MUTU 8
Yehova Amafuna Kuti Anthu Ake Akhale Oyera
“Kwa munthu wokhalabe woyera, mudzadzisonyeza kuti ndinu woyera.”—SALIMO 18:26.
1-3. (a) N’chifukwa chiyani mayi wachikondi amaonetsetsa kuti mwana wake ndi waukhondo? (b) N’chifukwa chiyani Yehova amafuna kuti anthu ake azikhala oyera?
TIYEREKEZE kuti mayi wachikondi akukonzekeretsa mwana wake kuti azipita kusukulu. Mayiyu akuonetsetsa kuti mwana wakeyo wasamba komanso wavala zovala zoyera. Zimenezi zimathandiza mwanayo kuti azioneka waukhondo komanso kuti anthu aziona kuti makolo ake amamusamalira.
2 Atate wathu Yehova amafuna kuti tizikhala aukhondo komanso oyera. (Salimo 18:26) Amadziwa kuti kukhala oyera n’kothandiza kwambiri kwa ifeyo. Komanso tikamayesetsa kukhala oyera, timalemekeza Yehova.—Ezekieli 36:22; werengani 1 Petulo 2:12.
3 Kodi kukhala oyera kumatanthauza chiyani? Nanga timapindula bwanji tikamayesetsa kukhala oyera? Tikamakambirana mayankho a mafunso amenewa, ganizirani zimene mukufunika kusintha kuti mukhale oyera.
N’CHIFUKWA CHIYANI TIYENERA KUKHALA OYERA?
4, 5. (a) N’chifukwa chiyani tiyenera kukhala oyera? (b) Kodi zimene zimachitika m’chilengedwechi zimasonyeza bwanji kuti Yehova amaona kuti ukhondo ndi wofunika?
4 Yehova ndi chitsanzo chabwino pa nkhani ya kukhala oyera ndipo chitsanzo chake chingatiphunzitse zambiri. (Levitiko 11:44, 45) Choncho chifukwa chachikulu chotichititsa kukhala oyera, ndi choti tikufuna ‘kutsanzira Mulungu.’—Aefeso 5:1.
5 Zimene zimachitika m’chilengedwechi zimasonyeza kuti Yehova amaona kuti ukhondo ndi wofunika. Iye anakonza zoti zinthu zina za m’chilengedwechi zizitha kuyeretsa mpweya komanso madzi a padzikoli. (Yeremiya 10:12) Pali zinthu zambiri zimene zimachitika zomwe zimathandiza kuti dziko lapansili lizitha kudziyeretsa ngakhale kuti anthu aliwononga kwambiri. Mwachitsanzo, pali tizilombo tina tating’onoting’ono kwambiri tomwe sitingathe kutiona ndi maso. Tizilombo timeneti ndi timene timathandiza kuyeretsa mpweya komanso madzi a padzikoli. Zimenezi zimachitika modabwitsa kwambiri. Nthawi zina asayansi amagwiritsanso ntchito tizilomboti akafuna kuyeretsa zinthu za m’chilengedwechi zomwe zawonongedwa.—Aroma 1:20.
6, 7. Kodi m’Chilamulo cha Mose munali malamulo ati osonyeza kuti atumiki a Yehova ayenera kukhala oyera?
6 Chilamulo chimene Mulungu anapatsa Aisiraeli kudzera mwa Mose chimasonyezanso kuti kukhala oyera n’kofunika. Mwachitsanzo, Aisiraeli ankafunika kukhala aukhondo kuti Yehova avomereze kulambira kwawo. Pa Tsiku la Mwambo Wophimba Machimo, mkulu wa ansembe ankafunika kusamba kawiri. (Levitiko 16:4, 23, 24) Komanso ansembe ena onse ankafunika kusamba m’manja komanso mapazi asanayambe kupereka nsembe. (Ekisodo 30:17-21; 2 Mbiri 4:6) Nthawi zina munthu amene sanamvere malamulo okhudza ukhondo, ankaphedwa.—Levitiko 15:31; Numeri 19:17-20.
7 Nanga bwanji masiku ano? Tingaphunzire zambiri kuchokera m’Chilamulo. (Malaki 3:6) Mwachitsanzo, Chilamulo chinkati atumiki a Yehova ayenera kukhala oyera. Mfundo za Yehova za makhalidwe abwino sizinasinthe. Choncho masiku anonso Yehova amafuna kuti atumiki ake azikhala oyera.—Yakobo 1:27.
KODI KUKHALA OYERA KUMATANTHAUZA CHIYANI?
