Zisonyezero Ziŵiri Zazikulu Kwambiri za Chikondi Zomwe Sizinapangidwepo ndi Kale Lonse
“Pakuti Mulungu anakonda dziko lapansi kotero, kuti anapatsa Mwana wake wobadwa yekha, kuti yense wakukhulupirira iye . . . akhale nawo moyo wosatha.”—YOHANE 3:16.
1. Kodi nchiyani chimene chikutanthauzidwa ndi mawu akuti “Mulungu ndi chikondi?”
MULUNGUndiye chikondi.” Mtumwi Yohane analankhula mawuwa kawiri. (1 Yohane 4:8, 16) Inde, Yehova Mulungu ali wachikondi ku utali wakuti iye alinso wanzeru, wolungama, ndi wamphamvu. Kuonjezerapo, iye ALI chikondi. Iye ali wolimbikitsa, ndi wotsanziridwa wa chikondi. Mungadzifunse inu mwini: ‘Kodi ndimadziwa nchifukwa ninji chimenecho chiri chowonadi? Kodi ndingapereke kwa wina wake kalongosoledwe komveka, kochirikizidwa ndi chitsimikiziro kapena zitsanzo kutsimikizira kuti Iye ali chikondi? Ndipo kodi ndi khalidwe lotani limene icho chiri nako pa moyo wanga ndi ntchito zanga?’
2. Kodi Mulungu wapereka zisonyezero zowonekera ziti za chikondi chake?
2 Ndi chikondi chokulira chotani nanga chimene Yehova Mulungu wapereka pa zolengedwa za umunthu zake za padziko lapansi! Taonani pa kukongola kwathunthu ndi ntchito ya maso athu, ntchito yodabwitsa ya mafupa athu olimba, mphamvu ya minofu yathu, ndi kumva kwa kukhudza kwathu. Tiri ndi chifukwa chakufuulira malingaliro a wamasalmo: “Ndikuyamikani chifukwa kuti chipangidwe changa nchoopsa ndi chodabwitsa.” Lingaliraninso, mapiri amphamvu, mitsinje yodikha ya madzi oyera, minda ya maluwa ya mungululu, ndi kulowa kwa dzuwa kwa ulemerero. “Ntchito zanu zichulukadi, Yehova! Munazichita zonse mwanzeru. Dziko lapansi lidzala nacho chuma chanu.”—Masalmo 139: 14; 104:24. .
3, 4. Kodi ndi zitsanzo ziti zimene Malemba Achihebri amapereka kaamba ka zisonyezero za chikondi cha Mulungu?
3 Zisonyezero za chikondi cha Mulungu sizinasiye pamene zolengedwa zake za umunthu zoyamba zinaukira. Mwachitsanzo, Yehova anasonyeza chikondi mwakuwalola anthu awiriwo kubala ana omwe akapindula ndi zopereka za Yehova kudzera mu “mbewu” yake yalonjezo. (Genesis 3:15) Pambuyo pake, iye anauza Nowa kukonza chingalawa kaamba ka kupulumutsira mtundu wa anthu ndi zolengedwa zina za padziko lapansi. (Genesis 6:13-21) Kenaka iye anasonyeza chikondi chachikulu kaamba ka Abrahamu, yemwe anatchedwa bwenzi la Yehova. (Genesis 18:19; Yesaya 41:8) M’kupulumutsa mbadwa za Abrahamu kuchokera ku ukapolo ku Igupto, Mulungu anapereka chisonyezero chowonjezereka cha chikondi chake, monga mmene tiwerengerera pa Deutronomo 7:8:“Chinali chifukwa chakuti Yehova anakukondani inu . . . kuti Yehova anakuturutsani inu ndi dzanja lamphamvu.”
