“Mphatso za Amuna” Zoperekedwa Kuti Zisamalire Nkhosa za Yehova
“Pamene iye anakwera kumwamba anatenga andende; napereka mphatso za amuna.”—AEFESO 4:8, NW.
1. Kodi mlongo wina wachikristu ananenanji za akulu mumpingo wakwawo?
“NDIKUTHOKOZA kwambiri kaamba ka mmene mumatisamalira. Mmene mumatimwetulira, chikondi chimene mumatisonyeza, ndi mmene mumatidera nkhaŵa, mumachita zimenezo mochokeradi pansi pa mtima. Nthaŵi zonse mumatchera khutu ku zodandaula zathu ndipo mumatilimbikitsa ndi mawu a m’Baibulo. Ndimapemphera kuti ndizikulemekezani nthaŵi zonse.” Ameneŵa ndi mawu amene mlongo wina wachikristu analembera akulu mumpingo wakwawo. Mwachionekere, iye anakhudzidwa mtima ndi chikondi chimene abusa achikristu achifundowo ankasonyeza.—1 Petro 5:2, 3.
2, 3. (a) Malinga n’kunena kwa Yesaya 32:1, 2, kodi akulu achifundo amasamalira motani nkhosa za Yehova? (b) Kodi mkulu ayenera kuchita motani kuti aonedwe monga mphatso?
2 Akulu ndi mphatso yochokera kwa Yehova kuti asamalire nkhosa zake. (Luka 12:32; Yohane 10:16) Nkhosa za Yehova n’zokondeka kwambiri kwa iye—amazikonda kwabasi, moti anachita kuzigula ndi mwazi wamtengo wapatali wa Yesu. Ndiye chifukwa chake Yehova amakondwera kwambiri akamaona kuti akulu akusamalira nkhosa zake mwachifundo. (Machitidwe 20:28, 29) Tamverani malongosoledwe a m’mawu aulosi onena za akulu kapena “akalonga” ameneŵa: “Munthu adzakhala monga pobisalira mphepo, ndi pousira chimphepo; monga mitsinje yamadzi m’malo ouma, monga mthunzi wa thanthwe lalikulu m’dziko lotopetsa.” (Yesaya 32:1, 2) Inde, iwo ayenera kuteteza, kutsitsimutsa, komanso kutonthoza nkhosa zake. Akulu amene amaŵeta nkhosa mwachifundo amayesetsa kuchita zimene Mulungu amayembekeza kwa iwo.
3 Akulu oterowo ndi amene Baibulo limawatcha “mphatso za amuna.” (Aefeso 4:8, NW) Pamene muganiza za mphatso, mumalingalira za chinthu china choperekedwa kuti chikwaniritse chosoŵa kapena choti chisangalatse wolandirayo. Mkulu angaonedwe kukhala mphatso ngati iye agwiritsa ntchito maluso ake kuperekera chithandizo chofunikira ndi kusungitsira chimwemwe pakati pa nkhosa. Kodi angachite motani zimenezo? Yankho lake, lopezeka m’mawu a Paulo pa Aefeso 4:7-16, limakulitsa chikondi cha Yehova pa nkhosa zake.
“Mphatso za Amuna”—Zimachokera Kuti?
4. Pokwaniritsa Salmo 68:18, kodi Yehova ‘anakwera motani kumwamba,’ ndipo ndani anali “mphatso za amuna”?
4 Pamene Paulo anagwiritsa ntchito mawu akuti “mphatso za amuna,” anagwira mawu Mfumu Davide, yemwe anati ponena za Yehova: “Munakwera kumka kumwamba, munapita nawo undende kuuyesa ndende; munalandira zaufulu [“mphatso”, NW] mwa anthu.” (Salmo 68:18) Aisrayeli atakhala m’Dziko Lolonjezedwa zaka zochulukirapo, Yehova mophiphiritsa ‘anakwera’ Phiri la Ziyoni nakhazikitsa Yerusalemu monga likulu la ufumu wa Israyeli, Davide nakhala mfumu yake. Koma kodi ndani anali “mphatso za amuna”? Anali amuna otengedwa ukapolo pamene dzikolo linagonjetsedwa. Ena mwa andende ameneŵa pambuyo pake anadzapatsidwa kwa Alevi kuti aziwathandiza ntchito pachihema chokumanapo.—Ezara 8:20.
