Ufulu Woperekedwa ndi Mulungu Umabweretsa Chimwemwe
‘Chimwemwe cha Yehova ndicho mphamvu yanu.’—NEHEMIYA 8:10.
1. Kodi chimwemwe nchiyani, ndipo nchifukwa ninji odzipatulira kwa Mulungu angakhale nacho?
YEHOVA amadzaza mitima ya anthu ake ndi chimwemwe. Mkhalidwe wa chimwemwe chachikulu kapena chisangalalo umenewu umadza mwakupeza kapena kuyembekezera zinthu zabwino. Anthu odzipatulira kwa Mulungu angakhale ndi maganizo oterowo chifukwa chakuti chimwemwe chiri chipatso cha mzimu wake woyera, kapena mphamvu yogwira ntchito. (Agalatiya 5:22, 23) Chotero ngakhale ngati ziyeso zopsinja zitigwera, tingakhalebe achimwemwe monga atumiki a Yehova, amene amatsogozedwa ndi mzimu wake.
2. Kodi nchifukwa ninji Ayuda anasekerera pachochitika chapadera m’tsiku la Ezara?
2 Pachochitika chapadera m’zaka za zana lachisanu B.C.E., Ayuda anagwiritsira ntchito ufulu wawo woperekedwa ndi Mulungu kuchita phwando lokondweretsa la Madyerero a Misasa m’Yerusalemu. Ezara ndi Alevi ena atawaŵerengera ndi kuwafotokozera Chilamulo cha Mulungu, ‘anapita anthu onse kudya ndi kumwa, ndi kutumiza magawo, ndi kusekerera kwakukulu; popeza anazindikira mawu amene adawafotokozera.’—Nehemiya 8:5-12.
Chimwemwe cha Yehova Ndicho Mphamvu Yathu
3. Kodi ‘chimwemwe cha Yehova’ chingakhale mphamvu yathu pansi pa mikhalidwe yotani?
3 Mkati mwa phwando limenelo, Ayuda anazindikira kuwona kwa mawu aŵa: ‘Chimwemwe cha Yehova ndicho mphamvu yanu.’ (Nehemiya 8:10) Chimwemwe chimenechi ndicho mphamvu yathunso ngati tichilimika mu ufulu woperekedwa ndi Mulungu monga Mboni zodzipatulira, zobatizidwa za Yehova. Oŵerengeka a ife anadzozedwa ndi mzimu woyera ndi kutengedwera m’banja la Mulungu monga oloŵa m’nyumba akumwamba ndi Kristu. (Aroma 8:15-23) Ambirife lerolino tiri ndi chiyembekezo cha moyo m’dziko lapansi laparadaiso. (Luka 23:43) Tiyenera kukhala achimwemwe chotani nanga!
4. Kodi nchifukwa ninji Akristu angapirire zovuta ndi chizunzo?
4 Ngakhale kuti tiri ndi ziyembekezo zabwino koposa, sikuli kokhweka kupirira zovuta ndi chizunzo. Komabe, tikhoza kuchita zimenezo chifukwa chakuti Mulungu amatipatsa mzimu wake woyera. Ndi mzimuwo tikhoza kukhala ndi chimwemwe ndi chikhutiro chakuti palibe chimene chingatilande chiyembekezo chathu kapena chikondi cha Mulungu. Ndiponso, tingakhale otsimikiza kuti Yehova adzakhala mphamvu yathu malinga ngati timkonda ndi mtima wathu wonse, moyo, nyonga, ndi maganizo.—Luka 10:27.
5. Kodi tingapeze kuti zifukwa zokhalira achimwemwe?
5 Anthu a Yehova amasangalala ndi madalitso olemera ndipo ali ndi zifukwa zambiri zokhalira achimwemwe. Zifukwa zina zokhalira achimwemwe zatchulidwa m’kalata ya Paulo yomka kwa Agalatiya. Zina zasonyezedwa m’malo ena m’Malemba. Kulingalira madalitso odzetsa chimwemwe ameneŵa kudzatisangulutsa.
