Kodi Zikumbutso za Yehova Mumazikonda Kwambiri?
“Moyo wanga unasamalira mboni zanu [“zikumbutso zanu,” NW]; ndipo ndizikonda kwambiri.”—SALMO 119:167.
1. N’kuti kwenikweni komwe zikumbutso za Yehova zatchulidwa mobwerezabwereza?
YEHOVA amafuna kuti anthu ake azikhala achimwemwe. Komabe, kuti tikhaledi ndi chimwemwe chenicheni tiyenera kuyenda m’chilamulo cha Mulungu ndi kusunga malangizo ake. Kuti tithe kuchita zimenezo, amatipatsa zikumbutso. Zikumbutsozi zatchulidwa mobwerezabwereza m’Malemba, makamaka mu Salmo 119, mwinamwake lolembedwa ndi Hezekiya, Kalonga wachinyamata wa Yuda. Nyimbo yosangalatsayi ikuyamba ndi mawu akuti: “Achimwemwe ndamene ali angwiro m’mayendedwe awo, oyenda m’chilamulo cha Yehova. Achimwemwe iwo akusunga zikumbutso zake, akum’funafuna ndi mtima wonse.”—Salmo 119:1, 2, NW.
2. Kodi zikumbutso za Mulungu n’zogwirizana motani ndi chimwemwe?
2 ‘Timayenda m’chilamulo cha Yehova’ mwa kudziŵa Mawu ake molondola ndi kuwagwiritsa ntchito m’moyo. Komabe, popeza kuti ndife opanda ungwiro, tifunikira zikumbutso. Mawu achihebri otembenuzidwa kuti “zikumbutso” akusonyeza kuti Mulungu amatikumbutsa chilamulo chake, malangizo, malemba, ndi malamulo ake. (Mateyu 10:18-20) Tidzakhala achimwemwe nthaŵi zonse ngati tidzapitiriza kusunga zikumbutso zimenezo, chifukwa chakuti zimatithandiza kupeŵa mbuna zauzimu zomwe zimadzetsa tsoka ndi chisoni.
Mamatirani ku Zikumbutso za Yehova
3. Kodi lemba la Salmo 119: 60, 61 limatipatsa chidaliro chotani?
3 Zikumbutso za Yehova zinali zamtengo wapatali kwa wamasalmo yemwe anaimba kuti: “Ndinafulumira, osachedwa, kusamalira malamulo anu. Anandikulunga nazo zingwe za oipa; koma sindinaiwala chilamulo chanu.” (Salmo 119:60, 61) Zikumbutso za Yehova zimatithandiza kupirira chizunzo chifukwa chakuti tili n’chidaliro chonse kuti Atate wathu wakumwamba angadule zingwe za zitsenderezo zomwe adani angatikulunge nazo. M’nthaŵi yake, amatilanditsa ku zipsinjo zoterozo kotero kuti tithe kugwira ntchito yolalikira Ufumu.—Marko 13:10.
4. Kodi tiyenera kutani tikalandira zikumbutso za Mulungu?
4 Nthaŵi zina, zikumbutso za Yehova zimatiwongolera. Tilabadiretu kuwongolera kumeneko nthaŵi zonse, monga momwe wamasalmo anachitira. Iye anati kwa Mulungu mwapemphero: “Mboni zanu [“zikumbutso zanu,” NW] zomwe ndizo zondikondwetsa . . . ndikonda mboni zanu [“zikumbutso zanu,” NW].” (Salmo 119:24, 119) Tili ndi zikumbutso zambiri za Mulungu kuposa zomwe wamasalmo anali nazo. Mawu ambirimbiri ogwidwa m’Malemba Achihebri omwe akupezeka m’Malemba Achigiriki amatikumbutsa osati za malangizo a Yehova okha kwa anthu ake pansi pa Chilamulo komanso za zifuno zake zokhudza mpingo wachikristu. Mulungu akaona kuti n’koyenera kutikumbutsa zinthu zokhudza malamulo ake, timayamikira kwambiri chitsogozo choterocho. Ndipo mwa ‘kumamatira ku zikumbutso za Yehova,’ timapeŵa kukodwa muuchimo zomwe zimanyansa Mlengi wathu ndi kutichotsera chimwemwe chathu.—Salmo 119:31.