5. (a) Kodi Paulo akusonyeza motani kuti Salmo 68:18 likukwaniritsidwa mumpingo wachikristu? (b) Ndi motani mmene Yesu ‘anakwerera kumwamba’?
5 M’kalata yake yolembera Aefeso, Paulo akusonyeza kuti kukwaniritsidwa kwakukulu kwa mawu a wamasalmoyo kukuchitika mumpingo wachikristu. Ponena za mawu a pa Salmo 68:18, Paulo analemba kuti: “Ndipo kwa yense wa ife chapatsika chisomo, monga mwa muyeso wa mphatso ya Kristu. Chifukwa chake iye akuti: [‘Pamene iye anakwera kumwamba anatenga andende; napereka mphatso za amuna’].” (Aefeso 4:7, 8) Paulo pano akugwiritsa ntchito salmoli kwa Yesu monga woimira Mulungu. Yesu ‘analilaka dziko lapansi’ mwa kukhalabe wokhulupirika. (Yohane 16:33) Iye anagonjetsanso imfa ndi Satana pamene Mulungu anamuukitsa kwa akufa. (Machitidwe 2:24; Ahebri 2:14) Mu 33 C.E., Yesu ataukitsidwa anakwera “popitiriratu, miyamba yonse”—pamwamba penipeni kuposa zolengedwa zonse zakumwamba. (Aefeso 4:9, 10; Afilipi 2:9-11) Monga wolakika, Yesu anatenga “andende” kwa mdani. Motani?
6. Kuyambira pa Pentekoste wa 33 C.E., kodi Yesu wokwerayo anayamba motani kufunkha nyumba ya Satana, ndipo anatani nawo ‘andendewo’?
6 Pamene anali padziko lapansi, Yesu anasonyeza mphamvu yake yoposa Satana mwa kumasula aja omangidwa m’nsinga za ziŵanda. Zinali ngati kuti Yesu anaphwasula nyumba ya Satana, nam’manga iye, ndi kufunkha katundu wake. (Mateyu 12:22-29) Tangoganizani kufunkha kwakukulu kumene Yesu anakuchita, ataukitsidwa ndi ‘kupatsidwa mphamvu zonse kumwamba ndi padziko lapansi’! (Mateyu 28:18) Kuyambira pa Pentekoste wa 33 C.E., Yesu wokwera kumwambayo, pokhala woimira Mulungu, anayamba kufunkha nyumba ya Satana mwa ‘kutenga andende’—amuna amene kwa nthaŵi yaitali anali muukapolo ku uchimo ndi imfa pansi pa mphamvu ya Satana. “Andende” ameneŵa anadzipereka kukhala “akapolo a Kristu, akuchita chifuniro cha Mulungu chochokera kumtima.” (Aefeso 6:6) Kunena kwake titero, kuti Yesu anawakwatula ku mphamvu ya Satana, ndipo powaika kumbali ya Yehova, anawapereka ku mpingo monga “mphatso za amuna.” Talingalirani mkwiyo wa Satana pamene iwowo anakwatulidwa m’manja mwake iye akupenya koma osatha kuchitapo kanthu.
7. (a) Kodi ‘mphatso za amunazo’ zimatumikira pamaudindo otani m’mipingo? (b) Ndi mwayi wotani umene Yehova wapereka kwa mwamuna aliyense amene akutumikira monga mkulu?
7 Kodi “mphatso za amuna” zimenezo zilimo mumpingo lero? Ndithudi zilimo! Zimatumikira monga akulu, zimagwira ntchito zolimba monga ‘alaliki, abusa, ndi aphunzitsi’ m’mipingo yoposa 87,000 ya anthu a Mulungu padziko lonse lapansi. (Aefeso 4:11) Satana amalakalaka kuona amuna ameneŵa akumachitira nkhanza nkhosazo. Koma chimenecho sindicho cholinga chimene Mulungu, kudzera mwa Kristu, wawaperekera iwo ku mpingo. M’malo mwake, Yehova wapereka amuna ameneŵa kuti mpingo usamalike bwino, ndipo iwo adzaŵerengeredwa mlandu kwa Mulungu pa nkhosa zimene iye waziikiza m’manja mwawo. (Ahebri 13:17) Ngati inuyo mukutumikira monga mkulu, Yehova wakupatsani mwayi wodabwitsa wakuti muonetse kukhala mphatso, kapena dalitso, kwa abale anu. Mutha kuchita zimenezo mwa kukwaniritsa maudindo anayi ofunika kwambiri.