Yamikirani Ufulu Woperekedwa ndi Mulungu
6. Kodi nchifukwa ninji Paulo anafulumiza Akristu a ku Galatiya kuchilimika?
6 Monga Akristu, tiri ndi dalitso losangalatsa lakuvomerezedwa pamaso pa Mulungu. Popeza kuti Kristu anamasula otsatira ake ku Chilamulo cha Mose, Agalatiya anafulumizidwa kuchilimika ndi kusadzibindikiritsa mu ‘goli la ukapolo’ limenelo. Bwanji nanga za ife? Ngati tinayesa kudzilungamitsa mwakusunga Chilamulo, tikachotsedwa kwa Kristu. Komabe, mothandizidwa ndi mzimu wa Mulungu, timadikirira chilungamo choyembekezeredwa chotulukapo kuchokera ku chikhulupiriro chogwira ntchito mwa chikondi, osati ku mdulidwe wakuthupi kapena ntchito za Chilamulo.—Agalatiya 5:1-6.
7. Kodi tiyenera kuuwona motani utumiki wopatulika wa Yehova?
7 Liri dalitso kugwiritsira ntchito ufulu wathu woperekedwa ndi Mulungu ‘kutumikira Yehova ndi chikondwerero.’ (Salmo 100:2) Ndithudi, uli mwaŵi wosayerekezereka kupereka utumiki wopatulika kwa ‘[Yehova, NW] Mulungu, Wamphamvuyonse, Mfumu . . . ya nthaŵi zosatha’! (Chivumbulutso 15:3) Ngati malingaliro a kusoŵa ulemu waumwini akufikirani, kungakhale kothandiza kuzindikira kuti Mulungu wakuyandikitsani kwa iye yekha kudzera mwa Yesu Kristu ndipo wakupatsani phande mu “ntchito yopatulika ya mbiri yabwino ya Mulungu.” (Aroma 15:16, NW; Yohane 6:44; 14:6) Ha, nzifukwa zotani nanga zokhalira achimwemwe ndi oyamikira kwa Mulungu!
8. Ponena za Babulo Wamkulu, kodi anthu a Mulungu ali ndi chiyani chowapangitsa kukhala achimwemwe?
8 Chochititsa chimwemwe china ndicho ufulu wathu woperekedwa ndi Mulungu kutuluka m’Babulo Wamkulu, ulamuliro wa dziko wa chipembedzo chonyenga. (Chivumbulutso 18:2, 4, 5) Ngakhale kuti mkazi wachigololo wachipembedzo ameneyu mophiphiritsira ‘akukhala pa madzi ambiri,’ kutanthauza “anthu, ndi makamu, ndi mitundu, ndi manenedwe,” iye sakhala, kapena kusonkhezera ndi kulamulira mwachipembedzo atumiki a Yehova. (Chivumbulutso 17:1, 15) Timasangalala m’kuunika kosangalatsa kwa Mulungu, pamene ochilikiza Babulo Wamkulu ali mumdima wauzimu. (1 Petro 2:9) Inde, kungakhale kovuta kumvetsetsa zinthu zina “zakuya za Mulungu.” (1 Akorinto 2:10) Koma mapemphero opempha nzeru ndi chithandizo cha mzimu woyera amatithandiza kumvetsetsa chowonadi Chamalemba chimene chimamasula mwauzimu iwo okhala nacho.—Yohane 8:31, 32; Yakobo 1:5-8.
9. Ngati titi tisangalale ndi dalitso lopitirizabe la kumasuka ku zolakwa zachipembedzo, kodi tiyenera kuchitanji?
9 Timasangalala ndi dalitso la ufulu wopitirizabe ku zolakwa zachipembedzo, koma kuti tisungebe ufulu umenewo, tiyenera kukana mpatuko. Agalatiya ankathamanga bwino makani Achikristu, koma ena ankawatsekereza kuti asamvere chowonadi. Kukokosa koipa kumeneko sikunali kochokera kwa Mulungu ndipo kunafunikira kupeŵedwa. Monga momwe chotupitsa pang’ono chimatupitsira mtanda wonse, aphunzitsi onyenga kapena kukhala ndi mzimu wampatuko kungaipitse mpingo wonse. Paulo analakalaka kuti ochilikiza mdulidwe ofuna kupatutsa chikhulupiriro cha Agalatiya asangodulidwa kokha koma adulidwe ziŵalo zawo zenizeni. Nkulankhula kwamphamvudi! Koma tiyenera kukhala otsimikiza motero pokana mpatuko ngati tikufuna kusunga ufulu wathu woperekedwa ndi Mulungu ku zolakwa zachipembedzo.—Agalatiya 5:7-12.