8. Kodi tiyenera kukhala oyera m’mbali ziti?
8 Yehova amaona kuti kukhala oyera sikumangotanthauza kusamba, kuchapa komanso kusamalira bwino pakhomo pathu. Timafunika kukhala oyera mbali zonse za moyo wathu. Mwachitsanzo, kulambira kwathu kuyeneranso kukhala koyera, tiyenera kukhala ndi makhalidwe abwino komanso tizipewa kuganizira zoipa. Tikatero ndi pamene Yehova amationa kuti ndife oyera.
9, 10. Kodi tingatani kuti kulambira kwathu kukhale koyera?
9 Kulambira koyera. Akhristufe sitingachite nawo zimene anthu a m’zipembedzo zonyenga amachita. Pamene Aisiraeli anali akapolo ku Babulo, ankakhala limodzi ndi anthu amene sankalambira Yehova. Koma ulosi wa Yesaya unasonyeza kuti Aisiraeli adzabwerera kwawo n’kukayambiranso kulambira koyera. Yehova anawauza kuti: “Tulukani mmenemo! Musakhudze chinthu chilichonse chodetsedwa. Chokani pakati pake! Khalani oyera.” Choncho Aisiraeli sankafunika kuphatikiza kulambira Mulungu ndi kulambira kwa anthu a ku Babulo. Ankayeneranso kupewa makhalidwe oipa a anthu a ku Babuloko komanso miyambo yawo.—Yesaya 52:11.
10 Masiku anonso Akhristu oona amapewa zimene zipembedzo zonyenga zimaphunzitsa. (Werengani 1 Akorinto 10:21.) Miyambo yambiri yotchuka padzikoli komanso zimene ambiri amakhulupirira ndi zochokera pa zimene zipembedzo zonyenga zimaphunzitsa. Mwachitsanzo, anthu ambiri amakhulupirira kuti munthu akafa, mzimu wake umapitirizabe kukhala ndi moyo. Pali miyambo yambiri imene anthu amachita chifukwa cha chikhulupiriro chimenechi. (Mlaliki 9:5, 6, 10) Akhristu ayenera kupewa miyambo imeneyi. Achibale athu angatikakamize kuti tizichita nawo miyamboyi. Koma ngati tikufuna kuti Yehova azitiona kuti ndife oyera, tiyenera kukana.—Machitidwe 5:29.
11. Kodi tingasonyeze bwanji kuti tili ndi khalidwe loyera?
11 Khalidwe labwino. Kuti Yehova azitiona kuti ndife oyera, tiyenera kupewa dama la mtundu uliwonse. (Werengani Aefeso 5:5.) Kudzera m’Baibulo, Yehova amatiuza kuti ‘tithawe dama.’ Amatiuzanso kuti anthu amene amachita dama, ndipo safuna kulapa, “sadzalowa mu ufumu wa Mulungu.”—1 Akorinto 6:9, 10, 18; onani Mawu Akumapeto 22.
12, 13. N’chifukwa chiyani tiyenera kuyesetsa kumaganiza zinthu zabwino?
12 Maganizo abwino. Nthawi zambiri munthu amachita zimene amaganiza. (Mateyu 5:28; 15:18, 19) Choncho ngati timaganiza zabwino, tingamachitenso zabwino. Komabe popeza si ife angwiro nthawi zina timakhala ndi maganizo olakwika. Tikangoyamba kuganiza zolakwika, tiziyesetsa kusiya nthawi yomweyo. Kupanda kutero, mumtima mwathu mungadzaze zinthu zoipa zokhazokha. Zikatero, tingayambe kufuna kuchita zimene takhala tikuganizazo. Kuti zimenezi zisatichitikire, tiziyesetsa kuganizira zinthu zabwino. (Werengani Afilipi 4:8.) Tizipewa zosangalatsa zachiwawa komanso zachiwerewere. Tizisamalanso ndi zimene timawerenga, kuonera komanso kulankhula.—Salimo 19:8, 9.
13 Monga taonera, kuti Mulungu apitirize kutikonda, tiyenera kukhala oyera pa nkhani ya kulambira, makhalidwe komanso zimene timaganiza. Koma Yehova amafunanso kuti tizikhala aukhondo.
TINGATANI KUTI TIZIKHALA AUKHONDO?
14. N’chifukwa chiyani tiyenera kukhala aukhondo?
14 Tikamakhala aukhondo komanso kuonetsetsa kuti pakhomo pathu ndi posamalidwa bwino, zinthu zimatiyendera bwino ifeyo komanso anthu ena. Mwachitsanzo, timakhala osangalala komanso anthu amatikonda. Koma pali chifukwa chinanso chotipangitsa kukhala aukhondo. Tikamakhala aukhondo, anthu otiona amalemekeza Mulungu. Mwachitsanzo, ngati pali mwana amene nthawi zonse amakhala wosasamba komanso amavala zakuda, mwina mungawaganizire zoipa makolo ake. Mofanana ndi zimenezi, ngati sitimadzisamalira ndipo sitioneka aukhondo, anthu sangaganize zabwino zokhudza Yehova. Paulo anati: “Sitikuchita chilichonse chokhumudwitsa, kuti utumiki wathu usapezedwe chifukwa. Koma tikusonyeza mwa njira ina iliyonse kuti ndife atumiki a Mulungu.”—2 Akorinto 6:3, 4.