5. Kodi m’motani momwe tingakondere kwambiri zikumbutso za Yehova?
5 Kodi zikumbutso za Yehova tiyenera kuzikonda motani? “Moyo wanga unasamalira mboni zanu [“zikumbutso zanu,”NW]; ndipo ndizikonda kwambiri,” anaimba motero wamasalmo. (Salmo 119:167) Tidzakonda kwambiri zikumbutso za Yehova ngati tidzaziona ndi kuzilandira monga malangizo a Tate yemwe amasamaladi za ife. (1 Petro 5:6, 7) Tifunikira zikumbutso zake, ndipo chikondi chathu pa izo chidzakula pakuona momwe tikupindulira nazo.
Chifukwa Chake Tifunikira Zikumbutso za Mulungu
6. N’chifukwa chimodzi chiti chomwe tifunikira zikumbutso za Yehova, ndipo n’chiyani chomwe chidzatithandiza kuzikumbukira?
6 Chifukwa chimodzi chomwe tifunikira zikumbutso za Yehova n’chakuti ndife anthu osachedwa kuiŵala. Buku la maumboni lotchedwa The World Book Encyclopedia limati: “Kaŵirikaŵiri, anthu amaiŵala zinthu zomwe anamva pakanthaŵi. . . . Mwinamwake inu zinakuchitikiranipo kuti nthaŵi inayake munalephera kukumbukira dzina linalake kapena nkhani inayake mutangotsala pang’ono kuitchula. . . . Kuiŵala kwakanthaŵi ngati kumeneku kumachitika mobwerezabwereza. Asayansi akuyerekezera ndi kuyesa kufufuza chinthu chomwe chasokonekera m’chipinda chodzaza katundu. . . . Njira yabwino yokhalira wotsimikiza kukumbukira nkhani inayake ndiyo kuiphunzira mobwerezabwereza ngakhale kuti nkhaniyo mukuidziŵa bwino.” Kuphunzira mwakhama komanso kubwerezabwereza kudzatithandiza kukumbukira zikumbutso za Mulungu ndi kuzigwiritsa ntchito kaamba ka ubwino wathu.
7. N’chifukwa chiyani zikumbutso za Mulungu zikufunika kwambiri lerolino kuposa ndi kale lonse?
7 Tifunikira zikumbutso za Yehova lerolino kuposa ndi kale lonse chifukwa chakuti kuipa kwafika pachimake m’mbiri ya anthu. Tikalabadira zikumbutso za Mulungu, timapeza nzeru zofunikira popeŵa kukopeka ndi njira zoipa zadzikoli. Wamasalmo anati: “Ndili nayo nzeru yakuposa aphunzitsi anga onse; pakuti ndilingalira mboni zanu [“zikumbutso zanu,” NW]. Ndizindikira koposa okalamba popeza ndinasunga malangizo anu. Ndinaletsa mapazi anga njira iliyonse yoipa, kuti ndisamalire mawu anu.” (Salmo 119:99-101) Mwa kusunga zikumbutso za Mulungu, tidzapeŵa “njira iliyonse yoipa” ndipo tidzapeŵa kuchita umo achitira anthu miyandamiyanda, “odetsedwa m’nzeru zawo, oyesedwa alendo pa moyo wa Mulungu.”—Aefeso 4:17-19.
