Kodi Bizinesi Yanu Idzakutayitsani Chiyani?
MKAZI wa pulezidenti wa dziko la ku South America anaimbidwa mlandu wa kupereka zikwi mazana ambiri za madola m’makampani a achibale ake mwa kunamiriza kuti zinali kupita m’mapangano a ntchito. Stockbroker wina wazaka 38 mu India anamangidwa ndi kulandidwa nyumba yake yokongola kwambiri ndi galimoto zake zokwanira 29 chifukwa cha kukhala ndi mbali mu mlandu wa kuba $1.6-biliyoni kupyolera m’mabanki ndi stock market. Mu Philippines, zikwi zambiri za nzika za chisumbu china zimakhalira moyo ntchito yosaloledwa ya kupanga mfuti zakumanja. Zikumveka kuti, kuti apitirizebe ndi ntchito yawo ya ndalama zambiri imeneyi, nthaŵi zonse amapatsa chiphuphu akuluakulu aboma kuti asachitepo kanthu.
Inde, kusaona mtima ndi chinyengo m’mabizinesi kuli kofala padziko lonse. Ndipo kaŵirikaŵiri zimatayitsa ozichitawo udindo ndi ulemu, ndiponso ndalama.
Bwanji ponena za inu? Kodi muli ndi bizinesi? Kapena kodi mukulingalira za kuyamba bizinesi? Kodi idzakutayitsani chiyani? Mosapeŵeka, kukhala ndi bizinesi kudzakutayitsani kanthu kena. Zimenezi si zoipa kwenikweni. Komabe, nkwanzeru kuŵerengera mtengo musanayambe bizinesi iliyonse kapena musanapange zosankha pa imene ilipo kale. (Luka 14:28) Bokosi limene lili patsamba 31 limasonyeza zotayika zina zimene muyenera kuzilingalira.
Mwachionekere, kukhala ndi bizinesi si kwapafupi. Kwa Mkristu, pali mathayo auzimu ndi a makhalidwe amene ayenera kuwalingalira. Kodi mungatayikidwe zinthuzo ndi kukhalabe wokhazikika kuuzimu? Kodi zotayika zina zimasemphana ndi makhalidwe abwino kwa inu? Kodi ndi makhalidwe otani amene adzakuthandizani kudziŵa zotayika zoyenera ndi zosayenera?
Sungani Ndalama Pamalo Ake
Ndalama nzofunika kuti muyendetse bizinesi, ndipo chiyembekezo chimakhala chakuti bizinesi idzabweretsa ndalama zokwanira zochirikizira banja. Komabe, zolinga za ndalama zingasokonezedwe mosavuta. Umbombo ungaloŵepo. Kwa anthu ambiri, pakaoneka ndalama zinthu zina zonse zimakankhidwira pambali. Komabe, mlembi wina wa buku la Baibulo la Miyambo, Aguri, anasonyeza lingaliro loyenera pamene anati: “Musandipatse umphaŵi, ngakhale chuma, mundidyetse zakudya zondiyenera.” (Miyambo 30:8) Iye anazindikira phindu la kukhala wokhutira ndi chakudya chokwanira chabe—sanafune “kupha chuma,” monga momwe ena amanenera m’bizinesi.
Komabe, umbombo ungachititse wina kuiŵala mkhalidwe umenewu pamene wotchedwa mwaŵi wadzaoneni upezeka. Mtumiki woyendayenda wa Mboni za Yehova m’dziko lina losatukuka anasimba nkhani yotero. Kampani ina yofuna investment capital inapereka chithunzi chakuti oikizira ndalama kwa iyo akaŵirikiza kaŵiri ndalama zawo mofulumira, mwinamwake m’miyezi yoŵerengeka chabe. Kupeza ndalama kosavuta kumeneku kunakopa ambiri kukaikiza ndalama zawo. Mtumiki woyendayendayo akuti: “Ena anasusukira kwambiri zimenezo. Sanali kufunsa mafunso okwanira, ndipo anakongola ndalama [kuti akaikize].”
