Lingaliro Labaibulo
Kodi Akazi ali Mbali ya pa Guwa la Nsembe?
“AKRISTU wamba ambiri samamvetsetsa nchifukwa ninji, ngati akazi angakhale olamulira, nduna zazikulu za boma, oweruza, asing’anga otumbula anthu, asayansi, angaletsedwe kuchita Mapwando a Imfa ya Yesu ndi mapwando aukwati,” akulemba tero mtsogoleri wachipembedzo wa Tchalitchi cha England Nicholas Stacey mu The Times ya ku London.
Ngakhale kuti Tchalitchi cha England chimaphunzitsa akazi kaamba ka utumiki wapadera, kufikira tsopano sichinavomerezepo akazi kutumikira monga ansembe ndi kupereka mgonero wake. Kodi mukuvomerezana ndi kaimidwe ka tchalitchi, kapena kodi mumakhulupirira kuti akazi ayenera kukhala pa guwa lansembe?
Chingagawanitse Matchalitchi
Nkhani ya akazi monga atsogoleri achipembedzo yakhala cholekanitsa pakati pa ziwalo za chipembedzo chimodzimodzi. Tchalitchi cha England chingagawanitse mopanda vuto mu mbali ziŵiri zosiyanasiyana za maphunziro pa nkhaniyi, akuchenjeza tero Dr. Graham Leonard, Bishopo wa ku London, mtsogoleri wachipembedzo wotsogolera kutsutsa kuikidwa manja kwa akazi monga ansembe. Anthu ena amapatsa mlandu kunyada pa kuika akazi kunja kwa guwa la nsembe, koma zambiri zikuphatikizidwamo.
Kwa zaka makumi, Tchalitchi cha England chakhala chikuyesayesa kugwirizanitsa kusiyana kwake ndi Roma. Koma m’kalata ya posachedwapa kwa Bishopo wamkulu wa ku Canterbury, papa ananena kuti kuvomereza kulikonse kwa akazi kukhala ansembe kungaike “m’maso mwa Tchalitchi cha Katolika, chokhumudwitsa chowonjezereka choletsa kupita patsogolo koteroko.”
Chinthu china chofunika, ngakhale kuli tero, chasiidwa m’kutsutsana kumeneku—Baibulo. Kodi akazi anatumikira motani mu mipingo ya Chikristu yoyambirira, ndipo ndi iti yomwe iyenera kukhala mbali yawo?
Olingana koma Osiyana
Pa kubadwa kwa mpingo wa Chikristu mu chaka cha 33 C.E., akazi limodzi ndi amuna analandira mzimu woyera. Umu ndi mongadi mmene m’neneri Yoweli ananeneratu mazana oyambirira, mtumwi Paulo analongosola tero.—Machitidwe. 1:13-15; 2:1-4, 13-18.
Pambuyo pake, Petro anafikira ku kuzindikira za chinthu china chofunika kwambiri: “Mulungu alibe tsankhu.” (Machitidwe 10:34) Mu tanthauzo lenileni, lemba limenelo limatanthauza kuti Mulungu saali “Woyang’ana pamaso.” “Woyang’ana pamaso” amasonyeza chizindikiro ndi kukonda munthu wina. M’nthaŵi zakale, mochulukira woweruza anali kuchitira chifundo wolemera osati wosauka. Kapena wozengedwa mlandu angaweruzidwe kudalira pa mtundu, thayo la mayanjano, banja, kapena unansi mmalo mwa kudalira pa nsonga. Koma Yehova amachita mosiyanako. Amachitira chifundo kokha aja omwe amaopa iye ndi kugwira ntchito m’chilungamo. Pamene chibwera ku chipulumutso, Mulungu samachitira ulemu ‘nkhope’ ya mwamuna kuposa ‘nkhope’ ya mkazi. Onse ali olingana kwa iye.—Machitidwe 10:35.
Chotero, Malemba amapereka kwa amuna ndi akazi Achikristu unyinji wofanana wa ulemu monga ziwalo za mpingo. Mtumwi Paulo analembera Akristu a ku Agalatiya kuti “muno mulibe kapolo kapena mfulu, muno mulibe mwamuna kapena mkazi; pakuti muli nonse mmodzi mwa Kristu Yesu.” Onse ali ndi kaimidwe kodzidalira kauzimu pamaso pa Mulungu; koma onse ali ogwirizana monga thupi la kapolo wake. Onse ali ofanana m’nyumba ya Mulungu.—Agalatiya 3:26-28.