Tumikiranani Mwachikondi
10. Kodi tiri ndi thayo lotani monga mbali ya ubale Wachikristu?
10 Ufulu woperekedwa ndi Mulungu watibweretsa m’gulu la abale achikondi, koma tiyenera kuchita mbali yathu kusonyeza chikondi. Agalatiya sanafunikire kugwiritsira ntchito ufulu wawo monga ‘chothandizira thupi’ kapena chodzikhululukira cha dyera lopanda chikondi. Anafunikira kutumikirana ndi chikondi. (Levitiko 19:18; Yohane 13:35) Nafenso tiyenera kupeŵa kujedana ndi kudana komwe kungatipangitse kuwonongana. Ndithudi, izi sizidzachitika ngati tisonyeza chikondi chapaubale.—Agalatiya 5:13-15.
11. Kodi tingakhale motani dalitso kwa ena, ndipo kodi iwo angatidalitse motani?
11 Mwakugwiritsira ntchito ufulu wathu woperekedwa ndi Mulungu mogwirizana ndi chitsogozo cha mzimu wa Mulungu, tidzasonyeza chikondi ndi kukhala dalitso kwa ena. Chiyenera kukhala chizoloŵezi kudzilola kulamulidwa ndi kutsogozedwa ndi mzimu woyera. Pamenepo sitidzakhoterera kukhutiritsa mopanda chikondi thupi lathu lochimwa lomwe ‘limalakalaka kutsutsana ndi mzimu.’ Ngati tikutsogozedwa ndi mzimu wa Mulungu, tidzachita zachikondi koma osati chifukwa chakuti malamulo amafuna kuti tigonjere ndipo chilango chimaperekedwa kwa olakwa. Mwachitsanzo, chikondi—osati lamulo lokha—chidzatiletsa kusinjirira ena. (Levitiko 19:16) Chikondi chidzatisonkhezera kulankhula ndi kuchita mwachifundo. Chifukwa chakuti timasonyeza chipatso cha mzimu cha chikondi, ena adzatidalitsa, kapena kunena zabwino za ife. (Miyambo 10:6) Ndiponso, kuyanjana nafe kudzakhala dalitso kwa iwo.—Agalatiya 5:16-18.
Chipatso Chosemphana
12. Kodi ndimadalitso ena ati ogwirizanitsidwa ndi kupeŵa ‘ntchito zathupi’ zochimwa?
12 Madalitso ambiri ogwirizana ndi ufulu wathu woperekedwa ndi Mulungu amadza mwakupeŵa ‘ntchito zathupi’ zochimwa. Monga anthu a Mulungu, mofala timapeŵa chisoni chachikulu chifukwa sitimachita dama, chidetso, ndi mkhalidwe wachisembwere. Mwakupeŵa kupembedza mafano, tiri ndi chimwemwe chotulukapo m’kukondweretsa Yehova pankhaniyi. (1 Yohane 5:21) Popeza kuti sitimalambira mizimu, tiri omasuka ku kulamulidwa ndi ziŵanda. Ubale wathu Wachikristu sumaipitsidwa ndi madano, ndewu, kaduka, zopsa mtima, zotetana, magawano, mipatuko, ndi njiru. Ndipo chimwemwe chathu sichimataika chifukwa cha kuledzera ndi mchezo. Paulo anachenjeza kuti iwo ochita ntchito zathupi sadzaloŵa Ufumu wa Mulungu. Komabe, chifukwa chakuti timalabadira mawu ake, tingamamatire ku chiyembekezo chachimwemwe cha Ufumu.—Agalatiya 5:19-21.
13. Kodi mzimu woyera wa Yehova umatulutsa zipatso zotani?
13 Ufulu woperekedwa ndi Mulungu umatibweretsera chimwemwe chifukwa chakuti Akristu amasonyeza zipatso za mzimu wa Yehova. Nkosavuta kuwona m’mawu a Paulo kwa Agalatiya kuti ntchito za thupi lochimwa ziri monga minga poyerekezera ndi zipatso zabwino za mzimu za chikondi, chimwemwe, mtendere, kuleza mtima, chifundo, kukoma mtima, chikhulupiriro, chifatso, ndi chiletso zozikidwa m’mitima yaumulungu. Pokhala otsimikiza mtima kukhala mosemphana ndi zilakolako za thupi lochimwa, timakhumba kutsogozedwa ndi mzimu wa Mulungu ndikukhala nawo. Mzimu umatipangitsa kukhala odzichepetsa ndi amtendere, osati ‘odzikuza, outsana, akuchitirana njiru.’ Nkosadabwitsa kuti kuli kosangalatsa kusonkhana ndi awo amene amasonyeza zipatso za mzimu!—Agalatiya 5:22-26.