8. Kodi tingakonzekere bwino motani kugonjetsa ziyeso za chikhulupiriro?
8 Zikumbutso za Mulungu zikufunikanso chifukwa chakuti zimatilimbitsa kuti tithe kupirira mayesero athu ambiri ‘m’nthaŵi ya chimaliziro’ ino. (Danieli 12:4) Popanda zikumbutso zimenezo tingakhale ‘akumva akuiŵala.’ (Yakobo 1:25) Koma kuphunzira Malemba mwakhama patokha kapena limodzi ndi mpingo mwa kugwiritsa ntchito zofalitsa zochokera kwa “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru” kudzatithandiza kupambana ziyeso za chikhulupiriro. (Mateyu 24:45-47) Zogaŵira zauzimu zimenezo zimatithandiza kuona zofunika kuchita kuti tikondweretse Yehova tikagwa m’chiyeso.
Kufunika kwa Misonkhano Yathu
9. Kodi “mphatso mwa amuna” ndani, ndipo amathandiza motani okhulupirira anzawo?
9 Chosoŵa chathu cha zikumbutso za Mulungu chimakwaniritsidwa m’njira ina pa misonkhano yachikristu, kumene abale oikidwa amapereka malangizo. Mtumwi Paulo analemba kuti mmene Yesu “anakwera kumwamba, anamanga ndende undende, naninkha zaufulu kwa anthu [“mphatso mwa amuna,” NW].” Paulo anawonjezera kuti: “[Kristu] anapatsa ena akhale atumwi; ndi ena aneneri; ndi ena alaliki; ndi ena abusa, ndi ena aphunzitsi; kuti akonzere oyera mtima ku ntchito ya utumiki, kumangirira thupi la Kristu.” (Aefeso 4:8, 11, 12) Tikuyamikiratu kwabasi “mphatso mwa amuna” zimenezi—akulu oikidwa—chifukwa chakuti zimatikumbutsa zikumbutso za Yehova tikasonkhana kuti tim’lambire!
10. Kodi mfundo yaikulu ya Ahebri 10:24, 25 n’jotani?
10 Kuyamikira zogaŵira zaumulungu kudzatisonkhezera kupezeka pa misonkhano yathu isanu yampingo mlungu uliwonse. Paulo anagogomezera kufunika kwa kusonkhana pamodzi nthaŵi zonse. Iye analemba kuti: “Tiganizirane wina ndi mnzake kuti tifulumizane ku chikondano ndi ntchito zabwino, osaleka kusonkhana kwathu pamodzi, monga amachita ena, komatu tidandaulirane, ndiko koposa monga momwe muona tsiku lilikuyandika.”—Ahebri 10:24, 25.
11. Kodi uliwonse wa misonkhano yathu ya mlungu ndi mlungu umatipindulitsa motani?
11 Kodi m’mayamikira zomwe misonkhano yathu imatichitira? Phunziro la Nsanja ya Olonda la mlungu ndi mlungu limalimbitsa chikhulupiriro chathu, limatithandiza kuchita mogwirizana ndi zikumbutso za Yehova, ndiponso limatilimbikitsa polimbana ndi “mzimu wa dziko lapansi.” (1 Akorinto 2:12; Machitidwe 15:31) Pa Msonkhano Wapoyera, okamba nkhani amapereka malangizo ochokera m’Mawu a Mulungu, kuphatikizapo zikumbutso za Yehova ndi “mawu a moyo wosatha” osangalatsa kwambiri a Yesu. (Yohane 6:68; 7:46; Mateyu 5:1–7:29) Maluso athu a kuphunzitsa amanoledwa pa Sukulu ya Utumiki wa Teokalase. Msonkhano wa Utumiki n’ngwamtengo wapatali chifukwa chakuti umatithandiza kupititsa patsogolo maluso athu a kupereka uthenga wabwino kunyumba ndi nyumba, ku maulendo obwereza, pa maphunziro a Baibulo apanyumba, ndi m’njira zinanso za utumiki wathu. Kagulu kochepa ka Phunziro la Buku la Mpingo kamatipatsa mwayi waukulu wolankhulapo zinthu zomwe nthaŵi zambiri zimakhudza zikumbutso za Mulungu.
12, 13. Kodi anthu a Mulungu m’dziko lina ku Asia anasonyeza motani kuyamikira misonkhano yachikristu?