4 Angakhale kuti Aisrayeli anapitirizabe kusonyeza kusayamikira ndi kuukira mobwerezabwereza, Mulungu sanawachotse iwo pa nthawi imodzi. M’malo mwake, iye mwachikondi anachonderera ndi iwo: “Bwererani kuleka njira zanu zoipa, muferanji inu anyumba ya Israyeli?” (Ezekieli 33:11) Komabe, angakhale kuti Yehova ali wotsanziridwa wa chikondi, iye analinso wolungama ndi wanzeru. Nthawi inafika chotero pamene anthu ake oukira anafikira pa malire a kupirira kwake! Iwo anafika pa nsonga yakuti “panalibe kuchiritsa,” chotero anawalola iwo kupita mu ukapolo ku Babulo. (2 Mbiri 36:15, 16) Ngakhale pamenepo chikondi cha Yehova sichinaime kotheratu. Iye anawona ku icho kuti pambuyo pa zaka 70 otsalira a iwo analoledwa kubwerera ku dziko lawo lobadwira. Chonde werengani Masalmo 126 ndi kuwona kuchokera ku iyo ndi motani mmene awo amene anabwerera anamvera ponena za icho.
Kukonzekera Kaamba ka Chisonyezero Chake Chachikulu Kwambiri cha Chikondi
5. Kodi nchifukwa ninji chinganenedwe kuti kutumizidwa kwa Mwana wake ku dziko lapansi kunali chisonyezero cha chikondi cha Mulungu?
5 Kupitirirabe mu mbiri nthawi inafika kaamba ka Yehova kupereka chisonyezero chake chachikulu kwambiri cha chikondi chake. Chinalidi chikondi cha kudzipereka. Kukonzekera kaamba ka ichi, Mulungu anapangitsa moyo wa Mwana wake wobadwa yekha kusinthidwa kuchoka ku mkhalidwe wauzimu kumwamba kupita m’mimba ya namwali Wachiyuda Mariya. (Mateyu 1:20-23; Luka 1:26-35) Tangolingalirani za chiyanjo chapadera chomwe chinalipo pakati pa Yehova ndi Mwana wake. Timawerenga ponena za kukhalapo kwa Yesu asanakhale munthu pansi pa chisonyezero chanzeru chochitidwira chitsanzo: “Ndinali pambali pake [Mulungu] ngati mmisiri, ndinamsekeretsa tsiku ndi tsiku ndi kukondwera pamaso pake nthawi zonse.” (Miyambo 8:30, 31) Chotero kodi simungavomereze kuti kulola Mwana Wake wobadwa yekha kuchoka pamaso pake inali nsembe kaamba ka Yehova?
6. Kodi ndi chikondwerero cha utate chotani chimene Yehova anayenera kukhala nacho mu moyo woyambirira wa Yesu?
6 Mosakaikira, Yehova anayang’ana ndi chidwi ndi chikondwerero chachikulu pakukula kwa mwana wake kuyambira pa kubadwa kunka mtsogolo. Mzimu woyera wa Mulungu unakuta Mariya kotero kuti chiri chonse chisawononge mwana womakulayo. Yehova anawonanso kuti Yosefe ndi Mariya anapita ku Betelehemu kaamba ka kulembetsa kotero kuti Yesu akabadwire kumeneko m’kukwaniritsa Mika 5:2. Kudzera mwa mngelo, Mulungu anachenjeza Yosefe ponena za makonzedwe akupha a Mfumu Herode, kumupangitsa Yosefe ndi banja lake kuthawira ku Igupto mpaka Herode atafa. (Mateyu 2:13-15) Mulungu angakhale atapitirizabe chikondwerero chake mkupita patsogolo kwa Yesu. Chinali chosangalatsa chotani kaamba ka Mulungu kuwona Yesu wa zaka zakubadwa 12 akuzizwitsa aphunzitsi ndi ena mu kachisi ndi mafunso ndi mayankho!—Luka 2:42-47.