Zifukwa Zina Zokhalira ndi Chimwemwe
14. Kodi ndichida chotani chimene timachifunikira m’nkhondo yathu yolimbana ndi mizimu yoipa?
14 Logwirizana ndi ufulu wathu woperekedwa ndi Mulungu ndilo dalitso la kutetezeredwa kwa Satana ndi ziŵanda. Kuti tipambane m’kulimbana kwathu ndi mizimu yoipa, tiyenera kuvala “zida zonse za Mulungu.” Tifunikira kudzimangira m’chuuno ndi chowonadi ndi chapachifuwa cha chilungamo. Mapazi athu ayenera kuvala chida cha mbiri yabwino ya mtendere. Chofunikanso chiri chikopa chachikulu cha chikhulupiriro, chomwe tikazima nacho mivi yonse yoyaka ya woipayo. Tiyenera kuvala chisoti cha chipulumutso ndikuponya ‘lupanga la mzimu,’ Mawu a Mulungu. Tiyeninso ‘tipemphere nthaŵi yonse mwa mzimu.’ (Aefeso 6:11-18) Ngati tivala chida chauzimu ndi kukana uchiŵanda, tikhoza kukhala opanda mantha ndi achimwemwe.—Yerekezerani ndi Machitidwe 19:18-20.
15. Kodi ndidalitso lachimwemwe lotani limene timakhala nalo chifukwa chokhala mogwirizana ndi Mawu a Mulungu?
15 Tiri ndi chimwemwe chifukwa chakuti khalidwe lathu limagwirizana ndi Mawu a Mulungu, ndipo tiri omasuka ku liŵongo lokantha ochita zoipa ambiri. ‘Tidziyesera tokha tikhale nacho nthaŵi zonse chikumbumtima chosatitsutsa cha kwa Mulungu ndi kwa anthu.’ (Machitidwe 24:16) Chifukwa chake, sitifunikira kuwopa chilango cha Mulungu chimene chidzagwera ochimwa mwadala, osalapa. (Mateyu 12:22-32; Ahebri 10:26-31) Mwakugwiritsira ntchito uphungu wa Miyambo 3:21-26, timazindikira kukwaniritsidwa kwa mawu amenewo: ‘Sunga nzeru yeniyeni ndi kulingalira; ndipo mtima wako udzatengapo moyo, ndi khosi lako chisomo. Pompo udzayenda m’njira yako osawopa, osapunthwa phazi lako. Ukagona, sudzachita mantha; udzagona tulo tokondweretsa. Usawope zowopsa zodzidzimutsa, ngakhale zikadza zopasula oipa; pakuti Yehova adzalimbitsa mtima wako, nadzasunga phazi lako lingakodwe.’
16. Kodi ndimotani mmene pemphero liriri lochititsa chimwemwe, ndipo kodi mzimu wa Yehova umachita mbali yotani m’chimenechi?
16 Chifukwa china chotipatsa chimwemwe ndicho ufulu wathu woperekedwa ndi Mulungu wakumfikira Yehova m’pemphero ndi chitsimikizo chakuti tidzamvedwa. Inde, mapemphero athu amayankhidwa chifukwa chakuti tiri ndi “kuopa Yehova,” kwaulemu. (Miyambo 1:7) Ndiponso, timathandizidwa kukhalabe m’chikondi cha Mulungu mwa ‘kupemphera mu mzimu woyera.’ (Yuda 20, 21) Timachita zimenezi mwakusonyeza mkhalidwe wamtima wolandirika kwa Yehova ndi mwakupemphera pansi pa chisonkhezero cha mzimu kaamba ka zinthu zogwirizana ndi chifuniro chake ndi Mawu ake, umene umatisonyeza mmene tingapempherere ndi zimene tingapemphe m’pemphero. (1 Yohane 5:13-15) Ngati tayesedwa kwambiri ndipo sitidziŵa zopempha, ‘mzimu uthandiza kufooka kwathu, nutipempherera ndi zobuula zosatheka kuneneka.’ Mulungu amayankha mapemphero oterowo. (Aroma 8:26, 27) Tiyeni tipempherere mzimu woyera ndi kuulola kukulitsa mwa ife zipatso zake zimene timafunikira mwapadera kuti tilake chiyeso chakutichakuti. (Luka 11:13) Tidzawonjezeranso chimwemwe chathu ngati mwapemphero ndi mwakhama tiphunzira Mawu a Mulungu ouziridwa ndi mzimu ndi mabuku Achikristu okonzedwa pansi pa chitsogozo cha mzimu.