Pamene ‘Kukonza’ Kuli Kofunikira
8. Kodi tonsefe nthaŵi zina timafunikira kukonzedwa m’njira zotani?
8 Choyamba, “mphatso za amuna” zimaperekedwa makamaka ‘kuti zikonze oyera mtima,’ anatero Paulo. (Aefeso 4:12) Nauni yachigiriki yomasuliridwa kuti ‘kukonza’ limatanthauza kubwezeretsa chinthu “m’malo mwake.” Monga anthu opanda ungwiro, tonse timafunikira kukonzedwa nthaŵi ndi nthaŵi—kuti kalingaliridwe kathu, maganizo, kapena mayendedwe athu abwezeredwe “m’malo mwake” mogwirizana ndi malingaliro ndi chifuniro cha Mulungu. Yehova wapereka mwachikondi “mphatso za amuna” kuti zitithandize kukonza mofunikira. Kodi zimachita motani zimenezo?
9. Kodi mkulu angathandize motani kukonza nkhosa imene yachimwa?
9 Nthaŵi zina, mkulu angafunsidwe kuti athandize nkhosa imene yachimwa, imene mwina ‘yagwidwa nako kulakwa.’ Kodi mkuluyo angathandize motani? “Mubweze wotereyo mu mzimu wa chifatso,” amatero Agalatiya 6:1. Chifukwa chake, popereka uphungu, mkulu sakayenera kukalipira wolakwayo, akumalankhula ndi mawu aukali. Uphungu uyenera kulimbikitsa, osati ‘kuopseza’ woulandirayo. (2 Akorinto 10:9; yerekezani ndi Yobu 33:7.) Munthuyo angakhale atagwidwa kale chisoni, choncho mbusa wachikondi amapeŵa kusweratu mzimu wake. Ngati n’koonekeratu kuti uphungu, kapena chidzudzulo champhamvu, chikuperekedwa mwachikondi, n’kothekera kwambiri kuti chidzakonza malingaliro kapena mayendedwe a wochimwayo, kumeneko ndiko kum’bweza iye.—2 Timoteo 4:2.
10. Kodi kukonza ena kumaphatikizapo chiyani?
10 Popereka “mphatso za amuna” kuti azitikonza, cholinga cha Yehova chinali choti akulu akhale otsitsimutsa mwauzimu ndi oyenera kutsanziridwa ndi anthu ake. (1 Akorinto 16:17, 18; Afilipi 3:17) Kukonza ena sindiko chabe kuwongolera aja ogwidwa nako kulakwa komanso kuthandiza okhulupirika kuti ayendebe molungama.a Lerolino, pokhalapo mavuto ambiri omwe amatipsinja, ambiri amafunikira kuwalimbikitsa kuti agwiritse. Ena angafunikire kuthandizidwa mwachifundo kuti akonzenso malingaliro awo m’njira ya Mulungu. Mwachitsanzo, Akristu okhulupirika ena akulimbana ndi maganizo amphamvu odziona kukhala opereŵera kapena osafunika kwenikweni. “Amantha mtima” oterowo angaganize kuti Yehova sadzawakonda konse ndi kuti ngakhale atayesetsa mwakhama chotani kutumikira Mulungu, iye sangazilandire ntchito zawo. (1 Atesalonika 5:14) Koma kalingaliridwe koteroko sikakugwirizana ndi mmene Mulungu amaoneradi alambiri ake.