7. Kodi ndi zisonyezero zitatu ziti zomwe zimatsimikizira chikondwerero cha Mulungu mu uminisitala wa Yesu?
7 Pambuyo pa zaka khumi mphambu zisanu ndi zitatu Yehova anali kuwona pamene Yesu anapita kwa Yohane Mbatizi kuti amumize. Kenaka iye mokondwerera anatumiza mzimu wake woyera pa Yesu ndi kunena kuti: “Uyu ndiye Mwana wanga wokondedwa, mwa iyeyu ndikondwera.” (Mateyu 3:17) Tate aliyense wa Chikristu angalingalire ndi chosangalatsa chotani mmene chinaliri kwa Mulungu kutsatira uminisitala wa Yesu ndi kuwona njira mu imene iye mwachindunji anatsogozera ulemerero wonse kwa Atate wake wakumwamba. Pa nthawi ina Yesu anatenga ena a atumwi ake paphiri lokwezeka. Kumeneko Yehova anamupangitsa Kristu kuwala ndi ulemerero woposa, ndipo Atate anati: “Uyu ndiye mwana wanga wokondedwa, mwa iyeyu ndikondwera, mverani iye.” (Mateyu 17:5) Yehova analola liwu lake kumvedwa kachitatu mkuyankha kwake kupembedzero la Yesu kwa Mulungu kuyeretsadzina lake. Yehova nati: “Ndalilemekeza ndipondidzalilemekezanso.” Mwachiwonekere ichi chinali kwenikweni kaamba ka phindu la Yesu popeza ena omwe anali naye anaganiza kuti mngelo analankhula, koma pamene ena anaganiza kuti kunachita bingu.—Yohane 12:28, 29.
8. Kodi ndimotani mmene mumadzimverera ponena za chikondi cha Mulungu?
8 Kodi nchiyani chomwe mwagamulapo kuchokera ku kubwereramo kwachidule uku kwa zochita za Mulungu kulinga kwa Mwana wake ndi chikondwerero chake mwa iye? Chiyenera kukhala chodziwikiratu kuti Yehova amakondadi Mwana wake wobadwa yekha. Ndi chimenecho m’maganizo, ndi kuyamikira mmene chifupifupi kholo liri lonse laumunthu lingamverere kulinga kwa mwana mmodzi yekha, lingalirani chimene chinachitika potsatira—imfa ya nsembe ya Yesu.
Chisonyezero Chachikulu Kwambiri cha Chikondi
9, 10. Kodi nchiyani chomwe chinali chisonyezero chachikulu kwambiri cha chikondi cha Mulungu kulinga ku mtundu wa anthu, kukwaniritsa uthenga uti wa Malemba?
9 Baibulo limasonyeza kuti Atate wathu wakumwamba ali wa chifundo. Timawerenga pa Yesaya 63:9 ponena za anthu ake Israyeli: “M’mazunzo awo onse iye anazunzidwa, ndipo mthenga wakuimirira pamaso pake anawapulumutsa; m’kukonda kwake ndi m’chisomo chake iye anawaombola, nawabereka nawanyamula masiku onse akale.” Chinali chozunza mowonjezereka chotani kwa Yehova kumva ndi kuwona Yesu “akulira mwamphamvu ndi misozi.” (Ahebri 5:7) Yesu anapemphera mu njira imeneyo m’munda wa Getsemane. Iye anapangidwa kukhala wandende, anakumana ndi chiyeso chosekedwa, anamenyedwa ndi kumangidwa zingwe, ndipo anali ndi chisoti chaminga choikidwa pa mutu pake. Kumbukirani, Atate wake wachikondi anali kuwona zonsezi. Iye anawonanso Yesu atakhumudwa pansi pa kulemera kwa mtengo wophera ndipo anawonanso Mwana wake pomalizira ali kupachikidwa pa mtengo wozunzirapo. Tiyeni tisaiwale kuti Mulungu akanalewetsa kuvutika kumeneku kumbali ya Mwana wake wokondedwa. Komabe Yehova anamulola Yesu kuvutika. motero. Popeza Mulungu ali ndi malingaliro, kwa iye kuchitira umboni zochitika izi mosakaikira kunapangitsa kupweteka komwe sanakhale nako ndi kale lonse ndipo sadzakhala nakonso.
10 M’kayang’anidwe ka zochitikazi, tingawone ndi tanthauzo lotani lomwe liri m’mawu a Yesu kwa Nikodemo: “Pakuti Mulungu anakonda dziko lapansi kotero, kuti anapatsa Mwana wake wobadwa yekha, kuti yense wakukhulupirira iye asatayike, koma akhale nawo moyo wosatha.” (Yohane 3:16) Wokhala ndi tanthauzo lofanafanalo ali mawu a Yohane, mtumwi wokondedwa wa Yesu: “Umo chidawonekera chikondi cha Mulungu kwa ife, chifukwa Mulungu anatuma Mwana wake wobadwa yekha alowe m’dziko lapansi . . . monga nsembe yowombola machimo athu.”—1 Yohane 4: 9, 10.