Odalitsidwa ndi Thandizo Lokhalapo Nthaŵi Zonse
17. Kodi zokumana nazo za Mose ndi mawu a Davide zimasonyeza motani kuti Yehova ali ndi anthu Ake?
17 Mwakugwiritsira ntchito ufulu wathu woperekedwa ndi Mulungu molondola, timakhala ndi chimwemwe chakudziŵa kuti Yehova ali nafe. Pamene mikhalidwe yoipa inachititsa Mose kuchoka mu Igupto, mwa chikhulupiriro ‘anapirira molimbika, monga ngati kuwona wosawonekayo.’ (Ahebri 11:27) Mose sanayende yekha; anadziŵa kuti Yehova anali naye. Mofananamo, ana a Kora anaimba kuti: ‘Mulungu ndiye pothaŵirapo pathu ndi mphamvu yathu, thandizo lopezekeratu m’masautso. Chifukwa chake sitidzachita mantha, lingakhale lisandulika dziko lapansi, angakhale mapiri asunthika, nakhala mkati mwa nyanja; chinkana madzi ake akokoma, nachita thovu, nagwedezeka mapiri ndi kudzala kwake.’ (Salmo 46:1-3) Ngati muli ndi chikhulupiriro chotero mwa Mulungu, sadzakusiyani konse. Davide anati: ‘Pakuti wandisiya atate wanga ndi amayi wanga, koma Yehova anditola.’ (Salmo 27:10) Kumadzetsa chimwemwe chotani nanga kudziŵa kuti Mulungu amasamalira atumiki ake kwambiri!—1 Petro 5:6, 7.
18. Kodi nchifukwa ninji amene ali ndi chimwemwe cha Yehova amakhala ndi ufulu woperekedwa ndi Mulungu ku nkhaŵa zambiri?
18 Pokhala ndi chimwemwe cha Yehova, tiri ndi ufulu woperekedwa ndi Mulungu ku nkhaŵa zambiri. ‘Musadere nkhaŵa konse,’ anatero Paulo, ‘komatu m’zonse ndi pemphero, ndi pembedzero, pamodzi ndi chiyamiko, zopempha zanu zidziŵike kwa Mulungu. Ndipo mtendere wa Mulungu wakupambana chidziŵitso chonse, udzasunga mitima yanu ndi maganizo anu mwa Kristu Yesu.’ (Afilipi 4:6, 7) Mtendere wa Mulungu uli bata losayerekezereka ngakhale m’mikhalidwe yopereka chiyeso kwambiri. Pokhala nawo mitima yathu imakhala bata—kenakake kabwino kwa ife mwauzimu, maganizo, ndi kuthupi. (Miyambo 14:30) Umatithandizanso kukhalabe olinganizika mwamaganizo, popeza timadziŵa kuti palibe chimene Mulungu amachilola chomwe chingativulaze kosatha. (Mateyu 10:28) Mtendere umenewu wotulukapo muunansi wathithithi ndi Mulungu kupyolera mwa Kristu uli wathu chifukwa tinadzipatulira kwa Yehova ndi kugonjera ku chitsogozo cha mzimu wake, womwe umatulutsa zipatso zonga chimwemwe ndi mtendere.