15, 16. Kodi tingatani kuti tizikhala aukhondo?
15 Kusamalira thupi lathu komanso zovala. Kudzisamalira n’kofunika kwambiri ndipo tiyenera kuchita zimenezi tsiku ndi tsiku. Mwachitsanzo, ngati n’zotheka tiyenera kusamba tsiku lililonse. Tiyeneranso kusamba m’manja ndi sopo makamaka tisanayambe kukonza chakudya, tisanayambe kudya, tikachoka kuchimbudzi komanso tikagwira chinthu chilichonse chakuda. Kusamba m’manja kumaoneka ngati nkhani yaing’ono, koma kumathandiza kuti tisafalitse matenda komanso tizilombo toyambitsa matenda. Kumathandizanso kuti anthu ambiri asafe. Ngati tilibe chimbudzi, tingapeze njira zina zabwino zoyenera kutsatira tikafuna kudzithandiza. Mwachitsanzo, Aisiraeli akale analibe zimbudzi. Koma akafuna kudzithandiza ankapita kutali ndi nyumba za anthu komanso zitsime ndipo ankakumba pansi n’kukwirira zonyansazo.—Deuteronomo 23:12, 13.
16 Sikuti timafunika kukhala ndi zovala zapamwamba, zodula kapena zafashoni. Chofunika n’choti zovala zathu zizikhala zaukhondo. (Werengani 1 Timoteyo 2:9, 10.) Timafuna kuti nthawi zonse anthu azitamanda Yehova akaona mmene tavalira.—Tito 2:10.
17. N’chifukwa chiyani tiyenera kuonetsetsa kuti pakhomo pathu ndi paukhondo?
17 Pakhomo pathu. Kaya timakhala kuti, tiyenera kuonetsetsa kuti pakhomo pathu ndi paukhondo. Tizionetsetsanso kuti zinthu zathu monga galimoto kapena njinga ndi zaukhondo, makamaka ngati timazigwiritsa ntchito popita kumisonkhano kapena mu utumiki. Paja tikamalalikira timauza anthu za dziko latsopano lokongola. (Luka 23:43; Chivumbulutso 11:18) Choncho tikamasamalira bwino pakhomo pathu, zingasonyeze kuti tikukonzekera kudzakhala m’dziko latsopano.
18. N’chifukwa chiyani tiyenera kuonetsetsa kuti malo athu olambirira ndi aukhondo?
18 Malo athu olambirira. Tikamasamalira pa Nyumba ya Ufumu komanso pa Malo a Msonkhano, timasonyeza kuti timaona kuti kukhala oyera n’kofunika. Nthawi zambiri anthu akabwera ku Nyumba ya Ufumu koyamba, amachita chidwi akaona kuti pamalopo pakuoneka paukhondo. Zimenezi zimalemekeza Yehova. Tonse tili ndi udindo woonetsetsa kuti Nyumba ya Ufumu yathu ndi yaukhondo komanso yokonzedwa bwino.—2 Mbiri 34:10.
TIYENERA KUSIYA MAKHALIDWE ONSE OIPA
19. Kodi tiyenera kupewa zinthu ziti?
19 Baibulo silitchula makhalidwe oipa onse amene tiyenera kupewa. Komabe m’Baibulo muli mfundo zomwe zingatithandize kudziwa makhalidwe amene Yehova amadana nawo. Mwachitsanzo, Yehova safuna kuti tizisuta fodya, tiziledzera kapena tizigwiritsa ntchito mankhwala osokoneza bongo. Ngati tikufuna kukhala mabwenzi ake, tiyenera kupewa zinthu zimenezi. Tikutero chifukwa mabwenzi a Yehova amaona kuti moyo ndi mphatso yamtengo wapatali. Zinthu zimenezi zingatidwalitse ifeyo kapena anthu ena komanso zingachititse kuti tife msanga. Anthu ambiri amasiya makhalidwe oipawa chifukwa choti safuna kuwononga thanzi lawo. Koma chifukwa chachikulu chimene ifeyo timasiyira makhalidwe amenewa n’choti timakonda Mulungu. Mtsikana wina anati: “Ndinayesetsa mpaka ndinasiya makhalidwe oipa amene ndinkachita. . . . Koma ndikudziwa kuti Yehova ndi amene anandithandiza chifukwa pandekha sindikanakwanitsa kusiya.” Tsopano tiyeni tikambirane mfundo 5 za m’Baibulo zimene zingathandize munthu kusiya makhalidwe oipa.