12 Kupezeka pa misokhano ya mpingo nthaŵi zonse kumatikumbutsa malamulo a Mulungu ndi kutithandiza kuti tikhalebe olimba mwauzimu m’kati mwa nkhondo, mavuto a zachuma, ndi ziyeso zina za chikhulupiriro chathu. Akristu ena ngati 70 m’dziko lina ku Asia anatsimikizira kuti misonkhano n’njofunika kwambiri. Akristu ameneŵa anathaŵa m’nyumba zawo ndi kukakamizika kukakhala kunkhalango. Pofunitsitsa kupitiriza kusonkhana nthaŵi zonse, anabwerera ku tauni yakwawo yosakazidwa ndi nkhondoyo, anasasula zotsalira pa Nyumba ya Ufumu, ndi kukaimanganso kunkhalangoko.
13 Anthu a Yehova omwe apirira kwa zaka zambiri m’nkhondo kumbali ina ya dziko lomwelo, akupitirizabe kum’tumikira mwachangu. Mmodzi wa akulu ku chigawo chimenecho anafunsidwa kuti: “N’chiyani chomwe chathandiza kwambiri kuti abale asabalalike?” Anayankha bwanji? “Kwa zaka 19, sitinaphonyepo msonkhano ngakhale umodzi. Nthaŵi zina chifukwa cha kuphulika kwa mabomba kapena chifukwa cha zovuta zina, abale ena amalephera kukafika ku malo osonkhanira, koma sizinalepheretse msonkhano uliwonse.” Ndithudi, abale ndi alongo okondedwa ameneŵa akuzindikira kufunika kwa ‘kusaleka kusonkhana kwawo pamodzi.’
14. Kodi tingaphunzirenji pa chizoloŵezi cha Anna wokalambayo?
14 Anna, mkazi wamasiye wa zaka 84 zakubadwa “sanachoka ku Kachisi.” Zotsatira zake zinali zakuti, Anna anali komweko pamene Yesu anam’bweretsa kukachisiko posapita nthaŵi atangobadwa. (Luka 2:36-38) Kodi m’mafunitsitsa kusaphonya misonkhano? Kodi mukuyesetsa mwakhama kuti musaphonye chigawo chilichonse m’misonkhano yathu yapadera ndi m’misonkhano yachigawo? Malangizo opindulitsa mwauzimu omwe timalandira m’misonkhano imeneyi amatipatsa umboni woonekeratu wakuti Atate wathu wakumwamba amasamalira anthu ake. (Yesaya 40:11) Nthaŵi zoterezi zimadzetsanso chimwemwe, ndipo kupezekapo kwathu kumasonyeza kuyamikira kwathu zikumbutso za Yehova.—Nehemiya 8:5-8, 12.
Zikumbutso za Yehova Zimatipatula
15, 16. Kodi kusunga zikumbutso za Yehova kumakhudza motani khalidwe lathu?
15 Kusunga zikumbutso za Mulungu kumatilekanitsa ndi dziko loipali. Mwachitsanzo, kumvera zikumbutso za Mulungu kumatithandiza kupeŵa kuchita chiwerewere. (Deuteronomo 5:18; Miyambo 6:29-35; Ahebri 13:4) Chiyeso chakuti tinene bodza, tichite mosaona mtima, kapena kuba tingachigonjetse mosavuta mwa kuchita mogwirizana ndi zikumbutso zaumulungu. (Eksodo 20:15, 16; Levitiko 19:11; Miyambo 30:7-9; Aefeso 4:25, 28; Ahebri 13:18) Kusunga zikumbutso za Yehova kumatithandiza kupeŵa kubwezera choipa, kusunga chakukhosi, kapena kunenera aliyense miseche.—Levitiko 19:16, 18; Salmo 15:1, 3.
