Ezara
8 Awa ndi mayina a atsogoleri a nyumba za makolo awo komanso mndandanda wa mayina wotsatira makolo a anthu amene ndinachoka nawo ku Babulo, mu ulamuliro wa Mfumu Aritasasita:+ 2 Pa ana a Pinihasi+ panali Gerisomu, pa ana a Itamara+ panali Danieli, pa ana a Davide panali Hatusi. 3 Pa ana a Sekaniya panali Zekariya wochokera kwa ana a Parosi. Iye anali ndi amuna amene analembetsa mayina awo okwana 150. 4 Pa ana a Pahati-mowabu+ panali Eliho-enai mwana wa Zerahiya. Iye anali ndi amuna 200. 5 Pa ana a Zatu+ panali Sekaniya mwana wa Yahazieli. Iye anali ndi amuna 300. 6 Pa ana a Adini+ panali Ebedi mwana wa Yonatani. Iye anali ndi amuna 50. 7 Pa ana a Elamu+ panali Yesaiya mwana wa Ataliya. Iye anali ndi amuna 70. 8 Pa ana a Sefatiya+ panali Zebadiya mwana wa Mikayeli. Iye anali ndi amuna 80. 9 Pa ana a Yowabu panali Obadiya mwana wa Yehiela. Iye anali ndi amuna 218. 10 Pa ana a Bani panali Selomiti mwana wa Yosifiya. Iye anali ndi amuna 160. 11 Pa ana a Bebai+ panali Zekariya mwana wa Bebai. Iye anali ndi amuna 28. 12 Pa ana a Azigadi+ panali Yohanani mwana wa Hakatani. Iye anali ndi amuna 110. 13 Pa ana a Adonikamu,+ omwe anali omaliza, panali anthu awa: Elifeleti, Yeyeli ndi Semaya. Iwo anali ndi amuna 60. 14 Pa ana a Bigivai+ panali Utai ndi Zabudi. Iwo anali ndi amuna 70.
15 Ndinawasonkhanitsa pamtsinje umene umafika ku Ahava+ ndipo tinamanga msasa pamenepo nʼkukhalapo masiku atatu. Koma nditafufuza bwinobwino anthuwo komanso ansembe, sindinapezepo Alevi. 16 Choncho ndinaitanitsa Eliezere, Ariyeli, Semaya, Elinatani, Yaribi, Elinatani, Natani, Zekariya ndi Mesulamu, omwe anali atsogoleri awo. Ndinaitanitsanso Yoyaribi ndi Elinatani, omwe anali alangizi. 17 Kenako ndinawalamula kuti apite kwa Ido yemwe anali mtsogoleri pamalo otchedwa Kasifiya. Ndinawauza mawu oti akauze Ido ndi abale ake, atumiki apakachisi* omwe anali ku Kasifiyako kuti atibweretsere atumiki apanyumba ya Mulungu wathu. 18 Popeza dzanja labwino la Mulungu wathu linkatithandiza, iwo anatibweretsera munthu wanzeru wochokera pakati pa ana a Mali+ mdzukulu wa Levi mwana wa Isiraeli. Dzina lake linali Serebiya+ ndipo anabwera limodzi ndi ana ake komanso abale ake. Onse pamodzi analipo 18. 19 Panalinso Hasabiya, yemwe anali pamodzi ndi Yesaiya wochokera pa ana a Merari,+ abale ake ndi ana awo. Onse pamodzi analipo 20. 20 Kuchokera pa atumiki apakachisi* amene Davide ndi akalonga anawaika kuti azitumikira Alevi, panali atumiki a pakachisi 220. Onsewa anawasankha pochita kuwatchula mayina awo.