20, 21. Kodi Yehova amafuna kuti tisiye makhalidwe ati?
20 “Okondedwanu, popeza talonjezedwa zinthu zimenezi, tiyeni tidziyeretse ndipo tichotse chinthu chilichonse choipitsa thupi kapena mzimu, kwinaku tikukwaniritsa kukhala oyera poopa Mulungu.” (2 Akorinto 7:1) Yehova amafuna kuti tisiye makhalidwe alionse amene angadetse maganizo komanso thupi lathu.
21 Chifukwa chachikulu chotipangitsa ‘kudziyeretsa ndiponso kuchotsa chinthu chilichonse choipitsa thupi kapena mzimu,’ chatchulidwa pa 2 Akorinto 6:17, 18. Palembali Yehova akutiuza kuti: “Musakhudze chinthu chodetsedwa.” Kenako akutilonjeza kuti: “Ndidzakulandirani. Ndidzakhala atate wanu, ndipo inu mudzakhala ana anga aamuna ndi aakazi.” Izi zikusonyeza kuti tikamapewa chilichonse chimene chingapangitse kuti Yehova azitiona kuti ndife odetsedwa, adzatikonda ngati mmene bambo amakondera ana ake.
22-25. Kodi ndi mfundo za m’Baibulo ziti zimene zingatithandize kuti tisiye makhalidwe odetsa?
22 “Uzikonda Yehova Mulungu wako ndi mtima wako wonse, moyo wako wonse, ndi maganizo ako onse.” (Mateyu 22:37) Lamulo lalikulu ndi limeneli. (Mateyu 22:38) Tiyenera kukonda Yehova ndi mtima wathu wonse, moyo wathu wonse komanso maganizo athu onse. Kodi tingamukonde bwanji chonchi ngati tikuchita zinthu zimene zingachepetse moyo wathu kapena zimene zingasokoneze maganizo athu? Tiyeni tiziyesetsa kuchita zinthu zosonyeza kuti timayamikira moyo umene anatipatsawu.
23 “[Yehova] amapatsa anthu onse moyo, mpweya ndi zinthu zonse.” (Machitidwe 17:24, 25) Kodi mnzanu atakupatsani mphatso yamtengo wapatali, mungaitaye kapena kuiwononga? Moyo ndi mphatso yamtengo wapatali ndipo timaiyamikira kwambiri. Choncho tiziyesetsa kuchita zinthu zimene zingachititse kuti anthu azitamanda Yehova.—Salimo 36:9.
24 “Uzikonda mnzako mmene umadzikondera wekha.” (Mateyu 22:39) Makhalidwe athu oipa angabweretsenso mavuto kwa anthu ena amene timawakonda. Mwachitsanzo, anthu amene amakhala m’nyumba imodzi ndi munthu amene amasuta fodya, angayambe kudwala chifukwa chopuma fungo la fodya. Choncho munthu akasiya kusuta, amasonyeza kuti amakonda anthu ena.—1 Yohane 4:20, 21.
25 “Pitiriza kuwakumbutsa kuti azigonjera ndi kumvera maboma ndiponso olamulira.” (Tito 3:1) M’mayiko ambiri muli malamulo oletsa kupezeka kapena kugwiritsa mankhwala osokoneza bongo. Popeza Yehova amatiuza kuti tizilemekeza boma, timamvera malamulo amenewa.—Aroma 13:1.
26. (a) Kodi tiyenera kuchita chiyani kuti Yehova azisangalala ndi kulambira kwathu? (b) N’chifukwa chiyani kukhala oyera pamaso pa Mulungu n’kwabwino kwambiri?
26 Ngati tikufuna kukhala mabwenzi a Yehova, mwina tingaone kuti tikufunika kusintha zinthu zina. Tikaona kuti tikufunikadi kusintha, tiyenera kusintha nthawi yomweyo. Sizikhala zophweka kusiya zinthu zomwe tinazolowera, koma titayesetsa tikhoza kusiya. Yehova amatilonjeza kuti atithandiza. Iye amatiuza kuti: “Ine Yehova ndine Mulungu wanu, amene ndimakuphunzitsani kuti zinthu zikuyendereni bwino, amene ndimakuchititsani kuti muyende m’njira imene muyenera kuyendamo.” (Yesaya 48:17) Tikamayesetsa kukhala oyera mbali zonse, timalemekeza Mulungu.