Mosiyana ndi amenewo, anthu ena aŵiri anakafufuza ofesi ya kampani imeneyi asanaikize ndalama. Pempho lawo lakuti aone malo awo ogwirira ntchito linakanidwa. Zimenezi zinawachititsa kuikayikira kampaniyo. Ichi chinakhaladi chitetezo kwa iwo, popeza kuti patapita milungu yoŵerengeka chabe, programu yachinyengoyo inavumbuluka, ndipo anthu anamangidwa. Tangolingalirani za kutayikidwa kwa awo amene sanafufuze poyamba. Iwo sanataye ndalama zokha komanso mwinamwake mabwenzi amene anawakongoza amene sanathe kuwabwezera pamene programuyo inagwa. M’nkhani za ndalama, kumakhala kwanzeru chotani nanga kugwiritsira ntchito chilangizo cha pa Miyambo 22:3: “Wochenjera aona zoipa, nabisala; koma achibwana angopitirira, nalipitsidwa”!
Sungani Mawu Anu
Bwanji ngati bizinesi siiyenda bwino? Salmo 15:4 limathokoza munthu amene asunga pangano lake ngakhale ngati kuchita motero kudzachititsa zinthu kusamuyendera bwino: “Atalumbira kwa tsoka lake, sasintha ayi.” Ndi kopepuka kwa munthu kusunga mawu ake pamene zinthu zikuyenda bwino. Koma kumakhala chiyeso cha umphumphu pamene kumutayitsa ndalama.
Kumbukirani chitsanzo cha m’Baibulo cha m’nthaŵi ya Yoswa. Agibeoni anayendetsa zinthu kotero kuti akalonga a Israyeli achite nawo pangano ndi kuti asawawononge. Kwenikweni, iwo anali mbali ya mtundu umene unaonedwa kukhala chiwopsezo kwa Israyeli. Pamene chinyengocho chinadziŵika, “ana a Israyeli sanawakantha, pakuti akalonga a msonkhano adawalumbirira kwa Yehova.” (Yoswa 9:18) Ngakhale kuti gulu limeneli linachokera ku dziko la adani, akalongawo anakuona kukhala kofunika kusunga mawu awo. Ndipo zochitika zotsatirapo zimasonyeza kuti zimenezi zinakondweretsa Yehova.—Yoswa 10:6-11.
Kodi inunso mudzasunga mapangano a bizinesi yanu ngakhale ngati zinthu siziyenda mmene munaganizira?a Kuchita zimenezo kudzakuchititsani kufanana kwambiri ndi Yehova, amene nthaŵi zonse amasunga mawu ake.—Yesaya 55:11.
Khalani Oona Mtima
Kuona mtima kuli paupandu, kapena pangozi ya kusoloka m’mabizinesi amakono. Ena m’mabizinesi ofanana ndi anu angagwiritsire ntchito njira zosaona mtima kuti apeze ndalama zochuluka. Angakhale osaona mtima posatsa malonda. Angabe dzina la kampani ina ndi kuliika pa chinthu chopanga iwo. Kapena angasonyeze chinthu chotchipa kukhala chodula. Zonsezi ndi njira za kusaona mtima. Amene amazichita ali ngati “oipa” amene, malinga ndi kunena kwa Asafu, “awonjezerapo pa chuma chawo,” mwachionekere mwa njira yachinyengo.—Salmo 73:12.
Kodi inu, monga Mkristu, mudzagwiritsira ntchito njira zachinyengo? Kapena kodi mungakonde kutsogozedwa ndi makhalidwe a Baibulo, monga akuti: “Sitinamchitira munthu chosalungama, sitinaipsa munthu, sitinachenjerera munthu”; “takaniza zobisika za manyazi, osayendayenda mochenjerera”; “miyeso yosiyana inyansa Yehova, ndi mulingo wonyenga suli wabwino”? (2 Akorinto 4:2; 7:2; Miyambo 20:23) Kumbukirani, myambitsi wa kusaona mtima sali wina aliyense koma Satana Mdyerekezi, “atate wake wa bodza.”—Yohane 8:44.
Ena angatsutse ndi kunena kuti: ‘Ndi kovuta kuchita bizinesi popanda kugwiritsira ntchito njira zosaona mtima mofanana ndi ena.’ Apa ndi pamene Mkristu angasonyezere chikhulupiriro chake mwa Yehova. Kuona mtima kumatsimikiziridwa kukhala kwenikweni pamene kuyesedwa mwa kukutayitsani kanthu kena. Kunena kuti munthu sangakhale ndi moyo popanda kukhala wosaona mtima ndiko kunena kuti Mulungu samasamalira amene amamkonda. Munthu amene ali ndi chikhulupiriro choona mwa Yehova amadziŵa kuti Mulungu angagaŵire zofunika kwa atumiki ake m’dziko lililonse ndi mumkhalidwe uliwonse. (Ahebri 13:5) Zoona, wina angafunikire kukhutira ndi ndalama zocheperapo poyerekezera ndi zimene anthu osaona mtima amapeza, koma kodi kumeneku sindiko kutayikidwa kanthu kwabwino kuti tikhale ndi dalitso la Mulungu?
