mu 1943, ndipo chimenechi chikufanana bwanji ndi lerolino? (b) Ndi mbali yotani imene amishonale akhala nayo m’chiwonjezeko chimenechi? Longosolani.
16 Mu 1943 panali kokha Mboni 126,329 zolalikira m’maiko 54. Nchiyani chomwe chiri mkhalidwe lerolino? Tsopano, zaka 45 pambuyo pake, pali zochulukira kuwirikiza nthaŵi 28, atumiki okangalika oposa mamiliyoni atatu ndi theka m’maiko ndi zisumbu za m’nyanja 212. Mbali yowonekera ya chiwonjezeko chimenechi yakhala chifukwa cha maziko abwino oyalidwa ndi amishonale oposa 6,000 omwe anamaliza maphunziro pa Sukulu ya Gileadi. Awa abwera kuchokera m’maiko 59 ndipo atumizidwa ku maiko osiyanasiyana 148 mkati mwa zaka makumi asanu zapita. Ndi thandizo lawo, m’malo mwa kokha Mboni zoposa zikwi zana limodzi kaamba ka dziko lonse, monga momwe zinaliri zaka 45 zapitazo, tsopano pali maiko khumi omwe lirilonse liri ndi atumiki oposa zikwi zana limodzi akulalikira ndi kuphunzitsa mbiri yabwino. Mu yambiri ya mitundu imeneyi, amishonale a ku Gileadi akhala achirikizi a ntchito yolengeza.
17. Ndi ziti zomwe ziri nsonga zitatu zazikulu zomwe zapangitsa ponse paŵiri ntchito ya umishonale Yachikristu yoyambirira ndi yamakono kukhala yokhutiritsa?
17 Kaya tikulozera ku ntchito ya umishonale Yachikristu yoyambirira kapena yamakono, pali nsonga zenizeni zomwe zapangitsa iyo kukhala yokhutiritsa. Imodzi iri kufikira anthu mwachindunji komwe kwatulukapo mu utumiki wa kunyumba ndi nyumba ndi kuchitira umboni mwamwaŵi, limodzinso ndi kakonzedwe ka phunziro la Baibulo la panyumba. (Yohane 4:7-26; Machitidwe 20:20) Nsonga ina iri uthenga wachindunji wopepuka ndi wozikidwa pa Baibulo womwe umawunikira Ufumu wa Mulungu monga yankho lokha lotheratu kaamba ka mavuto a mtundu wa anthu. (Machitidwe 19:8; 28:16, 23, 30, 31) Ndipo ambiri a amishonale athu akutumikira m’maiko osatukuka kumene chifuno kaamba ka ulamuliro wolungama wa Mulungu chiri chowonekera kwambiri. Nsonga yachitatu iri chikondi chimene Kristu anaphunzitsa ndi chimene amishonale athu amakono amasonyeza m’kuchita kwawo kwa tsiku ndi tsiku ndi anthu a mitundu yonse ndi ziyambi. Kulibe kukaikira kuti, zoposa zaka 45 zapitazo, amishonale a Watch Tower apanga kuthandizira kokulira ku kufutukuka kwa dziko lonse kwa gulu la Yehova.—Aroma 1:14-17; 1 Akorinto 3:5, 6.
Mzimu wa Upainiya Utenga Muzu
18. Ndani enanso amene atenga mzimu wofanana wachangu cha umishonale monga omaliza maphunziro a Gileadi?
18 Mosakaikira chitsanzo cha changu cha omaliza maphunziro a Gileadi chinasonkhezera ena ndi chikhumbo cha kukhala atumiki a nthaŵi zonse. Lerolino, pali mazana a zikwi za mboni zina za Yehova omwe atenga mzimu wofananawo wa changu cha umishonale. Awanso ali apainiya m’lingaliro lenileni, kutsatira m’mapazi a Yesu, “Mpainiya wa chipulumutso chawo.”—Ahebri 2:10; 12:2, Moffatt.
19. Nchiyani chomwe Mboni zambiri zokhala ndi mzimu wa upainiya zadzipereka mwaufulu kuchita, ndipo ndimotani mmene amadzimverera kukhala ofupidwa?
19 Chiyambire ma 1960 chakhala chovuta kwambiri kutumiza apainiya m’maiko ambiri. Sukulu ya Gileadi ya Baibulo ya Watchtower ikupitiriza kupereka amishonale, ku ukulu wothekera, mogwirizana ndi chifuno m’maiko akunja. Ngakhale kuli tero, pali munda waukulu wa dziko lonse kaamba ka Mboni zimenezo zomwe ziri ndi mzimu wowona wa upainiya. Ambiri adzipereka mwaufulu kupanga makonzedwe awo awo kutumikira m’maiko kumene chifuno chiri chokulira. Kodi muli mmodzi amene mungagwirizane nawo? Oterowo kaŵirikaŵiri achitira ndemanga kuti zovuta ndi kudzipereka kumalipiridwa mobwerezabwereza ndi chisangalalo chokulira cha kudyetsa chowonadi cha Ufumu kwa onga nkhosa m’maiko otukuka kumene. Iwo afupidwa makumi khumi m’kupeza “abale ndi alongo ndi amayi ndi ana” atsopano ndi m’kugawana ndi awa chiyembekezo chosangalatsa cha moyo wosatha mu “nthaŵi irinkudzayo.”—Marko 10:28-30.
20. (a) Ndani omwe akuchita mbali yokulira yolalikira m’maiko ambiri? (b) Kodi ndi chothekera motani kuti Japan imachitira ripoti chiwonkhetso cha maora ochulukira a utumiki wa m’munda chaka chirichonse kuposa chifupifupi dziko lina lirilonse? (c) Ndi funso lotani limene tikachita bwino kulingalira?