21 Kenako ndinalamula kuti tisale kudya tili kumtsinje wa Ahava komweko, kuti tidzichepetse pamaso pa Mulungu wathu nʼkumupempha kuti atitsogolere pa ulendo wathu, pamodzi ndi ana athu ndi katundu wathu yense. 22 Ndinachita manyazi kupempha asilikali kwa mfumu ndi okwera pamahatchi kuti atiteteze kwa adani mʼnjira, chifukwa tinali titauza mfumuyo kuti: “Dzanja labwino la Mulungu wathu limathandiza anthu onse omufunafuna,+ koma amasonyeza mkwiyo ndi mphamvu zake kwa onse omusiya.”+ 23 Choncho tinasala kudya nʼkupempha Mulungu wathu zimenezi ndipo iye anamva pempho lathu.+
24 Tsopano ndaika padera anthu 12 kuchokera pa atsogoleri a ansembe. Mayina awo ndi Serebiya komanso Hasabiya+ pamodzi ndi abale awo 10. 25 Ndiyeno ndinawayezera siliva, golide ndi ziwiya. Zimenezi zinali zopereka zimene mfumu, alangizi ake, akalonga ake ndi Aisiraeli onse amene anali kumeneko anapereka kunyumba ya Mulungu wathu.+ 26 Chotero ndinawayezera nʼkuwapatsa matalente* 650 a siliva, ziwiya 100 zasiliva zokwana matalente awiri, matalente 100 a golide, 27 mbale 20 zingʼonozingʼono zagolide zolowa zokwana madariki* 1,000 ndi ziwiya ziwiri zamkuwa wabwino wonyezimira mofiirira, zamtengo wapatali ngati golide.
28 Kenako ndinawauza kuti: “Inu ndinu oyera kwa Yehova.+ Ziwiyazi ndi zopatulika ndipo siliva komanso golideyu ndi nsembe yaufulu yopita kwa Yehova Mulungu wa makolo anu. 29 Muyangʼanire katunduyu mosamala mpaka atayezedwa pamaso pa atsogoleri a ansembe, atsogoleri a Alevi komanso akalonga a nyumba zamakolo a Aisiraeli ku Yerusalemu,+ mʼzipinda zodyera zapanyumba ya Yehova.” 30 Ansembe ndi Aleviwo analandira siliva ndi golide amene anayezedwayo ndiponso ziwiya zimene zinayezedwazo, kuti apititse zinthuzi ku Yerusalemu kunyumba ya Mulungu wathu.
31 Kenako tinachoka pamtsinje wa Ahava+ pa tsiku la 12 la mwezi woyamba+ kupita ku Yerusalemu. Dzanja la Mulungu wathu linkatithandiza pa ulendowu moti anatipulumutsa kwa adani ndiponso achifwamba mʼnjira. 32 Kenako tinafika ku Yerusalemu+ ndipo tinakhala kumeneko masiku atatu. 33 Pa tsiku la 4 tinayeza siliva, golide ndi ziwiya zija mʼnyumba ya Mulungu wathu.+ Titatero tinapereka zinthuzo kwa Meremoti+ mwana wa Uliya wansembe, yemwe anali limodzi ndi Eliezara mwana wa Pinihasi. Analinso limodzi ndi Yozabadi+ mwana wa Yesuwa ndi Nowadiya mwana wa Binui,+ omwe anali Alevi. 34 Zinthu zonsezo tinaziwerenga nʼkuziyeza, kenako tinalemba kulemera kwake. 35 Anthu amene anali ku ukapolo mʼdziko lina anapereka nsembe zopsereza kwa Mulungu wa Isiraeli. Anapereka ngʼombe zamphongo 12+ za Aisiraeli onse, nkhosa zamphongo 96,+ ana a nkhosa amphongo 77 ndi mbuzi zamphongo 12+ kuti zikhale nsembe yamachimo. Zonsezi anazipereka kuti zikhale nsembe zopsereza kwa Yehova.+
36 Kenako tinapereka malamulo a mfumu+ kwa masatarapi* a mfumu ndi abwanamkubwa a kutsidya lina la Mtsinje.*+ Malamulowo anathandiza anthuwo ndiponso anathandiza panyumba ya Mulungu woona.+