Kumbukirani, kusaona mtima kuli ngati mwala wobwerera kwa mwini wake utaponyedwa. Ngati wabizinesi adziŵika kukhala wosaona mtima, makasitomala ake ndi omuodetsa malonda kaŵirikaŵiri amamsiya. Iye angawagwire pamaso kamodzi, koma imeneyo ndiyo ingakhalenso nthaŵi yomaliza. Kumbali ina, wabizinesi woona mtima kaŵirikaŵiri amapatsidwa ulemu ndi ena. Samalani kuti musasochezedwe ndi lingaliro lonyenga lakuti, ‘Aliyense amachita, motero ZILIBE KANTHU.’ Chilangizo cha Baibulo nchakuti, “Usatsata unyinji wa anthu kuchita choipa.”—Eksodo 23:2.
Bwanji ngati mnzanu wa bizinesi amene mwakhala naye kwa nthaŵi yaitali sali Mkristu ndipo si nthaŵi zonse pamene amatsatira malangizo a Baibulo. Kodi kukakhala koyenera kugwiritsira ntchito zimenezi monga chodzikhululukira chopeŵera thayo lanu pamene chinthu chosemphana ndi malemba chikuchitika? Kumbukirani zitsanzo zonga Adamu ndi Sauli. M’malo mwa kupeŵa tchimo, iwo anagonja ku chitsenderezo cha ena ndi kuimba mlandu anzawo. Anatayikidwa kwakukulu chotani nanga!—Genesis 3:12, 17-19; 1 Samueli 15:20-26.
Chitani Nawo Moyenera Okhulupirira Anzanu
Kodi pali zotayikidwa zimene ziyenera kulingaliridwa poloŵa m’bizinesi ndi alambiri a Yehova anzanu? Pamene mneneri Yeremiya anagula munda m’mudzi wa kwawo wa Anatoti kwa msuwani wake, iye sanangompatsa ndalama ndi kugwirana chanza. M’malo mwake, iye anati: “Ndinalemba chikalatacho, ndichisindikiza, ndiitana mboni zambiri, ndiyesa ndalama m’miyeso.” (Yeremiya 32:10) Kuchita mapangano olembedwa koteroko kungaletse kusamvana kumene kungabukepo pambuyo pake ngati mikhalidwe isintha.
Koma bwanji ngati mbale Wachikristu akuoneka kuti wakuchitirani moipa pabizinesi? Kodi muyenera kumpereka kukhoti? Baibulo nlomvekera bwino kwambiri pamfundo imeneyi. “Kodi akhoza wina wa inu, pamene ali nawo mlandu pa mnzake, kupita kukaweruzidwa kwa osalungama, osati kwa oyera mtima?” anatero Paulo pofunsa. Bwanji ngati vuto silinathetsedwe mokhutiritsa panthaŵiyo? Paulo anawonjezera kuti: “Pamenepo pali chosoŵa konsekonse mwa inu, kuti muli nayo milandu wina ndi mnzake. Chifukwa ninji simusankhula kulola kuipsidwa? simusankhula chifukwa ninji kulola kunyengedwa?” Tangolingalirani za mbiri yoipa imene ingakhale pa gulu Lachikristu ngati akunja amva kuti Akristu oona akulimbana m’khoti! Kodi kungakhale kuti m’zochitika zoterozo chikondi cha pa ndalama ndicho chakula kuposa chikondi pa mbale? Kapena kodi wina waipitsidwa dzina ndipo kubwezera ndiko kwakhala chinthu chachikulu m’maganizo mwake? Uphungu wa Paulo umasonyeza kuti m’nkhani zoterozo kukakhala bwino kulola kutayikidwa kuposa kupita kukhoti.—1 Akorinto 6:1, 7; Aroma 12:17-21.