11. Kodi ndimotani mmene mtumwi Paulo amasonyezera chisonyezero chachikulu kwambiri cha chikondi cha Mulungu?
11 Inu mungamvetsetse, ndiyeno, nchifukwa ninji mtumwi Paulo pa Aroma 5:6-8, anagogomezera chikondi chokulira cha Yehova Mulungu m’mawu awa: “Pakuti pamene tinali chikhalire ofooka, pa nyengo yake Kristu anawafera osapembedza. Pakuti ndi chivuto munthu adzafera wina wolungama; pakuti kapena wina adzalimbika mtima kufera munthu wabwino. Koma Mulungu atsimikiza kwa ife chikondi chake cha mwini yekha m’menemo, kuti pokhala ife chikhalire ochimwa, Kristu adatifera.” Zowonadi, mkutumiza Mwana wake wobadwa yekha kubwera pano padziko lapansi, kuvutika, ndi kufa imfa yochititsa manyazi kwambiri, Yehova Mulungu anapanga chisonyezero cha chikondi chachikulu kwambiri.
Chisonyezero Chachiwiri Chachikulu Kwambiri
12, 13. (a) Kodi ndi mwanjira yotani mmene chisonyezero cha chikondi cha Yesu chinaliri chapadera? (b) Kodi ndi motani mmene Paulo akukokera chidwi ku chikondi chokulira cha Yesu?
12 ‘Nchiyani,’ mungafunse, ‘chomwe chinali chisonyezero chotsatirapo chachikulu kwambiri cha chikondi?’ Yesu Kristu anati: “Palibe munthu alinacho chikondi kuposa ichi, chakuti munthu ataya moyo wake chifukwa cha abwenzi ake.” (Yohane 15:13) Zowona, m’mbiri yonse ya munthu, pakhala ena omwe anapereka miyoyo yawo kaamba ka ena. Koma wawo unali moyo wokhala ndi malire; mwamsanga kapena mochedwerapo iwo anafa. Komabe, Yesu Kristu, anali munthu wangwiro wokhala ndi moyo wowongoka. Iye sanali kuyang’anizana ndi imfa ya cholowa monga mmene mtundu wonse wa anthu uliri; panalibenso wina wake amene mokakamiza akanatenga moyo wa Yesu popanda iye kuvomereza icho. (Yohane 10:18; Ahebri 7:26) Kumbukirani mawu ake: “Kapena uganiza kuti sindingathe kupemphera Atate wanga, ndipo iye adzanditumizira tsopano lino mabungwe a angelo oposa khumi ndi awiri?”—Mateyu 26:53; Yohane 10:17, 18.
13 Mowonjezera tingayamikire chikondi chophatikizidwamo m’zimene Yesu anachita mwakuyang’ana pa chochitika chotsatirachi: Iye anasiya malo ake aulemerero monga cholengedwa chauzimu kumwamba kumene iye anakhala monga mnzake wapafupi ndi wogwira ntchito mnzake wa Wolamulira wa dziko lonse ndi Mfumu ya nthawi zosatha. Chikhalirebe, chifukwa cha chikondi chopanda dyera, Yesu anachita monga momwe mtumwi Paulo akutiuzira: “Ameneyo, pokhala nawo mawonekedwe a Mulungu, sanachiyesa cholanda kukhala wofanana ndi Mulungu, koma anadzikhuthula yekha natenga mawonekedwe a kapolo nakhala m’mafanizidwe a anthu; ndipo popeza mawonekedwe ngati munthu, anadzichepetsa yekha nakhala womvera kufikira imfa ndiyo imfa ya pamtengo wozunzirapo.”—Afilipi 2:6-8.