16 Mwa kumvera zikumbutso za Mulungu, timakhalabe opatulika, kapena kuti olekanitsidwa, kuti tim’tumikire. Ndipotu n’kofunika kwambiri kukhala olekana ndi dzikoli! Popemphera kwa Yehova usiku wotsiriza wa moyo wake wapadziko lapansi, Yesu anapempherera ophunzira ake kuti: “Ine ndawapatsa iwo mawu anu; ndipo dziko lapansi linadana nawo, chifukwa sakhala a dziko lapansi, monga Ine sindikhala wa dziko lapansi. Sindipempha kuti muwachotse iwo m’dziko lapansi, koma kuti muwasunge iwo kuletsa woipayo. Sali a dziko lapansi monga Ine sindili wa dziko lapansi. Patulani iwo m’choonadi; mawu anu ndi choonadi.” (Yohane 17:14-17) Tipitirizetu kuyamikira Mawu a Mulungu, omwe amatilekanitsa kaamba ka utumiki wake wopatulika.
17. N’chiyani chomwe chingachitike ngati titanyalanyaza zikumbutso za Mulungu, ndiyeno tiyenera kuchitanji?
17 Monga atumiki a Yehova, tiyenera kukhalabe ovomerezeka kuchita utumiki wake. Komabe, ngati titanyalanyaza zikumbutso za Mulungu, tingagonjetsedwe ndi mzimu wadziko lino womwe ukuchirikizidwa kwambiri m’kalankhulidwe kake, m’mabuku ake, m’zosangalatsa zake, ndi m’mikhalidwe yake. Ndipotu sitifuna n’komwe kukhala okondetsa chuma, odzitamandira, odzikuza, osayamika, osamvera, aukali, aliuma, odzitukumula mtima, okonda zosangalatsa m’malo mokonda Mulungu—kungotchulapo yoŵerengeka chabe ya mikhalidwe yomwe anthu otalikirana ndi Mulungu amasonyeza. (2 Timoteo 3:1-5) Popeza kuti tikukhala m’katikati mwa masiku otsiriza a dongosolo la zinthu loipali, tiyeni tipitirizebe kupempherera thandizo la Mulungu kotero kuti tithe kupitirizabe kusunga zikumbutso za Yehova ndikuti potero ‘tizisamalire monga mwa mawu ake.’—Salmo 119:9.
18. Kusunga zikumbutso za Mulungu kungatisonkhezere kuchita zinthu zabwino zotani?
18 Zikumbutso za Yehova zimachita zambiri zoposa kungotichenjeza pazinthu zomwe sitiyenera kuchita. Kusunga zikumbutso zake kudzatichititsa zinthu zabwino, kutisonkhezera kukhulupirira Yehova kotheratu ndi kum’konda ndi mtima wathu wonse, moyo wathu wonse, nzeru zathu zonse, ndi mphamvu zathu zonse. (Deuteronomo 6:5; Salmo 4:5; Miyambo 3:5, 6; Mateyu 22:37; Marko 12:30) Zikumbutso za Mulungu zimatisonkhezeranso kukonda anansi athu. (Levitiko 19:18; Mateyu 22:39) Kwenikweni timasonyeza kukonda Mulungu ndi anansi athu mwa kuchita chifuno cha Mulungu ndi kuuza ena chidziŵitso cha Mulungu chopatsa moyo.—Miyambo 2:1-5.
Kusunga Zikumbutso za Yehova N’Kopatsa Moyo!
19. Kodi ena tingawasonyeze motani kuti kumvera zikumbutso za Yehova n’kothandiza ndi kopindulitsa?
19 Ngati tisunga zikumbutso za Yehova ndi kuthandiza ena kuchitanso chimodzimodzi, tidzadzipulumutsa tokha ndi iwo akumva ife. (1 Timoteo 4:16) Kodi ena tingawasonyeze motani kuti kumvera zikumbutso za Yehova n’kothandizadi ndi kopindulitsa. Mwa kugwiritsa ntchito mfundo zachikhalidwe za m’Baibulo m’moyo wathu. Poona zimenezo, awo onse “ofuna moyo wosatha” adzakhala ndi umboni wakuti njira yoperekedwa m’Mawu a Mulungu ndiyodi yabwino kwambiri kuilondola. (Machitidwe 13:48, NW) Adzaonanso kuti ‘Mulungu ali ndithu mwa ife’ ndipo adzasonkhezereka kugwirizana nafe m’kulambira Ambuye Mfumu Yehova.—1 Akorinto 14:24, 25.