20 M’kuwonjezerapo, pali mazana a zikwi za atumiki a Yehova lerolino omwe amachitira ripoti utumiki wopatulika mwezi uliwonse monga apainiya okhazikika kapena othandizira. Ambiri a awa amagwira ntchito mwakhama m’magawo a kwawo. M’maiko ambiri, awa amachita mbali yokulira ya kulalikira, ndipo kaŵirikaŵiri amaitanira pa nyumba zimodzimodzizo mlungu ndi mlungu. Chiyembekezo chawo cha Ufumu chikuwunikiridwa m’kawonekedwe kawo kowala ndi mkhalidwe wa chisangalalo pamene iwo akupanga mabwenzi atsopano ndi kukulitsa chikondwerero chokulira m’magawo mwawo. Apainiya ochulukira amatanthauza maora ochulukira owonongedwa m’kutamanda Mulungu. Kwa zaka zoposa khumi, Japan, kumene unyinji wa Mboni za Yehova ali omwe kale anali Abuda, yachitira ripoti chiwonkhetso cha maora ochulukira a utumiki wa m’munda chaka ndi chaka kuposa dziko lina lirilonse kunja kwa United States. Chimenecho chiri chifukwa chakuti chifupifupi theka la ofalitsa a Ufumu ake akuchita upainiya. Kodi nanunso mungakonze zochita zanu kugawana mu mwaŵi waukulu koposa uwu, utumiki wa upainiya?
21. (a) Ndimotani mmene Mboni zina zimene mkhalidwe wawo sumazitheketsa izo kulembetsa monga apainiya okhazikika zingasonyezerebe mzimu wa upainiya? (b) Ndimotani mmene achichepere angasonyezere mzimu wa upainiya?
21 Pali Mboni zina zomwe ziri “zachangu kaamba ka ntchito yabwino.” (Tito 2:14) Izo zimaphatikizapo anthu achikulire, awo okhala ndi umoyo wovutikira, ambiri okhala ndi mathayo a banja, ndi achichepere omwe adakali pa sukulu amene mikhalidwe yawo singawalole iwo kulembetsa monga apainiya okhazikika. Awa nawonso angasonyeze mzimu wa upainiya mwa kupereka chirikizo lolimbikitsa kwa apainiya, kugawana ndi iwo monga mmene kungathekere mu utumiki, ndi kusungirira mkhalidwe wabwino kulinga ku mwaŵi wawo weniweni wa kuchitira umboni. Achichepere angapange utumiki wa nthaŵi zonse wa Ufumu chonulirapo chawo ndipo, pamene abatizidwa, kugawana mu upainiya wothandizira kwa nthaŵi ndi nthaŵi. Mofanana ndi Timoteo wachichepere, iwo angasinkhesinkhe zinthu izi ndi cholinga chofuna kupanga kupita patsogolo kwauzimu limodzi ndi onse a anthu a Mulungu.—1 Timoteo 4:15, 16.
22. Mosasamala kanthu za mmene mkhalidwe wathu uliri m’moyo, nchiyani chomwe tiyenera kuchipanga kukhala chigamulo chathu, ndipo ndi chotulukapo chabwino chotani?
22 Mosasamala kanthu ndi mkhalidwe wathu m’moyo, lolani kuti tonsefe tifulumizidwe ndi mzimu wa Yehova kugawana kotheratu mu utumiki wake. Lolani kuti “dzanja la Yehova” lipitirize kukhala ndi aliyense wa ife kotero kuti chinganenedwe m’chigwirizano ndi zoyesayesa zathu zodzichepetsa kuti “mawu a [Yehova, NW] anachuluka mwamphamvu nalakika.”—Machitidwe 11:21; 19:20.
Mafunso Kaamba Ka Kubwereramo
◻ Ndimotani mmene ntchito ya umishonale Yachikristu inayambitsidwira, ndipo kodi iyo ikakhala yofutukuka motani?
◻ Ndi mbali yotani imene mtumwi Paulo anali nayo m’kufutukula ntchito ya umishonale?
◻ Ndimotani mmene ntchito ya umishonale inadzutsidwiranso m’nthaŵi zamakono?
◻ Ndi nsonga zotani zimene zapanga utumiki wa umishonale ndi wa upainiya kukhala wokhutiritsa?
◻ Ndimotani mmene tingakhalire ndi mzimu waupainiya lerolino?
[Tchati patsamba 13]
Ntchito ya Ufumu mu Maiko Khumi—1988
(Onsewa anachitira ripoti ofalitsa oposa 100,000)
Dziko Chiŵer.Chapamw. Avereji ya Maora a Opezekapo pa
cha Ofal Apainiya Kulalikira Chikumbutso
U.S.A. 797,104 96,947 161,478,732 1,822,607
Mexico 248,822 32,117 58,061,457 1,004,062
Brazil 245,610 22,725 44,218,022 718,414
Italy 160,584 25,477 43,354,687 330,461
Nigeria 134,543 14,022 27,800,623 398,555
Japan 128,817 52,183 60,626,840 297,171
Germany 125,068 8,416 22,029,942 215,385
Britain 113,412 11,927 22,103,713 211,060
Philippines 107,679 21,320 26,337,621 305,087
France 103,734 9,189 21,598,308 205,256
[Chithunzi patsamba 10]
Paulo ndi Barnaba anyamuka kukapititsa patsogolo ntchito ya umishonale