14. Kodi ndimotani mmene mneneri Yesaya anatsimikizirira ku chisonyezero chachikulu cha chikondi cha Yesu?
14 Kodi chimenecho sichinali chisonyezero cha chikondi? Icho mowonadi chinali—chachiwiri kokha kwa chija cha Yehova Mulungu, Atate wake wakumwamba. Mawu aulosi a Yesaya mutu 53 amatsimikizira ku zonse zimene Yesu anapirira: “Iye ananyozedwa ndipo kukanidwa ndi anthu; munthu wazisoni ndi wodziwa zowawa. . . . Zowonadi iye ananyamula zowawa zathu ndi kusenza zisozi zathu; koma ife timuyesa wokhomedwa, wokanthidwa ndi Mulungu, ndi wovutidwa. Koma iye analasidwa chifukwa cha zolakwa zathu, natundudzidwa chifukwa cha mphulupulu zathu. . . . ndipo ndi mikwingwirima yake ife tachiritsidwa. . . . Iye anathira moyo wake ku imfa.”—Yesaya 53: 3-5, 12.
15, 16. Kuti inali nsembe ya Yesu zingawonedwe kuchokera ku mawu ake ati?
15 Chifukwa cha zonse zimene zinamangidwa pamodzi ndi imfa yake, Yesu anapemphera m’munda wa Getsemane: “Atate, ngati nkutheka, chikho ichi chindipitirire ine; koma si monga ndifuna ine, koma inu.” (Mateyu 26:39) Kodi nchiyani chimene Yesu anali kupempha pamene ananena mawu amenewo? Kodi iye anali kufuna kupempha kuchotsedwa kukhala “Mwana wankhosa wa Mulungu amene achotsa chimo lake ladziko lapansi”? (Yohane 1:29) Icho sichikanatanthauza chimenecho, popeza kuti nthawi yonseyo Yesu anakhala ali kuuza ophunzira ake kuti iye adzavutika ndi kufa, angakhale kulongosola mtundu wa imfa imene iye adzafa. (Mateyu 16:21; Yohane 3:14) Chotero Yesu anayenera kukhala ndi china chake m’maganizo pamene anali kupemphera motero.
16 Mosakaikira Yesu anali wodera nkhawa ponena za mlandu wakuchitira mwano umene iye anawona kuti udzaperekedwa motsutsana ndi iye, liwongo loipa kwambiri limene Myuda akanakhala nalo. Nchifukwa ninji iye anali wodera nkhawa ponena za mlandu wabodza umenewu? Chifukwa chakuti imfa yake pansi pa mikhalidwe imeneyo ikanabweretsa chitonzo pa Atate wake wakumwamba. Inde, Mwana wopanda banga wa Mulungu, yemwe anakonda chilungamo ndi kudana nacho choipa ndi yemwe anabwera pa dziko lapansi kudzalemekeza dzina la Atate wake, anayenera tsopano kuphedwa ndi anthu a Mulungu monga wochitira mwano Yehova Mulungu.—Ahebri 1:9; Yohane 17:4.
17. Kodi nchifukwa ninji mtundu wa imfa imene Yesu analikuyang’anizana nayo inatsimikizira kukhala yovuta kwa iye?
17 Poyambirira mu utumiki wake Yesu ananena kuti: “Koma ndiri ndi ubatizo ndikabatizidwe nawo, ndipo ndikanikizidwa ine kufikira ukatsirizidwa!” (Luka 12:50) Tsopano panali pachimake pa ubatizo umenewo. Mwachiwonekere chimenecho ndicho chifukwa chake thukuta lake linagwa ngati madontho a mwazi pamene iye anapemphera. (Luka 22:44) Kuwonjezerapo, panali thayo lalikulu kwambiri lomwe linali pamapewa ake usiku umenewo. Thayo loposa kuthekera kwathu kwa kulimvetsetsa. Iye anadziwa kuti anayenera kutsimikizira kukhala wokhulupirika chifukwa ngati iye akanalephera, kukanakhala kuchititsidwa manyazi kotani nanga kwa Yehova! Satana akananena kuti iye anali wolondola ndi kuti Yehova Mulungu anali wabodza. Koma ndi kuchititsidwa manyazi kotani nanga kumene Satana Mdyerekezi anakumana nako chifukwa Yesu anatsimikizira kukhala wokhulupirika kufikira imfa! Mwakutero anatsimikizira Satana kukhala maziko abodza, wabodza wamphamvu, ndi woipa.—Miyambo 27:11.