Ndithudi, ilipo njira ya Malemba yothetsera mikangano yoteroyo mkati mwa mpingo. (Mateyu 5:37; 18:15-17) Pothandiza abale oloŵetsedwamo kuti atsatire njira zoyenera, oyang’anira Achikristu angapereke uphungu wothandiza kwa onse okhudzidwa. Kungaoneke kukhala kosavuta kuvomereza malangizo a Baibulo pokambitsirana zimenezo, koma kodi pambuyo pake mudzasonyeza kuti munamvetseradi mwa kugwiritsira ntchito uphungu wopatsidwawo? Kukonda Mulungu ndi Akristu anzathu kudzatikakamiza kuchita zimenezo.
Mosakayikira konse, kukhala ndi bizinesi kudzakutayitsani kanthu kena. Tikhulupirira kuti kudzakhala kutayikidwa kwanzeru. Pamene muyang’anizana ndi zosankha kapena mikhalidwe yokayikiritsa, kumbukirani kuti pali zinthu zambiri m’moyo zofunika kwambiri kuposa ndalama. Mwa kusunga ndalama m’malo ake, kusunga mawu athu, kukhala woona mtima, ndi kuchita ndi anzathu abizinesi m’njira Yachikristu, tingasamale ndi kuona kuti bizinesiyo siikutitayitsa nthaŵi yochuluka ndi ndalama zambiri, ndipo panthaŵi imodzimodziyo, tingakhalebe ndi mabwenzi athu, chikumbumtima chabwino, ndi unansi wabwino ndi Yehova.
[Mawu a M’munsi]
a Onani chitsanzo cha makono cha kusunga mawu a munthu m’bizinesi m’nkhani yakuti “My Word My Bond” mu Awake! ya May 8, 1988, masamba 11-13.
[Bokosi patsamba 31]
Zinthu Zimene Bizinesi Yanu Ingakutayitseni
Nthaŵi: Kuyendetsa bizinesi yanuyanu kaŵirikaŵiri kumatenga nthaŵi yochuluka kuposa kulembedwa ntchito pakampani. Kodi iko kudzadodometsa ndandanda yanu ya zochita, ndi kukusiyani ndi nthaŵi yochepa chabe yochita zinthu zauzimu zofunika? Kumbali yabwino, kodi mudzakhala wokhoza kulinganiza zinthu mwa njira yakuti mukhale ndi nthaŵi yochuluka yochitira chifuniro cha Mulungu? Ngati zili choncho, mukuchita bwino. Koma samalani! Zimenezi nzosavuta kunena osati kuchita.
Ndalama: Kupeza ndalama kumalira ndalama. Kodi chikufunika nchiyani kuti muyambe bizinesi yanu? Kodi muli nazo ndalama zoyambira? Kapena kodi mudzachita zokongola? Kodi muli pamalo abwino ngakhale zina zitatayika? Kapena kodi simungakhoze kubwezeretsa zotayikazo ngati zinthu siziyenda bwino?
Mabwenzi: Chifukwa cha mavuto obukapo m’zochita za tsiku ndi tsiku, mabizinesi a ambiri awatayitsa mabwenzi awo. Ngakhale kuti kuthekera kwa kupeza mabwenzi kumakhalapo, maudani amakhalanso othekera kwambiri. Bwanji ngati mabwenzi ameneŵa ali abale athu Achikristu?
Chikumbumtima Chabwino: Lingaliro lofala la bizinesi m’dziko la lero nlakuti “Watsala watsala” kapena “Kodi ndidzapindulapo chiyani?” Ana a sukulu oposa pa 70 peresenti pa kufufuza kochitidwa ku Ulaya ananenetsa kuti makhalidwe abwino alibe malo kwenikweni m’moyo wa bizinesi. Nzosadabwitsa kuti chinyengo, kusaona mtima, ndi machitachita okayikitsa a bizinesi akhala ofala. Kodi mudzakhumbira kutsatira zimenezo?
Unansi Wanu ndi Yehova: Kachitidwe kalikonse m’bizinesi kamene kamasemphana ndi malamulo ndi malangizo a Mulungu, ngakhale ngati kangakhale kofala m’bizinesi, kadzawononga unansi wa munthuyo ndi Mlengi wake. Zimenezi zingamutayitse chiyembekezo chake cha moyo wamuyaya. Kodi zimenezi sizikakhala kutayikidwa kopambanitsa kwa Mkristu wokhulupirika, mosasamala kanthu za phindu la zinthu zakuthupi limene lingakhalepo?
[Zithunzi patsamba 31]
Kodi nchiyani chimene chidzaletsa kusamvana pambuyo pake? Pangano lapakamwa kapena lolembedwa?