11. Kodi akulu angachitenji kuti athandize aja amene akulimbana ndi maganizo odziona kukhala opanda pake?
11 Akulu, kodi mungatani kuti muthandize oterowo? Mwachifundo kambiranani nawo umboni wa m’Malemba wosonyeza kuti Yehova amasamalira aliyense wa atumiki ake ndipo atsimikizireni kuti Malembaŵa amagwira ntchito kwa iwo monga munthu payekha. (Luka 12:6, 7, 24) Athandizeni kuona kuti Yehova ndiye ‘wawakoka’ kuti adzam’tumikire, chotero n’kosakayikitsa kuti iye akuwaona kukhala ofunika kwambiri. (Yohane 6:44) Atsimikizireni kuti si iwo okha amene akukumana ndi zimenezo—atumiki a Yehova ambiri okhulupirika akumanapo nazo. Mneneri Eliya nthaŵi ina anapsinjika maganizo kwambiri moti anakhumba kuti angofa basi. (1 Mafumu 19:1-4) Akristu odzozedwa ena a m’zaka za zana loyamba anadziona kukhala ‘otsutsidwa’ ndi mitima yawo. (1 Yohane 3:20) Komanso n’zolimbikitsa kudziŵa kuti okhulupirika a m’nthaŵi za m’Baibulo amenewo ‘ankamva zomwezi tizimva ife.’ (Yakobo 5:17) Muthanso kuŵerenga limodzi ndi opsinjika mtimawo nkhani zolimbikitsa za mu Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! Mulungu, amene amapereka “mphatso za amuna” zimenezo sangalephere kuona khama lanu lachikondi poyesetsa kubwezeretsa chidaliro mwa oterowo.—Ahebri 6:10.
“Kumangirira” Gulu la Nkhosa
12. Kodi mawu akuti “kumangirira thupi la Kristu” amasonyezanji, ndipo chinsinsi chake n’chiyani chomangirira nacho gulu la nkhosa?
12 Chachiŵiri, “mphatso za amuna” zimenezo zaperekedwa ndi cholinga choti ‘zimangirire thupi la Kristu.’ (Aefeso 4:12) Paulo pano akugwiritsa ntchito mawu okuluŵika. “Kumangirira” kumatikumbutsa ntchito yomanga, ndipo “thupi la Kristu” limatanthauza anthu—ziŵalo za mpingo wa Akristu odzozedwa. (1 Akorinto 12:27; Aefeso 5:23, 29, 30) Akulu afunikira kuthandiza abale awo kuti alimbe mwauzimu. Cholinga chawo ndicho ‘kumangirira osati kugwetsa’ gulu la nkhosa. (2 Akorinto 10:8) Chinsinsi chomangirira nacho gulu la nkhosa ndicho chikondi, pakuti “chikondi chimangirira.”—1 Akorinto 8:1.
13. Kodi kukhala wachifundo kumatanthauzanji, ndipo n’chifukwa chiyani kuli kofunika kuti akulu azisonyeza chifundo?
13 Mbali imodzi ya chikondi imene imathandiza akulu kumangirira gulu la nkhosa ndiyo chifundo. Kukhala wachifundo kumatanthauza kuganizira ena—kumvetsa maganizo ndi malingaliro awo, kuganizira zofooka zawo. (1 Petro 3:8) N’chifukwa chiyani kuli kofunika kuti akulu akhale achifundo? Chifukwa chachikulu n’chakuti Yehova—amene amapereka “mphatso za amuna”—ndi Mulungu wachifundo. Pamene atumiki ake akuvutika kapena kumva kupweteka, amawamvera chisoni. (Eksodo 3:7; Yesaya 63:9) Iye amaganizira zofooka zawo. (Salmo 103:14) Choncho, ndi motani mmene akulu angasonyezere chifundo?
14. Kodi akulu angasonyeze chifundo kwa ena m’njira zotani?
14 Pamene wina wolefulidwa apita kwa iwo, amatchera khutu, ndi kumvetsera malingaliro ake. Amayesa kumvetsa chiyambi, umunthu, ndi mikhalidwe ya abale awo. Ndiyeno pamene akulu apereka chithandizo chomangirira cha m’Malemba, kumakhala kosavuta kuti nkhosazo zichilandire chifukwa chikuchokera kwa abusa amene amamvetsa ndi kusamalira moona mtima. (Miyambo 16:23) Chifundo chimasonkhezeranso akulu kuganizira zofooka za ena ndi mmene anthuwo angamvere chifukwa cha zofookazo. Mwachitsanzo, Akristu ena moona mtima angadzimve amlandu chifukwa sathanso kuchita zochuluka potumikira Mulungu, mwina chifukwa cha ukalamba kapena kudwala. Komanso, ena angafunikire chilimbikitso kuti awongolere utumiki wawo. (Ahebri 5:12; 6:1) Chifundo chidzasonkhezera akulu kupeza “mawu okondweretsa” amene amalimbikitsa ena. (Mlaliki 12:10) Pamene nkhosa za Yehova zimangiriridwa ndi kulimbikitsidwa, chikondi chawo kwa Mulungu chimazisonkhezera kuti zichite zonse zomwe zingathe pom’tumikira iye!