20, 21. Zikumbutso za Mulungu ndi mzimu wake zidzatithandiza kuchita chiyani?
20 Mwa kupitirizabe kuphunzira Malemba, kutsatira zomwe tikuphunzirazo, ndi kugwiritsa ntchito zogaŵira zauzimu za Yehova mokwanira, tidzakonda kwambiri zikumbutso zake. Ngati titazimvera, zikumbutso zimenezi zidzatithandiza kuvala “umunthu watsopano umene unalengedwa monga mwa chifuniro cha Mulungu m’chilungamo chenicheni ndi kukhulupirika.” (Aefeso 4:20-24, NW) Zikumbutso za Yehova ndi mzimu wake woyera zidzatitheketsa kusonyeza chikondi, chimwemwe, mtendere, kuleza mtima, chifundo, kukoma mtima, chikhulupiriro, kufatsa, kudziletsa—mikhalidwe yosiyana kotheratu ndi njira za dziko logona m’mphamvu za Satanali! (Agalatiya 5:22, 23; 1 Yohane 5:19) Choncho, tiyenera kuyamikira pamene tikumbutsidwa za zofuna za Yehova paphunziro la Baibulo laumwini, ndi akulu oikidwa, komanso pamisonkhano yathu ya pampingo, misonkhano yapadera, ndi misonkhano ikuluikulu.
21 Chifukwa chakuti timasunga zikumbutso za Yehova, ndife achimwemwe ngakhale tizunzidwe chifukwa cha chilungamo. (Luka 6:22, 23) Timayembekezera Mulungu kutipulumutsa m’mikhalidwe yochititsa mantha kwambiri. Zimenezo n’zofunika kwambiri makamaka panopa pamene mitundu yonse akuisonkhanitsira ku “nkhondo ya tsiku lalikulu la Mulungu, Wamphamvuyonse” pa Harmagedo.—Chivumbulutso 16:14-16.
22. Kodi tiyenera kutsimikiza mtima kuchitanji ponena za zikumbutso za Yehova?
22 Kuti tidzalandire mphatso yamtengo wapatali ya moyo wosatha, tiyenera kukonda kwambiri zikumbutso za Yehova ndi kuzisunga ndi mtima wonse. Choncho tikhaletu ndi mzimu wa wamasalmo yemwe anaimba kuti: “Mboni zanu [“zikumbutso zanu,”NW] ndizo zolungama kosatha; mundizindikiritse izi, ndipo ndidzakhala ndi moyo.” (Salmo 119:144) Ndipotu tisonyeze kutsimikiza mtima koonekeratu m’mawu a wamasalmo akuti: “Ndinaitanira Inu [Yehova]: Ndipulumutseni, ndipo ndidzasamalira mboni zanu [“zikumbutso zanu,” NW]. (Salmo 119:146) Inde, tiyeni tisonyeze mwa mawu ndi zochita, kuti timakondadi kwambiri zikumbutso za Yehova.
Mungayankhe Bwanji?
• Kodi wamasalmo anaziona motani zikumbutso za Yehova?
• N’chifukwa chiyani tifunikira zikumbutso za Mulungu?
• Kodi misonkhano yathu imachita mbali yofunika yotani yokhudza zikumbutso zaumulungu?
• Kodi zikumbutso za Yehova zimatilekanitsa motani ndi dzikoli?
[Chithunzi patsamba 15]
Wamasalmo anakonda kwambiri zikumbutso za Yehova
[Zithunzi pamasamba 16, 17]
Potsatira chitsanzo cha Anna, kodi m’mayesetsa kusaphonya misonkhano?
[Chithunzi patsamba 18]
Kumvera zikumbutso za Yehova kumatilekanitsa monga oyera ndi ovomerezeka kuchita utumiki wake