19. Kodi ndimwakusumika mitima yathu pachiyani kumene kudzatithandiza kukhala achimwemwe?
19 Kusumika mitima yathu pa ufulu woperekedwa ndi Mulungu ndi chiyembekezo cha Ufumu kudzatithandiza kukhala achimwemwe. Mwachitsanzo, nthaŵi zina pangakhale zochepa zomwe tingachite ponena za thanzi loipa, koma tingapempherere nzeru ndi chilimbikitso kuti tipirire nalo ndipo tingapeze chitonthozo poganiza za thanzi lauzimu limene tikusangalala nalo tsopano ndi kuchiritsa kwakuthupi komwe kudzachitika mu ulamuliro wa Ufumu. (Salmo 41:1-3; Yesaya 33:24) Ngakhale kuti tingamapirire ndi zosoŵa lerolino, m’dziko lapansi Laparadaiso lomwe liri pafupi simudzakhala kusoŵa kwa zofunikira za moyo. (Salmo 72:14, 16; Yesaya 65:21-23) Inde, Atate wathu wakumwamba adzatisamalira tsopano ndipo adzakwaniritsa kotheratu chimwemwe chathu.—Salmo 145:14-21.
Samalirani Ufulu Wanu Woperekedwa ndi Mulungu
20. Malinga ndi Salmo 100:1-5, kodi tiyenera kudzipereka motani pamaso pa Yehova?
20 Monga anthu a Yehova, ndithudi tiyenera kusamalira ufulu woperekedwa ndi Mulungu umene watibweretsera chimwemwe ndi madalitso ambiri. Nkosadabwitsa kuti Salmo 100:1-5 limatilimbikitsa kufika pamaso pa Mulungu “ndi kumyimbira mokondwera.” Tiri ake a Yehova ndipo amatisamalira monga Mbusa wachikondi. Inde, ‘ndife anthu ake ndi nkhosa za pabusa pake.’ Kukhala kwake Mlengi ndi mikhalidwe yake yaikulu zimatipatsa chifuno chakuloŵa m’mabwalo a kachisi wake ndi chitamando ndi chiyamiko. Timasonkhezeredwa ‘kulemekeza dzina lake,’ kulankhula zabwino ponena za Yehova Mulungu. Ndiponso, nthaŵi zonse tikhoza kudalira kukoma mtima kwake kwachikondi, kapena chifundo kulinga kwa ife. “Mibadwo mibadwo” Yehova ali wokhulupirika, wosagwedera m’kusonyeza chikondi kwa iwo ochita chifuniro chake.
21. Kodi nchilimbikitso chotani chomwe chidaperekedwa m’kope loyamba la magazini ano, ndipo kodi tiyenera kuchitanji ndi ufulu woperekedwa ndi Mulungu?
21 Monga anthu opanda ungwiro, pakali pano sitingathe kuthaŵa ziyeso zonse. Komabe, ndi chithandizo cha Mulungu, tikhoza kukhala Mboni zolimba mtima ndi zachimwemwe za Yehova. Ofunika pankhaniyi ali mawu aŵa opezeka m’kope loyamba la magazini ano (July 1879): “Limba mtima . . . mbale kapena mlongo wanga Wachikristu, amene ukufunafuna mofooka kuthamanga m’njira yopapatiza. Usadere nkhaŵa ndi njira yovutayo; iyo yonse inalemekezedwa ndi kupatulikitsidwa ndi mapazi odalitsidwa a Ambuye. Ona minga iriyonse kukhala duŵa; thanthwe lakuthwa lirilonse kukhala posinthira, kukufulumizira ku chonulirapo. . . . Sumika maso ako pa mphotho.” Mamiliyoni ambiri omwe tsopano akutumikira Yehova amasumika maso awo pa mphotho ndi zifukwa zambiri zokhalira olimba mtima ndi achimwemwe. Chilimikani nawo pamodzi mu ufulu woperekedwa ndi Mulungu. Musaphonye chifuno chake, ndipo chimwemwe cha Yehova chikhaletu mphamvu yanu nthaŵi zonse.
Kodi Mungayankhe Motani?
◻ Kodi ndimotani mmene ‘chimwemwe cha Yehova’ chingakhalire mphamvu yathu?
◻ Polankhula mwachipembedzo, kodi ndimadalitso otani amene ufulu woperekedwa ndi Mulungu wabweretsa kwa anthu a Yehova?
◻ Kodi nchifukwa ninji tiyenera kutumikirana mwachikondi?
◻ Kodi ndimadalitso ena ati omwe ngogwirizanitsidwa ndi ufulu woperekedwa ndi Mulungu?
◻ Kodi ndimotani mmene anthu a Mulungu angakhalirebe achimwemwe?
[Chithunzi patsamba 23]
“Ona minga iriyonse kukhala duŵa; thanthwe lakuthwa lirilonse kukhala posinthira, kukufulumizira ku chonulirapo”