Amuna Amene Amalimbikitsa Mgwirizano
15. Kodi mawu akuti “umodzi wa chikhulupiriro” amatanthauzanji”?
15 Chachitatu, “mphatso za amuna” zaperekedwa kuti tikhale ndi “umodzi wa chikhulupiriro, ndi wa chizindikiritso cha Mwana wa Mulungu.” (Aefeso 4:13) Mawu akuti “umodzi wa chikhulupiriro” amaonetsa mgwirizano osati wa chikhulupiriro chokha komanso wapakati pa okhulupirirawo. Ichinso ndi chifukwa china chimene Mulungu waperekera “mphatso za amuna”—kulimbikitsa mgwirizano pakati pa anthu ake. Nanga amachita motani zimenezo?
16. N’chifukwa chiyani kuli kofunika kuti akulu asunge mgwirizano pakati pawo?
16 Choyamba, iwo eniwo ayenera kukhala ogwirizana. Ngati abusa ali ogaŵikana, nkhosa sizingasamaliridwe. Nthaŵi yofunika kwambiri imene ikanagwiritsidwa ntchito kuŵeta gulu la nkhosa ingamangotayikira pamisonkhano yaitali ndi kukangana basi pankhani zazing’ono. (1 Timoteo 2:8) Akulu sangangogwirizana pa nkhani ina iliyonse imene akambirana, pakuti ndi anthu okhala ndi maumunthu amene angasiyane kwambiri. Kugwirizana sikutanthauza kuti iwo asiya kukhala ndi malingaliro osiyana kapena kuti sayenera kuwalankhula m’njira yabwino pokambirana momasuka. Akulu amasunga mgwirizano wawo mwa kumvetsera mwaulemu kwa wina ndi mnzake popanda kuweruziratu. Ndipo malinga ngati palibe pulinsipulo la Baibulo limene likuphwanyidwa, aliyense ayenera kulolera ndi kuchirikiza chigamulo chomalizira cha bungwe la akulu. Mzimu wololera umasonyeza kuti iwo akutsogozedwa ndi “nzeru yochokera kumwamba,” imene ili “yamtendere, yaulere.”—Yakobo 3:17, 18.
17. Kodi akulu angathandize motani kusungitsa mgwirizano mumpingo?
17 Akulu ayeneranso kukhala maso kuti alimbikitse mgwirizano mumpingo. Pamene mikhalidwe yogaŵanitsa—monga miseche yovulaza, kukonda kuganizirana zoipa, kapena mzimu wa mikangano—iopseza mtendere, iwo amapereka uphungu wothandiza mwamsanga. (Afilipi 2:2, 3) Mwachitsanzo, mwina akulu angadziŵe za anthu ena okonda kwambiri kusuliza anzawo kapena okonda kududukira nkhani za ena, kapena kuti akazitape. (1 Timoteo 5:13; 1 Petro 4:15) Akuluwo adzayesa kuthandiza oterowo kuzindikira kuti mchitidwe umenewo umawombana ndi zimene Mulungu amatiphunzitsa ndi kuti “yense adzasenza katundu wake wa iye mwini.” (Agalatiya 6:5, 7; 1 Atesalonika 4:9-12) Mwa kugwiritsa ntchito Malemba, ayenera kufotokoza kuti Yehova amasiyira zinthu zambiri chikumbumtima chathu, ndipo aliyense wa ife sayenera kuweruza ena pankhani zoterozo. (Mateyu 7:1, 2; Yakobo 4:10-12) Kuti atumikire mogwirizana, payenera kukhala mkhalidwe wokhulupirirana ndi kulemekezana pampingo. Mwa kupereka uphungu wa m’Malemba pamene uli wofunikira, “mphatso za amuna” zimenezo zimatithandiza kusungitsa mtendere ndi mgwirizano.—Aroma 14:19.