18. Kodi nchifukwa ninji Yesu anali pansi pa kuvutika koopsa usiku umenewo?
18 Yehova Mulungu anali ndi chidaliro choterocho mu kumvera kwa Mwana wake kotero uti iye ananeneratu kuti Yesu adzatsimikizira kukhala wokhulupirika. (Yesaya 53:9-12) Ndiponso Yesu anadziwa kuti thayo la kusunga umphumphu linali pa iye. Iye akanatha ulephera. Iye akanatha kuchimwa. (Luka 12:50) Moyo wake wosatha ndi wa mtundu wonse a anthu unali pa sikelo usiku umenewo. Chinali chinthu chovuta kwambiri chotani! Ngati Yesu anafooka ndi kuchimwa, iye sakanatha upempha kaamba ka chifundo pa maziko nsembe ya winawake , monga mmene ife nthu opanda ungwiro tingachitire.
19. Kodi nchiyani chimene Yesu anakwaniritsa mwanjira yake yopada dyera?
19 Mwachiwonekere, kupirira kwa Yesu pa Nisan 14, 33 .E. , chinali chisonyezero chachikulu kwambiri cha chikondi chopanda dyera chomwe sichinapangidwepo ndi munthu aliyense, chachiwiri kokha ku chija cha Yehova ulungu. Ndipo ndi zinthu zazikulu zotani imene iye anakwaniritsa kaamba ka ife mwa mfa yake! Ndi imfa yake iye anakhala “Mwana ankhosa wa Mulungu amene achotsa chimo ake la dziko lapansi.” (Yohane 1:29) Iye anatsegula njira kaamba ka otsatira mapazi ake 14, 000 kukakhala mafumu ndi ansembe ndi kulamulira limodzi ndi iye kwa zaka chikwi. (Chivumbulutso 20:4, 6) Mkuwonjezerako, “khamu lalikulu” la “nkhosa zina” lerolino limapindula kuchokera ku nsembe ya Kristu ndipo lingayembekezere kupulumuka mapeto a dongosolo iri lakale la zinthu. Awa adzakhala oyambirira kusangalala ndi madalitso a paradaiso pa dziko lapansi. Mosakaikira kudzakhalanso mabiliyoni a mtundu wa anthu omwe adzaukitsidwa kuchokera kwa akufa monga chotulukapo cha zimene Yesu anachita. Iwonso, adzakhala ndi mwawi wa kusangalala ndi moyo wosatha pa Paradaiso pa dziko lapansi. (Chivumbulutso 7:9-14; Yohane 10:16; 5:28, 29) Mowonadi, “pakuti monga mawerengedwe amalonjezano a Mulungu ali, [iwo akhala, NW] Eya mwa iye,” kunena kuti, kudzera mwa Yesu Kristu.—2 Akorinto 1:20.
20. Kodi ndimotani mmene ife tiyenera kuvomerezera ku zisonyezero ziŵiri zazikulu kwambiri zachikondi ku mbali ya Yehova Mulungu ndi Yesu Kristu?
20 Chiri mowonadi choyenerera kusonyeza chiyamikiro kaamba ka zonse zimene Yehova Mulungu ndi Yesu Kristu anachita mmalo mwathu mwa kutipatsa ife zisonyezero zazikulu kwambiri zimenezi za chikondi. Timafunikiradi kuwapatsa iwo chiyamikiro choterocho, ndipo kuti tipinduledi mokulira ku icho, tiyenera kusonyeza chiyamikiro chimenecho. Nkhani yotsatirayi idzasonyeza zina za njira zabwino koposa mmene tingachitire ichi.
Kodi Mukukumbukira?
◻ Kodi ndi zisonyezero ziti za chikondi cha Mulungu zimene mtundu wonse wa anthu ungaziwone?
◻ Kodi tingadziwe motani kuti Yehova anavutika pamene anawona Mwana wake akuvutika?
◻ Kodi ndimotani mmene imfa ya Yesu mmalo mwa anthu iri yosiyana ndi ija ya ena omwe angakhale atapereka miyoyo yawo?
◻ Kodi tiyenera kuyambukiridwa motani ndi chikondi chomwe chinasonyezedwa kwa ife ndi Yehova ndi Yesu?