Mosasamala kanthu za chimenecho, pali kusiyana pakati pa mkazi ndi mwamuna mu mpingo. Koma monga mmene kusiyana kwachibadwa pakati pa mwamuna ndi mkazi sikuli chokhumudwitsa ku kuthandizana kwawo wina ndi m’nzake, chotero mwaŵi wosiyana umene amuna ndi akazi amasangalala nawo mkati mwa mpingo Wachikristu suyenera kukhala chokhumudwitsa ku chigwirizano cha mpingo. Kodi zosiyanazo ndi ziti?
Aphunzitsi—Liti ndipo kwa Yani?
Kusiyanako kumazikidwa pakati pa kuphunzitsa ndi ulamuliro. Akazi amaletsedwa kutumikira mmalo ophunzitsa mwalamulo mu mpingo ndi kusonyeza ulamuliro wauzimu pa ziwalo zina za mpingo. M’kalata yake yaubusa kwa Timoteo, Paulo momvekera bwino akunena kuti: “Koma sindilola inu kuti mkazi aphunzitse, kapena kulamulira mwamuna, koma akhale chete.”—1 Timoteo 2:12.
Paulo kenaka akuloza ku maziko a kusavomerezera akazi kukhala aphunzitsi—unansi woikidwa mwaumulungu pakati pa mwamuna ndi mkazi. “Pakuti Adamu anayamba kulengedwa, pamenepo Hava,” akulemba tero. (1 Timoteo 2:13) Mulungu akadalenga Adamu ndi Hava pa nthaŵi imodzimodziyo, koma sanatero. Adamu anakhalapo kwa nthaŵi ina Hava asanakhaleko. Kodi ichi sichimavumbula chifuno cha Mulungu kaamba ka Adamu kukhala wolamulira, kukhala mutu, mmalo mwa Hava? (1 Akorinto 11:3) Ndipo kuphunzitsa kuli, m’chenicheni, kuchita monga woyang’anira, kapena mutu, pa aja omwe akuphunzitsidwa. Aja ophunzitsidwa amamva ndipo mwakachetechete amaphunzira. Chotero, mu mpingo kokha amuna ayenera kukhala aphunzitsi ndi oyang’anira.
Kodi nsonga yakuti akazi safunikira kuphunzitsa mu mpingo ifunikira kupangitsa kukhumudwa ndi kukwiya? Ayi. Akazi ali aufulu kuphunzitsa ziphunzitso Zachikristu ndipo akuitanidwa kuchita chimenecho. M’lingaliro lotani ndipo pansi pa mikhalidwe yotani? Akazi okalamba angakhale “akuphunzitsa zokoma” kwa akazi ang’ono. Monga mmene Yunisi ndi mayi wake Loisi analangizira Timoteo, chotero akazi Achikristu amatsatira chitsanzo chawo m’kuphunzitsa ana awo mu “njira” ya chowonadi.—Tito 2:3-5; Machitidwe 9:2; 2 Timoteo 1:5.
Lerolino, akazi Achikristu nawonso amatsatira zitsanzo za Yuodiya ndi Santiki m’kulalikira mbiri yabwino poyera. (Afilipi 4:2, 3) Angakhale aphunzitsi mwakutsogoza maphunziro a Baibulo ndi anthu okondwerera. (Mateyu 28:20) Mazana a zikwi za akazi amapeza kukhutiritsidwa kwauzimu m’ntchito iyi yofulumira yolalikira ndi kuphunzitsa. Amalozera ena ku kukhazikitsidwa kwa dziko la chilungamo ndi mtendere pansi pa ulamuliro wa Yesu Kristu—chiyembekezo chomwe amagawana mofanana ndi abale awo Achikristu.—Masalmo 37:10, 11; 68:11.
[Mawu Otsindika patsamba 30]
Nkhani ya akazi monga atsogoleri achipembedzo yakhala cholekanitsa pakati pa ziwalo za chipembedzo chimodzimodzi