Kuteteza Gulu la Nkhosa
18, 19. (a) Kodi “mphatso za amuna” zimatiteteza kwa ndani? (b) Kodi ndi ngozi zina ziti zimene nkhosa ziyenera kutetezedwako, ndipo akulu amachita motani kuti ateteze nkhosazo?
18 Chachinayi, Yehova amapereka “mphatso za amuna” potiteteza kuti tisatengeke “ndi mphepo yonse ya chiphunzitso, ndi tsenga la anthu, ndi kuchenjerera kukatsata chinyengo cha kusokeretsa.” (Aefeso 4:14) Liwu la m’chinenero choyambirira lotembenuzidwa kuti “tsenga” akuti limatanthauza “kunama ndi mayere” kapena “luso lozimbaitsa mwamayere.” Kodi zimenezo sizikutikumbutsa machenjera amene ampatuko amagwiritsa ntchito? Pogwiritsa ntchito zigomeko zamachenjera, amatha kupotoza Malemba poyesa kunyengerera Akristu oona ndi kuwapatutsa pa chikhulupiriro chawo. Akulu ayenera kukhala maso poyang’anira “mimbulu yosautsa” yoteroyo!—Machitidwe 20:29, 30.
19 Nkhosa za Yehova ziyenera kutetezedwa ku ngozi zinanso. Mbusa wamakedzana Davide anateteza nkhosa za atate wake mopanda mantha ku zilombo zolusa. (1 Samueli 17:34-36) Lerolinonso, ikhoza kubuka mikhalidwe yofuna kuti abusa achikristu alimbe mtima pofuna kuteteza nkhosa za Yehova kwa aliyense amene angayese kuzichitira nkhanza kapena kuzipondereza, makamaka zija zosalimba kwambiri. Akulu sadzachedwa kuchotsa mumpingo ochimwira dala amene amagwiritsa ntchito machenjera, chinyengo, ndi chiwembu pofuna kulimbikitsa makhalidwe oipa.b—1 Akorinto 5:9-13; yerekezani ndi Salmo 101:7.
20. N’chifukwa chiyani tingamve kukhala otetezeka posamalidwa ndi “mphatso za amuna”?
20 Ha! tili oyamikira bwanji, pokhala ndi “mphatso za amuna” zimenezi. Iwo potisamalira mwachikondi, timamva kukhala otetezeka, pakuti amatikonza mwachifundo, natimangirira mwachikondi, akumasungitsa mgwirizano wathu, ndi kutiteteza molimba mtima. Koma kodi “mphatso za amuna” zimenezi ziyenera kuliona motani gawo lawo mumpingo? Ndipo tingasonyeze motani kuti timayamikira kukhala nazo? Nkhani yotsatira idzayankha mafunso ameneŵa.
[Mawu a M’munsi]
a M’Baibulo lachigiriki lotchedwa Septuagint, verebu imodzimodzi imeneyo yomasuliridwa kuti “kukonza” inagwiritsidwa ntchito pa Salmo 17[16]:5, pamene Davide wokhulupirikayo anapemphera kuti mapazi ake ayendebe m’mabande a Yehova.
b Mwachitsanzo, onani “Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga” mu Nsanja ya Olonda yachingelezi ya November 15, 1979, masamba 31-2, ndi nkhani yakuti “Tidane Nacho Choipa” m’kope la January 1, 1997, masamba 26-9.
Kodi Mukukumbukira?
◻ Kodi “mphatso za amuna” ndani, ndipo n’chifukwa chiyani Mulungu wazipereka ku mpingo kudzera mwa Kristu?
◻ Kodi akulu amakwaniritsa motani udindo wawo wokonza nkhosa?
◻ Kodi akulu angatani kuti amangirire okhulupirira anzawo?
◻ Kodi akulu angasungitse motani mgwirizano mumpingo?
[Chithunzi patsamba 10]
Chifundo chimathandiza akulu kulimbikitsa opsinjika mtima
[Chithunzi patsamba 10]
Mgwirizano pakati pa akulu umalimbikitsa mgwirizano mumpingo